LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwbr20 February
  • Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki
  • Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu—2020
  • Tumitu
  • FEBRUARY 3-9
  • FEBRUARY 10-​16
  • FEBRUARY 17-​23
  • FEBRUARY 24–MARCH 1
Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu—2020
mwbr20 February

Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki

FEBRUARY 3-9

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 12-​14

“Cipangano Cimene Cimakukhudzani”

it-1 522 ¶4

Cipangano

Cipangano ca Abulahamu. Cipangano ca Abulahamu ciyenela kuti cinayamba kugwila nchito pamene Abulamu (Abulahamu) anawoloka mtsinje wa Firate pa ulendo wake wopita ku Kanani. Koma Pangano la Cilamulo linapangidwa patapita zaka 430. (Agal. 3:​17) Yehova anakamba na Abulahamu pamene anali kukhala ku Mesopotamiya, mu mzinda wa Uri wa Akasidi. Anamuuza kuti apite ku dziko limene Mulungu adzamuonetsa. (Mac. 7:​2, 3; Gen. 11:31; 12:​1-3) Ekisodo 12:​40, 41 (LXX) imakamba kuti ca kumapeto kwa zaka 430 zokhala m’maiko a Iguputo na Kanani, “pa tsiku lomwe zinatha,” Aisiraeli amene anali mu ukapolo ku Iguputo anamasulidwa. Iwo anamasulidwa mu ukapolo ku Iguputo pa Nisani 14, mu 1513 B.C.E., pa tsiku la Pasika. (Eks. 12:​2, 6, 7) Izi zionetsa kuti Abulahamu anawoloka mtsinje wa Firate pa Nisani 14, mu 1943 B.C.E pa ulendo wake wopita ku Kanani, ndipo mwacionekele m’pamene cipangano ca Abulahamu cinayamba kugwila. Mulungu anaonekelanso kwa Abulahamu atafika ku Kanani mpaka ku Sekemu, ndipo anamufotokozela zowonjezeleka zokhudza lonjezo lake. Iye anati: “Ndidzapeleka dziko ili kwa mbewu yako,” kuonetsa kuti pali kugwilizana pakati pa cipangano cimeneci na lonjezo la mu Edeni, ndiponso zinavumbula kuti ‘mbewuyo’ idzakhala munthu, kutanthauza kuti idzacokela mu mzela wobadwila wa anthu. (Gen. 12:​4-7) Patapita nthawi, Yehova anafotokoza mbali zinanso zokhudza lonjezo limenelo, zopezeka pa Genesis 13:​14-​17; 15:18; 17:​2-8, 19; 22:​15-​18.

w89 7/1 3 ¶4

Cifukwa Cake Mufunika Kudziŵa Zoona Zake Ponena za Abulahamu

Linali lonjezo locititsa cidwi, ndipo Abulahamu anauzidwa lonjezoli maulendo ena osacepela aŵili. (Genesis 18:18; 22:18) Kuti akwanilitse lonjezolo, Mulungu adzaukitsa anthu a m’mabanjawo. Kukhalanso na moyo kwa oukitsidwawo kudzakhala dalitso lalikulu, cifukwa ambili a iwo adzakhalanso pa dziko lapansi limene lidzakhala Paradaiso wofanana na uja umene unatayika. Pambuyo pake, iwo adzaphunzitsidwa kuti akapeze dalitso la moyo wosatha.​—Genesis 2:​8, 9, 15-​17; 3:​17-​23.

