Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu
SEPTEMBER 2-8
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | AHEBERI 7-8
“Wansembe Mpaka Muyaya Monga mwa Unsembe wa Melekizedeki”
it-2 366
Melekizedeki
Melekizedeki anali Mfumu ya ku Salemu wakale komanso “wansembe wa Mulungu Wam’mwambamwamba,” Yehova. (Gen. 14:18, 22) Iye ndiye wansembe woyamba kuchulidwa m’Malemba. Anakhala pa udindowo ca kuciyambi kwa m’ma 1933 B.C.E. Iye anali mfumu ya ku Salemu. Dzina la mzindawu litanthauza ‘mtendele.’ Mtumwi Paulo anachula Melekizedeki kuti “Mfumu Yamtendele,” ndipo mogwilizana na dzina lake, anamuchula kuti “Mfumu Yacilungamo.” (Aheb. 7:1, 2) Zioneka kuti mzinda wakale wa Salemu unali likulu la mzinda umene unadzakhala Yerusalemu. Ndipo dzina lakuti Salemu linaphatikidwa ku dzina lakuti Yerusalemu, mzinda umene nthawi zina anali kuukamba kuti “Salemu.”—Sal. 76:2.
Abulamu (Abulahamu) kholo la Aisiraeli atagonjetsa Kedorelaomere, limodzi ndi mafumu amene anali naye, anapita ku Cigwa ca Save kapena kuti “Cigwa ca mfumu.” Kumeneko, Melekizedeki “anabweletsa mkate ndi vinyo. Iyeyu anali wansembe wa Mulungu Wam’mwambamwamba. Kenako anadalitsa Abulamu kuti: ‘Mulungu Wam’mwambamwamba adalitse Abulamu, iye amene anapanga kumwamba ndi dziko lapansi. Ndipo adalitsike Mulungu Wam’mwambamwamba, amene wapeleka okupondeleza m’manja mwako!’ ” Pamenepo, Abulahamu anapatsa mfumu ndi wansembe “cakhumi ca zilizonse” pa “zinthu zabwino kwambili zimene anafunkha” ku nkhondo atagonjetsa mafumu amene anagwilizana kuwaukila.—Gen. 14:17-20; Aheb. 7:4.
it-2 367¶4
Melekizedeki
Kodi Melekizedeki ‘analibe tsiku limene anabadwa komanso limene anamwalila’ m’lingalilo lanji?
Paulo anakamba mfundo yocititsa cidwi yokamba za Melekizedeki pamene anati: “Popeza kuti analibe bambo, analibe mayi, analibe mzele wa mibadwo ya makolo ndipo tsiku limene anabadwa komanso limene anamwalila silikudziŵika, koma anamucititsa kuti afanane ndi Mwana wa Mulungu, iye ndi wansembe kwamuyaya.” (Aheb. 7:3) Mofanana na anthu onse, Melekizedeki anacita kubadwa ndipo anamwalila. Ngakhale n’conco, dzina la atate ake kapena amayi ake silinachulidwe, ndipo makolo ake na mbadwa zake sadziŵika. Malemba sakambapo ciliconse cokhudza tsiku limene anabadwa komanso limene anamwalila. Mwa ici, Melekizedeki anali woyenela kucitila cithunzi Yesu Khristu, amene unsembe wake sudzatha. Melekizedeki sanakhale wansembe cifukwa coloŵa m’malo mwa munthu wina, ndipo analibe womuloŵa m’malo. N’cimodzi-modzinso Khristu. Iye sanacite kuloŵa m’malo mkulu wa ansembe wofanana naye. Baibo imaonetsa kuti palibe aliyense adzamuloŵa m’malo. Kuwonjezela apo, ngakhale kuti Yesu anabadwila m’fuko la Yuda ndiponso mu mzele wacifumu wa Davide, makolo ake aumunthu analibe gawo pa unsembe wake. Iye sanakhale wansembe komanso mfumu cifukwa ca makolo ake aumunthu. Anakhala na maudindo amenewa cifukwa ca lumbilo limene Yehova anapanga kwa iye.
it-2 366
Melekizedeki
Unsembe wa Khristu unacitilidwa cithunzi. Ulosi wocititsa cidwi wokamba za Mesiya pa lumbilo limene Yehova anapanga kwa ‘Mbuye’ wa Davide, ni wakuti: “Iwe ndiwe wansembe mpaka kale-kale, monga mwa unsembe wa Melekizedeki!” (Sal. 110:1, 4) Salimo louzilidwa limeneli linathandiza Aheberi kudziŵa kuti Mesiya wolonjezedwayo, ndiye anali kudzakhala wansembe komanso mfumu. M’kalata yake yopita kwa Aheberi, mtumwi Paulo anacotsa zikayikilo zonse pa cizindikilo ca woloseledwayo, inde za Yesu kuti “wakhala mkulu wa ansembe mpaka muyaya monga mwa unsembe wa Melekizedeki.”—Aheb. 6:20; 5:10; onani pa mutu wakuti CIPANGANO.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
w00 8/15 14 ¶11
Nsembe Zimene Zinakondweletsa Mulungu
11 “Mkulu wa ansembe aliyense aikidwa kupeleka mitulo, ndiponso nsembe,” anatelo mtumwi Paulo. (Aheberi 8:3) Onani kuti Paulo anagaŵa m’magulu aŵili zopeleka za mkulu wa ansembe wa Isiraeli wakale, ndizo “mitulo” ndi “nsembe,” kapena kuti ‘nsembe cifukwa ca macimo.’ (Aheberi 5:1) Kaŵili-kaŵili anthu amapatsa anzawo mitulo posonyeza cikondi ndi kuyamikila, ndiponso kuti akulitse ubwenzi wawo, kuti ayanjidwe, kapena kulandilidwa. (Genesis 32:20; Miyambo 18:16) Mofananamo, tingaone kuti zopeleka zambili zochulidwa m’Cilamulo zinali ngati “mitulo” kwa Mulungu pofunafuna kuti awalandile ndi kuwayanja. Kucimwila Cilamulo kunafuna kubwezela, ndipo kuti akonze zolakwazo, ‘nsembe cifukwa ca macimo’ zinali kupelekedwa. Pentatuke, maka-maka mabuku a Ekisodo, Levitiko, ndi Numeri, ili ndi nkhani zoculuka zokhudza nsembe ndi zopeleka zosiyana-siyana. Pamene kuli kwakuti kungakhale kovuta kwambili kuti tiloŵetse m’mutu ndi kumakumbukila tsatane-tsatane wake yense, mfundo zina zikulu-zikulu zokhudza nsembe zosiyana-siyanazo n’zofunika kuti tizilingalile.
it-1 523 ¶5
Cipangano
Kodi pangano la Cilamulo linaleka bwanji kugwila “nchito”?
Komabe, tingakambe kuti pangano la Cilamulo linaleka kugwila “nchito” pamene Mulungu kupitila mwa mneneli Yeremiya analengeza kuti padzakhala pangano latsopano. (Yer 31:31-34; Aheb. 8:13) Mu 33 C.E., pangano la Cilamulo linafafanizidwa pa maziko a imfa ya Khristu pa mtengo wozunzikilapo. (Akol. 2:14) Ndiyeno pangano latsopano linaloŵa m’malo pangano la Cilamuloco.—Aheb. 7:12; 9:15; Mac. 2:1-4.
SEPTEMBER 9-15
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | AHEBERI 9-10
“Mthunzi wa Zinthu Zabwino Zimene
Zikubwela”
it-1 862 ¶1
Cikhululukilo
Malinga na Cilamulo ca Mulungu, cimene cinapelekedwa kwa mtundu wa Aisiraeli, ngati munthu wacimwila Mulungu kapena mnzake, ndiye afuna kuti chimo lake likhululukidwe, coyamba anali kufunika kukonza zimene walakwitsazo mogwilizana na Cilamulo. Pambuyo pake, anali kupeleka nsembe ya magazi kwa Yehova. (Lev. 5:5–6:7) Paulo anakambanso mfundoyi kuti: “Inde, pafupi-fupi zinthu zonse zimayeletsedwa ndi magazi malinga ndi Cilamulo, ndipo popanda kukhetsa magazi anthu sangakhululukidwe macimo awo.” (Aheb. 9:22) Komabe, kupeleka nsembe za magazi a nyama sikunali kucotsa ucimo na kupangitsa munthu kukhala na cikumbumtima coyela. (Aheb. 10:1-4; 9:9, 13, 14) Mosiyana na zimenezi, pangano latsopano loloseledwa, linatheketsa kuti anthu azikhululukidwa m’ceni-ceni pa maziko a nsembe
ya dipo la Yesu Khristu. (Yer. 31:33, 34; Mat. 26:28;
1 Akor. 11:25; Aef. 1:7) Ngakhale pamene anali pano pa dziko lapansi, Yesu anaonetsa kuti ali na mphamvu zokhululukila macimo mwa kucilitsa munthu wakufa ziwalo.—Mat. 9:2-7.
cf 183 ¶4
“Pitiliza Kunditsatila”
4 Yesu atabwelela kumwamba, Malemba safotokoza ciliconse cokhudza mmene anamulandilila ndiponso cisangalalo cimene cinalipo atakumananso ndi Atate wake. Komabe, Baibo inanenelatu zimene zidzacitike Yesu akadzabwelela kumwamba. Ndipotu Ayuda anali kucita mwambo wina-wake wopatulika caka ciliconse, kwa zaka zoposa 1,500. Tsiku limodzi pa caka, mkulu wa ansembe anali kuloŵa m’Malo Oyela Koposa a kacisi kukawaza magazi a nsembe za Tsiku la Mwambo Wophimba Macimo pafupi ndi likasa la pangano. Pa tsiku limenelo, mkulu wa ansembe anali kuimila Mesiya. Ayuda anali kucita mwambo umenewo kuti macimo awo akhululukidwe. Koma Yesu atabwelela kumwamba, anakwanilitsa colinga ca mwambo umenewo kamodzi kokha, cifukwa anapeleka nsembe imene ingathandize anthu onse kuti macimo awo akhululukidwe. Iye atapita kumwamba, kumalo oyela kuposa ena aliwonse, anakaonekela pamaso pa Yehova ndi kupeleka moyo wake wangwilo kwa Atate wakewo kuti ukhale nsembe ya dipo. (Aheberi 9:11, 12, 24) Kodi Yehova analandila nsembeyo?
it-2 602-603
Ungwilo
Ungwilo Kupitila m’Cilamulo ca Mose. Cilamulo cimene cinapelekedwa kwa Aisiraeli kupitila mwa Mose, cinaphatikizapo zinthu monga kukhazikitsa wansembe komanso kupeleka nsembe zosiyana-siyana za nyama. Mogwilizana na mawu ouzilidwa a mtumwi Paulo, ngakhale kuti Cilamulo cinacokela kwa Mulungu komanso cinali ca ungwilo, cilamuloco, unsembe wake, komanso nsembe zopelekedwa, sizinabweletse ungwilo kwa anthu amene anali kucitsatila. (Aheb. 7:11, 19; 10:1) M’malo motimasula ku ucimo na imfa, Cilamuloco cinapangitsa kuti ucimo uonekele poyela. (Aroma 3:20; 7:7-13) Ngakhale n’conco, makonzedwe opatulika amenewa anakwanilitsa colinga ca Mulungu. Cilamulo cinali ngati “m’tsogoleli,” amene anatsogolela anthu kwa Khristu na kucitila cithunzi “zinthu zabwino zimene zikubwela.” (Agal. 3:19-25; Aheb. 10:1) Conco, pamene Paulo anakamba kuti “Cilamulo sicinathe kucita zimenezi pokhala cofooka cifukwa ca thupi” (Aroma 8:3), mwacionekele anatanthauza kuti mkulu wa ansembe waciyuda (amene anali kusankhidwa mwa lamulo kuti aziyang’anila makonzedwe a kapelekedwe ka nsembe, komanso amene anali kuloŵa ku Malo Oyela Koposa pa Tsiku La Mwambo Wophimba Macimo na nsembe za magazi), sakanakwanitsa “kupulumutsa kwathunthu” anthu amene anali kuwatumikila, mogwilizana na zimene Aheberi 7:11, 18-28 imafotokoza. Kupeleka nsembe kupitila mwa wansembe Aroni, kunali kupangitsa munthu kukhala na kaimidwe kabwino pamaso pa Mulungu. Komabe, nsembeyo sinali kucotselatu kapena kumasula munthu ku ucimo. Mtumwi Paulo anaonetsa zimenezi pokamba kuti nsembe zophimba macimo, sizinakwanitse kuthandiza anthu “kukhala angwilo,” m’cikumbumtima cawo. (Aheb. 10:1-4; yelekezelani na Aheb. 9:9) Mkulu wa ansembe sakanakwanitsa kupeleka mtengo wa dipo umene unali kufunika kuti tiwomboledwe ku ucimo. Unsembe wa Khristu na nsembe yake ndizo zinatheketsa zimenezi.—Aheb. 9:14; 10:12-22.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
w92 3/1 31 ¶4-6
Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga
Paulo ananena kuti imfa inafunika kuti mapangano pakati pa Mulungu ndi anthu agwile nchito. Mwacitsanzo, tinene pangano Lacilamulo. Mose anali nkhoswe yake, wocititsa kuvomelezana kumeneku pakati pa Mulungu ndi Isiraeli wakuthupi. Motelo Mose anacita mbali yofunika ndipo anali munthu amene anacita ndi Aisiraeli pamene anali kuloŵa m’panganolo. Motelo Mose anaonedwa monga wocititsa pangano waumunthu wa pangano Lacilamulo limene Yehova anayamba. Koma kodi Mose anayenela kutaya mwazi wamoyo wake kuti pangano Lacilamulolo liyambe kugwila nchito? Ayi. Mmalomwake nyama zinapelekedwa, mwazi wawo ukutenga malo a mwazi wa Mose.—Aheberi 9:18-22.
Nanga bwanji ponena za pangano latsopano pakati pa Yehova ndi mtundu wa Isiraeli wauzimu? Yesu Khristu anali ndi thayo lalikulu la umkhala pakati, Unkhoswe pakati pa Yehova ndi Isiraeli wauzimu. Ngakhale kuti Yehova anayambitsa pangano limeneli, linazikidwa pa Yesu Khristu. Pambali pokhala Nkhoswe yake, Yesu anacita mwacindunji m’thupi ndi amene akakhala oyamba kuloŵa m’panganolo. (Luka 22:20, 28, 29) Ndiponso, anayeneletsedwa kupeleka nsembe yofunika kuti panganolo ligwile nchito. Nsembe imeneyo sinali ya nyama koma ya moyo wangwilo waumunthu. Conco Paulo anakhoza kuchula Khristu monga wocititsa pangano waumunthu wa pangano latsopano. Pamene ‘Khristu analoŵa . . . m’mwamba momwe, kuwonekela tsopano pamaso pa Mulungu cifukwa ca ife,’ pangano latsopano linayamba kugwila nchito.—Aheberi 9:12-14, 24.
Polankhula za Mose ndi Yesu monga ocititsa mapangano aumunthu, Paulo sanali kunena kuti pali amene anayambitsa mapangano pakati pa aŵiliwo, amene kwenikweni anapangidwa ndi Mulungu. M’malomwake, anthu aŵiliwo analoŵetsedwamo kwambili monga nkhoswe m’kucititsa mapangano amenewo. Ndipo pazocitika zonse ziŵilizo, panafunikiladi imfa—nyama m’malo mwa Mose, ndi Yesu akupeleka nsembe mwazi wamoyo wakewo m’malo mwa awo okhala m’pangano latsopano.
it-1 249-250
Ubatizo
Luka anakamba kuti Yesu anapemphela pa nthawi ya ubatizo wake. (Luka 3:21) Komanso, wolemba kalata yopita kwa Aheberi anakamba kuti pamene Yesu Khristu anabwela “m’dziko” (osati pa nthawi imene iye anabadwa cifukwa sakanatha kuŵelenga na kukamba mawu amenewa, koma ni pa nthawi imene iye anadzipeleka kuti abatizike na kuyamba utumiki wake) anakamba mogwilizana na mawu a pa Salimo 40:6-8 (LXX) akuti: “Nsembe ndiponso zopeleka simunazifune, koma munandikonzela thupi. . . . Taonani! Ine ndabwela (mumpukutu munalembedwa za ine) kudzacita cifunilo canu, inu Mulungu wanga.” (Aheb. 10:5-9) Yesu anabadwila mu mtundu wa ciyuda, mtundu umene unali pa pangano na Mulungu. Panganolo linali kuchedwa, pangano la Cilamulo. (Eks. 19:5-8; Agal. 4:4) Conco, pamene Yesu anadzipeleka kuti abatizidwe na Yohane, anali kale pa ubale wapadela na Yehova Mulungu. Yesu panthawiyo anacita cinthu cina cofunika kwambili kuposa zimene cilamulo cinali kufuna kuti acite. Anadzipeleka kwa Atate wake Yehova kuti acite “cifunilo” ca Atate wakeyo, mwa kupeleka nsembe thupi lake ‘lokonzedwa’ na kuthetsa nsembe za nyama zimene zinali kupelekedwa malinga na Cilamulo. Mtumwi Paulo anati: “Mwa ‘cifunilo’ cimeneco, tayeletsedwa kudzela m’thupi la Yesu Khristu lopelekedwa nsembe kamodzi kokha.” (Aheb. 10:10) Cifunilo ca Atate kwa Yesu cinaphatikizapo nchito zogwilizana na Ufumu, ndipo Yesu anadzipeleka kucita utumiki umenewu. (Luka 4:43; 17:20, 21) Yehova analandila na kuvomeleza kudzipeleka kwa Mwana wake. Conco anamudzoza na mzimu woyela na kumuuza kuti: “Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa, ndimakondwela nawe.”—Maliko 1:9-11; Luka 3:21-23; Mat. 3:13-17.
