NYIMBO 70
Funa-funani Oyenelela
Yopulinta
1. Yesu analalikila mwakhama;
Anaphunzitsa co’nadi.
Anali kufufuza oyenela,
Kuti amvetsele uthenga.
Mwakuŵapatsa moni eninyumba,
Angamasuke na kumvela.
Koma ngati akana kumvetsela
Musaŵatsutse, muŵaleke.
2. Onse amene akulandilani
Amalandilanso Yesu.
Iwo adzapeza moyo wosatha
Ngati amvetsela uthenga.
Yehova adzakuuzani zonse
Zofunika kuti mukambe.
Mau anu akakhala okoma
Ofatsa adzakumvelani.
(Onaninso Mac. 13:48; 16:14; Akol. 4:6.)