LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w14 6/1 masa. 30-31
  • Kodi Pali Ciyembekezo Cotani Ponena za Makolo Anga Akale?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Pali Ciyembekezo Cotani Ponena za Makolo Anga Akale?
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • MUNTHU AMAFUNIKILA KUBATIZIKA KUTI AKAPULUMUKE
  • CIYEMBEKEZO CA M’BAIBULO
  • PAMENE OSALUNGAMA ADZAUKITSIDWA
  • “MULUNGU ALIBE TSANKHO”
  • Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2022
  • Akufa Adzauka Ndithu—Sitikaika Konse!
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2020
  • “Udzakhala Ndi Ine m’Paradaiso”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2022
  • Kodi Dzina Lanu Lilimo “M’buku la moyo”?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2022
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
w14 6/1 masa. 30-31

Pali Ciyembekezo Cotani Ponena za Makolo Anga Akale?

PA NTHAWI ina kale, nyuzipepala ya ku Korea inali ndi mutu wa nkhani wocititsa cidwi wakuti: “Kodi ‘Shim Cheong Wabwino’ Amene Sanali Kudziŵa Zilizonse za Yesu, Anapita ku Helo?”—The Chosun Ilbo.

Mutu wa nkhani umenewu unakhumudwitsa ena cifukwa m’nthano ya ku Korea, Shim Cheong ndi mtsikana wokondedwa amene wodzipeleka pa kuthandiza atate ake osaona. Kwa zaka zambili, iye wakhala wotamandika kwambili. Ndipo, kwa anthu a ku Korea, Shim Cheong ndi citsanzo cabwino ca mwana wodzipeleka.

Ambili amaona kuti kunena munthu wa conco kuti adzalandila cilango m’helo, cabe cifukwa cakuti sanali Mkristu wobatizika, n’kupanda cikondi, ndipo n’kokhumudwitsa. Anthu amaganizila kuti nkhani ya m’nthano imeneyi inacitika kale kwambili uthenga wonena za Kristu usanafike ku mudzi kwa mtsikanayu.

M’nyuzipepalayi, mkulu wacipembedzo wina anam’funsa ngati anthu amene anafa asanaphunzile za Yesu ali m’moto ku helo. Poyankha iye anati, “Sitingadziŵe, koma timangoganiza kuti mwina Mulungu Amawasamalila anthu amenewa.”

MUNTHU AMAFUNIKILA KUBATIZIKA KUTI AKAPULUMUKE

Buku lina linati, “Ubatizo ndi wofunika kuti munthu akapulumuke. Kristu mwini wake anati, ngati wina sanabadwenso ndi madzi ndi Mzimu Woyela, munthuyo sadzaloŵa mu Ufumu wa Mulungu.” Mwa ici, ena amaganiza kuti anthu amene anafa asanabatizike amakaponyedwa m’moto ku helo, kapena kuti amazunzidwa mwanjila ina.

Komabe, pali anthu ambili amene amaona kuti ciphunzitso cimeneci si coona. Anthu ambili anamwalila asanadziŵe coonadi ca m’Baibulo. Kodi anthuwo akuzunzidwa kwamuyaya? Nanga Baibulo limati ciani pa nkhani imeneyi?

CIYEMBEKEZO CA M’BAIBULO

Kukamba zoona, Baibulo limaonetsa kuti Mulungu saona anthu osadziŵa cifunilo cake kuti ndi osafunika. Lemba la Machitidwe 17:30 limatiuza kuti: “Mulungu analekelela nthawi ya kusadziŵa koteloko.” Cotelo, kodi Baibulo limanena kuti anthu amene anafa asanadziŵe Mulungu ali ndi ciyembekezo cotani?

Zimene Yesu anauza mmodzi wa ocita zoipa amene anapacikidwa pamodzi naye, zingatithandize kupeza yankho. Munthuyo anauza Yesu kuti: “Mukandikumbukile mukakaloŵa mu ufumu wanu.” Kodi Yesu anayankha kuti ciani? Anati: “Ndithu ndikukuuza lelo, Iwe udzakhala ndi ine m’Paladaiso.”—Luka 23:39-43.

Kodi Yesu pokamba zimenezo anali kulonjeza munthuyo kuti adzapita kumwamba? Iyai. Sizikanatheka kuti munthuyo akaloŵe kumwamba cifukwa ‘sanabadwenso’ m’madzi ndi mu mzimu. (Yohane 3:3-6) Cimene Yesu anali kulonjeza wocita zoipayo n’cakuti adzakhalanso ndi moyo, m’Paladaiso. Munthuyo pokhala Myuda, mwacionekele anali kudziŵa za Paladaiso wa pa dziko lapansi wochedwa munda wa Edeni, wochulidwa m’Baibulo. (Genesis 2:8) Lonjezo la Yesu linapatsa munthuyo ciyembekezo cotsimikizika cakuti adzaukitsidwa m’Paladaiso pa dziko lapansi latsopano.

Ndipo, Baibulo limalonjeza kuti kudzakhala “kuuka kwa olungama ndi osalungama omwe.” (Machitidwe 24:15) Anthu “osalungama” ndi aja amene sanali kucita zimene Mulungu amafuna cifukwa cosadziŵa cifunilo cake. Conco, Yesu adzaukitsa wocita zoipa wosalungama uja amene anakamba naye, pamodzi ndi anthu ena mamiliyoni, ngakhale mabiliyoni, amene anafa osadziŵa cifunilo Mulungu. Ndiyeno m’Paladaiso pa dziko lapansi, anthu amenewo adzaphunzitsidwa cifunilo ca Mulungu. Ndipo adzakhala ndi mwai woonetsa ngati amam’konda Mulungu mwa kumvela malamulo ake.

PAMENE OSALUNGAMA ADZAUKITSIDWA

“Osalungama” akadzaukitsidwa, kodi adzaweluzidwa malinga ndi zimene anali kucita akali moyo? Iyai. Pa Aroma 6:7 pamati: “Munthu amene wafa wamasuka ku ucimo wake.” Kukamba kwina, osalungama akamwalila ndiye kuti alipila macimo ao. Conco, panthawi ya ciweluzo, adzaweluzidwa malinga ndi nchito zao pambuyo pa kuukitsidwa, osati zimene anali kucita asanafe. Kodi io adzadalitsika motani?

Pambuyo pa ciukililo, osalungama adzakhala ndi mwai wophunzila malamulo a Mulungu amene adzadziŵika pamene mipukutu yophiphilitsa idzatsegulidwa. Pamenepo adzaweluzidwa “mogwilizana ndi nchito zao,” kuona ngati anali kumvela malamulo a Mulungu kapena ai. (Chivumbulutso 20:12, 13) Kwa osalungama ambili, umenewu udzakhala mwai woyamba, osati waciŵili, wophunzila cifunilo ca Mulungu ndi kucicita kuti akapeze moyo wosatha pa dziko lapansi.

Mfundo ya m’Baibulo imeneyi yathandiza anthu ambili kuyambanso kukhulupilila Mulungu. Yeong Sug ndi mmodzi wa io. Iye anakula monga Mkatolika wolimbikila, ndipo acibale ake ena anali ansembe. Pofuna kukhala sisitele wa Cikatolika, iye anapita kukakhala ku nyumba ya masisitele. M’kupita kwa nthawi, anacokako cifukwa cokhumudwa ndi zocitika za kumeneko. Cifukwa cina n’cakuti, sanavomeleze ciphunzitso ca moto wa ku helo, cifukwa anaona kuti kuzunza anthu koteloko n’kupanda cilungamo ndi cikondi.

Ndiyeno, Mboni ya Yehova inasonyeza Yeong Sug mau a m’Baibulo awa: “Pakuti amoyo amadziŵa kuti adzafa, koma akufa sadziŵa ciliconse. Iwo salandilanso malipilo alionse.” (Mlaliki 9:5) Mboniyo inam’thandiza kudziŵa kuti makolo ake akale amene anamwalila sakuzunzika m’moto wa ku helo, koma ali gone m’manda akuyembekeza kuukitsidwa.

Atadziŵa kuti anthu ambili sanamvepo coonadi ca m’Baibulo, Yeong Sug analabadila mau Yesu a pa Mateyu 24:14 akuti: “Uthenga wabwino uwu wa Ufumu udzalalikilidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse kenako mapeto adzafika.” Mlongo ameneyu tsopano amalalikila uthenga wabwino ndi kuuzako ena ciyembekezo cabwino ca m’Baibulo.

“MULUNGU ALIBE TSANKHO”

Baibulo limati: “Mulungu alibe tsankho. Iye amalandila munthu wocokela mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kucita cilungamo.” (Machitidwe 10:34, 35) Ici ndico cilungamo cimene tonse tingayembekezele kwa Mulungu, amene “amakonda cilungamo ndi ciweluzo.”—Salimo 33:5.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani