NYIMBO 72
Tilalikile Coonadi ca Ufumu
Yopulinta
1. Panali nthawi imene
Ise tinali mu mdima.
Yehova ‘natumiza
Kuwala kwa coonadi.
Ndipo ise tinadziŵa
Cifunilo ca Yehova.
Afuna tim’lambile
Na kulengeza za dzina lake.
Tilalika konse-konse—
Mu midzi na mu misewu.
Tigaŵila coonadi
Kwa aliyense wofuna.
Capamodzi tilengeze
Dzina la Atate wathu.
Ndipo tipitilize
Mpaka Yehova ‘tiuze: “Kwatha!”
(Onaninso Yos. 9:9; Yes. 24:15; Yoh. 8:12, 32.)