UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Mungakwanitse Kulalikila na Kuphunzitsa!
Mose poyamba anakayikila zakuti angakwanitse kucita nchito imene Yehova anamupatsa. (Eks. 4:10, 13) Kodi na imwe munadzikayikilapo? Kodi mukuphunzila Baibo na Mboni za Yehova? Kodi mumadzifunsa ngati mudzakwanitsa kulalikila ku nyumba na nyumba? Kapena ndimwe wacicepele amene amacita mantha kulalikila ku sukulu. Kapena mwina mumacita mantha kutengako mbali pa ulaliki wa pa foni kapena wapoyela. Pemphani Yehova kuti akupatseni mphamvu yake ya mzimu woyela. (1 Pet. 4:11) Khalani na cidalilo cakuti angakuthandizeni pa nchito iliyonse imene wakupatsani.—Eks. 4:11, 12.
TAMBANI VIDIYO YAKUTI KHALANI OLIMBA MTIMA . . . INU OFALITSA, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:
Kodi ni vuto lanji limene mlongo Aoyama anakumana nalo?
Kodi n’ciani cinam’thandiza kupeza mphamvu komanso kukhala wolimba mtima?—Yer. 20:7-9
Kodi anapindula bwanji powonjezela zocita potumikila Yehova?
Kodi Yehova angakuthandizeni kuthana na mavuto ati mu ulaliki?