Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu
NOVEMBER 5-11
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOHANE 20-21
“Kodi Umandikonda Ine Kuposa Izi?”
nwtsty mfundo zounikila pa Yoh. 21:15, 17
Yesu anafunsa Simoni Petulo: Makambilano a Yesu na Petulo amenewa, anacitika patangopita nthawi yocepa kucokela pamene Petulo anakana Yesu katatu. Yesu anafunsa Petulo mafunso atatu pofuna kudziŵa ngati anali kumukondadi. Anamufunsa mpaka “Petulo anamva cisoni.” (Yoh. 21:17) Pa Yoh. 21:15-17, Yohane anaseŵenzetsa mawu aŵili osiyana a Cigiriki akuti: a·ga·paʹo, kutanthauza kukonda, na phi·leʹo, kutanthauza kukonda kwambili. Kaŵili konse, Yesu anafunsa Petulo kuti: “Kodi ine umandikonda?” Pa mafunso onse aŵili, Petulo anayankha Yesu motsimikiza kuti “ndimakukondani kwambili.” Pothela pake, Yesu anam’funsa kuti: “Kodi ine umandikonda kwambili?” Apanso Petulo anayankha motsimikiza kuti amamukonda kwambili. Nthawi iliyonse pamene Petulo anayankha kuti amamukonda, Yesu anatsindika mfundo yakuti cikondico cifunika kusonkhezela Petulo kudyetsa na ‘kuweta’ ophunzila ake mwauzimu. Pa lembali ophunzilawo awachula kuti “ana a nkhosa.” (Yoh. 21:16, 17; 1 Pet. 5:1-3) Yesu analola Petulo kuti atsimikizile za cikondi cake pa iye katatu. Pambuyo pake, anamupatsa udindo wakuti asamalile nkhosa zake. Mwa kucita izi, Yesu anatsimikizila Petulo kuti anamukhululukila olo kuti anamukana katatu.
Kodi umandikonda ine kuposa izi?: Mawu akuti “kuposa izi,” anthu angawamvele mosiyana-siyana. Akatswili ena a Baibo amakamba kuti mawuwa atanthauza kuti, “kodi umandikonda ine kuposa mmene umakondela ophunzila enawa?” kapena “kodi umandikonda ine kuposa mmene ophunzila enawa amandikondela?” Komabe, mawuwa ayenela kuti amatanthauza kuti, “kodi umandikonda kuposa zinthu izi?” kutanthauza nsomba zimene anasodza kapena zinthu zogwilizana na nchito yawo yausodzi. Conco, lingalilo loonekela kwambili pa vesiyi n’lakuti: ‘Kodi umandikonda ine kuposa zinthu zakuthupi? Ngati n’conco, dyetsa ana a nkhosa anga.’ Funso limenelo linali loyenelela tikaganizila zimene Petulo anali atacita kumbuyoko. Olo kuti Petulo anali mmodzi wa ophunzila a Yesu oyambilila (Yoh. 1:35-42), iye sanayambile pamenepo kutsatila Yesu nthawi zonse. M’malomwake, anabwelela ku nchito yake yausodzi. Patapita miyezi ingapo, Yesu anaitana Petulo kuti aleke nchito yake imeneyo kuti akhale ‘msodzi wa anthu.’ (Mat. 4:18-20; Luka 5:1-11) Patapita nthawi yocepa kucokela pamene Yesu anamwalila, Petulo anakamba kuti apita kukapha nsomba, ndipo atumwi ena anamutsatila. (Yoh. 21:2, 3) Conco, zioneka kuti apa Yesu anali kukumbutsa Petulo za kufunika kopanga cosankha cotsimikizika: Kodi adzaika nchito yake yausodzi patsogolo mu umoyo wake, imene inali kuimilidwa na nsomba zambili zimene anagwilazo, kapena adzaika patsogolo nchito yodyetsa ana a nkhosa a Yesu mwauzimu, kapena kuti otsatila ake?—Yoh. 21:4-8.
