NYIMBO 77
Kuwala m’Dziko la Mdima
Yopulinta
(2 Akorinto 4:6)
1. Kuwala kukuunika,
m’Dziko la mdimali.
Tiuza anthu uthenga,
Wa ciyembekezo.
(KOLASI)
Uthenga wa M’lungu
Umawala kwambili,
m’Dziko la mdimali—
Umapatsa anthu,
Onse ciyembekezo—
Mwa Mulungu.
2. Ogona agalamuke,
Si nthawi yogona.
Auke, tiŵalimbitse.
Tiŵapemphelele.
(KOLASI)
Uthenga wa M’lungu
Umawala kwambili,
m’Dziko la mdimali—
Umapatsa anthu,
Onse ciyembekezo—
Mwa Mulungu.
(Onaninso Yoh. 3:19; 8:12; Aroma 13:11, 12; 1 Pet. 2:9.)