NYIMBO 140
Moyo Wosatha Watheka!
Yopulinta
1. Mokondwa timaona
Mu maganizo mwathu,
Paradai’so yafika,
Sitivutikanso.
(KOLASI)
Imba mokondwela!
Tamanda Yehova.
Sangalala
Cifukwa ca moyo wosatha.
2. Matenda, ukalamba,
Yehova adzacotsa.
Imfa nayo si’liko
Kulibe cisoni.
(KOLASI)
Imba mokondwela!
Tamanda Yehova.
Sangalala
Cifukwa ca moyo wosatha.
3. Tonsefe, panthawiyo,
Tidzatamanda M’lungu.
Nthawi zonse, mokondwa,
Tidzamuimbila.
(KOLASI)
Imba mokondwela!
Tamanda Yehova.
Sangalala
Cifukwa ca moyo wosatha.
(Onaninso Yobu 33:25; Sal. 72:7; Chiv. 21:4.)