SEPTEMBER 16-22
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | AHEBERI 11
“Cifukwa Cake Cikhulupililo N’cofunika”
Khalani na Cikhulupililo m’Malonjezo a Yehova
6 Lemba la Aheberi 11:1 (ŵelengani) limafotokoza bwino zimene cikhulupililo cimatanthauza. Cikhulupililo cimazikika pa zinthu ziŵili zimene sitingaone: (1) “zinthu zoyembekezeledwa.” Izi ziphatikizapo zinthu zimene Mulungu anatilonjeza kuti zidzacitika kutsogolo, koma zikalibe kucitika. Zinthu monga kucotsedwapo kwa zoipa zonse ndi kubwela kwa dziko latsopano. (2) “Zinthu zeni-zeni, ngakhale kuti n’zosaoneka.” Apa, liwu la Cigiriki lomasulidwa kuti “umboni wooneka,” limatanthauza “umboni wokhutilitsa” wa zinthu zeni-zeni zosaoneka. Zinthuzo zimaphatikizapo kukhalako kwa Yehova Mulungu, Yesu Khristu, angelo, komanso zocitika za Ufumu wa kumwamba. (Aheb. 11:3) Kodi tingaonetse bwanji kuti ciyembekezo cathu n’camoyo, ndi kuti timakhulupililadi zinthu zosaoneka zochulidwa m’Mawu a Mulungu? Tingaonetse mwa zokamba ndi zocita zathu. Apo ayi, ndiye kuti cikhulupililo cathu sicokwanila.
“Amapeleka Mphoto kwa Anthu Omufuna-funa Ndi Mtima Wonse”
Kodi pamafunika ciani kuti munthu asangalatse Yehova? Paulo ananena kuti: “Popanda cikhulupililo n’zosatheka kukondweletsa Mulungu.” Onani kuti Paulo sananene kuti popanda cikhulupililo n’zovuta kukondweletsa Mulungu. M’malomwake, iye ananena kuti n’zosatheka kukondweletsa Mulungu popanda chikhulupililo. M’mawu ena tingati, cikhulupililo n’cofunika kwambili kuti munthu akondweletse Mulungu.
Koma kodi tiyenela kukhala ndi cikhulupililo cotani kuti tikondweletse Yehova? Pakufunika zinthu ziŵili. Coyamba, tiyenela “kukhulupilila kuti iye alikodi.” Baibo ina inamasulila mawu amenewa kuti tiyenela “kukhulupilila kuti iye ndi weni-weni.” N’zosatheka kusangalatsa Mulungu ngati sitikhulupilila kuti iyeyo alipo. Komabe cikhulupililo ceni-ceni cimafuna zambili, cifukwa ngakhale ziŵanda nazonso, zimakhulupilila kuti Yehova alipo. (Yakobo 2:19) Cikhulupililo cakuti Mulungu alipo, ciyenela kutilimbikitsa kucita zomukondweletsa. Zimenezi zingasonyeze kuti cikhulupililo cathu ndi camphamvu ndipo cikhulupililo coteleci cimakondweletsa Mulungu.—Yakobo 2:20, 26.
Caciŵili, ‘tiyenela kukhulupilila kuti,’ Mulungu “amapeleka mphoto.” Munthu amene ali ndi cikhulupililo ceni-ceni amadziŵa kuti zimene akucita posangalatsa Mulungu, sizidzapita pacabe. (1 Akorinto 15:58) Tiyenela kudziŵa kuti sitingasangalatse Yehova ngati timakayikila kuti adzatipatsa mphoto. (Yakobo 1:17; 1 Petulo 5:7) Munthu yemwe amanena kuti Mulungu satisamalila, satiyamikila ndiponso kuti ndi woumila, sadziŵa Mulungu amene Baibo imanena.
Kodi Yehova amapeleka mphoto kwa ndani? Paulo ananena kuti amapeleka mphoto “kwa anthu omufuna-funa ndi mtima wonse.” Buku lina lomasulila Baibo inanena kuti mawu acigiriki amene anawamasulila kuti “omufuna-funa ndi mtima wonse” satanthauza ‘kungomufuna-funa’ cabe, koma amatanthauza “kulambila Mulungu mwakhama.” Buku linanso limafotokoza kuti velebu lacigiriki limeneli, limanena za kucita zinthu mobweleza-bweleza kapena mwakhama. Conco, Yehova amapeleka mphoto kwa anthu amene amamulambila ndi mtima wonse.—Mateyu 22:37.
Limbitsani Cikhulupililo Canu pa Zimene
Muyembekezela
10 M’caputa 11 ca Aheberi, mtumwi Paulo anachula mayeselo amene atumiki a Mulungu ambili osachulidwa maina anapilila. Mwacitsanzo, mtumwiyu anakamba za akazi acikhulupililo amene ana awo anafa. Pambuyo pake anawalandilanso pamene anaukitsidwa. Ndiyeno, anakambanso za anthu amene “sanalole kusiya cikhulupililo cawo kuti amasulidwe. Iwo anacita zimenezi kuti adzauke kwa akufa, komwe ndi kuuka kwabwino kwambili.” (Aheb. 11:35) Ngakhale kuti sindife otsimikiza za anthu amene Paulo anali kukamba, ena monga Naboti na Zekariya, anaphedwa mwa kuponyedwa miyala cifukwa comvela Mulungu ndi kucita cifunilo cake. (1 Maf. 21:3, 15; 2 Mbiri 24:20, 21) Danieli na anzake anali na ufulu wosankha kusiya cikhulupililo cawo kuti amasulidwe. Koma cikhulupililo cawo mu mphamvu za Mulungu, cinawacititsa ‘kutseka mikango pakamwa’ ndi ‘kugonjetsa mphamvu ya moto, titelo kukamba kwake.’—Aheb. 11:33, 34; Dan. 3:16-18, 20, 28; 6:13, 16, 21-23.
11 Cifukwa ca cikhulupililo cawo, aneneli monga Mikaya na Yeremiya ‘analandila mayeselo awo mwa kutonzedwa . . . ndi [kuikidwa] m’ndende.’ Enanso monga Eliya, “anayenda uku ndi uku m’zipululu, m’mapili, m’mapanga, ndi m’maenje a dziko lapansi.” Onsewa anapilila cifukwa anali na “ciyembekezo cotsimikizika ca zinthu zoyembekezeledwa.”—Aheb. 11:1, 36-38;
1 Maf. 18:13; 22:24-27; Yer. 20:1, 2; 28:10, 11; 32:2.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
it-1 804 ¶5
Cikhulupililo
Zitsanzo Zakale za Anthu a Cikhulupililo. Aliyense amene anachulidwa na Paulo kuti ali mu “mtambo wa mboni waukulu,” (Aheb. 12:1) anali na maziko a cikhulupililo. Mwacitsanzo, Abele mosakayikila anali kudziŵa za lonjezo la Mulungu lakuti “mbewu” idzaphwanya mutu wa “njoka.” Ndipo anaona kukwanilitsika kwa mawu a ciweluzo ca Yehova kwa makolo ake m’munda wa Edeni. Kunja kwa Edeni, Adamu na banja lake anali kudya cakudya kucokela m’thukuta la nkhope zawo, cifukwa nthaka inali itatembeleledwa. Ndipo minga na zitsamba zolasa zinayamba kumela m’nthaka. N’kutheka kuti Abele anaona kuti Hava anali kukhumba mwamuna wake, ndipo anaonanso kuti Adamu anali kulamulila mkazi wake. N’zosakayikitsa kuti amayi ake anakambapo za ululu wa pobeleka. Komanso, pa khomo loloŵela ku munda wa Edeni panali kulonda Akerubi, ndipo panali lupanga loyaka moto. (Gen. 3:14-19, 24) Zonsezi zinali “umboni wooneka,” ndipo zinathandiza Abele kukhala wotsimikiza kuti cipulumutso cidzabwela kupitila mu mbewu yolonjezedwa. Conco, cifukwa ca cikhulupililo, Abele “anapeleka kwa Mulungu” nsembe ya mtengo wapatali kuposa ya Kaini.—Aheb. 11:1, 4.
‘Mulungu Anakondwela Naye’
Nanga Baibo itanthauza ciani pamene ikamba kuti Inoki “anasamutsidwa kuti asafe mozunzika”? Yehova ayenela kuti anacotsa moyo wa Inoki pang’no-pang’ono kuti asaphedwe mwankhanza ndi adani ake. Koma izi zikalibe kucitika, “Mulungu anamucitila umboni kuti akukondwela naye.” Kodi Mulungu anacita bwanji zimenezo? Inoki atatsala pang’ono kufa, mwina Mulungu anamuonetsa masomphenya a dziko lapansi la paradaiso. Inoki anagona mu imfa ali na umboni umenewu wakuti Yehova akukondwela naye. Polemba za Inoki komanso amuna ndi akazi ena okhulupilika, mtumwi Paulo anati: “Onsewa anafa ali ndi cikhulupililo.” (Aheberi 11:13) N’kutheka kuti pambuyo pake, adani a Inoki anafuna-funa mtembo wake, koma ‘sanaupeze kwina kulikonse.’ Mwina Yehova anabisa mtembo wa Inoki n’colinga cakuti anthu asauseŵenzetse pocilikiza kulambila konama, kapena kuugwilitsila nchito m’njila zina zolakwika.
SEPTEMBER 23-29
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | AHEBERI 12-13
“Cilango—Umboni wakuti Yehova
Amatikonda”
w12 3/15 29 ¶18
Musamayang’ane “Zinthu za M’mbuyo”
18 Uphungu wopweteka. Nthawi zina zikhoza kumatiŵaŵa tikaganizila uphungu umene tinapatsidwa. Zimenezi zimakhala zopweteka komanso zofooketsa ndipo zikhoza kucititsa munthu kutaya mtima. (Aheb. 12:5) Nthawi zina munthu ‘angapeputse’ uphungu poukana kapena ‘kutaya mtima’ atauvomeleza. Zimenezi zimacititsa kuti uphunguwo usatithandize. Koma ndi bwino kutsatila mawu a Solomo akuti: “Gwila malangizo, usawataye. Uwasunge bwino cifukwa iwo ndiwo moyo wako.” (Miy. 4:13) Mofanana ndi dalaivala amene amatsatila zikwangwani za pamsewu, tiyeni tizilandila uphungu ndi kuugwilitsa nchito n’kupitiliza kuyang’ana kutsogolo.—Miy. 4:26, 27; ŵelengani Aheberi 12:12, 13.