kacitatu: Petulo anali atakana Mbuye wake katatu. Conco apa Yesu anam’patsa mwayi wakuti atsimikizile katatu zakuti amamukonda. Pamene Petulo anali kuyankha, Yesu anamuuza kuti afunika kuonetsa cikondi cimeneco mwa kuika utumiki wopatulika patsogolo mu umoyo wake. Petulo pamodzi na abale ena audindo, anafunika kudyetsa nkhosa za Khristu, kuzilimbikitsa, na kuziŵeta, kutanthauza otsatila ake okhulupilika. Ngakhale kuti otsatilawo anali odzozedwa, iwo anali kufunikabe kudyetsedwa mwauzimu.—Luka 22:32.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
nwtsty mfundo younikila pa Yoh. 20:17
Usandikangamile: Liwu la Cigiriki lakuti haʹpto·mai lingatanthauze “kugwila” kapena “kugwililila cinthu; kugwila cinthu mosalekeza.” Omasulila ena anamasulila mawu a Yesu amenewa kuti: “Osanigwililila.” Komabe, Yesu sanali kuletsa Mariya Mmagadala kuti asamugwilile. Takamba conco cifukwa azimayi ena amene anamuona ataukitsidwa, sanawaletse “kugwila mapazi ake.” (Mat. 28:9) Cioneka kuti Mariya Mmagadala anaopa kuti Yesu posacedwa apita kumwamba. Cifukwa cakuti Mariya anali kufunitsitsa kukhala na Mbuye wakeyo, anagwila Yesu mwamphamvu, sanamuleke kuti apite. Pofuna kumutsimikizila kuti sanali kupita nthawi yomweyo, Yesu anauza Mariya kuti aleke kumukangamila. M’malomwake, apite kwa ophunzila ake kukalengeza uthenga wakuti iye waukitsidwa.
nwtsty mfundo younikila pa Yoh. 20:28
Mbuyanga ndi Mulungu wanga!: Mawu ake eni-eni ni “Mbuye wa ine ndi Mulungu [ho the·osʹ] wa ine!” Akatswili a Baibo ena amaona kuti amenewa ni mawu ofuula opita kwa Yesu oonetsa kudabwa, koma m’ceni-ceni anali kupita kwa Mulungu, Atate wake. Komabe, ena amakamba kuti mawu a Cigiriki oyambilila aonetsa kuti mawuwa anali kupita kwa Yesu. Ngakhale zili conco, tanthauzo la mawu akuti “Mbuyanga ndi Mulungu wanga,” lifunika kugwilizana na Malemba onse ouzilidwa. Popeza malemba amaonetsa kuti Yesu anatumizila ophunzila ake uthenga wakuti, “Ine ndikukwela kwa Atate wanga ndi Atate wanu, kwa Mulungu wanga ndi Mulungu wanu,” palibe cifukwa comveka cokhulupilila kuti Tomasi anaganiza kuti Yesu ni Mulungu wamphamvuzonse. (Onani mfundo younikila pa Yoh. 20:17.) Ndipo Tomasi anali atadzimvelela yekha Yesu akupemphela kwa “Atate” wake, pamene anamutomola kuti “Mulungu yekhayo amene ali woona.” (Yoh. 17:1-3) Conco, Tomasi ayenela kuti anachula Yesu kuti “Mulungu wanga” pa zifukwa izi: Anali kuona Yesu monga “mulungu,” koma osati Mulungu wamphamvuzonse. (Onani mfundo younikila pa Yoh. 1:1.) Mwinanso iye anachula Yesu mmene atumiki a Mulungu anali kuchulila angelo otumidwa na Yehova, monga mmene Malemba Aciheberi amakambila. Tomasi ayenela kuti anali kuzidziŵa bwino nkhani za m’Baibo zoonetsa anthu, kapena olemba Baibo akuyankha kapena kukamba na mngelo wotumidwa na Mulungu ngati kuti akukamba na Yehova Mulungu. (Gwilizanitsani na Gen. 16:7-11, 13; 18:1-5, 22-33; 32:24-30; Ower. 6:11-15; 13:20-22.) Conco, Tomasi ayenela kuti anatomola Yesu kuti “Mulungu wanga” ali na maganizo amenewa. Iye anali kudziŵa kuti Yesu anali woimilako Mulungu woona komanso womukambilako.
NOVEMBER 12-18
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MACHITIDWE 1-3
“Mzimu Woyela Unatsanulidwa pa Mpingo Wacikhristu”
w86 12/1 peji 29 mapa. 4-5, 7
Zopeleka Zimene Zimasangalatsa Mtima
Pa tsiku loyamba limene mpingo wacikhristu unabadwa m’caka ca 33 C.E., Akhristu okwana 3,000 amene anali atangobatizika kumene anali “kugaŵana zinthu, kudya cakudya komanso kupemphela.” Cifukwa ciani? Kuti alimbitse cikhulupililo cawo mwa ‘kupitiliza kulabadila zimene atumwiwo anali kuphunzitsa.’—Mac. 2:41, 42.
Ayuda na anthu otembenukila ku Ciyuda anapita ku Yerusalemu, kuti akakhaleko pa nthawi ya Cikondwelelo ca Pentekosite cabe. Koma amene analandila Cikhristu anafuna kukhalakobe kuti aphunzile zambili na kulimbitsa cikhulupililo cawo. Cifukwa ca izi, panakhala vuto la cakudya komanso malo ogona. Ena mwa alendowo analibe ndalama zokwanila, koma ena anali na zambili. Conco anasonkhanitsa pamodzi zinthu, na kuyamba kuzigaŵila kwa osoŵa.—Mac. 2:43-47.
Anthu anali kugulitsa minda na nyumba zawo, komanso kugaŵana zinthu mwakufuna kwawo. Panalibe kukakamiza aliyense kugulitsa zinthu zake kapena kupeleka cuma cake ayi. Ndipo olemelawo sanali kugulitsa zinthu zawo zonse cabe kuti alingane na osauka ayi. Anacita zimenezo cifukwa ca mmene zinthu zinakhalila pa nthawiyo kwa okhulupilila anzawo, komanso cifukwa ca cikondi cawo. Anafunanso kucita zonse zotheka pofuna kupititsa patsogolo zinthu za Ufumu.—Yelekezelani 2 Akorinto 8:12-15.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
it-2 peji 61 pala.1
Yesu Khristu
“Mtumiki Wamkulu wa moyo.” Monga njila yotionetsela cisomo ca Atate wake, Khristu Yesu anapeleka moyo wake wangwilo monga nsembe. Izi zinapangitsa kuti zikhale zotheka Khristu na otsatila ake osankhidwa kukalamulila pamodzi kumwamba, komanso kuti anthu adzakhale na moyo wosatha padziko mu Ufumu wake. (Mat. 6:10; Yoh. 3:16; Aef. 1:7; Aheb. 2:5; onani pa mutu wakuti DIPO.) Yesu anakhala “Mtumiki Wamkulu [“Kalonga,” KJ; JB] wa moyo” wa anthu a mitundu yonse. (Mac. 3:15) Mawu a Cigiriki amene anaseŵenzetsa apa atanthauza “mfumu yotsogolela.” Mawu olingana na amenewa anawaseŵenzetsa pokamba za Mose (Mac. 7:27, 35) monga “wolamulila” mu Isiraeli.
cl peji 265 pala. 14
Mulungu “Wokhululukila”
14 Kukhululukila kwa Yehova kukufotokozedwanso pa Machitidwe 3:19 kuti: ‘Cifukwa cake lapani, bwelelani kuti afafanizidwe macimo anu.’ Mawu akuti “afafanizidwe” atembenuzidwa ku mawu acigiriki amene angatanthauze kuti “kupukuta, . . . kufufuta kapena kuwononga.” Malinga n’kunena kwa akatswili ena a Baibulo, mawuŵa amaphiphilitsila kufufuta zimene munthu analemba. Kodi zimenezi zinkatheka bwanji? Inki imene anali kulembela kaŵili-kaŵili m’masiku akale anali kuipanga posakaniza mkala, manthova a mitengo, ndi madzi. Akangotha kulemba ndi inki yoteloyo, munthu ankatha kutenga cinkhupule conyowa n’kufufuta zimene analembazo. Pamenepatu tikuona cithunzi cokongola kwambili ca cifundo ca Yehova. Iye akatikhululukila macimo athu, zimakhala ngati kuti watenga cinkhupule n’kufufuta macimowo.
NOVEMBER 19-25
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MACHITIDWE 4-5
“Anapitiliza kulankhula Mawu a Mulungu Molimba Mtima”
w08 9/1 peji 15, bokosi
Mmene Mawu Anakhalila Malemba Opatulika—
Kulemba M’nthawi ya Atumwi
Kodi Atumwi Anali Osaphunzila?
Olamulila komanso akulu a ku Yerusalemu “ataona mmene Petulo ndi Yohane anali kulankhulila molimba mtima, komanso atazindikila kuti anali anthu osaphunzila ndiponso anthu wamba, anadabwa kwambili.” (Machitidwe 4:13) Kodi atumwi analidi osaphunzila, kapena osadziŵa kulemba na kuŵelenga? Pamfundo imeneyi, buku lina lotanthauzila nkhani za m’Baibulo linati: “Mawu amenewa ndi ofunika kuwamvetsa bwino cifukwa sakutanthauza kuti Petulo [ndi Yohane] sanapite ku sukulu ndipo sankadziŵa kulemba ndi kuŵelenga. Koma amene anayankhula mawuwa ankangosonyeza kuti ankadziona kuti anali apamwamba kuyelekezela ndi atumwiwo.”—The New Interpreter’s Bible.
w08 5/15 peji 30 pala. 6
Mfundo Zazikulu za M’buku la Machitidwe
4:13—Kodi n’cifukwa ciani anthu ananena kuti Petulo ndi Yohane anali osaphunzila? Sikuti iwo anali osaphunzila, koma anali kuchedwa “osaphunzila ndiponso anthu wamba” cifukwa cakuti sanapite ku sukulu za Arabi kukaphunzila zacipembedzo.
it-1 peji 128 pala. 3
Mtumwi
Zocitika mu Mpingo Wacikhristu. Mzimu wa Mulungu umene unatsanulidwa pa atumwi pa Pentekosite unawalimbikitsa ngako. Macaputa 5 oyambilila a m’buku la Machitidwe a Atumwi, aonetsa kuti atumwi analibe mantha ndiponso anali kulengeza molimba mtima uthenga wabwino na kuukitsidwa kwa Yesu, ngakhale kuti anali kuikiwa m’jele, kukwapulidwa, na kuopsezedwa kuti adzaphedwa ndi olamulila. Pambuyo pa Pentekosite m’masiku amenewo, mphamvu ya mzimu woyela inacititsa kuti atumwi atsogolele bwino. Zotulukapo zake zinakhala zakuti mpingo wacikhristu unakula kwambili. (Mac. 2:41; 4:4) Utumiki wawo unayamba kucitika kwambili mu Yerusalemu, kenako unayamba kucitikanso ku Samariya, ndiyeno m’kupita kwa nthawi kulikonse kumene kunali anthu.—Mac. 5:42; 6:7; 8:5-17, 25; 1:8.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
it-1 peji 514 pala. 4
mwala wapakona
Salimo 118:22 imakamba kuti mwala umene omanga anaukana udzakhala “mwala wofunika kwambili wapakona” (Mu Ciheberi ni roʼsh pin·nahʹ). Yesu anagwila mawu amenewa a ulosi, ndipo anakamba kuti iye mwini ndiye “mwala wapakona wofunika kwambili” (Mu Cigiriki ni ke·pha·leʹ go·niʹas, kapena kuti mutu wapakona). (Mat. 21:42; Maliko 12:10, 11; Luka 20:17) Mwala umene umakhala pamwamba kwambili pa cimango umakhala woonekela. Mofananamo, Yesu ni mwala wapamwamba kwambili mu mpingo wacikhristu wa odzozedwa, umene amauyelekezela na kacisi wauzimu. Petulo anaseŵenzetsa Salimo 118:22 pokamba za Khristu. Iye anaonetsa kuti Khristu anali “mwala” umene anthu anaukana, koma umene Mulungu anausankha kuti ukhale mwala wapakona.—Mac. 4:8-12; onaninso 1 Pet. 2:4-7.
w13 3/15 peji 15 pala. 4
Petulo ndi Hananiya Ananama, Kodi Tikuphunzilapo Ciani?
Hananiya ndi mkazi wake anagulitsa munda wawo kuti apeleke ndalama zothandizila anthu amenewa. Hananiya anatenga ndalama za mundawu n’kupita nazo kwa atumwi n’kunena kuti zinali zonse zimene anagulitsila mundawo. Koma limenelitu linali bodza cifukwa iye anali atasunga ndalama zina. Mulungu anathandiza Petulo kudziŵa za bodzali ndipo Petuloyo anauza Hananiya kuti: “Pamenepa sikuti wanamiza anthu ayi, koma Mulungu.” Nthawi yomweyo Hananiya anagwa pansi n’kumwalila. Patatha maola atatu, mkazi wake anafika. Iye sanadziŵe zimene zinacitikila mwamuna wake ndipo nayenso ananama. Zitatele iyenso anagwa n’kufa.
NOVEMBER 26–DECEMBER 2
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MACHITIDWE 6-8
“Mpingo Wacikhristu Watsopano Uyesedwa”
bt peji 41 pala. 17
“Ife Tiyenela Kumvela Mulungu Monga Wolamulila”
Mu mpingo wacikhristu umene unali utangoyamba kumenewo, munayambika vuto lina limene likanausokoneza. Kodi vuto lake linali lotani? Ophunzila ambili amene ankabatizidwa anali ocokela kumadela ena osati ku Yerusalemu ndipo anatsalila kwa kanthawi kuti aphunzile zambili asanabwelele kwawo. Ophunzila a ku Yerusalemu anapeleka ndalama mwakufuna kwawo kuti athandize alendowo kupeza cakudya ndiponso zinthu zina zofunika. (Mac. 2:44-46; 4:34-37) Pa nthawiyi, mu mpingowo munayamba vuto lina limene linafunika kulithetsa mosamala kwambili. Vutoli linayamba cifukwa “akazi amasiye acigiriki anali kunyalanyazidwa pa kagaŵidwe ka cakudya ca tsiku ndi tsiku.” (Mac. 6:1) Koma akazi amasiye aciheberi sankanyalanyazidwa. Apa zikuoneka kuti vuto linali tsankho. Vuto limeneli lingagawanitse mpingo mosavuta poyelekezela ndi mavuto ena.
bt peji 42 pala. 18
“Ife Tiyenela Kumvela Mulungu Monga Wolamulila”
Atumwi, amene anali ngati bungwe lolamulila la mpingo umene unkakula kwambiliwo, anaona kuti sicinali cinthu canzelu kuti iwowo ‘asiye nchito yophunzitsa mawu a Mulungu n’kuyamba kugaŵa cakudya.’ (Mac. 6:2) Conco, pofuna kuthetsa vutoli, iwo anauza ophunzila kuti afufuze amuna okwana 7 “amene ali ndi mzimu komanso nzelu zoculuka,” omwe atumwiwo angaŵaike kuti ayang’anile “nchito yofunikayi.” (Mac. 6:3) Panafunikadi amuna oyenelela cifukwa nchito yake sinali yongogaŵa cakudya koma anafunikanso kuti azisunga ndalama, azigula zinthu ndiponso azilemba ciliconse cokhudza ndalamazo. Amuna onse amene anasankhidwawo anali ndi mayina acigiriki, ndipo zimenezi mwina zinathandiza kuti akazi amasiye odandaula aja asangalale. Ataona zinthu zimene zikuwayeneletsa pa udindowo ndiponso atapemphelela nkhaniyo, atumwiwo anaika amuna 7 amenewo pa udindo woyang’anila “nchito yofunikayi.”
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
bt peji 45 pala. 2
“Sitefano, Anali Wodzazidwa ndi Cisomo Komanso Mphamvu”
Pa nthawiyi, nkhope ya Sitefano inkaoneka modabwitsa kwambili. Oweluzawo atamuyang’ana, anaona kuti nkhope yake inkaoneka ngati “nkhope ya mngelo.” (Mac. 6:15) Angelo amapeleka uthenga wocokela kwa Yehova Mulungu, ndipo n’cifukwa cake sacita mantha, satekeseka ndipo ndi amtendele. Umu ndi mmene Sitefano analili ndipo ngakhalenso oweluza amene ankadana naye kwambiliwo anaona zimenezo. N’cifukwa ciani iye sanatekeseke?
bt peji 58 pala. 16
Kulengeza “Uthenga Wabwino Wonena za Yesu”
Akhristu masiku ano ali ndi mwayi wogwila nawo nchito imene Filipo ankagwila. Kaŵili-kaŵili, iwo amauza anthu uthenga wa Ufumu ngakhale pamene sali mu ulaliki. Mwacitsanzo, amacita zimenezi akakhala pa ulendo. Akakumana ndi munthu wacidwi, nthawi zambili zimakhala zoonekelatu kuti zimenezi sizinacitike mwa mwayi. Iwo amadziŵa kuti zinthu ngati zimenezi ziyenela kucitika cifukwa Baibulo limanena momveka bwino kuti angelo akutsogolela nchito yolalikila n’colinga coti uthengawu ufike kwa anthu a “fuko lililonse, cinenelo ciliconse, ndi mtundu uliwonse.” (Chiv. 14:6) Yesu ananenelatu kuti angelo adzatitsogolela pa nchito yathu yolalikila. Mufanizo lake la tiligu ndi namsongole, Yesu ananena kuti m’nthawi yokolola, kapena kuti mapeto a nthawi ino, amene adzagwile ntchito yokololayi “ndi angelo.” Iye ananenanso kuti angelo amenewa “adzacotsa mu ufumu wake zinthu zonse zopunthwitsa ndiponso anthu osamvela malamulo.” (Mat. 13:37-41) Pa nthawi yomweyi, angelowo adzasonkhanitsa anthu amene adzalamulile mu Ufumu wa kumwamba. Kenako, adzasonkhanitsanso “khamu lalikulu” la anthu a “nkhosa zina,” amene Yehova akufuna kuwakokela m’gulu lake.—Chiv. 7:9; Yoh. 6: 44, 65; 10:16.