LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w14 11/1 masa. 10-13
  • Kodi Ufumu wa Mulungu Unayamba Liti Kulamulila? (Mbali 1)

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Ufumu wa Mulungu Unayamba Liti Kulamulila? (Mbali 1)
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • PITILIZANI ‘KUFUFUZA’ KUTI MUMVETSETSE
  • LOTO LA NEBUKADINEZARA
  • NKHANI YAIKULU YA M’BUKULI
  • “PADUTSE NTHAWI ZOKWANILA 7”
  • Umoyo Wabwino Koposa (The Best Life Ever)
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Msonkhano (2016)
  • Ufumu wa Mulungu Ukulamulila Pali Pano!
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Tizitengelapo Phunzilo pa Zolakwa Zathu
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano —2017
  • Zimene Tiphunzilamo m’Buku la Yona
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano —2017
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
w14 11/1 masa. 10-13
A Zulu ndi a Zimba akambilana za Ufumu wa Mulungu

KUKAMBILANA NDI MUNTHU WINA NKHANI ZA M’BAIBULO

Kodi Ufumu wa Mulungu Unayamba Liti Kulamulila?—Mbali 1

Nkhani yotsatilayi ikuonetsa mmene a Mboni za Yehova amacitila akamakambilana ndi anthu nkhani za m’Baibulo. Tiyelekeze kuti a Zulu ndi a Mboni, ndipo afika pa khomo la bambo Zimba.

PITILIZANI ‘KUFUFUZA’ KUTI MUMVETSETSE

A Zulu: A Zimba, kunena zoona, ndimakondwela kukambilana nanu za m’Baibulo kumene timakhala nako nthawi zonse.a Ulendo wapita, munafunsa funso lokhudza Ufumu wa Mulungu. Munafunsa cifukwa cake ife a Mboni za Yehova timakhulupilila kuti Ufumu wa Mulungu unayamba kulamulila mu 1914.

A Zimba: N’zoona, cifukwa cakuti ndinaŵelenga cofalitsa canu cimene cinakamba kuti Ufumu wa Mulungu unayamba kulamulila mu 1914. Zimenezi zinandidabwitsa kwambili popeza kuti inu mumakamba kuti zonse zimene mumakhulupilila ndi za m’Baibulo.

A Zulu: N’zoona, timatelo.

A Zimba: Inenso ndinaŵelenga Baibulo lonse. Koma sindikumbukila kuti ndinaonako paliponse pamene panalembedwa caka ca 1914. Ndinayesanso kufufuza m’Baibulo ya pa intaneti za caka ca “1914.” Koma, namonso mulibiletu caka cimeneci.

A Zulu: A Zimba, ndikuyamikilani kwambili pa zifukwa ziŵili. Coyamba, cifukwa munaŵelenga Baibulo lonse. Izi zikuonetsa kuti mumakonda kwambili Mau a Mulungu.

A Zimba: Zikomo. Ndimalikonda cifukwa palibe buku lina loposa Baibulo.

A Zulu: N’zoona zimenezo. Ndipo caciŵili, ndikuyamikilani poyesetsa kufufuza yankho la funso lanu m’Baibulo. Munacita ndendende zimene Baibulo limatilimbikitsa kucita: Kupitiliza ‘kufufuza’ kuti timvetsetse.b Zikomo kwambili cifukwa ca khama lanu.

A Zimba: Zikomo. Ndikufunitsitsa kudziŵa zambili. Ndipo nditafufuzanso za caka cimeneci ca 1914 m’bukuli limene timagwilitsila nchito pophunzila Baibulo, ndinapezamo mfundo zoonjezeleka. Linakamba za loto lina la mfumu lokhudza mtengo waukulu umene unagwetsedwa, kenako unaphukilanso. Kaya ndi mmenemo, sindikumbukila bwinobwino.

A Zulu: O-o-o n’zoona. Umenewo ndi ulosi wolembedwa mu Danieli caputala 4. Umakamba za loto limene Mfumu Nebukadinezara wa ku Babulo analota.

A Zimba: Ehee! ndi imeneyo. Ulosiwo ndinauŵelenga mobwelezabweleza. Koma kukamba zoona, sindikuona kugwilizana kulikonse ndi Ufumu wa Mulungu kapena caka ca 1914.

A Zulu: Sindinu nokha a Zimba amene mukulephela kumvetsetsa ulosiwo. Ngakhale mneneli Danieli sanamvetsetse bwinobwino tanthauzo la zimene anauzilidwa kulemba.

A Zimba: Zoona?

A Zulu: Inde. Pa Danieli 12:8, iye anakamba kuti: “Tsopano ine ndinamva zimene ananenazo, koma sindinadziŵe tanthauzo lake.”

A Zimba: Ndiye kuti sindine ndekha eti! Zimenezo zandipatsako mphamvu.

A Zulu: Zoona zake n’zakuti, Danieli sanadziŵe tanthauzo la maulosiwo cifukwa cakuti nthawi ya Mulungu inali isanakwane yakuti anthu azindikile tanthauzo la maulosi amenewo. Koma masiku ano, tingamvetsetse bwinobwino tanthauzo la maulosiwo.

A Zimba: N’cifukwa ciani mukutelo?

A Zulu: Cabwino, onani zimene vesi lotsatila likunena. Pa Danieli 12:9 pamati: “Mauwa asungidwa mwacisinsi ndipo atsekedwa ndi kumatidwa kufikila nthawi ya mapeto.” Conco, tanthauzo la maulosiwa linayenela kudziŵika mtsogolo, ‘m’nthawi yamapeto.’ Ndipo monga mmene tidzaphunzilila kutsogoloku m’phunzilo lathu la Baibulo, tidzaona kuti maumboni onse aonetsa kuti tikukhala m’nthawi imeneyo.c

A Zimba: Kodi n’zotheka kundifotokozela tanthauzo la ulosi wa Danieli?

A Zulu: Cabwino, tiyeni tikambilane.

LOTO LA NEBUKADINEZARA

A Zulu: Tiyambe ndi kufotokoza mwacidule zimene Mfumu Nebukadinezara inaona m’loto lake. Ndiyeno tidzambilana tanthauzo la lotolo.

A Zimba: Cabwino.

Mfumu Nebukadinezara alota mtengo waukulu

A Zulu: M’loto lake Nebukadinezara anaona mtengo umene unakula kwambili mpaka kufika kumwamba. Ndiyeno anamva mthenga wa Mulungu akukamba kuti mtengowo udulidwe. Ndiyeno Mulungu anati citsa cake cisiidwe m’nthaka. Pakapita “nthawi zokwanila 7,” mtengowo unayenela kuphukilanso.d Coyamba ulosiwu unali kukhudza Mfumu Nebukadinezara ameneyo. Ngakhale kuti anali mfumu yochuka monga mtengo umene unakula mpaka kufika kumwamba, iye anadulidwa mpaka patadutsa “nthawi zokwanila 7.” Kodi mukukumbukila zimene zinacitika?

A Zimba: Iyai, sindikumbukila.

A Zulu: Cabwino, palibe vuto. Baibulo limaonetsa kuti Nebukadinezara anacita misala kwa zaka 7. Panthawi imeneyo, iye sanathe kulamulila monga mfumu. Koma nthawi zokwanila 7 zitatha, Nebukadinezara anacila misala yake ndi kuyambanso kulamulila.e

A Zimba: Ndikumvetsa zimene mukunena. Koma kodi zonsezi zikukhudza bwanji Ufumu wa Mulungu ndi caka ca 1914?

A Zulu: Mwacidule ulosiwu uli ndi kukwanilitsidwa kwa mbali ziŵili. Mbali yoyamba inakwanilitsidwa pamene ulamulilo wa Mfumu Nebukadinezara unasokonezedwa. Mbali yaciŵili inakhudza kusokonezedwa kwa ulamulilo wa Mulungu. Conco kukwanilitsidwa kwaciŵili kumeneku ndi kumene kuli kogwilizana ndi Ufumu wa Mulungu.

A Zimba: Mudziŵa bwanji kuti ulosiwo uli ndi kukwanilitsidwa kwaciŵili kumene kukukhudza Ufumu wa Mulungu?

A Zulu: Coyamba, umboni timaupeza mu ulosi umenewo. Mogwilizana ndi Danieli 4:17, ulosiwo unapelekedwa “ndi colinga cakuti anthu adziŵe kuti Wam’mwambamwamba ndiye woyenela kulamulila maufumu a anthu, ndiponso adziŵe kuti iye akafuna kupeleka ulamulilo kwa munthu aliyense amamupatsa.” Kodi mau akuti “maufumu a anthu” mwawaona?

A Zimba: Inde, Baibulo lanena kuti “Wam’mwambamwamba ndiye wolamulila wa maufumu a anthu.”

A Zulu: Mwayankha bwino. Koma kodi muganiza kuti “Wam’mwambamwamba” ameneyo ndani?

A Zimba: Ndiganiza kuti ndi Mulungu.

A Zulu: N’zoona. Conco pamenepa ndi pomwe timadziŵila kuti ulosiwu sukamba za Nebukadinezara cabe. Ulosiwu ukuphatikizapo “ufumu wa anthu,” umene ndi ulamulilo wa Mulungu pa anthu. Ndipo zimenezi n’zomveka makamaka tikaŵelenga ulosiwu wonse.

A Zimba: Mukutanthauza ciani?

NKHANI YAIKULU YA M’BUKULI

A Zulu: Buku la m’Baibulo la Danieli limafotokoza za nkhani yaikulu imeneyi nthawi zambili. Kaŵilikaŵili limachula za kukhazikitsidwa kwa Ufumu wa Mulungu pansi pa ulamulilo wa Mwana wake, Yesu. Mwacitsanzo tiyeni tiŵelenge pa Danieli 2:44. Mungaŵelengepo?

A Zimba: Inde. Pamati: “M’masiku a mafumu amenewo, Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa Ufumu umene sudzaonongedwa ku nthawi zonse. Ufumuwo sudzapelekedwa kwa mtundu wina uliwonse wa anthu, koma udzaphwanya ndi kuthetsa maufumu ena onsewo, ndipo udzakhalapo mpaka kalekale.”

A Zulu: Zikomo, mwaŵelenga bwino. Kodi muganiza kuti vesili likukamba za Ufumu wa Mulungu?

A Zimba: Hmm. Ndikaikila.

A Zulu: Cabwino, koma onani kuti lembali lanena kuti Ufumuwu “udzakhalapo mpaka kalekale.” Mwacionekele ndi Ufumu wa Mulungu wokha umene udzakhalapo mpaka kalekale osati boma lililonse la anthu. Si conco?

A Zimba: Ee, n’zoona.

A Zulu: Palinso ulosi wina wa m’buku la Danieli umene ukunena za Ufumu wa Mulungu. Ndi ulosi wolembedwa pa Danieli 7:13, 14. Ponena za wolamulila wamtsogolo, ulosiwo umati: “Anamupatsa ulamulilo, ulemelelo, ndi ufumu kuti anthu a mitundu yosiyanasiyana azimutumikila. Ulamulilo wake udzakhalapo mpaka kalekale ndipo sudzatha. Ufumu wake sudzaonongedwa.” Kodi ndi mau ati amene si acilendo mu ulosiwu?

A Zimba: Ndi mau akuti ufumu.

A Zulu: N’zoona zimenezo. Ndipo sikuti ndi ufumu wina uliwonse. Onani kuti ulosiwu wanena kuti Ufumu umenewu adzalamulila “anthu a mitundu yosiyanasiyana ndi olankhula zinenelo zosiyanasiyana.” M’mau ena tinganene kuti Ufumu umenewu udzalamulila dziko lonse lapansi.

A Zimba: Sindinali kudziŵa tanthauzo la lembali. Koma mukunenadi zoona, cifukwa ndi zimene lembali lanena.

A Zulu: Onaninso zimene ulosi ukunena: “Ulamulilo wake udzakhalapo mpaka kalekale ndipo sudzatha. Ufumu wake sudzawonongedwa.” Kodi mwaona kuti ulosiwu ukugwilizana ndi ulosi umene taŵelenga pa Danieli 2:44?

A Zimba: Inde ukugwilizana.

A Zulu: Mwacidule tiyeni tibweleze zimene takambilana. Ulosi wa pa Danieli capitala 4 unalembedwa kuti anthu adziŵe kuti “Wam’mwambamwamba ndiye Wolamulila wa maufumu a anthu.” Mwacionekele, ulosiwu sunali kudzakwanilitsidwa pa Nebukadinezara cabe, koma unali kudzakwanilitsa mbali ina yofunika kwambili. Ndipo m’buku lonse la Danieli, timapezamo maulosi ena okhudza Ufumu wa Mulungu mu ulamulilo wa Mwana wake. Conco ulosi wa pa Danieli capitala 4 ukukhudza Ufumu wa Mulungu, siconco kodi?

A Zimba: Ndi mmenemo. Koma sindikuonabe kugwilizana ndi caka ca 1914.

“PADUTSE NTHAWI ZOKWANILA 7”

A Zulu: Kumbukilani kuti mtengo wa mu ulosiwu unali kuimila Mfumu Nebukadinezara. Ulamulilo wake unasokonezedwa pamene mtengo unadulidwa ndi kusiidwa kwa nthawi zokwanila 7, atacita misala. Nthawi zokwanila 7 zinatha pamene misala ya Nebukadinezara inatha ndi kuyambanso ulamulilo wake. M’kukwanilitsidwa kwaciŵili kwa ulosi umenewu, ulamulilo wa Mulungu unasokonezedwa kwa kanthawi, koma sizinatanthauze kuti ulamulilo wa Mulungu unalephela ai.

A Zimba: Mutanthauza ciani?

A Zulu: Ndikutanthauza kuti pamene mafumu aciisiraeli anali kulamulila m’Yelusalemu m’nthawi za Baibulo, zinali ngati akukhala pa “mpando wacifumu wa Yehova.”f Polamulila anthu ake, io anali kuimila Mulungu. Conco ulamulilo wa mafumuwo unali kuimila ulamulilo wa Mulungu. Koma patapita nthawi, ambili mwa mafumu amenewo analeka kumvela Mulungu, ndipo anthu ambili amene io anali kulamulila anatsatilanso citsanzo cao coipa. Cifukwa cakuti Aisiraeli anapanduka, Mulungu analola kuti agonjetsedwe ndi Ababulo mu 607 B.C.E. Motelo kucokela nthawiyo, m’Yelusalemu munalibe mfumu imene inali kuimila Yehova. Mwa njila imeneyo tingaone kuti ulamulilo wa Mulungu unasokonezedwa. Kodi zimene ndikufotokoza zimveka?

A Zimba: Inde.

A Zulu: Conco caka ca 607 B.C.E. cinali ciyambi ca nthawi zokwanila 7, kapena nyengo ya nthawi pamene ulamulilo wa Mulungu unasokonezedwa. Pa kutha kwa nthawi zokwanila 7, Mulungu anali kudzakhazikitsa wolamulila watsopano wakumwamba kuti akhale woimila ulamulilo wake. Apa ndi pamene maulosi ena amene timaŵelenga m’buku la Danieli anali kudzakwanilitsidwa. Koma funso lofunika kwambili ndi lakuti: Ndi liti pamene nthawi zokwanila 7 zinatha? Tikapeza yankho la funsoli, kudzakhala kosavuta kudziŵa pamene Ufumu wa Mulungu unayamba kulamulila.

A Zimba: O-oo, ndikumvetsa tsopano, mutanthauza kuti nthawi zokwanila 7 zinatha mu 1914?

A Zulu: Mwakamba zoona, ndi mmenedi zilili!

A Zimba: Koma tidziŵa bwanji zimenezo?

