Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki
MAY 4-10
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 36-37
“Yosefe Anacitilidwa Nsanje”
‘Tamvelani Maloto Awa’
Baibo imayankha kuti: “Abale ake ataona kuti bambo awo anali kum’konda kwambili Yosefe kuposa iwo onse, anayamba kudana naye, moti sankatha kulankhula naye mwamtendele.” (Genesis 37:4) Nsanje yawo inali yomveka, koma kunali kupanda nzelu kucita kukhala na nsanje yoipa ngati imeneyo. (Miyambo 14:30; 27:4) Kodi munacitapo nsanje poona kuti winawake akukondedwa kapena kupatsidwa ulemu umene inu munali kuufuna? Kumbukilani abale ake a Yosefe. Nsanje yawo inawapangitsa kucita zinthu zimene patsogolo pake anadziimba nazo mlandu. Citsanzo cawo cimakumbutsa Mkhristu aliyense kuti cimakhala cinthu canzelu ‘kusangalala ndi anthu amene akusangalala.’—Aroma 12:15.
Yosefe anazindikila kuti abale ake anali kumuzonda kwambili. Conco, kodi iye anabisa mkanjo wapadela umene anapatsidwa ndi atate ake, abale ake atamuyandikila? Ayenela kuti anali ataganizapo kutelo. Koma kumbukilani kuti Yakobo anafuna kuti mkanjowo ukhale cizindikilo ca kukoma mtima na cikondi. Popeza kuti Yosefe anali kufuna kuti atate ake apitilize kum’dalila, iye anapitilizabe kuvala mkanjo umene anam’patsa. Citsanzo cake n’cofunika kwambili kwa ife. Ngakhale kuti Atate wathu wa kumwamba alibe tsankho, nthawi zina amasankha atumiki ake ena okhulupilika na kuwakomela mtima. Kuwonjezela apo, amawapempha kukhala osiyana na dzikoli limene ladzaza na makhalidwe oipa. Mofanana na mmene mkanjo wapadela wa Yosefe unalili, khalidwe la Akhristu oona, liyenela kukhala losiyana ndi la anthu otizungulila. Khalidwe limeneli limapangitsa anthu ena kuticitila nsanje na kutizonda. (1 Petulo 4:4) Kodi Mkhristu ayenela kudzibisa kuti si mtumiki wa Mulungu? Iyai—Yosefe sanabise mkanjo wake.—Luka 11:33.
‘Tamvelani Maloto Awa’
Malotowo anacokela kwa Yehova Mulungu. Anali maulosi, ndipo Mulungu anafuna kuti Yosefe apeleke uthenga umene unali m’malotowo. Tinganene kuti Yosefe anafunika kucita zinthu monga mmene aneneli a m’tsogolo anali kudzacitila pofotokoza mauthenga a Mulungu na ziweluzo zake kwa anthu Ake osamvela.
Mwanzelu, Yosefe anauza abale ake kuti: “Tamvelani maloto amene ine ndinalota.” Abale akewo anamvetsela malotowo, koma sanakondwele nawo ngakhale pang’ono. Iwo anamuyankha kuti: “Kodi iweyo ndithu ukuganiza kuti ungadzakhale mfumu yathu? Moti ukuona kuti ungadzatilamulile ife?” Nkhaniyo imapitiliza kuti: “Kwa iwo maloto amenewo ndi mawu akewo cinakhala cifukwa cinanso comudela.” Yosefe atafotokoza loto laciŵili kwa atate ake ndiponso kwa abale ake, zinthu zinangoipilaipila. Timaŵelenga kuti: “Bambo ake anam’dzudzula kuti: ‘Kodi maloto walotawa akutanthauza ciani? Kodi ineyo ndithu ndi mayi akowa, komanso abale akowa tidzagwada pansi pamaso pa iwe?’” Komabe, Yakobo anapitiliza kuganizilapo pa mawu a Yosefe. Moti iye anadzifunsa kuti, kodi mnyamata ameneyu angakhale kuti amalankhula na Yehova?—Genesis 37:6, 8, 10, 11.
Yosefe sanali mtumiki woyamba kapena womaliza wa Yehova kuuzidwa kuti apeleke uthenga wa ulosi wosakondweletsa anthu, komanso wom’bweletsela mazunzo. Yesu ndiye anali wopeleka uthenga wamkulu kuposa anthu amene anacitila umboni uthenga wotelo, cakuti anauza otsatila ake kuti: “Ngati anazunza ine, inunso adzakuzunzani.” (Yohane 15:20) Akhristu a misinkhu yonse angaphunzile zambili pa cikhulupililo na kulimba mtima kwa Yosefe.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
it-1 678
Edomu
(Edomu) [Cofiila], Aedomu
Edomu linali dzina lina limene Esau anapatsiwa, mphundu mnzake wa Yakobo. (Gen. 36:1) Anapatsidwa dzinali cifukwa anagulitsa udindo wake monga woyamba kubadwa pofuna cakudya ca mphodza cofiila. (Gen. 25:30-34) N’zocititsa cidwi kuti pobadwa Esau anali wofiila kwambili (Gen. 25:25), ndipo nthaka ya malo amene iye na mbadwa zake anapita kukakhala inali yofiilanso.
it-1 561-562
Kuyang’anila
M’busa akakamba kuti adzasunga kapena kuteteza nkhosa, anali kuonetsa kuti wavomela mwalamulo kuyang’anila nyamazo. Anali kutsimikizila mwini wake wa nyamazo kuti adzazidyetsa na kudziteteza kuti zisabedwe, kuti zikabedwa adzamulipila. Koma udindo wake unali na malile, lamulo limenelo linali kukamba kuti woyang’anilayo sanali kukhala na mlandu ngati cinthu cina cacitikila nyamazo cimene munthuyo sakanatha kucitapo kanthu, monga kudyedwa na cilombo ca kuchile. Kuti amasuke ku mlandu wokhudza udindo wake monga woyang’anila, anafunikila kupeleka umboni wa zimene zinacitika. Mwacitsanzo, anafunikila kuonetsa mwini wake mbali zina zotsala za nyama yakufayo. Mwini wake akapenda umboniwo, anafunika kuuza woyang’anila nyamazo kuti alibe mlandu.
Mfundo imeneyi inali kugwilanso nchito kwa munthu aliyense amene anapatsidwa udindo woyang’anila katundu, ngakhalenso m’banja. Mwacitsanzo, mwana wamwamuna wamkulu anali na udindo mwalamulo woyang’anila abale ake komanso azilongosi ake. Conco, tingamvetse cifukwa cake Rubeni monga mwana wamkulu anadela nkhawa za moyo wa Yosefe pamene abale ake ena anakamba zakuti amuphe. “Iye anati: ‘Ayi, tisacite kuwononga moyo wake.’ . . . ‘Musakhetse magazi ayi . . . musamuvulaze.’ Nkhaniyi ili pa Genesis 37:18-30. “Colinga cake cinali cakuti amupulumutse kwa iwo ndi kum’bwezela kwa bambo ake.” Ndipo pamene Rubeni anapeza kuti Yosefe kulibe, anada nkhawa kwambili moti “anang’amba zovala zake” ndipo anafuula kuti: “Mwana ujatu kulibe! Kalanga ine, ndilowela kuti ine?” Anali kudziŵa kuti adzapatsidwa mlandu cifukwa ca kusoŵa kwa Yosefe. Pofuna kupewa mlanduwo, abale ake mwamacenjela anapeleka umboni wabodza wakuti Yosefe anaphedwa na cilombo cakuchile. Anacita mwa kuviika mkanjo wa Yosefe m’magazi a mbuzi. Ndiyeno anapeleka umboniwo kwa Yakobo tate wawo, amene anali woweluza wawo. Yakobo anagamula kuti Rubeni analibe mlandu poona mkanjo wa Yosefe wamagazi umene abale ake anapeleka monga umboni. Mwa ici, Yakobo anatsimikiza kuti Yosefe anali ataphedwa.—Gen. 37:31-33.
MAY 11-17
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 38-39
“Yehova Sanamusiye Yosefe”
‘Ndingacitilenji Coipa Cacikulu N’kucimwila Mulungu?’
Baibo imakamba kuti: “Tsopano Yosefe uja, Aisimaeli anapita naye ku Iguputo, ndipo kumeneko anakam’gulitsa kwa Potifara. Potifara anali Mwiiguputo, yemwe anali nduna ya panyumba ya Farao, komanso mkulu wa asilikali olondela mfumu.” (Genesis 39:1) Lembali litithandiza kuona mmene Yosefe ananyozekela pogulitsidwa kaciŵili. Anangokhala ngati katundu wamalonda! Ganizilani mmene anali kumvelela pamene Potifara anamutenga na kumapita naye kunyumba kwake kudutsa m’njila za mumzinda mwa anthu pikiti-pikiti. Ndipo m’mbali mwa njilayi munali mashopu ambili-mbili.
Atafika kunyumba ya Potifara, zimene Yosefe anaona zinali zacilendo zokha-zokha. Iye anali asanaonepo nyumba yotelo cibadwile. Kuyambila ali mwana, anali kukhala m’mahema ndipo anali kungokhalila kusamuka-samuka na nkhosa zawo. Popeza Potifara anali wolemela, anali na cinyumba cacikulu kwambili komanso cokongola. Akatswili ofukula zinthu zakale amakamba kuti anthu a ku Iguputo anali kukhala na minda ya maluŵa yokongola kwambili. M’mbali mwa mindayi anali kubyalamo mitengo, komanso mkati mwake anali kukumbamo madamu omwe anali kubyalamo zomela zina za m’madzi. Nyumba zina anali kuzimanga pakati pa minda ya maluŵa, ndipo izi zinali kupangitsa kuti m’nyumbamo muziloŵa kamphepo kayazi-yazi. Nyumba zimenezi zinali kukhala na mawindo ambili, zipinda zogonamo zambili komanso cipinda codyelamo cacikulu. Anali kumanganso nyumba zogonamo anchito.
‘Ndingacitilenji Coipa Cacikulu N’kucimwila Mulungu?’
Sitidziŵa zambili za mmene ndende za akaidi ku Iguputo zinalili pa nthawiyo. Akatswili ofukula zinthu zakale anapeza malo olingana na amenewa. Zioneka kuti ndendezo zinali na citetezo cokhwima, komanso zinali kukhala na zipinda zamdima. Yosefe anafotokoza kuti ndende imene anaikidwamo inali ngati ‘dzenje,’ zimenezi zikuonetsa kuti munthu akapitako anali kuona kuti kwake kwatha. (Genesis 40:15, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu) Buku la Masalimo limaonetsa kuti Yosefe anali kukhala mozunzika kwambili m’ndende imeneyi. Limati: “Anasautsa mapazi ake ndi matangadza, anam’manga ndi maunyolo.” (Salimo 105:17, 18) Nthawi zina akaidi a ku Iguputo anali kuwamanga manja kumbuyo, ndipo ena anali kuwamangilila citsulo m’khosi. Yosefe zinali kumupweteka poona kuti akuzunzidwa popanda cifukwa.
Ndipo sikuti Yosefe anangokhala m’ndendemu kanthawi kocepa. Baibo imaonetsa kuti anakhalamo kwa zaka zambili. Iye sanali kuganiza zoti adzatulukanso m’ndendeyi. Ndiye kodi n’ciani cinam’thandiza kuti asataye mtima?
Baibo imati: “Yehova anapitilizabe kukhala ndi Yosefe ndi kumusonyeza kukoma mtima kosatha.” (Genesis 39:21) Zinthu monga matangadza, zipupa za ndende, komanso malo a mdima, sizingalepheletse Yehova kukonda atumiki ake. (Aroma 8:38, 39) N’zosakayikitsa kuti pa nthawi imene Yosefe anali m’ndende anali kupemphela kwa Atate wake wakumwamba n’kumamuuza nkhaŵa zake. Zimenezi zinamuthandiza kuti akhale na mtendele wa m’maganizo umene “Mulungu amene amatitonthoza m’njila iliyonse” amapeleka. (2 Akorinto 1:3, 4; Afilipi 4:6, 7) Kodi Yehova anam’thandizanso bwanji Yosefe? Baibo imakamba kuti Yehova anacititsa “mkulu wa ndende kum’konda Yosefe.”
