UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Kunola Luso Lathu Mu Ulaliki—Kuthandiza Anthu a “Maganizo Abwino” Kukhala Ophunzila
CIFUKWA CAKE N’KOFUNIKA: Yehova amapangitsa mbewu za coonadi kukula m’mitima ya anthu amene ali na “maganizo abwino,” kuti ‘akapeze moyo wosatha.’ (Mac. 13:48; 1 Akor. 3:7) Tikakhala mu ulaliki, timagwila nchito pamodzi na Mulungu mwa kulunjika maganizo athu pa anthu amene amacitapo kanthu pa zimene aphunzila. (1 Akor. 9:26) Ophunzila Baibo afunika kudziŵa kuti ubatizo wacikhristu ni wofunika kuti akapulumuke. (1 Pet. 3:21) Tingawathandize kukhala ophunzila a Yesu mwa kuwathandiza kuti apange masinthidwe mu umoyo wawo, azilalikila na kuphunzitsa, ndiponso kuti adzipatulile kwa Yehova.—Mat. 28:19, 20.
MMENE TINGACITILE:
Kumbutsani ophunzila Baibo kuti mumaphunzila nawo n’colinga cakuti ‘adziŵe’ Yehova na kum’kondweletsa.—Yoh. 17:3
Athandizeni kupita patsogolo mwauzimu mwa kugonjetsa zopinga, monga zizoloŵezi zoipa komanso kuyanjana na anthu oipa
Asanabatizike muziŵalimbikitsa. Akabatizika muziŵalimbikitsabe.—Mac. 14:22
TAMBITSANI VIDIYO YAKUTI YEHOVA MULUNGU ADZAKUTHANDIZANI, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AYA:
N’ciani cingapangitse munthu kuyopa kudzipatulila na kubatizika?
Kodi akulu angawathandize bwanji ophunzila Baibo kupita patsogolo mwauzimu?
Kodi lemba la Yesaya 41:10 litiphunzitsa ciani za Yehova?
Ni makhalidwe ati amene angatithandize kutumikila Yehova movomelezeka, ngakhale kuti ndise opanda ungwilo?
Kodi timagwila bwanji nchito na Yehova popanga ophunzila?