A Zulu: Pamene Yesu anali pa dziko lapansi, anaonetsa kuti nthawi zokwanila 7 zinali zisanathe.g Conco, nyengoyi iyenela kukhala nthawi yaitali kwambili. Nthawi zokwanila 7 zinayamba zaka zambilimbili Yesu asanabwele pa dziko lapansi, ndipo zinapitiliza ngakhale atabwelela kumwamba. Tisaiŵale kuti tanthauzo la maulosi a m’buku la Danieli anali cinsinsi mpaka “nthawi ya mapeto.”h N’zocititsa cidwi kuti ca m’ma 1800, ophunzila Baibulo oona mtima anayamba kufufuza ndi kuphunzila maulosi amenewa mosamala kwambili. Iwo anayamba kuzindikila kuti nthawi zokwanila 7 zidzatha mu 1914. Ndipo zinthu zikuluzikulu zimene zakhala zikucitika padziko lapansi kuyambila cakaco, zikutitsimikizila kuti Ufumu wa Mulungu unayambadi kulamulila mu 1914. M’cakaci m’pamene masiku otsiliza, kapena kuti nthawi ya mapeto a dziko lino anayamba. Ndikhulupilila kuti takambilana zinthu zambili zatsopano zofunika kuziganizila.

A Zimba: Zoonadi, ndifunika kukaŵelenganso nkhaniyi kuti ndiimvetsetse bwino.

A Zulu: Musade nkhawa. Inenso zinanditengela nthawi kuti ndimvetse maulosi amenewa ndi kukwanilitsidwa kwake. Sindikukaikila kuti zocepa zimene takambilanazi, zakuthandizani kuona kuti zimene Mboni za Yehova zimakhulupilila ponena za Ufumu zimacokela m’Baibulo.

A Zimba: N’zoona. Ndipo nthawi zonse ndimasangalala kuti zikhulupililo zanu zimacokela m’Baibulo.

A Zulu: Ndikuona kuti inunso mumalikhulupilila Baibulo. Koma monga mmene ndinali ndakambila, simungathe kumvetsetsa zinthu zonsezi pa nthawi imodzi. Mwina mulinso ndi mafunso ena. Mwacitsanzo, taona kuti nthawi zokwanila 7 zikukhudza Ufumu wa Mulungu ndi kuti nthawi zimenezi zinayamba mu 607 B.C.E. Koma, kodi timadziŵa bwanji kuti nthawi zokwanila 7 zimenezi zinathadi mu 1914?i

A Zimba: Eya, ndinali kufuna kufunsa funso limeneli.

A Zulu: Baibulo ndi limene limatithandizanso kudziŵa utali weniweni wa nthawi zokwanila 7. Kodi mungakonde kuti tidzakambilane nkhaniyi ndikadzabwelanso?j

A Zimba: Palibe vuto.

Kodi m’Baibulo muli nkhani ina imene sumumvetsetsa? Kodi mumacita cidwi ndi zimene a Mboni za Yehova amakhulupilila kapena zimene amacita? Ngati ndi conco, musazengeleze kufunsa mmodzi wa Mboni za Yehova. Iye adzakondwela kwambili kukambilana nanu nkhani zimenezi.

a A Mboni za Yehova ali ndi njila yabwino imene amatsatila pokambilana Baibulo ndi anthu kwaulele pa nkhani zosiyanasiyana.

b Miyambo 2:3-5.

c Onani nkhani 9 m’buku la Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Ipezekanso pa Webusaiti yathu pa www.jw.org.

d Danieli 4:13-17.

e Danieli 4:20-36.

f 1 Mbiri 29:23.

g Ponena za ulosi wokhudza masiku otsiliza Yesu anati: “Anthu amitundu ina adzapondaponda Yerusalemu [amene akuimila ulamulilo wa Mulungu], kufikila nthawi zoikidwilatu za anthu amitundu inawo zitakwanila.” (Luka 21:24) Conco tinganene kuti kusokonezedwa kwa ulamulilo wa Mulungu kunali kudakalipo pamene Yesu anali padziko lapansi ndipo kunayenela kupitilizabe mpaka m’masiku otsiliza.

h Danieli 12:9.

i Onani masamba 215 mpaka 218 a buku la Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni. Buku limeneli likupezekanso pa Webusaiti yathu ya www.jw.org.

j Nkhani yotsatila m’nkhani zimenezi idzafotokoza mavesi a m’Baibulo amene amatiunikila kuti tidziŵe utali wa nthawi zokwanila 7.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani