-
Ndandanda ya Mlungu wa March 25Utimiki Wathu wa Ufumu—2013 | March
-
-
Ndandanda ya Mlungu wa March 25
MLUNGU WA MARCH 25
Nyimbo 76 ndi Pemphelo
□ Phunzilo la Baibo la Mpingo:
bt mutu 20 ndime 16-20 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibo: Luka 4–6 (Mph. 10)
Na. 1: Luka 4:22-39 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Kodi Mitundu ya Anthu Inacokela Kuti?—rs tsa 234 ndime 2-tsa 235 ndime 1 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Pali Umboni Wotani Wosonyeza Kuti Yesu Anaukitsidwa?—1 Akor. 15:3-7 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 111
Mph. 5: Kuyambitsa Maphunzilo a Baibo pa Ciŵelu Coyamba mu April. Mwa kugwilitsila nchito ulaliki wacitsanzo uli patsamba 8, onetsani mmene tingayambitsile phunzilo pa Ciŵelu coyamba mu April. Limbikitsani onse kutengako mbali.
Mph. 25: “Mmene mungagwilitsile nchito kabuku kakuti Uthenga Wabwino Wocokela kwa Mulungu!” Mafunso ndi mayankho. Pokambilana ndime 6, citani zitsanzo ziŵili.
Nyimbo 97 ndi Pemphelo
-
-
Zocitika Zokhudza UlalikiUtimiki Wathu wa Ufumu—2013 | March
-
-
Zocitika Zokhudza Ulaliki
-
-
Mmene Tingagwilitsile Nchito Kabuku Kakuti Uthenga Wabwino Wocokela kwa Mulungu!Utimiki Wathu wa Ufumu—2013 | March
-
-
Mmene Tingagwilitsile Nchito Kabuku Kakuti Uthenga Wabwino Wocokela kwa Mulungu!
Kabuku Katsopano Kanalembedwa Kuti Katithandize Kupanga Maulendo Obwelelako ndi Kuyambitsa Maphunzilo a Baibo
1. Kodi ndi kabuku katsopano kati kamene kanatuluka pa Msonkhano wa Cigawo wakuti “Tetezani Mtima Wanu!” kamene kanalembedwa kuti katithandize kupanga maulendo obwelelako ndi kuyambitsa maphunzilo a Baibo?
1 Pa Msonkhano wa Cigawo wakuti “Tetezani Mtima Wanu!” Tinasangalala kulandila kabuku katsopano kotithandiza kupanga maulendo obwelelako ndi kuyambitsa maphunzilo a Baibo. Kabuku kakuti Uthenga Wabwino Wocokela Kwa Mulungu kaloŵa m’malo kabuku kakuti Mulungu Amafunanji? Mofanana ndi kabuku kakuti Mulungu Amafunanji?, kabuku kameneka kali ndi nkhani zifupi-zifupi. Kaamba ka zimenezi, kabukuka kadzatithandiza kuti tizitha kuyambitsa maphunzilo a Baibo acidule panyumba paulendo woyamba. Mosiyana ndi kabuku ka Mulungu Amafunanji, kamene kanali kufotokoza zimene munthu ayenela kucita kuti akhale Mkristu, zimene zimakhala zovuta kuzivomeleza kwa munthu amene wangoyamba kuphunzila Baibo, kabuku katsopanoka kakamba kwambili za uthenga wabwino wopezeka m’Baibo—Mac. 15:35.
2. N’cifukwa ciani kabuku ka Uthenga Wabwino kanalembedwa?
2 N’cifukwa ciani kabuku kameneka kanalembedwa? Abale padziko lapansi akhala akufunsa ngati pangakhale cofalitsa cofeŵa cimene cingakope anthu kuyamba kuphunzila coonadi, m’buku la Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni, limene timagwilitsila nchito potsogoza maphunzilo a Baibo. Anthu amene amacita mantha kuphunzila Baibo mwa kugwilitsila nchito buku, kaŵili-kaŵili amakhala ofunitsitsa kuliphunzila mwa kugwilitsila nchito kabuku. Kuonjezela pamenepa, kabuku ndi kosavuta kutembenuza m’zinenelo zambili.
3. Kodi kabukuka n’kosiyana bwanji ndi zofalitsa zina zophunzitsila Baibo?
3 Mmene Kanalembedwela: Zofalitsa zathu zambili zophunzitsila Baibo, zimalembedwa m’njila yakuti munthu angaziŵelenga payekha ndi kumvetsetsa coonadi popanda wom’thandiza. Kabukuka ndi kosiyanako. Kanalembedwa m’njila yakuti munthu amene aphunzila Baibo aziphunzitsidwa ndi wina wake. Conco, pamene tikagaŵila kwa munthu, tiyenela kuŵelenga ndi kukambilana naye ndime imodzi kapena ziŵili. Ndime zake ndi zazifupi, cakuti mungazikambilane ndi munthu mwacidule panyumba kapena kunchito. Ngakhale kuti ndi bwino kuyambila m’phunzilo 1, mungayambe kuphunzila phunzilo lililonse m’kabukuka.
4. Kodi kabukuka kamatithandiza bwanji kuphunzitsa mwacindunji kucokela m’Baibo?
4 M’zofalitsa zathu zambili, mayankho a mafunso amapezeka m’ndime. Komabe, mayankho ambili m’kabukuka amapezeka m’Baibo. Anthu ambili amafuna kuphunzila kucokela m’Baibo osati m’zofalitsa zathu. Conco, pafupi-fupi malemba onse sanagwidwe mau. Koma malembawo ayenela kuŵelengedwa m’Baibo. Zimenezi zimathandiza ophunzila Baibo kudziŵa kuti zimene akuphunzila zicokela kwa Mulungu.—Yes. 54:13.
5. N’cifukwa ciani n’kofunika kuti mphunzitsi azikonzekela bwino phunzilo lililonse?
5 Kabukuka sikafotokoza malemba onse. N’cifukwa ciani? Colinga n’cofuna kulimbikitsa wophunzila Baibo kuti azifunsa mafunso ndi kuti mphunzitsi azikhala ndi mpata wogwilitsila nchito luso lake la kuphunzitsa. Conco, n’kofunika kwambili kukonzekela bwino phunzilo lililonse. Koma muyenela kupewa kukamba zambili pocititsa phunzilo. N’zoona kuti timakonda kufotokoza Malemba, koma zimakhala zothandiza kwambili ngati tipatsa mpata wophunzila Baibo kuti afotokoze maganizo ake pa Malemba. Tikamagwilitsila nchito mafunso mwaluso, tingam’thandize kuti amvetsetse tanthauzo la lemba lililonse.—Mac. 17:2.
-