“Mukamapemphela Muzinena Kuti, ‘Atate’ ”
Bambo wacikondi amalangiza ana ake cifukwa amafuna kuti anawo akadzakula adzakhale anthu odalilika. (Aefeso 6:4) Bambo woteleyu amaonetsetsa kuti ana ake akutsatila malangizo komabe sacita zimenezi mwankhanza. Mofanana ndi bambo wotele, nthawi zina Atate wathu wakumwamba angaone kuti tikufunika kulangizidwa. Koma nthawi zonse Mulungu amatilangiza mwacikondi ndipo saticitila nkhanza. Mofanana ndi Atate wake, Yesu sanali wankhanza, ngakhale pamene ophunzila ake anali kucedwa kuyamba kutsatila malangizo amene anawapatsa.—Mateyu 20:20-28; Luka 22:24-30.
“Mvelani Malangizo Kuti Mukhale Anzelu”
18 N’zoona kuti cilango cimakhala coŵaŵa. Koma coŵaŵa ngako ni mavuto amene tingakumane nawo cifukwa cokana cilango kapena uphungu. (Aheb. 12:11) Ganizilani zitsanzo ziŵili izi: Ca Kaini na ca Mfumu Zedekiya. Pamene Kaini anakwiya kwambili n’kufuna kupha Abele, Mulungu anam’patsa uphungu Kaini. Anati: “N’cifukwa ciani wapsa mtima conco, ndipo nkhope yako yagwelanji? Ukasintha n’kucita cabwino, sindikuyanja kodi? Koma ngati susintha kuti ucite cabwino, ucimo wamyata pakhomo kukudikilila, ndipo ukulakalaka kukudya. Kodi iweyo suugonjetsa?” (Gen. 4:6, 7) Koma Kaini sanamvele. Ndipo ucimo unamugonjetsa. Kaini anadzibweletsela mavuto aakulu amene akanatha kuwapewa. (Gen. 4:11, 12) Ha! Akanalandila cilango ca Mulungu, sembe sanakumane na mavuto amenewo.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
w11 9/15 17-18 ¶11
Tiyeni Tithamange Mpikisano Mopilila
11 Sikuti ‘mtambo wa mboni waukuluwu’ ndi anthu omwe anali kungoonelela anthu akuthamanga ayi. Koma iwo anali kuthamanga nawo mu mpikisanowo mpaka kukamaliza. Ngakhale kuti iwo anamwalila, mophiphilitsila angatengedwe kukhala akatswili amene akuthandiza ena omwe angoyamba kumene kuthamanga. Ndiye tangoyelekezelani mmene wothamanga watsopano angamvele poona kuti anthu akumucemelela ndipo amene akumucemelelawo ndi akatswili. Iye akhoza kuyesetsa kwambili kuti apambane. Mtambo wa mboniwu umasonyeza kuti ngakhale titakumana ndi mavuto ambili, tikhoza kupambana n’kulandila mphoto. Conco kuganizila kwambili citsanzo ca “mtambo wa mboni” kukanathandiza Akhristu aciheberi kukhala olimba mtima ndiponso ‘kuthamanga mpikisano mopilila.’ Ifenso tikamaganizila citsanzo cimeneci tikhoza kucita cimodzi-modzi.
w89 12/15 22 ¶10
Pelekani Nsembe Zimene Zimakondweletsa Yehova
10 Cotelo Aheberi anafunikila kupewa ‘kutengedwa ndi maphunzitso amitundu-mitundu ndi acilendo’ a Ayuda. (Agalatiya 5:1-6) Simwaziphunzitso zotelozo koma ‘mwa cisomo ca Mulungu ndi pamene mtima ungalimbitsidwe’ kotelo kuti akhalebe okhazikika m’coonadi. Mwacionekele ena anatsutsa ponena za zakudya ndi nsembe, popeza kuti Paulo ananena kuti mtima sunalimbitsidwe “ndi zakudya, zimene iwo anazitsata sanapindula nazo.” Mapindu auzimu amatuluka ku kudzipeleka kwaumulungu ndi kuyamikila dipo, osati kucokela ku kudela nkhaŵa kopambanitsa ponena za kudya zakudya zinazake ndi kusunga masiku ena. (Aroma 14:5-9) Ndiponso, nsembe ya Khristu inapangitsa nsembe za Alevi kusagwila nchito.—Aheberi 9:9-14; 10:5-10.
SEPTEMBER 30–OCTOBER 6
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YAKOBO 1-2
“Zimene Zimabweletsa Ucimo na Imfa”
g17.4 14
Mayeselo
Munthu amayesedwa akakopeka ndi zinazake maka-maka zikakhala zolakwika. Mwacitsanzo, tiyelekezele kuti muli mu shopu ndiye mwaona cinthu cinacake ndipo mwakopeka naco. Kenako mukuyamba kuganiza kuti mukhoza kuba cinthuco cifukwa palibe amene akukuonani. Koma mukuona kuti cikumbumtima canu cikukuletsani. Ndiyeno mukucotsa maganizo olakwikawo. Pamenepa tinganene kuti mwapambana mayeselo.
ZIMENE BAIBO IMANENA
Munthu akakumana ndi mayeselo sizitanthauza kuti ndi woipa. Baibo imasonyeza kuti anthu onse amakumana ndi mayeselo. (1 Akorinto 10:13) Koma cofunika kwambili ndi zimene timacita tikakumana ndi mayeselowo. Anthu ena amaganizila kwambili za zinthu zolakwika ndipo kenako amazicita. Pamene ena akayamba kuganiza zinthu zolakwika amazicotsa mwamsanga m’maganizo mwawo.
“Munthu aliyense amayesedwa mwa kukopedwa ndi kukodwa m’cilakolako cake.”—Yakobo 1:14.
g17.4 14
Mayeselo
Baibo imafotokoza zimene zimacitika kuti munthu afike pocita zoipa. Lemba la Yakobo 1:15 limati: “Cilakolako [colakwika] cikatenga pakati, cimabala chimo.” Mwacidule tingati munthu akamaganizila kwambili zinthu zolakwika, amafika poti sangathe kudziletsa mpaka atacita zoipazo. Komabe ngakhale zili conco, n’zotheka kupewa zilakolako zoipa.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
it-2 253-254
Kuunika
Yehova ni “Atate wa zounikila zonse zakuthambo.” (Yak. 1:17) Iye “ndiye Wopeleka dzuŵa kuti liziwala masana, woikila mwezi malamulo, wopeleka nyenyezi kuti ziziwala usiku.” (Yer. 31:35) Kuwonjezela apo, iye ndiye Gwelo la kuwala konse kwauzimu. (2 Akor. 4:6) Malamulo ake, zigamulo, na mawu ake, ni zounikila kwa anthu amene amalola kuti ziwatsogolele. (Sal. 43:3; 119:105; Miy. 6:23; Yes. 51:4) Wamasalimo anati: “Cifukwa ca kuwala kocokela kwa inu, tikuona kuwala.” (Sal. 36:9; yelekezelani na Sal 27:1; 43:3) Monga mmene kuwala kwa dzuŵa kumawonjezekela kucokela m’bandakuca mpaka “tsiku litakhazikika,” nayonso njila ya olungama, mounikilidwa na nzelu za Mulungu, imawonjezeleka kuwala. (Miy. 4:18) Munthu akamatsatila njila ya Yehova ndiye kuti akuyenda m’kuwala kwake. (Yes. 2:3-5) Kumbali ina, ngati munthu ayang’ana zinthu na maganizo olakwika kapena ali na zolinga zoipa, ndiye kuti ali mu mdima waukulu wauzimu. Mogwilizana na zimenezi Yesu anati: “Ngati diso lako lili loipa, thupi lako lonse lidzacita mdima. Conco ngati kuwala kumene kuli mwa iwe ndiko mdima, ndiye kuti mdimawo ndi wandiweyani!”—Mat. 6:23; Deut. 15:9; 28:54-57; Miy. 28:22; 2 Pet. 2:14.
it-2 222 ¶4
Cilamulo
“Lamulo Lacifumu.” “Lamulo lacifumu” ni lapamwamba komanso lofunika pa malamulo ena amene mfumu imakhala nawo pogwilizanitsa anthu. (Yak. 2:8) Colinga ca pangano la Cilamulo ni kulimbikitsa khalidwe lacikondi. Ndipo lamulo lakuti “uzikonda mnzako mmene umadzikondela wekha” (lamulo lacifumu), linali laciŵili pa malamulo amene Cilamulo conse cinazikidwapo, kuphatikizapo zolemba za Aneneli. (Mat. 22:37-40) Ngakhale kuti Akhristu sali pansi pa pangano la Cilamulo, iwo amagonjela lamulo la Mfumu Yehova na Mwana wake, Mfumu Yesu Khristu mogwilizana na pangano latsopano.