it-2 213 ¶3

Cilamulo

Malinga na maumboni akale, akatswili ena amakhulupilila kuti kale pa nthawi yogulitsa malo, wogula anali kum’pititsa pa malo oonekela bwino kuti aone malowo, na malile ake onse. Wogulayo akakamba kuti “nayaona,” mawuwo anali citsimikizo cakuti wavomeleza mwalamulo. Pamene Yehova anauza Abulahamu lonjezo lakuti adzalandila dziko la Kanani, iye coyamba anauzidwa kuti akayang’ane m’mbali zonse zinayi za dziko. Abulahamu sanakambe mawu akuti “naliona,” mwina cifukwa cakuti Mulungu anakamba kuti adzapeleka Dziko Lolonjezedwalo kwa mbewu yake m’tsogolo. (Gen. 13:​14, 15) Monga woimilako Aisiraeli pa za malamulo, Mose anauzidwa kuti “ayang’ane” dzikolo, cakuti ngati mfundo imene tafotokozayi ni yoona, ndiye kuti mwakutelo iye anapeleka malowo mwalamulo kwa Aisiraeli, ndipo iwo anali kudzalandila malowo pansi pa utsogoleli wa Yoswa. (Deut. 3:​27, 28; 34:4; onaninso zimene Satana anaonetsa Yesu pa Mat. 4:⁠8.) Kacitidwe kena kalamulo pogula malo kanali kuyendela malowo, kapena kuloŵamo. (Gen. 13:17; 28:13) M’zolembedwa zina zakale, pa cipepala cogulitsila malo anali ­kuikapo ngakhale ciŵelengelo ca mitengo ­inali pamalowo.​—Yelekezelani Gen. 23:​17, 18.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

w16.05 5 ¶12

Tizithetsa Mikangano Mwamtendele

Baibo imaonetsa kuti atumiki a Mulungu angakhalebe pamtendele ngakhale kuti pali kusamvana pakati pawo. Mwacitsanzo, Abulahamu na Loti, onse anali na ziŵeto zambili, ndipo abusa awo anayamba kukangana cifukwa ca kucepa kwa malo odyetselako ziŵeto. Abulahamu anafuna kukhalabe pamtendele na Loti, conco anam’patsa mwayi wosankha malo abwino. (Genesis 13:​1, 2, 5-9) Cimeneci ni citsanzo cabwino cimene tiyenela kutengela. Kodi Abulahamu anavutika cifukwa copatsa Loti malo abwino? Ayi ndithu. Patangopita nthawi yocepa, Yehova analonjeza Abulahamu kuti adzam’patsa zoculuka kuposa zimene analuza. (Genesis 13:​14-​17) Kodi tiphunzilapo ciani? Ngakhale titaluza zinazake pofuna kukhazikitsa mtendele, Yehova adzatidalitsa.

it-2 683 ¶1

Wansembe

Melekizedeki mfumu ya ku Salemu anali wansembe (ko·henʹ) wapadela kwambili. Palibe paliponse m’Baibo pamene pakamba za makolo ake, kubadwa kwake, kapena imfa yake. Unsembe wake sanacite kuulandila ngati coloŵa, ndipo sanaloŵedwe m’malo na munthu wina. Melekizedeki anali mfumu komanso wansembe. Unsembe wake unali wapamwamba kuposa wa Alevi, cifukwa Levi nayenso anapeleka cakhumi kwa Melekizedeki, popeza anali akali m’ciuno mwa Abulahamu pamene Abulahamuyo anapeleka cakhumi kwa Melekizedeki ndipo anadalitsidwa. (Gen. 14:​18-​20; Aheb. 7:​4-​10) M’zinthu zimenezi, Melekizedeki anali cithunzi ca Yesu Khristu, amene ni “wansembe mpaka muyaya monga mwa unsembe wa Melekizedeki.”​—Aheb. 7:​17.

FEBRUARY 10-​16

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 15-​17

“Yehova anasintha dzina la Abulamu na Sarai​—Cifukwa?”

it-1 817

Colakwa, Kupeza Colakwa

Kumbali ina, njila ya munthu komanso zocita zake nthawi zambili zimakhala na zolakwa. Anthu onse anatengela ucimo kwa Adamu. (Aroma 5:​12; Sal. 51:⁠5) Koma Yehova, alibe colakwa ciliconse, ndipo ni wacifundo, ‘adziŵa bwino mmene anatiumbila, amakumbukila kuti ndife fumbi.’ (Sal. 103:​13, 14) Iye anaona munthu wokhulupilika na womvela Nowa, kukhala “wopanda colakwa pakati pa anthu a m’nthawi yake.” (Gen. 6:⁠9) Analamula Abulahamu kuti, “Yenda pamaso panga ndipo ukhale wolungama.” (Gen. 17:⁠1) Ngakhale kuti amuna amenewa anali opanda ungwilo ndiponso anafa, Yehova amene “amaona mmene mtima ulili,” anawaona kukhala opanda colakwa. (1 Sam. 16:7; yelekezelani na 2 Maf. 20:3; 2 Mbiri 16:⁠9) Iye analamula Aisiraeli kuti, “Ukhale wopanda colakwa pamaso pa Yehova Mulungu wako.” (Deut. 18:13; 2 Sam. 22:24) Mulungu anapeleka Mwana wake wosalakwa (Aheb. 7:​26) monga nsembe ya dipo, ndipo pa maziko amenewa, amaona anthu amene amaonetsa cikhulupililo na kumvela kukhala ‘olungama,’ kapena kuti opanda colakwa. Panthawi imodzi-modzi, iye amakhalabe woweluza wacilungamo komanso wopanda colakwa.​—Aroma 3:​25, 26

it-1 31 ¶1

Abulahamu

Nthawi inapitapo. Ndipo iwo anali atakhala ku Kanani zaka pafupi-fupi 10, koma Sara anapitilizabe kukhala wopanda mwana. Conco Sara anaganiza zopeleka Hagara kapolo wake waciiguputo kwa Abulahamu kuti amubelekele mwana. Abulahamu anavomeleza. Conco mu 1932 B.C.E., Isimaeli anabadwa, pamene Abulahamu anali na zaka 86. (Gen. 16:​3, 15, 16) Patapitanso nthawi yaitali, mu 1919 B.C.E., pamene Abulahamu anali na zaka 99, Yehova analamula amuna onse a m’nyumba ya Abulahamu kuti adulidwe. Ici cinali cizindikilo kapena cisindikizo cocitila umboni za cipangano capadela cimene cinalipo pakati pa iye Yehova na Abulahamu. Pa nthawi imodzi-modziyi, Yehova anasintha dzina la Abulamu kukhala Abulahamu, cifukwa anali kudzamupangitsa kukhala “tate wa mitundu yambili.” (Gen. 17:​5, 9-​27; Aroma 4:​11) Ndiyeno patangopita nthawi yocepa, angelo atatu amene Abulahamu anaceleza m’dzina la Yehova, analonjeza kuti Sara adzakhala na pakati ndipo adzabeleka mwana, inde m’caka cotsatila!​—Gen. 18:​1-​15.

w09 2/1 13

Maina Atanthauzo

Mulungu anasinthanso mayina a anthu ena pofuna kulosela cinthu cinacake. Mwacitsanzo, anasintha dzina la Abulamu, lotanthauza “Atate Akwezeka” kukhala Abulahamu, “Tate wa Khamu la Anthu.” Ndipo mogwilizana ndi dzina lake, Abulahamu anakhaladi tate wa mitundu yambili. (Genesis 17:​5, 6) Ganizilaninso dzina la mkazi wa Abulahamu, Sarai, limene linali kutanthauza “Wolongolola.” Taganizilani mmene anakondwelela pamene Mulungu anasintha dzina lake kukhala “Sara,” lotanthauza “Mfumukazi,” kuonetsa kuti adzakhala kholo la mafumu.​—Genesis 17:​15, 16.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

it-1 460-​461

Kuŵelengela Nthawi

Yehova anauza Abulamu (Abulahamu) kuti: “Udziŵe ndithu kuti mbewu yako idzakhala mlendo m’dziko la eni, ndipo idzatumikila eni dzikolo. Iwo adzasautsa mbewu yako kwa zaka 400.” (Gen. 15:13; onaninso Mac. 7:​6, 7) Pamene Mulungu anakamba zimenezi n’kuti Isaki, “mbewu” yolonjezedwa yodzalandila colowa asanabadwe. Mu 1932 B.C.E. kapolo waciiguputo Hagara anabelekela Abulahamu mwana dzina lake Isimaeli, ndipo mu 1918 B.C.E. Isaki anabadwa. (Gen. 16:16; 21:⁠5) Tikaŵelenga cafutambuyo zaka 400 kucokela pamene Aisiraeli anamasulidwa mu ukapolo ku Iguputo, pamene mazunzo awo anatha (Gen. 15:14), zaka zimenezi zitifikitsa mu 1913 B.C.E., pa nthawi imene Isaki anali na zaka pafupi-fupi zisanu. Cioneka kuti panthawiyi, Isaki anali ataleka kale kuyamwa, ndipo anali “mlendo” m’dziko la eni, panthawiyi anali atayamba kuzunzidwa na Isimaeli mwa “kumuseka,” apa n’kuti Isimaeli ali na zaka pafupi-fupi 19. (Gen. 21:​8, 9) Masiku ano, anthu angaone kuti kuseka Isaki kumene Isimaeli anacita, siinali nkhani, koma si mmene zinalili pa nthawi imeneyo. Umboni wa zimenezi ni mmene Sara anacitila, komanso zimene Mulungu ananena pamene Sara anakamba kuti Hagara na mwana wake Isimaeli athamangitsidwe. (Gen. 21:​10-​13) Komanso, kuona kuti cocitikaci cinalembedwa mwatsatane-tsane m’Mawu a Mulungu, kutithandiza kudziŵa ciyambi ca zaka 400 za mazunzo zimene zinaloseledwa, komanso kuti nthawiyo siinathe mpaka pamene Aisiraeli anamasulidwa mu ukapolo ku Iguputo.​—Agal. 4:​29.

it-1 778 ¶4

Ekisodo

“M’badwo Wacinayi.” Kumbukilani kuti Yehova anauza Abulahamu kuti mu m’badwo wacinayi, mbadwa zake zidzabwelela ku dziko la Kanani. (Gen. 15:16) M’zaka zonse 430 kucokela pamene cipangano ca Abulahamu cinayamba kugwila nchito, mpaka pamene Aisiraeli anamasulidwa mu ukapolo ku Iguputo, panapita mibadwo yoposa inayi. Izi ziphatikizapo kuŵelengela zaka za anthu amene anakhala moyo wautali panthawiyo, monga mwa zolembedwa. Koma m’ceni-ceni Aisiraeli anakhala ku Iguputo zaka 215 cabe. ‘Mibadwo inayi’ ya Aisiraeli kucokela pamene analoŵa mu Iguputo ingagaŵidwe mwanjila iyi, mwacitsanzo kuseŵenzetsa cabe fuko limodzi la Aisiraeli, fuko la Levi: (1) Levi, (2) Kohati, (3) Amuramu, komanso (4) Mose.​—Eks. 6:​16, 18, 20.

FEBRUARY 17-​23

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 18-​19

“Woweluza wa Dziko Lonse Lapansi’ Awononga Mizinda ya Sodomu na Gomora”

w17.04 18 ¶1

“Woweluza wa Dziko Lonse” Amacita Cilungamo Nthawi Zonse

“KODI Woweluza wa dziko lonse lapansi sadzacita colungama?” (Gen. 18:25) Pofunsa funso limeneli, Abulahamu anaonetsa kuti anali kukhulupilila kuti Yehova adzaŵeluza molungama mizinda ya Sodomu na Gomora. Anali kudziŵa kuti Yehova sangacite zinthu mopanda cilungamo mwa “kupha olungama pamodzi ndi oipa.” Iye anakamba motsimikiza kuti Mulungu ‘sangacite zimenezo ayi.’ Patapita zaka 400, Yehova anakamba mawu aya ponena za iye mwini: ‘Thanthwe, nchito yake ndi yangwilo, njila zake zonse ndi zolungama. Mulungu wokhulupilika, amene sacita cosalungama. Iye ndi wolungama ndi wowongoka.’​—Deut. 31:19; 32:⁠4.

