Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki
MARCH 2-8
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 22-23
“Mulungu . . . Anamuyesa Abulahamu”
w12 1/1 23 ¶4-6
Kodi N’cifukwa Ciani Mulungu Anauza Abulahamu Kuti Apeleke Mwana Wake Nsembe?
Ganizilani mawu amene Yehova anauza Abulahamu. Iye anati: “Tenga Isaki mwana wako mmodzi yekhayo, mwana wako amene umamukonda kwambiliyo, ndipo . . . ukamupeleke nsembe yopseleza.” (Genesis 22:2) Onani kuti ponena za Isaki, Yehova anakamba kuti mwana wako “amene umamukonda kwambiliyo.” Yehova anali kudziŵa kuti Isaki anali munthu wofunika kwambili kwa Abulahamu. Anali kudziŵanso mmene iyemwini anali kukondela Mwana wake, Yesu. Yehova amakonda kwambili Yesu moti kaŵili konse analankhula ali kumwamba ndipo anamuchula kuti, “Mwana wanga wokondedwa.”—Maliko 1:11; 9:7.
Komanso onani kuti pamene Yehova anauza Abulahamu kuti apeleke nsembe mwana wake, anagwilitsa nchito mawu osonyeza kumupempha. N’zodziŵikilatu kuti Abulahamu atamva pempho limeneli anamva cisoni kwambili. N’cimodzi-modzinso na mmene Yehova anamvela pamene anali kuona Mwana wake wokondedwa akuzunzidwa kenako n’kuphedwa. Pa nthawi imeneyi, Yehova anamva ululu kwambili. Ziyenela kuti aka kanali koyamba komanso komaliza kuti Yehova amve ululu waconco.
Conco, ngakhale kuti tingaganize kuti zimene Yehova anapempha Abulahamu kucita zinali zovuta, tiyenela kukumbukilanso kuti iye sanalole munthu wokhulupilika ameneyu kuti apelekedi mwana wakeyo nsembe. Yehova analetsa Abulahamu kuti asaphe Isaki, pofuna kumuthandiza kuti asakhale na cisoni cimene kholo limakhala naco mwana wake akamwalila. Ngakhale nconco, Yehova sanalepheletse imfa ya “Mwana wake koma anamupeleka m’malo mwa ife tonse.” (Aroma 8:32) N’cifukwa ciani Yehova analola kuti mwana wake aphedwe? Iye anacita zimenezi n’colinga cakuti “tipeze moyo.” (1 Yohane 4:9) Nkhani ya Abulahamuyi imatithandiza kumvetsa cikondi cacikulu cimene Mulungu ali naco pa ife. Kodi zimenezi sizingaticititse kuti nafenso tizimukonda kwambili?
w12 10/15 23 ¶6
Mvelani Mulungu Kuti Mupindule na Malumbilo Ake
Pofuna kutsimikizila anthu ocimwa, Yehova Mulungu anali kulumbila pogwilitsa nchito mawu monga akuti: “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Pali ine Mulungu wamoyo.” (Ezek. 17:16) Baibo imafotokoza maulendo oposa 40 pamene Yehova Mulungu analumbila. Citsanzo codziŵika bwino n‘cokhudza Abulahamu. Kwa zaka zambili, Yehova anacita mapangano ndi Abulahamu osonyeza kuti Mbewu yolonjezedwa idzacokela m’banja la Abulahamu na mwana wake Isaki. (Gen. 12:1-3, 7; 13:14-17; 15:5, 18; 21:12) Kenako Yehova anauza Abulahamu kuti acite zinthu zovuta kwambili. Anamuuza kuti apeleke nsembe mwana wake wokondedwa. Nthawi yomweyo, Abulahamu anamvela ndipo atatsala pang’ono kupeleka Isaki, mngelo wa Mulungu anamuletsa. Kenako Mulungu anati: “Ndikulumbila pali dzina langa, kuti cifukwa ca zimene wacitazi, posakana kupeleka mwana wako yekhayo, ndidzakudalitsa ndithu. Ndiponso ndidzachulukitsadi mbewu yako ngati nyenyezi zakumwamba, monganso mcenga wa m’mphepete mwa nyanja. Komanso mbewu yako idzalanda cipata ca adani ake. Kudzela mwa mbewu yako, mitundu yonse ya padziko lapansi idzapeza madalitso ndithu cifukwa cakuti wamvela mawu anga.”—Gen. 22:1-3, 9-12, 15-18.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
Yehova Anamucha kuti “Bwenzi Langa”
Asanasiye atumiki ake, Abulahamu anawauza kuti: “Inu tsalani pano ndi buluyu, ine ndi mwana wangayu tikupita uko kukalambila, tikupezani.” (Gen. 22:5) Kodi pamenepa Abulahamu anatanthauza ciani? Kodi anali kuwanamiza kuti adzabwelela ndi Isaki pamene akudziŵa kuti adzam’peleka nsembe? Iyai sanali kuwanamiza. Baibo imakamba kuti Abulahamu anali kudziŵa kuti ‘Mulungu ali ndi mphamvu zoukitsa [Isaki]’ kwa akufa. (Ŵelengani Aheberi 11:19.) Abulahamu anali kudziŵa kuti Yehova ndiye anamupatsa mphamvu zoti akhale na mwana ngakhale kuti iye ndi Sara anali okalamba kwambili. (Aheb. 11:11, 12, 18) Cotelo, anali kudziŵa kuti palibe cimene Yehova angalephele. Abulahamu sanali kudziŵa kuti cicitike n’ciani. Koma anali na cikhulupililo cakuti panthawi ina iliyonse, Yehova akhoza kuukitsa Isaki kuti malonjezo ake onse akwanilitsidwe. Ndiye cifukwa cake Abulahamu amachedwa “tate wa onse . . . okhala ndi cikhulupililo.”
it-1 853 ¶5-6
Kudziŵilatu za Kutsogolo, Kukonzelatu
Kusankha kudziŵilatu kapena kusadziŵilatu zakutsogolo. Mosiyana na ciphunzitso cakuti Mulungu anakonzelatu zonse zakutsogolo, pali mfundo yakuti Mulungu amacita kusankha kuti adziŵiletu za kutsogolo kapena kuti amacita zinthu mozindikila poseŵenzetsa mphamvu yake yodziŵilatu za kutsogolo. Mfundoyi ni yogwilizana na miyezo yolungama ya Mulungu komanso zimene Mawu ake amakamba ponena za makhalidwe ake. Pali malemba ena amene amaonetsa kuti si zoona kuti Mulungu amadziŵilatu na kukonzelatu zonse za kutsogolo. Malembawo amaonetsa kuti Mulungu amapenda mmene zinthu zilili na kupanga cosankha mogwilizana na zimene wapeza.
N’cifukwa cake pa Genesis 11:5-8 pamakamba kuti Mulungu anayang’ana padziko lapansi kuti aone mmene zinthu zinalili pa Babele, ndipo pa nthawi yomweyo anadziŵa zoyenela kucita kuti asokoneze nchito yosagwilizana na cifunilo cake imene anthu anali kugwila kumeneko. Ndiyeno panthawiyo anadziŵa zocita kuti asokoneze anthu amene anali kumanga nsanja mosagwilizana na cifunilo cake. Komanso kuipa kwa anthu a mu Sodomu na Gomora kutaculuka, Yehova anauza Abulahamu kuti afuna afufuze (mwa kuseŵenzetsa angelo), kuti aone ‘ngati akucitadi monga mwa kudandaula kumene anamva ndiponso ngati zocita zawo zilidi zoipa conco.’ Anatinso: “Ndikufuna ndidziŵe zimenezi.” (Gen. 18:20-22; 19:1) Mulungu anakamba kuti anafuna ‘kupalana ubwenzi na Abulahamu,’ kapena kuti kumudziŵa bwino. Ndipo Abulahamu atamumvela mpaka kufika pofuna kupeleka nsembe Isaki, Yehova anati, “Tsopano ndadziŵa kuti ndiwe woopa Mulungu, pakuti sunakane kupeleka kwa ine mwana wako mmodzi yekhayo.”—Gen. 18:19; 22:11, 12; yelekezelani na Neh. 9:7, 8; Agal. 4:9.