‘Ndingacitilenji Coipa Cacikulu N’kucimwila Mulungu?’
Baibo imati: “Yehova anapitilizabe kukhala ndi Yosefe ndi kumusonyeza kukoma mtima kosatha.” (Genesis 39:21) Zinthu monga matangadza, zipupa za ndende komanso malo a mdima sizingacititse kuti Yehova asiye kukonda atumiki ake. (Aroma 8:38, 39) N’zosakayikitsa kuti pa nthawi imene Yosefe anali m’ndende anali kupemphela kwa Atate wake wakumwamba n’kumamuuza nkhaŵa zake. Zimenezi zinamuthandiza kuti akhale na mtendele wa m’maganizo umene “Mulungu amene amatitonthoza m’njila iliyonse” amapeleka. (2 Akorinto 1:3, 4; Afilipi 4:6, 7) Kodi Yehova anamuthandizanso bwanji Yosefe? Baibo imakamba kuti Yehova anacititsa “mkulu wa ndende kum’konda Yosefe.”
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
it-2 555
Onani
Onani [Liwuli licokela kutanthauzo la mawu akuti “mphamvu zanga zobelekela; mphamvu zambili koposa”]
Anali mwana waciŵili wa Yuda kwa mkazi wacikanani dzina lake Sua. (Gen. 38:2-4;1 Mbiri 2:3) Ere mkulu wake wa Onani anaphedwa na Yehova cifukwa anali kucita zoipa. Anaphedwa panthawi imene analibe mwana. Conco, Yuda anauza Onani kuti acite cikwati ca cokolo na Tamara, mkazi amene anali wa Ere. Ngati akanabeleka mwana, mwanayo sakanakhala wa Onani. Ndipo mwanayo ndiye akanalandila coloŵa ca mwana woyamba wa Ere, kumbali ina ngati sanabale mwana wodzalandila coloŵa, Onani ndiye akanatenga coloŵa cimeneco. Nthawi zonse akagona na Tamara, anali “kutaya pansi umuna wake.” Apa sindiye kuti Onani anali kudzipukusa malisece ayi, cifukwa nkhaniyo imakamba kuti “nthawi zonse akagona ndi mkazi wa m’bale wakeyo,” anali kutaya pansi mbewu yake yacimuna. Mwacionekele anali kulekeza panjila pogonana. Onani anali kutayila pansi mwadala mbewu yake yacimuna kuti isaloŵe m’cibelekelo ca Tamara. Iye anaphedwa na Yehova cifukwa ca kusamvela atate ake, kusilila kwake mwansanje, komanso cifukwa ca kucimwila makonzedwe a banja, osati cifukwa cakuti anali kudzipukusa ayi. Pa nthawi imene Onani anaphedwa analibe mwana.—Gen. 38:6-10; 46:12; Num. 26:19.
w04 1/15 30 ¶4-5
Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga
Yuda analakwa cifukwa sanapeleke Tamara kwa mwana wake wamwamuna Sela, monga mwa lonjezo. Komanso anagona na mkazi amene anamuganiza kuti anali hule ya pakacisi. Uku kunali kucimwila Mulungu, cifukwa analamula kuti kugonana kuzingocitika kwa anthu okwatilana okha basi. (Genesis 2:24) Komabe, sikuti Yuda anagonadi na mkazi wadama ayi. M’malo mwake, iye mosadziŵa anatenga malo a mwana wake Sela pa ukwati wapacilamu ndipo anakhala tate wa ana ovomelezeka mwa lamulo.
Kunena za Tamara, zimene iye anacita sicinali ciwelewele. Amphundu ake aamuna sanaonedwe ngati ana apathengo. Boazi wa ku Betelehemu atakwatila mtsikana wacimoabu Rute paukwati wapacimulamu, akulu-akulu a ku Betelehemu anakamba zinthu zabwino kwambili zokhudza mwana wa Tamara, Perezi, pouza Boazi kuti: “Ndipo kudzela mwa ana amene Yehova adzakupatsa kwa mtsikanayu, nyumba yako ikhale ngati nyumba ya Perezi, amene Tamara anabelekela Yuda.” (Rute 4:12) Perezi akupezekanso pa mndandanda wa maina a makolo a Yesu Khristu.—Mateyu 1:1-3; Luka 3:23-33.
MAY 18-24
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 40-41
“Yehova Anapulumutsa Yosefe”
“Kodi Mulungu Sindiye Amamasulila Maloto?”
Ngakhale kuti wopelekela cikho uja anamuiŵala Yosefe, Yehova sanamuiŵale. Usiku wina, Mulungu anapangitsa Farao kulota maloto aŵili odabwitsa. M’maloto oyamba, mfumuyo inaona ng’ombe 7 zikutuluka mumtsinje wa Nailo, ndipo ng’ombezo zinali zokongola m’maonekedwe komanso zonenepa. Kenako anaonanso ng’ombe zina 7 zonyansa komanso zowonda. Ng’ombe zowondazo zinayamba kudya zonenepa zija. Pambuyo pake, Farao analota maloto ena. Analota ngala za tirigu 7 zazikulu bwino zikutuluka paphesi limodzi. Kenako anaona ngala zina 7 zikutuluka pambuyo pa zoyambazo. Ngalazo zinali zonyala komanso zowauka, ndipo zinameza ngala 7 zazikulu bwino zija. Kutaca m’mawa, Farao anavutika kwambili maganizo. Cotelo anaitanitsa ansembe onse amatsenga ndi amuna anzelu onse a mu Iguputo kuti amasulile malotowo. Koma onse analephela. (Genesis 41:1-8) Mwina anthuwo anasoŵelatu conena kapena anali kumasulila zinthu zotsutsana. Mulimonse mmene zinalili, Farao anagwilitsidwa mwala. Komabe, iye anali kufunitsitsa kudziŵa tanthauzo la malotowo.
Kenako, wopelekela cikho uja anakumbukila Yosefe. Cikumbumtima cake citamuvuta, anauza Farao kuti iye na mkulu wa ophika mkate analota maloto ali m’ndende zaka ziŵili zapitazo, ndipo mnyamata wina wanzelu amene ali m’ndendemo anamasulila malotowo. Mwamsanga, Farao anatuma anthu kuti akaitane Yosefe kundendeko.—Genesis 41:9-13.
“Kodi Mulungu Sindiye Amamasulila Maloto?”
Yehova amakonda anthu odzicepetsa komanso okhulupilika. Conco n’zosadabwitsa kuti anathandiza Yosefe kudziŵa tanthauzo la maloto amene amuna anzelu komanso ansembe analephela kumasulila. Yosefe anafotokoza kuti maloto aŵili a Farao anali na tanthauzo limodzi. Anati popeza Farao analota kaŵili malotowo, ndiye kuti Yehova anatsimikiza mtima kucita zimenezo. Ng’ombe zonenepazo, ndiponso ngala 7 zooneka bwino, zinali kuimila zaka 7 zimene anthu mu Iguputo anali kudzakhala na cakudya cambili. Koma ng’ombe zowonda ndiponso ngala zopanda kanthu zinali kuimila zaka 7 za njala zimene zinali kudzabwela pambuyo pa zaka za cakudya cambili. Iye ananenanso kuti cakudya conse ca m’dzikolo cidzatha cifukwa ca njalayo.—Genesis 41:25-32.
“Kodi Mulungu Sindiye Amamasulila Maloto?”
Farao anasunga lonjezo lake, ndipo patapita nthawi yocepa anaveka Yosefe malaya amtengo wapatali. Farao anapatsanso Yosefe cheni yam’khosi yagolide, mphete yacifumu, galeta laciŵili laulemu, komanso ulamulilo wopita kulikonse m’dzikolo kukagwila nchito yake yosonkhanitsa cakudya. (Genesis 41:42-44) Conco, pa tsiku limodzi cabe Yosefe anacoka m’ndende na kukakhala m’nyumba ya mfumu. Patsikulo, pouka m’mawa iye anali mkaidi wonyozeka, koma pokagona usiku anali wolamulila waciŵili kwa Farao. Pamenepa n’zoonekelatu kuti iye anadalitsidwa cifukwa cokhulupilila Yehova Mulungu. Pa zaka zonsezo, Yehova anaona mavuto onse amene mtumiki wake anali kukumana nawo. Iye anathetsa mavuto a Yosefe panthawi yoyenela ndiponso m’njila yoyenela. Colinga ca Yehova sicinali kungothetsa mavuto amene Yosefe anali kukumana nawo, koma anali kufunanso kuti adzateteze mtundu wa Isiraeli mtsogolo. M’nkhani yotsatila, tidzaona mmene Mulungu anacitila zimenezi.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
Kodi Mudziŵa?
N’cifukwa ciani Yosefe anagela tsitsi pokaonekela pamaso pa Farao?
Buku la Genesis limanena kuti Farao analamula zoti mkaidi wina waciheberi amasulidwe mwamsanga. Anali kufuna kuti mkaidiyo akamasulile maloto ake amene anali atamuzunguza mutu. Mkaidiyo anali Yosefe, ndipo anali atakhala m’ndende kwa zaka zingapo. Ngakhale kuti Farao anali kumufuna mwamsanga, Yosefe anayamba wagela tsitsi coyamba. (Genesis 39:20-23; 41:1, 14) Zimene anacita zionetsa kuti anali kudziŵa bwino cikhalidwe ca anthu a ku Iguputo.
Mitundu yambili kuphatikizapo Aheberi, anali kukonda kusunga ndevu. Koma mosiyana na zimenezi, buku lina limanena kuti, “ni anthu a ku Iguputo okha amene sanali kugwilizana na zakuti munthu azisunga ndevu.”—McClintock and Strong’s Cyclopedia of Biblical, Theological, and Ecclesiastical Literature.
Kodi anthu a ku Iguputo anali kugela ndevu zokha? Magazini inanso inakamba kuti munthu akamapita kwa Farao anali kufunika kudzikonza bwino-bwino ngati kuti akupita ku kacisi. (Biblical Archaeology Review) Ngati zimenezi zili zoona, ndiye kuti Yosefe anali kufunika kucotsa tsitsi lonse pathupi lake.
w09 11/15 28 ¶14
Tiyenela Kukhala Aulemu Popeza Ndife Atumiki a Mulungu
14 Makolo oopa Mulungu m’nthawi za m’Baibo anali kuyesetsa kuphunzitsa ana awo ulemu kunyumba. Onani mmene Abulahamu na mwana wake Isaki anali kulankhulilana mwaulemu pa Genesis 22:7. Nayenso Yosefe anaonetsa kuti anaphunzitsidwa bwino na makolo ake. Ataikidwa m’ndende, Yosefe anali kulankhula mwaulemu ngakhale kwa akaidi anzake. (Gen. 40:8, 14) Mawu amene Yosefe analankhula kwa Farao anaonetsa kuti iye anaphunzitsidwa mmene angalankhulile mwaulemu kwa munthu waudindo wapamwamba.—Gen. 41:16, 33, 34.
MAY 25-31
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 42-43
“Yosefe Acita Zinthu Modziletsa Kwambili”
“Kodi Ine Ndatenga Malo a Mulungu?”
Koma Yosefe anaŵazindikila abale akewo. Atawaona akumugwadila poonetsa ulemu, anakumbukila zimene analota zaka zambili m’mbuyomo. Nkhaniyi imati: “Nthawi yomweyo Yosefe anakumbukila maloto” onena kuti abale ake adzamugwadila, amene Yehova anamulotetsa ali mnyamata. (Genesis 37:2, 5-9; 42:7, 9) Ndiye kodi Yosefe anacita bwanji? Kodi anathamanga n’kuwakumbatila? Kapena anaganiza zowabwezela zoipa zomwe anamucitila zija?
“Kodi Ine Ndatenga Malo a Mulungu?”
