NYIMBO 85
Tilandilane Wina Ndi Mnzake
Yopulinta
1. Inu nonse takulandilani,
Mwabwela kuti muphunzile,
Mau a M’lungu, na njila zake.
Tiyamike Yehova potiitana.
2. Tiyamika Atate Yehova,
Tili na ‘bale acikondi.
Nthawi zonse amatilandila,
Tilandile obwela kudzasonkhana.
3. Yehova afuna anthu onse,
Aphunzile co’nadi cake.
Mwa Mwana wake atiitana.
Tilandile onse mocoka mu’mtima.
(Onaninso Yoh. 6:44; Afil. 2:29; Chiv. 22:17.)