MARCH 9-15
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 24
“Mkazi wa Isaki”
“Inde Ndipita”
Abulahamu anacita pangano ndi Eliezere lakuti sadzatengela Isaki mkazi pakati pa akazi acikanani. N’cifukwa ciani? Cifukwa Akanani sanali kulemekeza ngakhale kulambila Yehova Mulungu. Abulahamu anali kudziŵa kuti Yehova adzawononga anthu amene anali kucita zinthu zoipa. Iye sanafune kuti mwana wake wokondedwa Isaki, akwatile mkazi pakati pa anthu a makhalidwe oipa amenewo. Anadziŵanso kuti mwana wake ndi amene anali kudzakwanilitsa malonjezo a Mulungu.—Genesis 15:16; 17:19; 24:2-4.
“Inde Ndipita”
Eliezere anapitiliza kuuza amene anamulandila kuti, atafika pa citsime pafupi ndi Harana, anapemphela kwa Yehova Mulungu. Iye anapempha Yehova kuti amuthandize kusankha mkazi amene Isaki anafunika kukwatila. Nanga anacita bwanji zimenezi? Eliezere anapempha Mulungu kumutsimikizila kuti mkazi amene afuna kuti Isaki akakwatile akamupeze ku citsime. Akadzamupempha madzi akumwa, iye adzapatse Eliezere madzi ndi kumwetsa ngamila zake zonse. (Genesis 24:12-14) Kodi ndani anabwela ndi kucita ndendende zimenezo? Anali Rabeka. Ganizilani mmene Rabeka akanamvelela, akanamva nkhani imene Eliezere anafotokozela acibale ake.
wp16.3 14 ¶6-7
“Inde Ndipita”
Kutatsala milungu yocepa kuti ayambe ulendo wake, Eliezere anafunsa Abulahamu za nkhaniyi kuti: “Bwanji ngati mkaziyo sakabwela nane?” Abulahamu anamuyankha kuti: “Udzamasuka ku lumbiloli.” (Genesis 24:39, 41) Banja la Betuele linali kulemekeza ufulu wa mtsikana. Eliezere anakondwela kwambili kuona kuti zinthu zonse zayenda bwino, cakuti tsiku lotsatila m’maŵa, anapempha kuti abwelele ku Kanani ndi Rabeka. Komabe, banjalo linafuna kuti Rabeka akhale nao kwa masiku ena 10. Pamapeto pake, nkhaniyo inatha motele: “Tiyeni timuitane mtsikanayo kuti timve zimene iyeyo anene.”—Genesis 24:57.
Tsopano Rabeka anafunika kupanga cosankha cacikulu pamoyo wake. Kodi iye adzakamba ciani? Kodi adzacondelela atate ake ndi mlongo wake kuti asamulole kupita kudziko lacilendo? Kapena, kodi adzaona kuti ni mwayi kutengako mbali pa zocitika zimene zinaonekelatu kuti zinali kutsogoleledwa na Yehova? Zimene anayankha zinaonetsa mmene anali kumvelela pa nkhani imene inali kudzasintha umoyo wake. Iye anati: “Inde ndipita.”—Genesis 24:58.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
“Inde Ndipita”
Tsiku lina madzulo atanyamula madzi mu mtsuko wake, mwamuna wina wacikulile anathamanga kudzakumana naye. Mwamunayo anati: “Conde ndipatse madzi a mumtsuko wako ndimweko pang’ono.” Iye anapempha madziwo mwaulemu ndi modzicepetsa. Rabeka anazindikila kuti mwamunayo wacokela kutali. Conco, mwamsanga anatula pansi mtsuko ndi kupatsa mwamunayo madzi kuti amwe. Iye anaona kuti mwamunayo alinso ndi ngamila 10 zimene zinali gone pafupi ndi comwelamo ziŵeto, cimene munalibe madzi. Cifukwa ca mmene mwamunayo anali kumuyang’anila, Rabeka anayesetsa kukhala woolowa manja mmene angathele. Conco, iye anati: “Nditungilanso madzi ngamila zanu mpaka zitamwa mokwanila.”—Genesis 24:17-19.
Onani kuti Rabeka sanangodzipeleka kupatsa cabe madzi ngamila 10, koma anaonetsetsa kuti ngamilazo zamwa madzi mokwanila. Ngamila imodzi ikakhala ndi ludzu kwambili, ingamwe madzi okwana malita 95. Ngati ngamila zonse 10 zinali ndi ludzu kwambili, ndiye kuti Rabeka anagwila nchito yotunga madzi kwa maola ambili. Zikuoneka kuti ngamila zimenezo zinali ndi ludzu kwambili. Koma, kodi Rabeka anadziŵa kuti ngamilazo zinali ndi ludzu kwambili? Iyai. Iye anali wofunitsitsa kugwila nchito mwakhama kuti aonetse kuti waceleza mwamuna wacikulile amene anali wacilendo. Mwamunayo analandila thandizo lake. Ndiyeno, iye anali kuyang’anitsitsa Rabeka pamene anali kuthamangathamanga ndi mtsuko wa madzi kuti adzaze comwelamo ziŵeto.—Genesis 24:20, 21.
wp16.3 13, Mawu apansi.
“Inde Ndipita”
Inali nthawi ya m’madzulo. Baibo sionetsa utali wa nthawi imene Rabeka anakhala ku citsime. Sionetsanso kuti anthu a m’banja lake anali atagona pamene iye anamaliza nchitoyo, kapena kuti wina wa m’banja lake anamulondola cifukwa cocedwa kufika panyumba.
“Inde Ndipita”
Pothela pake, tsiku limene tafotokoza kuciyambi kwa nkhani ino linafika. Pamene gulu la ngamila linali kudutsa m’dziko la Negebu, dzuŵa likuloŵa, Rabeka anaona mwamuna akuyenda m’chile. Mwamunayo anali kuoneka kuti ndi wokoma mtima. Nkhaniyo imati, “mwamsanga [Rabeka] anatsika pangamila,” sanayembekezele ngamila kugwada pansi. Atatelo anafunsa mtumiki kuti: “Kodi munthu akubwela apoyo kucokela m’chile kudzakumana nafe ndani?” Atauzidwa kuti ni Isaki, iye anatenga nsalu yophimba kumutu n’kudziphimba nayo. (Genesis 24:62-65) N’cifukwa ciani anacita zimenezi? Zimene anacitazo zinali cizindikilo cakuti akulemekeza munthu amene anali kudzakhala mwamuna wake. Ulemu waconco, umaoneka wacikale masiku ano. Komabe, tonse amuna ndi akazi tingaphunzilepo kanthu pa kudzicepetsa kwa Rabeka. Ndani wa ife amene sangafune kukhala na khalidwe lofunika limeneli?
MARCH 16-22
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 25-26
“Esau Anagulitsa Udindo Wake Monga Woyamba Kubadwa”
it-1 1242
Yakobo
Yakobo anali wosiyana na Esau, mwana wa pamtima wa Isaki. Esau anali wokonda m’chile, kamwendo m’njila, komanso wosaka nyama. Koma Baibo imakamba kuti Yakobo anali “kukhala nthawi yambili m’mahema. Iye anali munthu wosalakwa [m’Ciheberi, tam].” Anali munthu wa phee woweta nyama komanso wodalilika pogwila nchito za pakhomo, ndipo amayi ake anali kumukonda kwambili. (Gen. 25:27, 28) M’mavesi ena a m’Baibo, liwu la Ciheberi limeneli lakuti tam linagwilitsidwa nchito pokamba za anthu oyanjidwa na Mulungu. Mwacitsanzo, “anthu okonda kukhetsa magazi amadana ndi aliyense wopanda colakwa,” koma Yehova akutitsimikizila kuti “tsogolo la munthu [wosalakwa] ndi lamtendele.” (Miy. 29:10; Sal. 37:37) Munthu wosunga umphumphu Yobu, “anali munthu wopanda colakwa [m’Ciheberi, tam], wowongoka mtima.”—Yobu 1:1, 8; 2:3.
N’cifukwa Ciani Tiyenela Kuonetsa Kuyamikila?
N’zomvetsa cisoni kuti anthu ena ochulidwa m’Baibo, sanaonetse mzimu woyamikila. Mwacitsanzo, olo kuti Esau analeledwa na makolo amene anali kukonda Yehova na kum’lemekeza, iye sanayamikile zinthu zopatulika. (Ŵelengani Aheberi 12:16.) Kodi anaonetsa bwanji kusayamikila? Mosaganiza bwino, Esau anagulitsa udindo wake monga woyamba kubadwa kwa mng’ono wake Yakobo, posinthanitsa na cakudya cabe ca mphodza. (Gen. 25:30-34) Pambuyo pake, Esau anadzimvelela cisoni kwambili cifukwa ca zimene anacita. Koma popeza kuti sanayamikile mwayi umene anali nawo, sanafunikile kudandaula pamene anamanidwa madalitso a mwana woyamba kubadwa.
it-1 835
Woyamba Kubadwa, Zoyambilila
Kuyambila kale-kale, mwana woyamba kubadwa anali na malo olemekezeka m’banja, ndipo ndiye anali kukhala wotsogolela m’banja ngati tate wamwalila. Iye anali kulandila magawo aŵili a cuma ca Atate ake. (Deut. 21:17) Pa cakudya, Yosefe anaika Rubeni pa malo oyambilila cifukwa ndiye anali woyamba kubadwa. (Gen. 43:33) Koma si nthawi zonse pamene Baibo imalemekeza mwana woyamba kubadwa mwa kumuchula koyambilila pakati pa ana ena. Kaŵili-kaŵili imayambila kuchula mwana wolemekeza kwambili kapena wokhulupilika kwambili pa anawo m’malo mwa woyamba kubadwa.—Gen. 6:10; 1 Mbiri 1:28; yelekezelani na Gen. 11:26, 32; 12:4.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
Mafunso Ocokela Kwa Oŵelenga
Tsopano tiyeni tikambilanenso lemba la Aheberi 12:16, limene limati: “Muonetsetsenso kuti pasakhale wadama kapena aliyense wosayamikila zinthu zopatulika, ngati Esau, amene anapeleka udindo wake monga woyamba kubadwa pousinthanitsa ndi cakudya codya kamodzi kokha.” Ni mfundo yanji maka-maka imene mtumwi Paulo anali kukamba pa lembali?
Mtumwi Paulo pamenepa sanali kufotokoza za mzela wobadwila wa Mesiya. Iye anali atangolimbikitsa kumene Akhristu ‘kuwongola njila zimene mapazi awo anali kuyendamo.’ Mwa ici, iwo akanalandila “kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu.” Koma kucita ciwelewele kukanawalepheletsa kulandila kukoma mtimako. (Aheb. 12:12-16) Mwa kucita ciwelewele, iwo akanakhala ngati Esau, amene analephela ‘kuyamikila zinthu zopatulika,’ cifukwa cocita dyela na zinthu zakuthupi.
Esau anakhalako m’nthawi ya makolo akale, ndipo n’kutheka kuti nthawi zina anali kukhala na mwayi wopelekako nsembe. (Gen. 8:20, 21; 12:7, 8; Yobu 1:4, 5) Koma cifukwa cokonda zinthu zakuthupi, iye anasinthanitsa mwayi umenewo na cakudya ca mphodza codya kamodzi kokha. Mwina iye anacita izi pofuna kupewa mavuto amene analoseledwa kuti adzacitikila mbadwa za Abulahamu. (Gen. 15:13) Esau anaonetsanso kuti anali kukonda zinthu zakuthupi ndi kusayamikila zinthu zopatulika, mwa kukwatila akazi aŵili a mitundu ina. Izi zinabweletsa cisoni kwa makolo ake. (Gen. 26:34, 35) Iye anali wosiyana ngako na Yakobo, amene anaonetsetsa kuti wakwatila mkazi wolambila Mulungu woona.—Gen. 28:6, 7; 29:10-12, 18.
it-2 245 ¶6
Bodza
Baibo imaletsa kukamba Bodza. Koma izi sizitanthauza kuti munthu afunika kuulula zinthu kwa munthu amene safunika kuzidziŵa. Yesu Khristu anatilangiza kuti: “Musamapatse agalu zinthu zopatulika, kapena kuponyela nkhumba ngale zanu, kuopela kuti zingaponde-ponde ngalezo kenako n’kutembenuka ndi kukukhadzulani.” (Mat. 7:6) N’cifukwa cake Yesu pa zocitika zina sanali kuulula zonse kapena kupeleka mayankho acindunji pa mafunso ena. Anali kucita izi cifukwa coopa kuti zingabweletse mavuto. (Mat. 15:1-6; 21:23-27; Yoh. 7:3-10) Mwacionekele tiyenela kuona cimodzi-modzi zimene Abulahamu, Isaki, Rahabe, na Elisa anakamba posoceletsa alonda komanso popewa kuulula mfundo zonse kwa anthu osalambila Yehova.—Gen. 12:10-19 na caputa 20; 26:1-10; Yos. 2:1-6; Yak. 2:25; 2 Maf.6:11-23.
MARCH 23-29
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 27-28
“Yakobo Analandila Madalitso Omuyenelela”
w04 4/15 11 ¶4-5
Rebeka Anali Mkazi Wolimbikila Nchito Ndiponso Woopa Mulungu
Baibo silifotokoza ngati Isaki anali kudziŵa zakuti Esau adzakhala kapolo wa Yakobo. Mulimonse mmene zinalili, Rabeka na Yakobo anali kudziŵa kuti Esau ndiye anayenela kudalitsidwa. Rabeka sanacedwe kucitapo kanthu atangomva kuti Isaki afuna kudalitsa Esau akam’phikila nyama yam’chile imene anali kukonda kwambili. Rabeka anali asanasiyebe kulimbikila na kucita cangu pogwila nchito monga mmene anali kucitila ali mtsikana. ‘Anauza’ Yakobo kuti am’patsile tuŵana twa mbuzi tuŵili, kuti aphikile mwamuna wake cakudya comwe anali kucikonda kwambili. Kenako Yakobo adzanamizile kuti ni Esau n’colinga coti akalandile madalitsowo. Yakobo anakana. Bambo wake akanatha kutulukila cinyengo cakeco akanam’tembelela. Rabeka analimbikilabe kuti Yakobo acite zimenezo. Anati: “Tembelelo limenelo libwele kwa ine m’malo mwa iwe mwana wanga.” Conco, anaphika cakudyaco, anacititsa Yakobo kuoneka ngati Esau, ndipo anamuuza kuti apite kwa mwamuna wake.—Genesis 27:1-17.
Malemba sakamba cifukwa cake Rabeka anacita zimenezi. Anthu ambili amati analakwa, koma Baibo siitelo, ndipo Isaki sanam’dzudzule Yakobo atatulukila kuti ndiye walandila madalitso. M’malo mwake Isaki anawonjezela madalitsowo. (Genesis 27:29; 28:3, 4) Rabeka anali kudziŵa zimene Yehova analosela zokhudza ana ake. Motelo anali kucita zinthu mofuna kuonetsetsa kuti Yakobo walandila madalitso amene anayenela kulandila. Izi zinali zogwilizana kwambili na cifunilo ca Yehova.—Aroma 9:6-13.
w07 10/1 31 ¶2-3
Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga
Baibo siikamba mwatsatane-tsatane cifukwa cimene Rabeka na Yakobo anacitila zimenezi, koma imaonetsa kuti zinacitika mosayembekezeleka. Tiyenela kudziŵa kuti Mawu a Mulungu satsutsa kapena kuvomeleza zimene Rabeka na Yakobo anacita. Conco, nkhani imeneyi silimbikitsa kunama kapena kucita cinyengo. Komabe, Baibo imatithandiza kumvetsa zimene zinacitika.
Coyamba, Baibo imasonyeza kuti Yakobo ni amene anali woyenela kudalitsidwa osati Esau. Yakobo anali atagula ukulu kwa mkulu wake wosayamikilayu amene anaugulitsa na cakudya cifukwa ca njala. Esau “ananyoza ukulu wake.” (Genesis 25:29-34) Conco, mwa kupita kwa bambo ake, Yakobo anali kufuna madalitso amene analidi ake.
it-1 341 ¶6
Dalitso
M’masiku a Abulahamu, Isaki na Yakobo, tate akatsala pang’ono kufa, kambili anali kudalitsa ana ake. Kucita izi kunali kofunika kwambili. Conco, Isaki anadalitsa Yakobo poganiza kuti anali Esau, mwana wake woyamba kubadwa. Isaki anakamba kuti Yakobo adzadalitsidwa ndipo adzakhala na zinthu zambili kuposa m’bale wake Esau. Mosakayikila Isaki anapempha Yehova kuti apeleke dalitso cifukwa panthawiyo iye anali wokalamba komanso wakhungu. (Gen. 27:1-4, 23-29; 28:1, 6; Aheb. 11:20; 12:16, 17) Pambuyo pake Isaki atadziŵa kuti anadalitsa Yakobo, anabwelezenso kumudalitsa ndipo anamuwonjezela madalitso ena. (Gen. 28:1-4) Yakobo nayenso asanamwalile, anadalitsa ana aŵili oyambilila a Yosefe. Pambuyo pake, anadalitsa ana ake. (Gen. 48:9, 20; 49:1-28; Aheb. 11:21) Mofananamo, Mose asanamwalile anadalitsa mtundu wonse wa Aisiraeli. (Deut. 33:1) Pa zocitika zonsezi, zotulukapo zake zinaonetsa kuti anthu amenewa anali kulosela za kutsogolo. Nthawi zina, podalitsa munthu, wodalitsa anali kuika manja pamutu pa amene akudalitsidwayo.—Gen. 48:13, 14.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
w06 4/15 6 ¶3-4
Cinsinsi Cokambitsana Bwino na Mwamuna Kapena Mkazi Wanu
Kodi Isaki na Rabeka anaphunzila luso la kukambitsana bwino? Mwana wawo Esau atakwatila ana aakazi aŵili a Heti, m’banjamo munabuka mavuto. Ndipo Rabeka “anali kuuza Isaki nthawi ndi nthawi” kuti: “Ndafika ponyansidwa nawo moyo wanga cifukwa ca ana aakazi acihetiwa. Ngati Yakobo [mwana wawo wamng’ono] atenga mkazi kuno pakati pa ana aciheti ngati amenewa, ndi bwino ndingofa!” (Genesis 26:34; 27:46) Mwacionekele, Rabeka anakamba mosapita m’mbali zinthu zimene zinali kumudetsa nkhawa.
Isaki anauza Yakobo, mphundu mnzake wa Esau, kuti asakwatile ana aakazi a ku Kanani. (Genesis 28:1, 2) Mfundo ya Rabeka inamveka. Apa mwamunayu na mkazi wake analankhulana bwino pa nkhani yovuta kwambili ya pabanja pawo, ndipo anapeleka citsanzo kwa ife masiku ano. Nanga bwanji ngati tasiyana maganizo na mnzathu? Kodi tingacite bwanji?
w04 1/15 28 ¶6
Mfundo Zazikulu za M’buku la Genesis—Cigawo Caciŵili
28:12, 13—Kodi loto la Yakobo lokhudza “makwelelo” linatanthauza ciani? “Makwelelo” amenewa, amene mwina anali kuoneka ngati masitepe a miyala okwela m’mwamba, anaonetsa kuti pamakhala kulankhulana pakati pa okhala padziko lapansi na a kumwamba. Angelo a Mulungu amene anali kukwela na kutsika pa makwelelowo, anaonetsa kuti angelo amatumikila m’njila yofunika kwambili pakati pa Yehova na anthu amene iye amawayanja.—Yohane 1:51.
MARCH 30–APRIL 5
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 29-30
“Yakobo Akwatila”
w03 10/15 29 ¶6
Yakobo Anaona Zinthu Zauzimu Kukhala Zofunika
Anthu anali kutomelana mwa kupeleka cimalo ku banja la mkazi. Pambuyo pake Cilamulo ca Mose cinadzaika masekeli 50 monga mtengo wa anamwali amene agwililidwa. Katswili wina wamaphunzilo, Gordon Wenham, ananena kuti “ndalama za cimalo sizinali kuposa pamenepa,” koma nthaŵi zambili cimaloco cinali kukhala ca ndalama “zocepa kwambili.” (Deuteronomo 22:28, 29) Yakobo sakanatha kupeleka cimaloco. Conco, anadzipeleka kuti agwilile nchito Labani zaka zisanu na ziŵili. Wenham anapitiliza kuti: ‘Popeza kuti kale m’masiku a Ababulo malipilo a anthu apisiweki anali pakati pa hafu ya sekeli na sekeli imodzi pamwezi, (kutanthauza pakati pa masekeli 42 ndi 84 m’zaka 7 zathunthu), Yakobo analonjeza Labani cimalo cabwino kwambili kuti atenge Rakele.’ Labani anavomela na mtima wonse.—Genesis 29:19.
w07 10/1 8-9
Moyo Wawo Unali Wovuta Koma “Anamanga Nyumba ya Isiraeli”
Kodi Leya anagwilizana nazo zakuti acitile Yakobo zacinyengo? Kapena kodi anangocita zimenezi pomvela atate ake? Kodi Rakele anali kuti nthawi imeneyo? Kodi anali kudziŵa zimene zinali kucitika? Ngati anali kudziŵa, kodi anamva bwanji mumtima mwake? Kodi akanakana kucita zofuna za atate ake ovutawo? Baibo sipeleka mayankho a mafunso amenewa. Kaya Rakele na Leya anamva bwanji, zimene tikudziŵa n’zakuti Yakobo anakwiya kwambili atatulukila zimenezi. Iye anakangana na Labani osati ana akewo. Yakobo anati: “Kodi si Rakele amene ndakugwililani nchito? N’cifukwa ciani mwandipusitsa conci?” Labani anayankha kuti: “Kwathu kuno, mwambo sulola kukwatitsa wamng’ono mkulu wake asanakwatiwe. Usangalale mokwanila ndi mkaziyu mlungu wonse wokondwelela ukwati wake. Kenako ndidzakupatsa mkazi winayu, komatu udzandigwilila nchito zaka zina 7.” (Genesis 29:25-27) Motelo, Yakobo anakakamizidwa kucita mitala, ndipo zimenezi zinayambitsa nsanje yoopsa m’banja lake.
it-2 341 ¶3
Cikwati
Cikondwelelo. M’nthawi ya Aisiraeli, pa cikwati sipanali kucitika mwambo wapadela womangitsa cikwati. Ngakhale n’telo, panali kukhala cikondwelelo ndipo anthu anali kusangalala kwambili. Pa tsiku la cikwati, mkwatibwi anali kukonzekela bwino kwambili kunyumba kwawo. Coyamba iye anali kusamba, na kudzola mafuta onunkhila. (Yelekezelani na Rute 3:3; Ezek. 23:40.) Ndipo nthawi zina mothandizidwa na om’pelekeza, iye anali kuvala covala ca pacifuwa na covala cacitali coyela, cimene kambili cinali kukhala cokongola komanso colukidwa mwaluso kulingana na ndalama zimene anali nazo. (Yer. 2:32; Chiv. 19:8; Sal. 45:13, 14) Anali kudzikongoletsa na zodzikongoletsela monga masikiyo na zibangili, ngati akwanitsa kucita zimenezo. (Yes. 49:18; 61:10; Chiv. 21:2) Ndiyeno anali kuvala covala cacitali copepuka cimene cinali kumuphimba kucoka kumutu mpaka kumapazi. (Yes. 3:19, 23) Ndiye cifukwa cake zinali zosavuta kwa Labani kupusitsa Yakobo mwa kum’patsa Leya m’malo mwa Rakele. (Gen. 29:23, 25) Rabeka nayenso anavala cophimba kumutu pamene anatsala pang’ono kukumana na Isaki. (Gen. 24:65) Kucita izi kunaonetsa kuti mkwatibwi ni wogonjela kwa mkwati, amene anali kudzakhala mutu wake. —1 Akor. 11:5, 10.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
it-1 50
Kutenga Mwana Kukhala Wako
Rakele na Leya anali kuona kuti ana amene Yakobo anabeleka kwa adzakazi awo anali ana awo, obadwila pa mawondo awo. (Gen. 30:3-8, 12, 13, 24) Ana amenewa analandila coloŵa pamodzi ndi ana amene Yakobo anabeleka kwa akazi ake amene anaŵakwatila mwalamulo. Iwo anali ana eni-eni a Yakobo, ndipo analinso a Rakele na Leya cifukwa anawabeleka na adzakazi awo.
w04 1/15 28 ¶7
Mfundo Zazikulu za M’buku la Genesis—Cigawo Caciŵili
30:14, 15—N’cifukwa ciani Rakele anataya mwayi wokhala na pakati mwa kuusinthanitsa na mandereki? M’nthaŵi zakale, zipatso za mtengo wa mandereki anali kuziseŵenzetsa monga mankhwala ogonetsa tulo ndiponso monga mankhwala othandiza munthu kuti asamamve kupweteka kwa minofu. Anthu anali kukhulupililanso kuti zipatso zimenezo zinali na mphamvu yoyambitsa cilakolako cogonana ndiponso kuthandiza munthu kukhala na mphamvu yobeleka kapena kuthandiza mkazi kukhala na pakati. (Nyimbo ya Solomo 7:13) Ngakhale kuti Baibo sifotokoza colinga ca Rakele pocita zimenezi, iye ayenela kuti anaganiza kuti zipatso za mandereki zikanamuthandiza kukhala na pakati na kuthetsa kunyozedwa cifukwa cosabeleka. Komabe, panapita zaka zingapo kudzafika pamene Yehova ‘anam’patsa mphamvu zobeleka.’—Genesis 30:22-24.