Mwina zimene zinacitikila Yosefe, sizingakucitikileni imwe ndendende. Koma masiku ano anthu a m’mabanja ambili amazondana komanso amacitilana nsanje. Za conco zikacitika, anthu ambili amaganiza zobwezela. Koma ni bwino kutengela citsanzo ca Yosefe. Tingacitenso bwino kuganiza zimene tingacite kuti tikondweletse Yehova za conco zikacitika. (Miyambo 14:12) Musaiwale kuti kukhala pa mtendele ndi anthu a m’banja lathu komanso na Mulungu n’kofunika kwambili.—Mateyu 10:37.
“Kodi Ine Ndatenga Malo a Mulungu?”
Yosefe anakonza zoŵayesa abale akewo kuti aone ngati anasintha. Anayamba na kulankhula nawo mwaukali kudzela mwa womasulila. Anawauza abale akewo kuti anali akazitape ndipo abwela kudzaona dziko lawolo. Koma iwo anakanitsitsa kuti si akazitape ndipo anamuuza zakuti ali na mng’ono wawo amene watsala kunyumba. Yosefe atamva kuti mng’ono wake akali moyo, anakondwela kwambili. Komabe anayesetsa kuugwila mtima kuti asadziŵike kuti wakondwela na zimene wamvela. Kenako anawauza kuti: “Ndikuyesani.” Ndiyeno anawauza kuti adzabwele na mng’ono wawoyo kuti adziŵe ngati anali kukamba zoona. Atakambilana nawo kwa kanthawi, anawauza kuti apite kukatenga mng’ono wawoyo, koma mmodzi wa iwo atsale ndipo akhale mkaidi.—Genesis 42:9-20.
it-2 108 ¶4
Yosefe
Cifukwa ca zimene zinali kuwacitikila, abale ake a Yosefe anayamba kuona kuti akulandila cilango cocokela kwa Yehova cifukwa comugulitsa ku ukapolo zaka za kumbuyoko. Pa maso pa m’bale wawo amene panthawiyo anali asanamuzindikilebe, anayamba kukambilana za colakwa cawo. Pamene Yosefe anamvela zimene anali kukambilana zoonetsa kulapa, anakhudzidwa mtima kwambili cakuti anacoka pamaso pawo na kukalila. Pobwelela, Yosefe anatenga Simiyoni n’kumumanga kufikila nthawi imene abale akewo adzabwele na m’bale wawo wamng’ono.—Gen. 42:21-24.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
it-2 795
Rubeni
Makhalidwe abwino ena a Rubeni anaonekela kwambili pamene anacondelela abale ake 9 kuti aponye Yosefe m’citsime copanda madzi m’malo momupha. Rubeni anacita izi na colinga cakuti mwamseli abwelele na kukapulumutsa Yosefe m’citsimeco. (Gen. 37:18-30) Patapita zaka zoposa 20, abale ake amenewa atayamba kukambilana kuti iwo anali kuonedwa ngati akazitape ku Iguputo cifukwa cocitila m’bale wawo zacipongwe, Rubeni anawakumbutsa kuti iye sanagwilizane nawo pamene anafuna kupha Yosefe. (Gen. 42:9-14, 21, 22) Komanso, pamene Yakobo anakana kuti iwo atenge Benjamini n’kupita naye ku Iguputo pa ulendo wawo waciŵili, Rubeni ni amene anapeleka ana ake aŵili monga cikole, iye anati: “Ndikapanda kudzam’bwezela kwa inu Benjamini, mudzaphe ana anga aŵili.”—Gen. 42:37.
w04 1/15 29 ¶1
Mfundo Zazikulu za M’buku la Genesis—Cigawo Caciŵili
43:32—N’cifukwa ciani kwa Aiguputo kudya pamodzi na Aheberi kunali konyansa? Kweni-kweni, zimenezi zinali conco mwina cifukwa ca kusankhana zipembedzo kapena mtundu. Aiguputo anali kunyansidwanso ndi abusa. (Genesis 46:34) Cifukwa ciani? Abusa ayenela kuti anali anthu otsika kwambili ku Iguputo. Kapena mwina cifukwa cakuti malo olima anali ocepa, Aiguputo anali kunyansidwa ndi anthu amene anali kufuna-funa malo odyetselako ziŵeto.