LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lfb phunzilo 21 tsa. 54-tsa. 55 pala. 2
  • Mlili wa Namba 10

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mlili wa Namba 10
  • Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Nkhani Zofanana
  • Mose Ndi Aroni Aonana Ndi Farao
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Milili Itatu Yoyambilila
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Mfumu Yoipa Ilamulila Ku Iguputo
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Mose Anasankha Kulambila Yehova
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
Onaninso Zina
Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
lfb phunzilo 21 tsa. 54-tsa. 55 pala. 2
Mwamuna waciisiraeli apaka magazi pakhomo la nyumba yake

PHUNZILO 21

Mlili wa Namba 10

Mose analonjeza Farao kuti sadzabwelanso kwa iye. Koma pocoka, anauza Farao kuti: ‘Pakati pa usiku, mwana wamwamuna aliyense woyamba kubadwa wa Aiguputo adzafa. Kuyambila mwana wa Farao mpaka ana a akapolo ake, onse adzafa.’

Ndiyeno Yehova anauza Aisiraeli kuti akonze cakudya capadela. Anati: ‘Iphani mwana wa nkhosa wamphongo kapena wa mbuzi wa caka cimodzi. Mupake magazi ake pa mafelemu a pa makomo anu. Muwoche nyama yake, muidye pamodzi na mkate wopanda cofufumitsa. Muzidya mutavala nsapato zanu, kukonzekela ulendo. Usiku wa lelo nidzakumasulani.’ Ganizila cabe cimwemwe cimene Aisiraeli anali naco!

Pakati pa usiku, mngelo wa Yehova anapita pa nyumba iliyonse mu Iguputo. Ndipo anapha mwana wamwamuna woyamba pa nyumba iliyonse imene sanawaze magazi pakhomo. Koma mngeloyo anali kupitilila nyumba zimene zinali zowaza magazi. Pa banja lililonse la Aiguputo, kaya lolemela kapena losauka, panali malilo. Koma kwa Aisiraeli sikunafe mwana olo mmodzi.

Ngakhale mwana wa Farao anaphedwa. Apa lomba Farao anakhaula. Ndipo anauza Mose na Aroni kuti: ‘Nyamukani, khamani cokani. Pitani mukatumikile Mulungu wanuyo. Tengani na nyama zanu, pitani!’

Mwezi wathunthu ukuŵala usiku, Aisiraeli anacoka mu Iguputo, mwa dongosolo la mabanja awo na mafuko awo. Amuna aciisraeli analipo 600,000. Panalinso akazi ambili pamodzi ndi ana awo. Komanso, anthu ena ambili anapita nawo pamodzi kuti nawonso akalambile Yehova. Apa lomba Aisiraeli anamasuka!

Kuti Aisiraeli azikumbukila mmene Yehova anawapulumutsila, anali kukonza cakudya capadela caka ciliconse. Cakudya cimeneco cinali kuchedwa Pasika.

Aisiraeli acoka mu Iguputo

“Ndakusiya ndi moyo kuti ndikusonyeze mphamvu zanga, ndi kuti dzina langa lilengezedwe padziko lonse lapansi.”—Aroma 9:17

Mafunso: Kodi cinacitika n’ciani pa mlili wa namba 10? Nanga Aisiraeli anafunika kucita ciani kuti adziteteze ku mlili umenewo?

Ekisodo 11:1–12:42; 13:3-10

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani