PHUNZILO 3
Gwilitsilani Nchito Mafunso
Mateyu 16:13-16
ZOFUNIKILA: Mafunso aluso angakuthandizeni kuwakopa cidwi omvela anu, kulingalila nawo, na kugogomeza mfundo zofunika.
MOCITILA:
Kukopa cidwi na kucipitiliza. Funsani mafunso osafuna yankho othandiza munthu kuganiza.
Athandizeni kumvetsa nkhaniyo. Athandizeni kutsatila mfundo zanu mwa kuwafunsa mafunso angapo owathandiza kuona mfundo.
Gogomezani mfundo zofunika. Funsani funso locititsa cidwi kuti mumveketse lingalilo lofunika. Pambuyo pokambilana kapena kufotokoza mfundo yofunika, kapenanso potsiliza makambilano anu, funsani mafunso obweleza.