PHUNZILO 1
Mawu Oyamba Ogwila Mtima
Machitidwe 17:22
ZOFUNIKILA: Mawu anu oyamba afunika kukopa cidwi, kuchula nkhani yanu, komanso kuonetsa mmene nkhaniyo ikuwakhudzila omvela anu.
MOCITILA:
Kukopa cidwi. Sankhani funso, mfundo, cocitika, kapena nkhani ya pa nyuzi imene omvela anu angacite nayo cidwi.
Chulani nkhani yanu. Onetsetsani kuti mawu anu oyamba akumveketsa bwino nkhani yanu kwa omvela, na colinga ca ulaliki wanu.
Onetsani cifukwa cake nkhaniyo ni yofunika. Kambani zinthu zothandizadi kwa omvela anu. Afunika kumvetsa bwino-bwino mmene nkhaniyo ingawathandizile.