LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • th phunzilo 7 tsa. 10
  • Kukamba Zoona Zokha-Zokha Komanso Zokhutilitsa

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kukamba Zoona Zokha-Zokha Komanso Zokhutilitsa
  • Citani Khama pa Kuŵelenga na Kuphunzitsa
  • Nkhani Zofanana
  • Kachulidwe ka Malemba Koyenela
    Citani Khama pa Kuŵelenga na Kuphunzitsa
  • Kumveketsa Phindu ya Nkhani
    Citani Khama pa Kuŵelenga na Kuphunzitsa
  • Gwilitsilani Nchito Mafunso
    Citani Khama pa Kuŵelenga na Kuphunzitsa
  • Yesetsani Kuwafika pa Mtima Omvela
    Citani Khama pa Kuŵelenga na Kuphunzitsa
Onaninso Zina
Citani Khama pa Kuŵelenga na Kuphunzitsa
th phunzilo 7 tsa. 10

PHUNZILO 7

Kukamba Zoona Zokha-Zokha Komanso Zokhutilitsa

Lemba losagwila mawu

Luka 1:3

ZOFUNIKILA: Muzitenga mfundo zanu ku magwelo odalilika kuti omvela anu azikhutila nazo.

MOCITILA:

  • Pezani magwelo odalilika. Mfundo zanu zizitsamila pa Mawu a Mulungu. Ngati n’kotheka, ŵelengani mwacindunji. Ngati muchula mfundo yokhudza za sayansi, nkhani ya pa nyuzi, kapena cocitika cina cake, kapenanso umboni wina wake, tsimikizilani pasadakhale kuti magwelo anu ni odalilika komanso ni azoona.

  • Gwilitsilani nchito magwelowo moyenelela. Fotokozani malemba mogwilizana na nkhani yake, uthenga wonse wa m’Baibo, komanso na zofalitsa za “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu.” (Mat. 24:45) Ngati mugwilitsila nchito umboni wocokela ku magwelo akunja, useŵenzetseni mogwilizana na magwelo ake, komanso colinga ca wolemba wake.

    Tumalangizo tothandizila

    Osakamba mfundo kapena ziŵelengelo mowonjezela. Samalani pokamba, kuti “anthu ena” asakhale “anthu ambili,” “nthawi zina” zisakhale “nthawi zonse,” komanso “mwinamwake” isakhale “mwacionekele.”

  • Kambilanani umboni. Mukaŵelenga lemba kapena kuchula gwelo linalake, funsani mafunso mwaluso, kapena chulani citsanzo cothandiza omvela kuona mfundo yanu.

MU ULALIKI

Pokonzekela ulaliki, ganizilani mafunso amene mungafunsidwe, ndipo fufuzani za mmene mungawayankhile. Ngati womvela wafunsa funso koma mulibe yankho, m’pempheni kuti mukabwelenso pambuyo pokafufuza yankho.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani