CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | EZEKIELI 32-34
Udindo Waukulu wa Mlonda
Alonda anali kukhala pa mpanda wa mzinda ndi m’nsanja zake kuti azicenjeza anthu za adani amene angabwele. Yehova anasankha Ezekieli kukhala “mlonda wa nyumba ya Isiraeli” wophiphilitsa.
33:7
Ezekieli anacenjeza Isiraeli kuti ciweluzo cidzabwela kwa iwo ngati sadzasiya njila zawo zoipa
Nanga ise timalengeza uthenga wanji wocoka kwa Yehova?
33:9, 14-16
Mwa kucenjeza anthu, Ezekieli anapulumutsa moyo wake ndi wa anthu ena.
N’ciani ciyenela kutituntha kulengeza mwacangu uthenga umene Yehova watipatsa?