LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb20 April tsa. 8
  • Kodi Cofunika Koposa kwa Ine N’ciani?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Cofunika Koposa kwa Ine N’ciani?
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2020
  • Nkhani Zofanana
  • Acicepele, Kodi Mumaika Zolinga Zauzimu Patsogolo?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2018
  • Khalani na Zolinga Zauzimu Kuti Mulemekeze Mlengi Wanu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2004
  • “N’cifukwa Ciyani Akhristu Ayenela Kuyesetsa Kuwonjezela Utumiki Wawo?”
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2022
  • Pitanibe Patsogolo Kuuzimu
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2020
mwb20 April tsa. 8
Yakobo akugwebana na mngelo.

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Kodi Cofunika Koposa kwa Ine N’ciani?

Yakobo anagwebana na mngelo kuti alandile cinthu cofunika kwambili, cimene ni dalitso la Yehova. (Gen. 32:24-31; Hoseya 12:3, 4) Nanga bwanji ife? Kodi timayesetsa kumvela Yehova kuti tilandile dalitso lake? Mwacitsanzo, kodi tingasankhe citi pakati pa kupita ku misonkhano ya mpingo kapena kukagwila nchito ya ovataimu? Ngati siticita kaso kupatsa Yehova nthawi yathu, mphamvu, na cuma cathu, iyenso adzatikhuthulila ‘madalitso oti tidzasoŵa powalandilila.’ (Mal. 3:10) Adzatitsogolela na kutiteteza ndipo adzatisamalila pa zosoŵa zathu.—Mat. 6:33; Aheb. 13:5

TAMBITSANI VIDIYO YAKUTI SUMIKANI MAGANIZO PA ZOLINGA ZAUZIMU, PAMBUYO PAKE, YANKHANI MAFUNSO AYA:

  • Mlongo amene ni mpainiya akugwila nchito yomasulila cinenelo ca manja.

    Kodi mlongo anayesedwa bwanji na cinthu cimene amakonda?

  • Mlongo mmodzi-modziyo agwila nchito mpaka usiku mu ofesi.

    Kodi nchito yathu ingakhale bwanji ciyeso kwa ise?

  • Timoteyo aŵelenga mpukutu usiku ataimilila capafupi na windo.

    N’cifukwa ciani Timoteyo anafunika kupitiliza kudziikila zolinga ngakhale pamene anali wokhwima kuuzimu?—1 Tim. 4:16

  • Mpainiya na mlongo wina akupatsa moni Phunzilo la Baibo pamene afika panyumba pake kuti aphunzile naye Baibo.

    Kodi cofunika koposa mu umoyo wanu n’ciani?

    Tingaonetse bwanji nchito “yofunika ngako” kwa ise?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani