LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb18 October tsa. 8
  • Akhristu Oona Amadziŵika na Cikondi—Kuteteza Mgwilizano Wathu Wapadela

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Akhristu Oona Amadziŵika na Cikondi—Kuteteza Mgwilizano Wathu Wapadela
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2018
  • Nkhani Zofanana
  • Zonsezi Zinatheka Cifukwa ca Kumwetulila!
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2021
  • Sungani Mgwilizano wa Mpingo
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Mmene Akhristu Enieni Tingawadziŵile
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2018
mwb18 October tsa. 8

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Akhristu Oona Amadziŵika na Cikondi—Kuteteza Mgwilizano Wathu Wapadela

CIFUKWA CAKE N’KOFUNIKA: Usiku wakuti maŵa Yesu aphedwa, anapemphela kuti ophunzila ake “akhale mu umodzi weni-weni.” (Yoh. 17:23) Kuti tikhale ogwilizana, tifunika kuonetsana cikondi cimene “sicisunga zifukwa.”—1 Akor. 13:5.

MMENE TINGACITILE:

  • Tengelani citsanzo ca Yehova mwa kuyang’ana zabwino mwa ena

  • Muzikhululukila ena na mtima wonse

  • Mukakambilana ndipo nkhaniyo yatha, osaiutsanso.—Miy. 17:9

TAMBITSANI VIDIYO YAKUTI “MUZIKONDANA”—MUSAMASUNGE ZIFUKWA, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:

  • M’mbali yoyamba ya vidiyo, kodi Helen anaonetsa bwanji kuti anali ‘kusunga zifukwa’?

  • M’mbali yaciŵili ya vidiyo, kodi Helen anacita ciani kuti agonjetse maganizo oipa na kukhala na maganizo oyenela?

  • Kodi Helen anathandizila bwanji kuti mpingo ukhale wogwilizana?

Alice, Helen, na Susan

N’ndani amene amavulazika kwambili ngati tisunga zifukwa?

CITSANZO CA M’BAIBO COFUNIKA KUCISINKHA-SINKHA: Mtumwi Paulo anayang’anabe pa makhalidwe abwino a Yohane Maliko, olo kuti anam’khumudwitsapo kumbuyoko.—Mac 13:13; 15:37, 38; 2 Tim. 4:11.

DZIFUNSENI KUTI, ‘Ningaonetse bwanji kuti sin’nasungile cakukhosi munthu amene ananikhumudwitsa?’

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani