PHUNZILO 8
Mafanizo Ophunzitsadi Kanthu
Mateyu 13:34, 35
ZOFUNIKILA: Phunzitsani mwaluso pogwilitsila nchito mafanizo osavuta kumva kwa omvela anu, komanso kumveketsa mfundo zofunika.
MOCITILA:
Sankhani mafanizo osavuta. Monga mmene Yesu anacitila, gwilitsilani nchito zinthu zing’ono-zing’ono kumveketsa zinthu zikulu-zikulu, komanso zinthu zosavuta kumveketsa zinthu zovuta. Musaphatikizepo mbali zina zosafunikila kweni-kweni zimene zingacolowanitse fanizolo. Onetsetsani kuti fanizo limenelo likugwilizanadi na mfundo imene mufuna kuphunzitsa, kuti musawasokoneze omvela anu.
Ganizilani omvela anu. Sankhani mafanizo ophatikizapo zinthu zokhudza omvela anu. Koma samalani kuti mafanizo anu asakhale ocititsa manyazi omvela anu, kapena oŵakhumudwitsa.
Phunzitsani mfundo zazikulu. Mafanizo anu aziphunzitsa mfundo zazikulu, osati tumbali tocepa. Onetsetsani kuti omvela anu asakakumbukile fanizo cabe, koma maka-maka phunzilo lake.