LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lfb phunzilo 6 tsa. 20-tsa. 21 pala. 5
  • Anthu 8 Anapulumuka na Kulowa m’Dziko Latsopano

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Anthu 8 Anapulumuka na Kulowa m’Dziko Latsopano
  • Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Nkhani Zofanana
  • Cingalawa ca Nowa
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Cigumula Cacikulu
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Nowa Apanga Cingalawa
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Anam’sunga “Pomupulumutsa Pamodzi ndi Anthu Ena 7”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
Onaninso Zina
Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
lfb phunzilo 6 tsa. 20-tsa. 21 pala. 5
Cimvula cikugwa ndipo combo ciyandama pamadzi

PHUNZILO 6

Anthu 8 Anapulumuka na Kuloŵa m’Dziko Latsopano

Nowa, banja lake, na vinyama atuluka m’cingalawa

Nowa na banja lake, komanso vinyama, anangena m’cingalawa. Yehova anavala citseko, ndipo mvula inayamba kugwa. Mvulayo inagwa maningi cakuti combo cimeneco cinayamba kuyandama pamadzi. M’kupita kwa nthawi, dziko lonse lapansi linamila m’madzi. Anthu onse oipa amene anali kunja kwa cingalawa anafa. Koma Nowa na banja lake anali otetezeka mkati mwa cingalawa. Iwo anakondwela ngako kuti anamvela zimene Yehova anawauza.

Cimvula cinagwa kwa masiku 40 usana na usiku. Kenako cinaleka. Ndiyeno, pang’ono-pang’ono madzi anayamba kucepa. Potsilizila, combo cija cinakhazikika pa phili. Koma pansi panali madzi kulikonse. Conco Nowa na banja lake sakanatuluka m’cingalawa pa nthawiyo.

Pang’ono-pang’ono, madzi anayamba kuphwila. Nowa pamodzi na banja lake anakhala m’cingalawa kuposa caka cimodzi. Ndiyeno Yehova anawauza kuti atuluke m’cingalawa kuti akhale m’dziko looneka monga latsopano. Iwo anamuyamikila ngako Yehova cifukwa cowapulumutsa. Cakuti anapeleka nsembe yowonga zikomo kwa Yehova.

Utawaleza

Yehova anakondwela nayo nsembe imene iwo anapeleka. Nakulonjeza kuti sadzawononganso ciliconse pa dziko lapansi na cigumula ca madzi. Ndipo anaika utawaleza m’mwamba monga cikumbutso ca lonjezo limenelo. Kodi unauonapo utawaleza?

Pambuyo pa zonsezi, Yehova anauza Nowa na banja lake kuti ayambe kubala ana na kudzaza dziko lapansi.

“Nowa analowa m’cingalawa. Anthu ananyalanyaza zimene zinali kucitika mpaka Cigumula cinafika n’kuwaseselatu onsewo.”—Mateyu 24:38, 39

Mafunso: N’ciani cinacitika pamene Yehova anavala citseko ca cingalawa? Kodi utawaleza umatikumbutsa ciani?

Genesis 7:1–9:17

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani