LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwbr20 June
  • Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki
  • Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu—2020
  • Tumitu
  • JUNE 1-7
  • JUNE 8-14
  • JUNE 15-​21
  • JUNE 22-28
  • JUNE 29–JULY 5
Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu—2020
mwbr20 June

Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki

JUNE 1-7

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 44-45

“Yosefe Anakhululukila Abale Ake”

w15 5/1 14-15

“Kodi Ine Ndatenga Malo a Mulungu?”

Abale ake atanyamuka, Yosefe anauza mtumiki wake kuti awatsatile. Atawapeza, anaŵauza kuti aba kapu ya Yosefe. Kenako anayamba kufufuza kapuyo m’matumba awo ndipo anaipeza m’thumba la Benjamini. Zitatelo, onse anabwelelanso kwa Yosefe. Apa Yosefe anapeza mpata woti ayesenso abale ake. Yuda ni amene anali kulankhula m’malo mwa onse. Anacondelela Yosefe kuti awakhululukile mpaka anafika ponena kuti awatenge onse 11, kuti akhale akapolo a ku Iguputo. Koma Yosefe anakana n’kunena kuti Benjamini yekha ndiye akhale kapolo wake cifukwa ni amene wapezeka na kapu, ena apite.​—Genesis 44:2-17.

Koma Yuda atamva zimenezi, anamva cisoni kwambili moti anayankha kuti: “M’bale wake wa mimba imodzi anamwalila, moti anatsala yekha, ndipo bambo amam’konda kwambili.” Ziyenela kuti zinam’khudza kwambili Yosefe atamva mawu amenewa cifukwa anadziŵa kuti akunena za iye. Yosefe anali mkulu wake wa Benjamini ndipo mayi awo anali a Rakele. Mayi awo anamwalila pamene anali kubeleka Benjamini. Mofanana na bambo ake, a Yakobo, Yosefe ayenela kuti anali kukumbukilabe amayi ake cifukwa anali kuwakonda kwambili. Yosefe anali kukonda kwambili Benjamini cifukwa anali ana a mayi mmodzi.​—Genesis 35:18-20; 44:20.

Yuda anapitiliza kucondelela Yosefe kuti asatenge Benjamini n’kukhala kapolo wake. Mpaka anauza Yosefe kuti atenge iye m’malo mwa Benjamini. Kenako ananena mawu okhudza mtima kwambili. Anati: “Ndingathe bwanji kupita kwa bambo anga ndilibe mwanayu? Ayi, sindikufuna kukaona bambo anga akuzunzika ndi cisoni.” (Genesis 44:18-34) Zimenezi zinasonyezelatu kuti Yuda anasintha kwambili. Zinaonetsa kuti analapa zoipa zija zimene anacitila Yosefe komanso kuti tsopano anali wacifundo komanso woganizila ena.

Apa Yosefe analephela kupilila. Conco, anauza anthu onse kuti atuluke kukhale cabe abale ake. Atatelo analila mofuula cakuti mawu ake anamveka ku nyumba kwa mfumu Farao. Kenako, anadziulula kwa abale ake kuti: “Ndine Yosefe!” Abale ake anadabwa kwambili na zimenezi. Koma Yosefe anawakumbatila poonetsa kuti anawakhululukila. (Genesis 45:1-15) Apa Yosefe anaonetsa kuti anatengela Yehova, amene amakhululuka na mtima wonse. (Salimo 86:5) Kodi inunso mumakhululuka na mtima wonse?

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

it-2 813

Kung’amba Zovala

Cizindikilo cofala pakati pa Ayuda, komanso pakati pa anthu a kum’mawa coonetsa kuti munthu ali na cisoni maka-maka pamene wamvela kuti wacibululu wapafupi wamwalila. Nthawi zambili anali kung’amba covala kutsogolo kuti pacifuwa pokha paonekele, sikuti anali kung’amba covala conse n’kukhala cosayenela kuvala.

Koyamba pamene izi zimachulidwa m’Baibo, ni pamene Rubeni, mwana wamkulu wa Yakobo, amene atabwelako anapeza kuti Yosefe mulibe m’citsime, iye anang’amba zovala zake, ndipo anati, “Mwana ujatu kulibe! Kalanga ine, ndilowela kuti ine?” Monga mwana woyamba, Rubeni anali na udindo woyang’anila maka-maka m’bale wake wacicepele. Atate ake a Yakobo atauzidwa cimene cinapha mwana wawo, nawonso anag’amba zovala zawo na kuvala ciguduli polila malilo (Gen. 37:29, 30, 34), ndipo pamene abale ake a Yosefe anali ku Iguputo, anaonetsa cisoni cawo mwa kung’amba zovala zawo pamene Benjamini anaimbidwa mlandu wakuti ni kawalala.​—Gen. 44:13.

w04 8/15 15 ¶15

Odedwa Popanda Cifukwa

15Kodi n’ciani cingatithandize kuti tisawawidwe mtima kwambili ndi anthu amene amatizonda popanda cifukwa? Kumbukilani kuti adani athu akulu-akulu ni Satana na ziŵanda zake. (Aefeso 6:12) Ngakhale kuti anthu ena amatizunza mwadala, ambili amene amatsutsa anthu a Mulungu amacita zimenezo mosadziŵa kapena mocita kutunthiwa ndi anthu ena. (Danieli 6:4-16; 1 Timoteyo 1:12, 13) Yehova afuna kuti “anthu onse” apeze mwayi ‘wopulumuka ndi kufika pozindikila coonadi.’ (1 Timoteyo 2:4) Ndipo ena amene kale anali kutitsutsa tsopano ni abale athu Acikhristu cifukwa coti aona makhalidwe athu abwino. (1 Petulo 2:12) Komanso, tingaphunzilepo mfundo yabwino pa citsanzo ca Yosefe mwana wa Yakobo. Ngakhale kuti Yosefe anavutika kwambili cifukwa ca abale ake, iye sanawasungile cakukhosi. Cifukwa ciani? Anatelo cifukwa coona kuti nkhaniyo inali kukhudzanso Yehova, amene anali kuyendetsa zinthu pofuna kukwanilitsa colinga Cake. (Genesis 45:4-8) Mofananamo, Yehova angacititse kuti kuzunzidwa kwathu popanda cifukwa kuthandize kubweletsa ulemelelo pa dzina lake.​—1 Petulo 4:16.

JUNE 8-14

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 46-47

“Thandizo la Cakudya pa Nthawi ya Njala”

w87 5/1 15 ¶2

Kupulumutsa Moyo mu Nthawi ya Njala

2Zaka zisanu na ziŵili za cakudya coculuka zinatha, ndipo njala inayamba monga mmene Yehova anakambila—njala osati mu Iguputo mokha koma “padziko lonse lapansi.” Pamene anthu anjala mu Iguputo anayamba kulila kwa Farao kaamba ka mkate, Farao anawauza kuti: “Pitani kwa Yosefe! Zilizonse zimene akuuzeni, citani zomwezo.” Yosefe anagulitsa tiligu kwa Aiguputo kufikila ndalama zawo zinatha. Kenako, iye anayamba kulandila ziŵeto zawo monga malipilo. Pomalizila, anthuwo anabwela kwa Yosefe, ndi kunena kuti: “Mutigule limodzi ndi minda yathu potipatsa cakudya kuti tikhale akapolo a Farao.” Cotelo Yosefe anagulila Farao dziko lonse la Aiguputo.​—Genesis 41:53-57; 47: 13-20.

kr 234-​235 ¶11-12

Ufumu Ukwanilitsa Cifunilo ca Mulungu Padziko Lapansi

11Zinthu zoculuka. M’dzikoli muli njala ya kuuzimu. Baibo inakambilatu kuti: “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Taonani, masiku akubwela pamene ndidzatumiza njala m’dziko. Njala imeneyo siidzakhala ya cakudya kapenanso ludzu lofuna madzi ayi, koma idzakhala njala ndiponso ludzu lofuna kumva mawu a Yehova.’” (Amosi 8:11) Kodi nzika za Ufumu wa Mulungu zilinso na njala ya kuuzimu? Yehova anafotokoza kusiyana kumene kudzakhalapo pakati pa anthu ake na adani ake. Iye anati: “Atumiki anga adzadya, koma inuyo mudzakhala ndi njala. Atumiki anga adzamwa, koma inuyo mudzakhala ndi ludzu. Atumiki anga adzasangalala, koma inuyo mudzacita manyazi.” (Yes. 65:13) Kodi mwaona kukwanilitsidwa kwa mawu amenewa?

12Timalandila cakudya cakuuzimu coculuka monga madzi a mumtsinje umene ukukulila-kulila. Mabuku othandiza kuphunzila Baibo kuphatikizapo zinthu zina zomvetsela monga mavidiyo, misonkhano ya mpingo ndiponso misonkhano ikului-kulu, komanso zinthu zina zopezeka pa Webusaiti yathu, zonsezi ni cakudya cakuuzimu cimene timalandila m’dziko lino limene likuvutika na njala ya kuuzimu. (Ezek. 47:1-12; Yow. 3:18) Kodi simukusangalala kuona kuti Yehova akukwanilitsa malonjezo ake mwa kutipatsa zinthu zoculuka masiku ano? Kodi mumayesetsa kudya pathebulo la Yehova nthawi zonse?

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

it-1 220 ¶1

Macitidwe Oonetsa Cikhalidwe

Kutseka maso a munthu amene wamwalila. Pamene Yehova anauza Yakobo kuti: “Yosefe ndi amene adzakutseke maso” (Gen. 46:4), anatanthauza kuti Yosefe ni amene adzatseka maso a Yakobo pa imfa yake. Kambili, mwana woyamba ndiye anali na udindo wocita zimenezi. Conco, zioneka kuti apa Yehova anaonetsa Yakobo kuti udindo wa mwana woyamba uyenela kupita kwa Yosefe.​—1 Mbiri 5:2.

nwtsty mfundo younikila pa Mac. 7:14

Onse pamodzi analipo anthu 75: N’kutheka kuti Stefano sanagwile mawu pa lemba linalake m’Malemba Aciheberi, pamene anakamba kuti ana onse a Yakobo ku Iguputo analiko 75. Ciŵelengelo cimeneci, sicipezeka m’Malemba Aciheberi acimasorete. Pa Gen. 46:26 pamati: “Ana onse a Yakobo otuluka m’ciuno mwake, amene anali nawo ku Iguputo, analipo 66 onse pamodzi, osawelengela akazi a ana ake.” Vesi 27 ipitiliza kuti: “Onse a m’nyumba ya Yakobo amene anali nawo ku Iguputo analipo 70.” Apa anthu amenewa akuŵelengedwa m’njila ziŵili zosiyana. Ciŵelengelo coyamba ciyenela kuti n’ca mbadwa zake zeni-zeni cabe, pamene ciŵelengelo caciŵili cikuphatikizapo onse pamodzi, amene anapita kukakhala ku Iguputo. Ciŵelengelo ca mbadwa za Yakobo cikuchulidwanso pa Eks. 1:5 na pa Deut. 10:22. Pamalembawa pakuchulidwa anthu “70.” Stefano ayenela kuti anachula ciŵelengelo cacitatu cimene cikuphatikizapo acibululu ena a Yakobo. Ena amakamba kuti ciwelengelo cimeneci cikuphatikizapo ana ndi azidzukulu a ana a Yosefe, Manase na Efuraimu, amene akuchulidwa pa lemba la Gen. 46:20 mu Baibo ya Septuagint. Ena amakamba kuti ciŵelengelo cimeneci ciphatikizapo akazi a ana a Yakobo, amene sanaikidwepo pa ciŵelengelo cochulidwa pa Gen. 46:26. Conco onse pamodzi ayenela kuti anali anthu “75.” Komanso, zioneka kuti ciŵelengelo cimeneci cinalimo m’mipukutu ya Malemba Aciheberi amene anali ofala m’nthawi ya atumwi. Kwa zaka zambili, akatswili akhala akudziŵa kuti ciŵelengelo ca anthu “75” ndiye ciŵelengelo cinalipo pa Gen. 46:27 na pa Eks. 1:5 m’Baibo yacigiriki ya Septuagint. Kuwonjezela apo, m’zidutswa ziŵili zamipukutu yaciheberi za Eks. 1:5 zimene anapeza ku Nyanja Yakufa mu 1900, anaseŵenzetsanso ciŵelengelo ca anthu “75.” Mwina namba imene Stefano anachula inali pa umodzi wa mipukutu yakale imeneyi. Mosasamala kanthu kuti n’ziti zolondola, namba imene Stefano anachula ikutithandiza kudziŵa ciŵelengelo ca mbadwa zonse za Yakobo.

JUNE 15-​21

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 48-​50

“Acikulile Ali na Zambili Zotiphunzitsa”

it-1 1246 ¶8

Yakobo

Atatsala pang’ono kumwalila, Yakobo anadalitsa zidzukulu zake, ana a Yosefe, ndipo motsogoleledwa na Mulungu, anaika Efuraimu mwana wam’g’ono patsogolo pa wamkulu Manase. Ndiyeno kwa Yosefe, amene analandila magawo aŵili a coloŵa ca mwana woyamba, Yakobo anati: “Ndikukuwonjezela gawo limodzi la dziko kuposa abale ako, limene ndinalanda Aamori ndi lupanga langa ndi uta wanga.” (Gen. 48:1-22; 1 Mbiri 5:1) Popeza Yakobo anagula mwamtendele malo a kufupi na Sekemu kwa ana aamuna a Hamori (Gen. 33:19, 20), zioneka kuti pokamba lonjezo limeneli kwa Yosefe, Yakobo anaonetsa cikhulupililo. Iye analosela zakuti akanani adzagonjetsedwa ndi mbadwa zake kutsogolo. Analosela monga kuti ndiye wawagonjetsa kale na lupanga lake na uta wake. Magawo aŵili a Yosefe a dela logonjetsedwa limenelo, anaphatikizapo magawo aŵili amene anapatsidwa ku fuko la Efuraimu na Manase.

it-2 206 ¶1

Masiku Otsiliza

Ulosi wa Yakobo Atatsala Pang’ono Kumwalila. Pamene Yakobo anauza ana ake aamuna kuti “Sonkhanani pamodzi kuti ndikuuzeni zimene zidzacitika kwa inu m’masiku am’tsogolo,” anatanthauza nthawi ya kutsogolo pamene mawu ake adzayamba kukwanilitsidwa. (Gen. 49:1) Zaka zoposa 200 m’mbuyomo, Yehova anali atauza Abramu (Abulahamu), ambuye ake a Yakobo, kuti mbadwa zawo zidzasautsidwa kwa zaka 400. (Gen. 15:13) Conco, nthawi ya kutsogolo imene Yakobo anakamba kuti “m’masiku am’tsogolo” siinayambe mpaka zaka 400 zamasautso zitatha. (Kuti mudziŵe zambili za mu Genesis 49, ŵelengani nkhani zokhudza ana aamuna a Yakobo, zopezeka pa tumitu tochedwa na maina awo.) Pambuyo pake, Ulosi umenewu unali kuyembekezeledwa kudzakwanilitsidwanso pa “Isiraeli wa Mulungu” wauzimu.​—Agal. 6:16; Aroma 9:6.

w07 6/1 28 ¶10

Okalamba Ni Dalitso kwa Anthu Ocepelapo Msinkhu

10Okalamba angathandizenso okhulupilila anzawo. Paukalamba wake, Yosefe mwana wa Yakobo anakamba cinthu cosonyeza kuti anali na cikhulupililo. Ali na zaka 110, “anapeleka lamulo lokhudza mafupa ake,” kuti Aisiraeli akadzatuluka mu Iguputo, adzatenge mafupa ake. Zimenezi zinathandiza kwambili olambila oona mamiliyoni ambili amene anakhalako pambuyo pake. (Aheberi 11:22; Genesis 50:25) Lamulo limenelo linathandiza Aisiraeli kusataya ciyembekezo cawo pazaka zambili za ukapolo umene analowamo Yosefe atamwalila, ndipo linawatsimikizila kuti adzalanditsidwa.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

w04 6/1 15 ¶4-5

Odala Ni Amene Amapatsa Mulungu Ulemelelo

4Asanaloŵe m’Dziko Lolonjezedwa, a fuko la Gadi mu Isiraeli anapempha kuti akhale m’dela labwino kusungilamo ziŵeto kum’maŵa kwa mtsinje wa Yorodano. (Numeri 32:​1-5) Kukhala m’delalo kunali na mavuto ake. Nthawi ya nkhondo, mafuko akumadzulo anali kutetezedwa na cigwa ca Yorodano cimene cinali cochinga cacilengedwe. (Yoswa 3:13-17) Koma za dela la kum’maŵa kwa Yorodano, buku lakuti The Historical Geography of the Holy Land, lolembedwa na George Adam Smith limati: “[Delalo] n’lafulati, ndipo lilibe cochinga ciliconse, lili pa cikweza ca Arabiya. Conco mafuko anjala amene amangoyendayenda akhala akuliloŵelela kuyambila kale, ndipo ena a iwo amatelo mwaunyinji wawo caka ciliconse kufuna-funa msipu.”

5Kodi fuko la Gadi likanakwanitsa bwanji kupilila vuto losatha limenelo? Kale, zaka zambili nthawi imeneyo isanafike, kholo lawo Yakobo pomwalila analosela kuti: “Kunena za Gadi, gulu la acifwamba lidzamuukila, koma iye adzawathila nkhondo, ndipo acifwambawo pothawa iye adzawakantha koopsa.” (Genesis 49:19) Kungowaona koyamba, mawu amenewa angamveke monga osalimbikitsa. Koma kunena zoona, anali lamulo kwa fuko la Gadi kuti iwo azibwezela. Yakobo anawalonjeza kuti iwo akatelo, achifwambawo adzathawa ndi manyazi, ndipo Agadiwo adzawalondola m’mbuyo kuwapitikitsa.

it-1 289 ¶2

Benjamini

Luso lomenya nkhondo la mbadwa za Benjamini, linafotokozedwa mu ulosi umene Yakobo analosela atatsala pang’ono kumwalila. Pokamba za mwana wake ameneyu, Yakobo anati: “Benjamini adzapitiliza kukhadzula ngati mmbulu. M’mawa adzadya nyama imene wagwila, ndipo madzulo adzagawa zimene wafunkha.” (Gen. 49:27) Abenjamini anali kudziŵika na luso lawo loponya miyala pomenya nkhondo. Iwo anali kuponya miyala na dzanja la manja kapena lamanzele ndipo anali ‘amaluli’ (kapena kuti sanali kuphonya). (Ower. 20:16; 1 Mbiri 12:2) Woweluza Ehudi, wa fuko la Benjamini anali wamanzele, anapha Mfumu Egiloni imene inali yopondeleza. (Ower. 3:15-21) Zikuonekanso kuti kunali “m’mawa” mu ufumu wa Isiraeli, kuti fuko la Benjamini, ngakhale kuti linali laling’ono kwambili pa mafuko onse,” litulutse mfumu yoyamba ya Isiraeli, Sauli mwana wa Kisi, amene anamenyana koopsa na Afilisiti. (1 Sam. 9:15-17, 21) Cimodzi-modzinso pa nthawi ya “madzulo” ya mtundu wa Aisiraeli, fuko la Benjamini linatulutsa mfumukazi Esitere na Nduna Yaikulu Moredekai, amene anateteza Aisiraeli kuti asawonongedwe kothelatu mu Ufumu wa Perisiya.​—Esitere 2:5-7.

JUNE 22-28

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKISODO 1–3

“Ndidzakhala Amene Ndidzafune Kukhala”

w13 3/15 25 ¶4

Muzilemekeza Dzina Lalikulu la Yehova

4Ŵelengani Ekisodo 3:​10-​15. Mose ali na zaka 80, Mulungu anam’patsa nchito yovuta kwambili. Anam’lamula kuti: “Ukatulutse anthu anga ana a Isiraeli ku Iguputo.” Mose anayankha mwaulemu pomufunsa Yehova funso locititsa cidwi losonyeza kuti anali kufuna kudziŵa dzina la Mulungu. Koma popeza pa nthawiyi n’kuti dzina la Mulungu likudziŵika kale, n’cifukwa ciani Mose anafunsa funso limeneli? Iye anali kufuna kudziŵa zambili zokhudza Mulungu yemwe ni mwini wake wa dzinali. Mose anali kudziŵa kuti zimenezi zidzathandiza Aisiraeli kukhulupilila kuti Mulunguyo awapulumutsadi. Nkhaŵa imene Mose anali nayo inali yoyenela cifukwa Aisiraeli anali atakhala akapolo kwa zaka zambili. Mwina iwo sakanakhulupilila kuti Mulungu wamakolo awo angawapulumutsedi. Komanso Aisiraeli ena anali atayamba kulambila milungu ya Aiguputo.​—Ezek. 20:7, 8.

kr 43, bokosi

TANTHAUZO LA DZINA LA MULUNGU

DZINA lakuti Yehova linacokela ku liwu laciheberi limene limatanthauza kuti “kukhalako.” Akatswili ena amanena kuti liwu limeneli ni mneni wosonyeza cinthu cimene cimacititsa kuti cinacake cicitike. Motelo anthu ambili amaona kuti dzina la Mulungu limatanthauza kuti “Iye Amacititsa Kukhala.” Tanthauzo limeneli ni loyeneleladi Yehova cifukwa cakuti iye ndiye Mlengi. Iye analenga cilengedwe conse kuphatikizapo zolengedwa zanzelu ndipo akupitilizabe kukwanilitsa colinga cake.

Conco, kodi yankho limene Yehova anapeleka kwa Mose pa Ekisodo 3:13, 14 limatanthauzanji? Mose anafunsa kuti: “Nditati ndakafika kwa ana a Isiraeli ndi kuwauza kuti, ‘Mulungu wa makolo anu wandituma kwa inu,’ iwo n’kundifunsa kuti, ‘Dzina lake ndani?’ Ndikawayankhe kuti ciani?” Yehova anam’yankha Mose kuti: “Ndidzakhala Amene Ndidzafune Kukhala.”

Pamenepa, Mose sanali kupempha Yehova kuti amuuze dzina lake. Mose na Aisiraeli anali kudziŵa kale dzina la Mulungu. Koma Mose anali kufuna kuti Yehova afotokoze zinthu zolimbikitsa zosonyeza kuti iye ni Mulungu wotani kweni-kweni, na kuti dzina lake limatanthauza ciani. Conco, pamene ananena kuti, “Ndidzakhala Amene Ndidzafune Kukhala,” Yehova anali kuulula mfundo ina yocititsa cidwi ya mmene iye alili. Mfundo yake ni yakuti, pa cocitika ciliconse, Mulungu amakhala ciliconse cimene cikufunikila kuti akwanilitse colinga cake. Mwacitsanzo, kwa Mose na Aisiraeli, Yehova anakhala Mpulumutsi, Wopeleka Malamulo, Wosamalila, na zina zotelo. Motelo, Yehova amasankha kukhala ciliconse cimene cikufunikila kuti akwanilitse colinga cake kwa anthu ake. Komabe, dzina lakuti Yehova limatanthauza zambili kuonjezela pa mfundo yakuti iye amasankha kukhala ciliconse cimene akufuna. Dzinali limatanthauzanso kuti Mulungu angapangitse cilengedwe cake kukhala cimene iye akufuna kuti akwanilitse colinga cake.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

g04 4/8 6 ¶5

Kodi Mose Anali Munthu Weni-weni Kapena Wongopeka?

Koma kodi n’zomvekadi kuganiza kuti mwana wamkazi wa mfumu wa ku Iguputo akanasunga mwana wotelo? Inde, cifukwa cipembedzo ca ku Iguputo cinali kuphunzitsa kuti munthu sadzapita kumwamba popanda kusonyeza cifundo ena. Ndipo pankhani yotenga mwana wa munthu wina, katswili wa zinthu zakale zofukulidwa pansi dzina lake Joyce Tyldesley anati: “Akazi a ku Iguputo anali na ufulu wofanana ndi wa amuna. Tikangotengela zimene zinalembedwa, akazi nawo anali na ufulu wonse pankhani ya zamalamulo ndiponso zacuma, ndipo . . . analinso na ufulu pankhani yotenga mwana wa munthu wina.” Cikalata cina cakale ca ku Iguputo cimakambako za mayi wina wa ku Iguputo amene anapeza cilolezo coti akapolo ake akhale ana ake. Pankhani yolemba nchito mayi ake a Mose kuti akhale mayi woyamwitsa cabe mwanayo, buku lochedwa The Anchor Bible Dictionary imati: “Zolemba nchito mayi ake a Mose kuti azimuyamwitsa . . . n’zogwilizana na zimenenso zinali kucitika ku Mesopotamiya munthu akaloledwa kutenga mwana wa munthu wina.”

w04 3/15 24 ¶4

Mfundo Zazikulu za M’buku la Ekisodo

3:1—Kodi Yetero anali wansembe wotani? M’nthawi zakale, mutu wa banja unali kukhala wansembe wa banja lakelo. Zikuoneka kuti Yetero anali mtsogoleli wa fuko la Amidyani. Popeza Amidyani anali mbadwa za Abulahamu kudzela mwa Ketura, mwina anali kudziŵako za kulambila Yehova.​—Genesis 25:1, 2.

JUNE 29–JULY 5

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

“Ine Ndidzakhala Nawe Polankhula”

w10 10/15 13-14

Kodi Yehova Amaona Bwanji Kupeleka Zifukwa Pofuna Kudzikhululukila?

“Siningathe.” Mwina mukhoza kumaona kuti sindimwe woyenelela kulalikila uthenga wabwino. M’nthawi yakale, atumiki a Yehova ena anali kuona kuti sangathe kugwila bwino nchito imene Yehova anawapatsa. Mwacitsanzo, taganizilani za Mose. Yehova atam’patsa nchito yoti acite, Mose anati: “Pepani Yehova, ine sinditha kulankhula, kuyambila kale-kale, kapena pamene mwalankhula ndi ine mtumiki wanu. Pakuti ndimalankhula movutikila ndipo ndine wa lilime lolemela.” Yehova atamulimbikitsa, Mose ananenabe kuti: “Pepani Yehova. Conde, tumizani wina aliyense amene mungam’tumize.” (Eks. 4:10-13) Kodi Yehova anacita ciani?

w14 4/1 9 ¶5-6

Kodi Mumaona “Wosaonekayo”?

5Mose asanapite ku Iguputo, Mulungu anam’phunzitsa mfundo yofunika kwambili. Pambuyo pake, Mose analemba mfundoyi m’buku la Yobu kuti: “Kuopa Yehova ndiko nzelu.” (Yobu 28:28) Kuti Yehova athandize Mose kukhala ndi mantha ndi kucita zinthu mwanzelu, anamuonetsa kusiyana kumene kulipo pakati pa anthu ndi Mulungu Wamphamvuzonse. Mulungu anam’funsa kuti: “Anapatsa munthu pakamwa ndani, kapena ndani amapanga munthu wosalankhula, wogontha, woona kapena wakhungu? Kodi si ine, Yehova?”​—Eks. 4:11.

6Kodi zimenezi zinam’phunzitsa ciani Mose? Mose sanafunikile kuopa cifukwa anatumidwa na Yehova. Ndipo Mulungu anali kudzam’thandiza kuti apeleke uthenga wake kwa Farao. Ndiponso, Farao sanali kanthu pomuyelekezela na Yehova. Ndipo iyi sinali nthawi yoyamba kuti moyo wa atumiki a Mulungu ukhale pa ngozi mu Iguputo. Mwina Mose anakumbukila mmene Yehova anatetezela Abulahamu, Yosefe ndi iye mwini pamene anali pansi pa ulamulilo wa mafumu ena aciiguputo. (Gen. 12:17-19;41:14, 39-41; Eks. 1:22–2:10) Cifukwa cokhulupilila Yehova, “Wosaonekayo,” Mose molimba mtima anapita kwa Farao kukamuuza mawu onse amene Yehova ananena.

w10 10/15 14

Kodi Yehova Amaona Bwanji Kupeleka Zifukwa Pofuna Kudzikhululukila?

Yehova sanalole kuti Mose asagwile nchito imene anam’patsayi. M’malomwake, iye anauza Aroni kuti athandize Mose pa nchito imeneyi. (Eks. 4:14-17) M’zaka zotsatila, Yehova anathandiza Mose ndipo anam’patsa zinthu zonse zofunika kuti agwile bwino nchito imene anam’patsa. Masiku anonso muyenela kukhulupilila kuti Yehova adzagwilitsa nchito Akhristu anzanu aluso kuti akuthandizeni kucita utumiki. Koposa zonse, Mawu a Mulungu amatitsimikizila kuti Yehova adzatithandiza kukhala oyenela kugwila nchito imene iye watipatsa.​—2 Akor. 3:5; onani bokosi lakuti, “Zaka Zimene Ninasangalala Kwambili pa Moyo Wanga.”

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

w04 3/15 28 ¶4

Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga

Mawu a Zipora akuti “ndinu mkwati wa magazi kwa ine” ni mawu acilendo. Kodi mawu amenewa akuonetsa ciani za iye? Mwa kutsatila zimene pangano la mdulidwe linafuna, Zipora anavomeleza kucita pangano na Yehova. Pangano la Cilamulo limene anapangana na Aisiraeli patapita nthawi, linaonetsa kuti m’panganolo, Yehova angakhale ngati mwamuna ndipo Aisiraeliwo ngati mkazi. (Yeremiya 31:32) Motelo, pokamba Yehova (kudzela mwa mngelo amene anali kumuimila) kuti “mkwati wa magazi,” Zipora aoneka kuti anali kuvomeleza kugonjela mfundo za m’panganolo. Zinali ngati kuti wavomeleza kukhala monga mkazi m’pangano la mdulidwe, ndipo Yehova Mulungu ndiye mwamuna wake. Mulimonse mmene zinalili, cifukwa cocita zinthu mwamsanga pomvela zimene Mulungu anafuna, mwana wakeyo sanaphedwe.

it-2 12 ¶5

Yehova

“Kudziwa” sikutanthauza cabe kungozindikila zinthu zina zake kapena munthu wina wake. Munthu wopanda pake Nabala anali kudziŵa dzina la Davide koma anafunsabe kuti, “Kodi Davide ndani?” M’njila ina, iye anali kufunsa kuti, “Kodi iye amadziona kuti ni ndani?” (1 Sam. 25:9-11; yelekezani na 2 Sam. 8:13) Izi n’zofanana na zimene Farao anakamba polankhula na Mose. Anati: “Yehova ndani kuti ndimvele mawu ake, ndi kulola Aisiraeli kuti apite? Ine sindikum’dziwa Yehova ngakhale pang’ono, komanso, sindilola kuti Aisiraeli apite.” (Eks. 5:1, 2) Ndi mawu amenewa, mwacionekele Farao anali kutanthauza kuti sanali kudziŵa Yehova monga Mulungu woona kapena kuti iye ali na mphamvu pa mfumu ya Iguputo na zocitika za mu umoyo wake, kapenanso kuti iye ali na mphamvu zokwanilitsa cifunilo Cake mogwilizana na zimene Mose na Aroni analengeza. Koma panthawiyi, Farao na Aiguputo onse, kuphatikizapo Aisiraeli, anali kudzadziŵa tanthauzo leni-leni la dzina limenelo, komanso mwini wake amene aimila dzinalo. Monga mmene Yehova anaonetsela Mose, izi zinaphatikizapo kukwanilitsa cifunilo Cake pa Aisiraeli, kuwamasula, na kuwapatsa Dziko Lolonjezedwa, uku akukwanilitsa pangano limene anapanga na makolo awo. Mwanjila imeneyi, monga mmene Mulungu anakambila kuti: “Inuyo mudzadziwadi kuti ine ndine Yehova Mulungu wanu.”—Eks. 6:4-8.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani