Kumanzele: Banja la Beteli ku Brooklyn linakondwelela Krisimasi komaliza mu 1926; kulamanja: Anthu amaona kuti Mboni za Yehova n’zosiyana ndi anthu ena
CIGAWO 3
Mfundo za Ufumu—Kufunafuna Cilungamo ca Mulungu
YELEKEZELANI kuti mukuyenda pamseu, kenako mukuona aneba anu, ndipo mukupatsana nao moni. Mutatelo, aneba anuwo akukuitanani. Masiku ano, mwakhala mukuona kuti aneba anuwo amakonda kukuyang’anitsitsani mukamayenda pamseu ndi banja lanu. Mutafika pamene anebawo ali, io akunena kuti: “Ndifunseko, n’cifukwa ciani inu mumasiyana ndi anthu ena?” Inu mukuyankha kuti: “N’cifukwa ciani mwafunsa?” Aneba anuwo akuyankha kuti: “Ndifuna kudziŵa ngati ndinu a Mboni. Ndimaona kuti ndinu osiyana kwambili ndi anthu ena onse, ndipo zocita zanu zimasiyana ndi za zipembezo zina. Mwacitsanzo simukondwelela maholide, ndipo simulowelela ndale ndiponso simucita nao nkhondo kapena kusuta fodya. Banja lanu limaoneka kuti limatsatila mfundo za makhalidwe abwino. N’ciani cimene cimakusiyanitsani?”
Inu mudziŵa kuti yankho lake ndi lakuti: Ufumu wa Mulungu ndi umene ukutitsogolela, ndipo Yesu monga Mfumu akupitilizabe kutiyenga. Iye akutithandiza kutsatila mapazi ake n’colinga cakuti tikhale anthu osiyana ndi anthu ena m’dziko loipa lino. M’cigawo cino, tidzaphunzila zimene Ufumu wa Mesiya wakhala ukucita poyenga anthu a Mulungu mwakuuzimu, mwamakhalidwe ndiponso monga gulu, n’colinga cakuti Yehova apatsidwe ulemelelo.