w18.08 30 ¶4

Kuleza Mtima Kumatanthauza Kupilila Tili na Colinga

Pa nkhani ya kuleza mtima, Yehova ndiye citsanzo cabwino kwambili cimene tiyenela kutengela. (2 Pet. 3:​15) M’Mawu a Mulungu muli nkhani zambili zosonyeza mmene Yehova anaonetsela kuleza mtima kwakukulu. (Neh. 9:​30; Yes. 30:​18) Mwacitsanzo, kodi Yehova anacitanji pamene Abulahamu anam’funsa mafunso pa colinga cake cofuna kuwononga Sodomu? Iye sanam’dule mawu Abulahamu pamene anali kukamba. M’malomwake, anamvetsela moleza mtima funso lililonse limene Abulahamu anafunsa, komanso nkhawa zake. Ndiyeno Yehova anaonetsa kuti anamvetsa nkhawa za Abulahamu, ndipo anamutsimikizila kuti sakanawononga mzinda wa Sodomu, olo mukanapezeka cabe anthu 10 olungama. (Gen. 18:​22-​33) Ndithudi! Yehova ni citsanzo cabwino ngako pa nkhani yomvetsela moleza mtima na kusakwiya msanga.

w10 11/15 26 ¶12

Yehova Ndiye Ambuye Wathu Wamkulu Koposa

Sitikukayikila kuti posacedwapa Yehova adzasonyeza kuti ni woyenela kulamulila. Tikutelo cifukwa cakuti iye sangalole kuti zinthu zoipa zizingocitikabe ndipo tikudziŵa kuti tikukhala m’masiku otsiliza. Yehova anawononga anthu oipa pa nthawi ya Cigumula. Iye anawononga mizinda ya Sodomu na Gomora komanso Farao na asilikali ake. Nayenso Sisera na asilikali ake komanso Sanakeribu na asilikali a Asuri sanathe kulimbana na Wam’mwambamwamba. (Gen. 7:​1, 23; 19:​24, 25; Eks. 14:​30, 31; Ower. 4:1​5, 16; 2 Maf. 19:​35, 36) Conco n’zosakayikitsa kuti Yehova Mulungu sadzalekelela mpaka kale-kale anthu amene salemekeza dzina lake ndiponso amene amacitila nkhanza Mboni zake. Ndipo panopa tikuona cizindikilo ca kukhalapo kwa Yesu komanso ca mapeto a nthawi yoipa ino.​—Mat. 24:⁠3.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

w88 5/15 23 ¶4-5

Kodi Alipo Amene Anaonapo Mulungu?

Tsopano tingathe kumvetsa cifukwa cake Abulahamu anakamba na mngelo wolankhulila Mulungu monga kuti akukamba na Yehova Mulungu iyemwini. Popeza mngeloyo analankhula ndendende zimene Mulungu anafuna kuuza Abulahamu, ndipo anali pamenepo kuimila Mulungu, ndiye cifukwa cake nkhani ya m’Baibo imeneyi imakamba kuti “Yehova anaonekela kwa Abulahamu.”​—Genesis 18:⁠1.

Kumbukilani kuti mngelo wolankhulila Mulungu angatumize mauthenga a Mulunguyo mwacindunji monga mmene foni kapena wailesi imapelekela mawu athu kwa munthu wina. Conco, tingamvetsetse cifukwa cake Abulahamu, Mose, Manowa, komanso anthu ena anakambila na angelo ovala matupi aumunthu ngati kuti akukamba na Mulungu. Ngakhale kuti anthuwo anaona angelowo na ulemelelo wa Yehova, iwo sanaone Mulungu. Izi sizitsutsana ngakhale pang’ono na mawu a mtumwi Yohane akuti: “Palibe munthu anaonapo Mulungu ndi kale lonse.” (Yohane 1:​18) Amunawo anangoona angelo oimila Mulungu, osati Mulungu iyemwini.

w19.06 20 ¶3

Thandizani Ena Kupilila Nkhawa Zawo

Loti anapanga cosankha colakwika cokakhala mu mzinda wa Sodomu, mmene munali anthu a khalidwe lonyansa laciwelewele. (Ŵelengani 2 Petulo 2:​7, 8) Mzinda wa Sodomu unali wolemela. Koma Loti anakumana na mavuto ambili cifukwa cokhala mumzinda umenewo. (Gen. 13:​8-​13; 14:12) Mwacitsanzo, mkazi wake ayenela kuti anaukonda kwambili umoyo wa mumzindawo. Ayenelanso kuti anali kugwilizana kwambili ndi anthu ena a mu mzindawo. Izi zinapangitsa kuti asamvele Yehova. Ndipo pa mapeto pake, anawonongedwa pamene Mulungu anagwetsa moto na sulufule mu Sodomu. Ganizilaninso za ana aŵili a Loti. Amuna aŵili amene anawatomela, anaphedwa pamene mzindawo unawonongedwa. Loti anataikilidwa mkazi wake wokondedwa, katundu, na nyumba. (Gen. 19:​12-​14, 17, 26) Kodi Yehova anamulekelela Loti panthawi yovuta imeneyi cifukwa cakuti anapanga cosankha colakwika? Iyai.

FEBRUARY 24–MARCH 1

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 20-​21

“Yehova Amakwanilitsa Malonjezo Ake Nthawi Zonse”

wp17.5 14-​15

Mulungu Anamucha Mfumukazi

Kodi kuseka kwa Sara kuonetsa kuti analibe cikhulupililo? Iyai. Baibo imati: “Mwa cikhulupililo, Sara nayenso analandila mphamvu yokhala ndi pakati ngakhale kuti anali atapitilila zaka zobeleka, cifukwa anaona kuti wolonjezayo ndi wokhulupilika.” (Aheberi 11:11) Sara anali kum’dziŵa Yehova, anali kudziŵa kuti angakwanilitse lonjezo lililonse. N’ndani amene safuna kukhala na cikhulupililo ca conco? Tifunika kum’dziŵa bwino Mulungu amene analemba Baibo. Tikatelo, tidzaona kuti mpake Sara kukhala na cikhulupililo cimene anali naco. Zoona Yehova ni wokhulupilika, ndipo amakwanilitsa malonjezo ake. Nthawi zina, angacite zimenezo m’njila imene ingatidabwitse kapena kuikaikila.

“MVELA MAWU AKE”

Ali na zaka 90, Sara anakondwela kwambili kuona kuti zimene anali kulaka-laka mu umoyo wake zacitika. Anabeleka mwana apo n’kuti mwamuna wake wokondedwa ali na zaka 100. Abulahamu anacha mwanayo kuti Isaki, kapena kuti “Kuseka,” monga mmene Mulungu anakambila. Yelekezani kuti mukuona Sara akumwetulila uku akukamba kuti: “Mulungu wandipatsa cifukwa cosangalalila. Tsopano aliyense akamva zimenezi asangalala nane.” (Genesis 21:⁠6) Mphatso ya Yehova yozizwitsa imeneyi inam’sangalatsa masiku ake onse. Komabe, mphatsoyo inabweletsa udindo waukulu kwa iye.

Pamene Isaki anali na zaka 5, banja lonse linakonza phwando lalikulu, kukondwelela kuti mwanayo wacoka ku bele. Koma panali vuto. Timaŵelenga kuti Sara anali ‘kuona’ khalidwe loipa. Isimaeli, mwana wa zaka 19 wa Hagara, anapitiliza kuvutitsa Isaki wacicepele. Kuvutitsaku sikunali kwa maseŵela cabe. Mtumwi Paulo anauzilidwa kulemba za khalidwe la Isimaeli kuti kunali kuzunza. Sara anaona kuti kuvutitsa kumeneku kunali kuika moyo wa mwana wake pa ciwopsezo. Anali kudziŵa kuti Isaki sanali cabe mwana wamba, koma anali na mbali yofunika kwambili pa colinga ca Yehova. Conco, molimba mtima anakamba na Abulahamu mosapita m’mbali. Anapempha kuti Abulahamu athamangitse Hagara na Isimaeli.​—Genesis 21:​8-​10; Agalatiya 4:​22, 23, 29.

Kodi Abulahamu anacitanji? Timaŵelenga kuti: “Abulahamu anaipidwa nazo kwambili zimenezi cifukwa ca mwana wake.” Abulahamu anali kum’konda Isimaeli, ndipo monga kholo sanafune kukhala zii. Komabe, Yehova anali kuidziŵa nkhani yonse. Conco, nayenso analoŵelelapo. Timaŵelenga kuti: “Koma Mulungu anauza Abulahamu kuti: ‘Usaipidwe ndi ciliconse cimene Sara wakhala akunena kwa iwe cokhudza mnyamatayo ndiponso kapolo wakoyo. Mvela mawu ake, cifukwa amene adzachedwa mbewu yako adzacokela mwa Isaki.” Yehova anatsimikizila Abulahamu kuti Hagara na mwana wake adzawasamalila. Abulahamu anagonjela mokhulupilika.​—Genesis 21:​11-​14.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

wp17.3 12, mawu apansi

“Ndiwe Mkazi Wokongola M’maonekedwe Ako”

Sara anali mlongosi wa Abulahamu. Atate awo anali Tera, koma amayi awo anali osiyana. (Genesis 20:12) Ngakhale kuti cikwati caconco si coyenela masiku ano, n’kofunika kuganizila mmene zinthu zinalili kalelo. Anthu anali pafupi na ungwilo umene Adamu na Hava anataya. Conco, kwa iwo kukwatilana ndi wacibululu sikunabweletse vuto lililonse kwa ana amene anali kubeleka. Koma patapita zaka 400, anthu anali atatalikilana kwambili na ungwilo. Panthawi imeneyo, Cilamulo ca Mose cinaletsa vikwati va pa cibululu.​—Levitiko 18:⁠6.

w89 7/1 20 ¶9

Abulahamu​—Citsanzo Kwa Onse Ofuna Ubwenzi wa Mulungu

Abulamu anacitanso cinthu cina coonetsa kuti anali na cikhulupililo. Nkhaniyo imati: “Iye anamanga pamalopo guwa lansembe la Yehova.” (Genesis 12:⁠7) Mwacionekele, izi zinaphatikizapo kupeleka nsembe ya nyama, cifukwa liwu la Ciheberi lakuti “guwa la nsembe,” limatanthauza “malo opelekela nsembe.” Pambuyo pake, Abulamu anabweleza kucita zinthu zoonetsa cikhulupililo zimenezi m’mbali zina za dzikolo. Kuwonjezela apo, iye ‘anaitanila pa dzina la Yehova.’ (Genesis 12:8; 13:18; 21:33) Mawu Aciheberi akuti “kuitanila pa dzina” amatanthauzanso “kulengeza (kulalikila) dzinalo.” Banja la Abulamu komanso Akanani ayenela kuti anamumva iye akulengeza molimba mtima dzina la Mulungu wake, Yehova. (Genesis 14:​22-​24) Mofananamo, onse ofuna kukhala pa ubwenzi na Mulungu masiku ano, ayenela kuitanila pa dzina lake m’cikhulupililo. Izi ziphatikizapo kugwila nawo nchito yolalikila poyela. Inde “nthawi zonse tizitamanda Mulungu. Tizicita zimenezi monga nsembe imene tikupeleka kwa Mulungu, yomwe ndi cipatso ca milomo yathu. Timagwilitsa nchito milomo imeneyi polengeza dzina lake kwa anthu ena.”​—Aheberi 13:15; Aroma 10:⁠10.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani