CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | MATEYU 1-3
“Ufumu Wakumwamba Wayandikila”
Mavalidwe na maonekedwe cabe a Yohane anali kuonetselatu kuti umoyo wake unali wosalila zambili, na kuti anali wodzipeleka kothelatu pa kucita cifunilo ca Mulungu
Udindo wapadela wa Yohane wokhala kalambula bwalo wa Yesu unaposa utumiki uliwonse umene anacitapo
Umoyo wosalila zambili umatithandiza kucita zoculuka potumikila Mulungu, ndipo timakhala wokhutila. Tingapeputse umoyo wathu mwa . . .
kudziŵa zofunikila kweni-kweni
kupewa kugula zinthu zosafunikila
kupanga bajeti imene tingakwanitse
kugulitsa, kupatsa ena, kapena kutaya zinthu zimene sitiseŵenzetsa
kubweza nkhongole
kucepetsako ma ovataimu pa nchito yakuthupi
Cakudya ca Yohane cinali kuphatikizapo dzombe na uci
Umoyo wosalila zambili udzanithandiza kukwanilitsa colinga canga ca . . .