Nyimbo 143
Kuwala m’Dziko la Mdima
Yopulinta
(2 Akorinto 4:6)
Kuwala kukuunika,
m’Dziko la mdimali.
Tiuza anthu uthenga
wa ciyembekezo.
(KOLASI)
Uthenga wa M’lungu
Umawala kwambili,
m’Dziko la mdimali—
Umapatsa anthu,
Onse ciyembekezo—
Mwa Mulungu.
Ogona agalamuke
Si nthawi yogona.
Auke, tiwalimbitse.
Tiŵapemphelele.
(KOLASI)
Uthenga wa M’lungu
Umawala kwambili,
m’Dziko la mdimali—
Umapatsa anthu,
Onse ciyembekezo—
Mwa Mulungu.
(Onaninso Yoh. 3:19; 8:12; Aroma 13:11, 12; 1 Pet. 2:9.)