LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwbr20 April masa. 1-4
  • Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki
  • Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu—2020
  • Tumitu
  • APRIL 13-19
  • APRIL 20-26
  • APRIL 27–MAY 3
Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu—2020
mwbr20 April masa. 1-4

Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki

APRIL 13-19

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 31

“Yakobo na Labani Acita Pangano la Mtendele”

it-1 883 ¶1

Galeeda

Yakobo na Labani anakambilana nkhani imene anasemphanapo maganizo, ndiyeno anayanjana, kenako anacita pangano. Mwa ici, Yakobo anaimika mwala wacikumbutso na kuuza “abale” ake kuti aunjike miyala, mwina monga thebulo, ndipo anadyelapo cakudya ca panganolo. Ataunjika miyalayo, Labani anacha malowo amene dzina lake m’Ciaramu (M’cisiriya) ni “Yegara-sahaduta,” koma Yakobo anawacha “Galeeda,” dzina lofanana nalo m’Ciheberi. Labani anati: “Mulu wa miyalawu [M’ciheberi., gal] ndi mboni [M’ciheberi., ʽedh] yathu lelo pakati pa ine ndi iwe.” (Gen. 31:44-48) Mulu wa miyala (na cipilila ca mwala) zinali kucitila umboni kwa anthu onse odutsa pamalopo. Zinali monga mmene vesi 49 ikambila kuti: “Nsanja ya Mlonda [M’ciheberi., mits·pahʹ],” kutanthauza kucitila umboni kuti Yakobo na Labani anagwilizana zakuti adzasunga mtendele pakati pawo ndiponso pakati pa mabanja awo. (Gen. 31:50-53) Pambuyo pake, anthu anayamba kugwilitsila nchito miyala monga mboni m’njila yofanana na imeneyi.—Yos. 4:4-7; 24:25-27.

it-2 1172

Nsanja ya Mlonda

Yakobo anaunjika mulu wa miyala na kuucha “Galeeda” (kutanthauza “Mulu wa Umboni”) ndiponso “Nsanja ya Mlonda.” Ndiyeno Labani anati: “Yehova ayang’anile pakati pa ine ndi iwe, pamene tisiyana wina ndi mnzake.” (Gen. 31:45-49) Mulu wa miyala umenewu unali kucitila umboni kuti Yehova anali kuyang’ana kuti aone ngati Yakobo na Labani anali kusunga pangano lawo la mtendele.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

it-2 1087-1088

Aterafi

Zimene akatswili ofukula zinthu zakale anapeza ku Mesopotamiya komanso kumadela owazungulila, zionetsa kuti munthu akakhala na mafano a aterafi, unali kukhala umboni wakuti anali woyenelela kulandila colowa ca banja. Malinga na zolembedwa za pa mwala wina wosema umene anaupeza ku Nuzi, zionetsa kuti m’zocitika zina, mkamwini akakhala na aterafi anali kukhala na mphamvu zokaonekela kukhoti, ndipo anali na ufulu wotenga cuma ca apongozi ake amene anamwalila. (Ancient Near Eastern Texts, yolembedwa na J. Pritchard, mu 1974, mapeji. 219, 220, na ftn 51) Mwina Rakele, pokhala na maganizo amenewa, anaona kuti m’pake kutenga aterafi a atate ake, cifukwa ca zacinyengo zimene iwo anacitila mwamuna wake Yakobo. (Yelekezelani na Gen. 31:14-16.) Kukhala na aterafi kunali kofunika kwambili cifukwa kunali kupangitsa munthu kukhala na ufulu wolandila colowa. Izi zikuonetsanso cifukwa cimene cinapangitsa Labani kukhala na nkhawa yakuti akalande aterafiwo, iye anafika mpaka potenga abale ake paulendo wa masiku 7 wolondola Yakobo. (Gen. 31:19-30) Yakobo sanadziŵe ciliconse pa zimene Rakele anacita (Gen. 31:32), ndipo palibe paliponse pamene paonetsa kuti nthawi ina iye anagwilitsila nchito aterafiwo kuti atenge coloŵa ca ana a Labani. Yakobo analibe nawo nchito mafano. Ndi iko komwe, aterafiwo ayenela kuti anatayidwa pamene Yakobo anafocela milungu yonse yacilendo imene anthu a m’banja lake anapeleka kwa iye. Anaifocela pansi pa mtengo waukulu pafupi na Sekemu.—Gen. 35:1-4.

w13 3/15 21 ¶8

Yehova Ni Malo Athu Okhalamo

8 Yakobo atafika ku Harana, amalume ake a Labani anamulandila bwino, kenako anam’patsa Leya na Rakele kuti akhale akazi ake. Koma Labani anayamba kupusitsa Yakobo, n’kumusinthila malipilo ake maulendo 10. (Gen. 31:41, 42) Ngakhale zinali conco, Yakobo anapilila zonse zimenezi, ndipo sanali kukayikila kuti Yehova apitiliza kumusamalila. Yehova anamusamaliladi. Pa nthawi imene Mulungu anamuuza kuti abwelele ku Kanani, Yakobo anali na “ziweto zambili, anchito aakazi ndi aamuna, ngamila ndi abulu.” (Gen. 30:43) Poyamikila Mulungu mocokela pansi pa mtima, Yakobo anapemphela kuti: “Ine ndine wosayenelela kukoma mtima kosatha ndi kukhulupilika konseku, kumene mwandionetsa ine mtumiki wanu. Ndinawoloka Yorodano ndilibe kanthu, koma ndodo yokha, ndipo tsopano ndili ndi magulu aŵiliwa.”—Gen. 32:10.

APRIL 20-26

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 32-33

“Kodi Mukulimbikila kuti Mupeze Madalitso?”

w03 8/15 25 ¶3

Kodi Mukufuna Yehova Mwakhama?

M’Malemba muli zitsanzo zambili za anthu amene anayesetsa kwambili kufuna Yehova. Mmodzi wa iwo anali Yakobo, amene anagwebana mwamphamvu na mngelo wa Mulungu mpaka mbandakuca. Mngelo ameneyu anali na thupi la munthu. Pacifukwa cimeneci, Yakobo anapatsidwa dzina lakuti Isiraeli (Wolimbana na Mulungu) cifukwa ‘analimbana ndi Mulungu,’ kapena kuti anakakamila, kuyesetsa, kugwebana na Mulungu. Mngeloyo anam’dalitsa cifukwa ca kulimbika kwake.—Genesis 32:24-30.

it-2 190

Kulemala, kukhala wolemala

Kulemala kwa Yakobo. Tsiku lina Yakobo ali na zaka pafupi-fupi 97, analimbana na mngelo wa Mulungu usiku wonse. Iye sanagonje pogwebana na mngeloyo mpaka atam’dalitsa. Polimbana, mngeloyo anagwila nsukunyu ya ciŵelo (nchafu) ca Yakobo cakuti inacoka pamalo pake. Zotulukapo zake, Yakobo anayamba kuyenda motsimphina. (Gen. 32:24-32; Hos. 12:2-4) Izi zinali kukumbutsa Yakobo kuti ‘analimbana ndi Mulungu [mngelo wa Mulungu] ndi anthu, ndipo potsilizila pake [iye] anapambana,’ mogwilizana na zimene mngelo anakamba. Koma m’ceni-ceni iye sanam’gonjetse mngelo wamphamvu wa Mulungu. Cinali colinga ca Mulungu cimene analolela Yakobo kulimbana na mngelo. Anali kufuna kudziŵa ngati Yakobo anali wofunitsitsa kulandila madalitso a Mulungu na kuwayamikila.

it-1 1228

Isiraeli

1. Dzina limene Mulungu anapatsa Yakobo pamene anali na zaka pafupi-fupi 97. Tsiku lina usiku pamene Yakobo anali kudutsa m’cigwa ca Yaboki paulendo wake wokakumana na m’bale wake Esau, anayamba kulimbana na munthu amene pambuyo pake anam’zindikila kuti ni mngelo. Cifukwa cakuti Yakobo anapilila pa kugwebana kumeneku, dzina lake linasinthidwa kukhala Isiraeli, monga cizindikilo cakuti Mulungu wam’dalitsa. Pofuna kuti azikumbukila zimenezi, Yakobo anacha malowo Penieli kapena kuti Penueli. (Gen. 32:22-31) Pambuyo pake, kusinthidwa kwa dzina lake kunatsimikizilidwa na Mulungu pamene Yakobo anali ku Beteli, ndipo kucokela nthawiyo mpaka pamene anamwalila, kambili Yakobo anali kuchulidwa kuti Isiraeli. (Gen. 35:10, 15; 50:2; 1 Mbiri 1:34) Dzina lakuti Isiraeli limapezeka nthawi zoposa 2,500 m’Baibo, koma kambili dzinali limakamba za mbadwa za Yakobo monga mtundu.—Eks. 5:1, 2.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

w10 6/15 22 ¶10-11

Kulankhula Mwaulemu Kumathandiza Kuti Tizikhala Bwino na Ŵanthu

10 Kulankhula mwaulemu ndiponso momasuka kumathandiza kuti anthu azigwilizana komanso azikhala mwamtendele. Ndipo kuyesetsa kuti tizigwilizana kwambili ndi anthu, kungathandize kuti tizilankhulana nawo momasuka. Kuyesetsa kupeza mpata woti tiziceza na ŵena, kuwathandiza, kuwapatsa mphatso ndiponso kuwaceleza, kungathandizenso kuti tizilankhula nawo momasuka. Mwakucita zimenezi, ‘tingaunjike makala a moto’ pa anthuwo ndipo zimenezi zingacititse kuti makhalidwe awo abwino aonekele ndipo zingakhale zosavuta kuti tizilankhulana nawo bwino-bwino.—Aroma 12:20, 21.

11 Yakobo anali kudziŵa kuti kucitila ena zabwino kumathandiza kuti anthu agwilizanenso. Pa nthawi ina, m’bale wake Esau anakwiya kwambili ndipo Yakobo anathaŵa poopa kuti amupha. Patapita zaka zambili iye anaganiza zobwelela kwawo. Esau anapita kukam’cingamila atatenga amuna okwana 400. Yakobo anapempha Yehova kuti am’thandize. Kenako anatumizila Esau mphatso zambili za ziŵeto. Mphatso zimenezi zinathandiza kwambili. Pamene anakumana, n’kuti mtima wa Esau utakhala kale m’malo, moti anathamangila Yakobo n’kumukumbatila.—Gen. 27:41-44; 32:6, 11, 13-15; 33:4, 10.

it-1 980

Mulungu, Mulungu wa Isiraeli

Cifukwa ca zimene zinacitika atakumana na mngelo wa Yehova ku Penieli, Yakobo anapatsidwa dzina lakuti Isiraeli. Ndipo atakumana mwamtendele na m’bale wake Esau, iye anakhala ku Sukoti kenako anapita ku Sekemu. Kumeneko, iye anagula malo kwa ana a Hamori ndipo anamangapo hema wake. (Gen. 32:24-30; 33:1-4, 17-19) “Atatelo, anamangapo guwa lansembe n’kulicha Mulungu, Mulungu wa Isiraeli.” (Gen. 33:20) Mwakuchula dzina lake latsopano lakuti Isiraeli poliphatikiza na dzina la guwa lansembe, Yakobo anaonetsa kuti anavomeleza na kuyamikila dzinalo. Ndiponso Mulungu anam’teteza pom’tsogolela paulendo wobwelela ku Dziko Lolonjezedwa. Dzina limeneli limapezeka cabe kamodzi m’Malemba.

APRIL 27–MAY 3

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 34-35

“Zotulukapo Zoopsa za Mayanjano Oipa”

w97 2/1 30 ¶4

Sekemu Mzinda wa m’Cigwa

Kodi anyamata amumzinda anamuona bwanji namwali ameneyu amene anali kucezela mzinda wawo kaŵili-kaŵili—mwacionekele ali yekha? Mwana wa kalonga “anaona mtsikanayu, . . . anamutenga n’kumugwilila.” Kodi n’cifukwa ninji Dina anadziloŵetsa m’ngozi mwa kugwilizana na Akanani aciwelewele? Kodi cingakhale cifukwa cakuti anali kufuna kuceza na atsikana a msinkhu wake? Kodi anali cabe wouma khosi, ndiponso wodzidalila monga azilongosi ake ena? Ŵelengani nkhaniyi m’Genesis, na kuyesa kumvetsetsa nsautso na manyazi amene Yakobo na Leya anawamva cifukwa ca maulendo a mwana wawo okaceza ku Sekemu na zotulukapo zake zoipa.—Genesis 34:1-31; 49:5-7; onaninso Nsanja ya Mlonda, June 15, 1985, peji 31.

lvs 124 ¶14

“Thaŵani Dama”

14 Kwa Sekemu, zimene anacitazo zinali zoyenela komanso zacibadwa. Cifukwa cokhumbila Dina, “anamutenga n’kumugwilila.” (Ŵelengani Genesis 34:1-4.) Vuto limeneli linaputa mavuto ena amene anabweletsa tsoka pa Dina, na banja lawo lonse.—Genesis 34:7, 25-31; Agalatiya 6:7, 8.

w09 9/1 21 ¶1-2

Kodi Muyenela Kucita Ciani Wina Akakukhumudwitsani?

Nthawi zambili anthu amafuna kubwezela kuti mtima wawo ukhale pansi. Mwacitsanzo, Baibo imanena kuti ana a Yakobo, amene anali kholo laciheberi, atamva kuti Sekemu, amene anali wacikanani wagwilila mlongo wawo Dina, ‘anapwetekedwa mtima kwambili ndipo anakwiya koopsa.’ (Genesis 34:1-7) Pobwezela zinacitikazo, ana aŵili a Yakobo anakonza ciwembu copha Sekemu na abale ake. Simeyoni na Levi atapusitsa amuna a mumzindawu wa ku Kanani, analowa n’kukapha Sekemu ndi amuna onse.—Genesis 34:13-27.

Kodi zimenezi zinathetsa nkhaniyo? Ayi, cifukwa Yakobo atamva zimene ana ake anacita, anawadzudzula kuti: “Mwandiputila cidani, ndipo mwandinunkhitsa kwa anthu a m’dziko lino, . . . ndipo iwowa ndithu asonkhana pamodzi n’kutiukila. Atithila nkhondo n’kutitha tonse, ine ndi banja langa.” (Genesis 34:30) Inde, m’malo mothetsa nkhaniyo, kubwezela kunakulitsa vutolo. Tsopano Yakobo na banja lake anali kukhala mwamantha, ndipo anayenela kusamala poopa anthu a m’mizinda yoyandikana nawo amene anakwiya na zimene zinacitikazo. Zioneka kuti pofuna kupewa zimenezi, Mulungu analangiza Yakobo na banja lake kuti asamukile ku Beteli.—Genesis 35:1, 5.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

it-1 600 ¶4

Debora

1. Mlezi wa Rabeka. Pamene Rabeka anali kucoka ku nyumba kwa atate ake a Betuele kupita ku Palesitina kukakwatiwa na Isaki, Debora anapita naye pamodzi. (Gen. 24:59) Pambuyo potumikila m’nyumba ya Isaki kwa zaka, Debora anakhala m’banja la Yakobo, mwina pambuyo pa imfa ya Rabeka. Mwacionekele, Debora anamwalila pambuyo pa zaka 125 kucokela pamene Isake anakwatila Rabeka, ndipo anamuika ku Beteli munsi mwa mtengo waukulu. Mtengowo anaucha (Aloni-bakuti, kutanthauza “Cimtengo Cacikulu Colililapo”), kuonetsa kuti Yakobo na banja lake anali kum’konda kwambili.—Gen. 35:8.

w17.12 14

Mafunso Ocokela Kwa Oŵelenga

M’nthawi ya Aisiraeli, kodi kukhala pa mzele wa makolo a Mesiya kunadalila kukhala woyamba kubadwa?

M’mbuyomu, takambapo zoonetsa zimenezi. Ndipo zinaoneka kukhala zogwilizana na lemba la Aheberi 12:16. Limati Esau ‘sanayamikile zinthu zopatulika,’ ndipo “anapeleka [kwa Yakobo] udindo wake monga woyamba kubadwa pousinthanitsa ndi cakudya codya kamodzi kokha.” Izi zinamveka ngati kuti pamene Yakobo anatenga udindo wokhala woyamba kubadwa, analoŵa pa mzela wa makolo a Mesiya.—Mat. 1:2, 16; Luka 3:23, 34.

Komabe, kuzionanso bwino nkhani za m’Baibo kuonetsa kuti munthu sanafunikile kukhala woyamba kubadwa kuti akhale kholo la Mesiya. Tiyeni tioneko maumboni ena:

Pa ana a Yakobo (Isiraeli), woyamba kubadwa mwa Leya anali Rubeni. Pambuyo pake, Yakobo anabala Yosefe, mwana wake woyamba kwa mkazi wake wokondeka, Rakele. Pamene Rubeni anacita colakwa, udindo monga woyamba kubadwa unacoka kwa iye n’kupita kwa Yosefe. (Gen. 29:31-35; 30:22-25; 35:22-26; 49:22-26; 1 Mbiri 5:1, 2) Ngakhale n’conco, mzele wa makolo a Mesiya sunapitile mwa Rubeni kapena Yosefe, koma mwa Yuda, mwana wacinayi wa Yakobo kwa Leya.—Gen. 49:10.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani