PHUNZILO 10
Kusintha-sinthako Mawu
Miyambo 8:4, 7
ZOFUNIKILA: Mveketsani bwino malingalilo, ndipo akhudzeni mtima omvela anu posintha-sinthako mphamvu ya mawu, kuwakweza kapena kuwatsitsa, komanso liŵilo lake.
MOCITILA:
Muzisintha-sinthako mphamvu ya mawu anu. Wonjezelani mphamvu ya mawu pogogomeza mfundo yaikulu, komanso polimbikitsa omvela anu. Citaninso cimodzi-modzi poŵelenga mawu a ciweluzo a m’Malemba. Cepetsani mphamvu ya mawu pofuna kukopa cidwi, kapena pochula zoopsa, olo zodetsa nkhawa.
Muzisiyanitsa kamvekedwe ka mawu anu. Kwezani kamvekedwe ka mawu anu poonetsa kusangalala, ukulu wa cinthu, msenga kaya kuti mtunda. Tsitsani mawu anu poonetsa cisoni kapena nkhawa.
Siyanitsani liŵilo la mawu anu. Lankhulani mofulumila kuonetsa cisangalalo. Koma musathamange pofuna kumveketsa mfundo zofunika.