Nyimbo 151
Ana a Mulungu Adzaonekela
Yopulinta
Nthawi yafika Yehova
Aonetse onse.
Ana ake osankhidwa
na mzimu woyela.
(KOLASI)
Ana a Yehova M’lungu
Adzaonekela.
Pamodzi na Yesu Mfumu
Adzalamulila.
Otsalila odzozedwa
Adzaitanidwa.
Adzasonkhana pamodzi,
na Khristu kumwamba.
(KOLASI)
Ana a Yehova M’lungu
Adzaonekela.
Pamodzi na Yesu Mfumu
Adzalamulila.
(BILIJI)
Capamodzi adzaononga
onse oipa.
Na cimwemwe, kwa muyaya,
adzalamulila.
(KOLASI)
Ana a Yehova M’lungu
Adzaonekela.
Pamodzi na Yesu Mfumu
Adzalamulila.
(Onaninso Dan. 2:34, 35; 2 Akor. 4:18.)