Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki
MAY 3-9
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | NUMERI 27-29
“Tengelani Citsanzo ca Yehova ca Kupanda Tsankho”
w13 6/15 10 ¶14
Makhalidwe a Yehova Ndi Amtengo Wapatali
14Ana aakazi asanuwo anapita kwa Mose n’kumufunsa kuti: “Kodi dzina la bambo athu licotsedwe ku banja lawo cifukwa cakuti analibe mwana wamwamuna?” Ndiyeno anacondelela kuti: “Conde, tipatseni colowa pakati pa abale awo a bambo athu.” Koma Mose sananene kuti, ‘Kodi mwaiwala zimene malamulo amanena?’ M’malomwake, “anapeleka dandaulo lawolo pamaso pa Yehova.” (Num. 27:2-5) Kodi Yehova anayankha bwanji? Iye anauza Mose kuti: “Ana aakazi a Tselofekadi akunena zoona. Uwapatsedi malo monga colowa cawo, pakati pa abale a bambo awo. Colowa ca bambo awoco cikhale cawo.” Koma Yehova sanasiyile pomwepo. Anasintha lamulolo n’kunena kuti: “Mwamuna akamwalila wopanda mwana wamwamuna, muzipeleka colowa cake kwa mwana wake wamkazi.” (Num. 27:6-8; Yos. 17:1-6) Kuyambila nthawi imeneyo, akazi onse a ku Isiraeli amene anakumana ndi vuto limeneli anali kuthandizidwa.
w13 6/15 11 ¶15
Makhalidwe a Yehova Ndi Amtengo Wapatali
15Apa Mulungu anacita zinthu mokoma mtima ndiponso mopanda tsankho. Yehova anacita zinthu na akazi ovutikawo mwaulemu ngati mmene anali kucitila na Aisiraeli ena amene zinthu zinali kuwayendela bwino. (Sal. 68:5) Pali nkhani zambili m’Baibo zoonetsa kuti Yehova sakondela pocita zinthu na atumiki ake onse.—1 Sam. 16:1-13; Mac. 10:30-35, 44-48.
w13 6/15 11 ¶16
Makhalidwe a Yehova Ndi Amtengo Wapatali
16Kodi tingatsanzile bwanji Yehova pa nkhani yocita zinthu mopanda tsankho? Kumbukilani kuti kucita zinthu mopanda tsankho kumayambila mumtima. Koma ife anthu timakonda kuganiza kuti, ‘Aa ine ndilibe tsankho ndipo siniyang’ana nkhope pocita zinthu.’ Ngakhale zili conco, mukhoza kuvomeleza kuti nthawi zina sitingaone bwino-bwino vuto lathu. Ndiyeno kodi tingadziŵe bwanji mmene anthu ena amationela pa nkhani imeneyi? Kumbukilani zimene Yesu anacita pofuna kudziŵa maganizo a anthu ena. Iye anafunsa anzake amene anali kuwadalila kuti: “Kodi anthu akumanena kuti Mwana wa munthu ndani?” (Mat. 16:13, 14) Mwina nanunso mungafunse mnzanu amene mukuona kuti sangakubisileni zinthu kuti akuuzeni ngati mumadziŵika kuti ndinu wopanda tsankho kapena ayi. Kodi mungatani ngati atakuuzani kuti muli na kamtima kokondela anthu amtundu winawake, ochuka kapena acuma? Muyenela kupempha Yehova kucokela pansi pa mtima kuti akuthandizeni kusintha n’colinga coti muzimutsanzila kwambili pa nkhani yocita zinthu mopanda tsankho.—Mat. 7:7; Akol. 3:10, 11.
Kufufuza Cuma Cauzimu
it-2 528 ¶5
Nsembe
Nsembe zacakumwa. Nthawi zambili nsembe zacakumwa zinali kupelekedwa pamodzi na nsembe zina, maka-maka pamene Aisiraeli analoŵa m’Dziko Lolonjezedwa. (Num. 15:2, 5, 8-10) Nsembe yacakumwa inali vinyo (“cakumwa coledzeletsa”) ndipo anali kuithila paguwa lansembe. (Num. 28:7, 14; yelekezelani na Eks. 30:9; Num. 15:10.) Mtumwi Paulo analembela Akhristu a ku Filipi kuti: “Ngakhale kuti ndikudzipeleka ngati nsembe yacakumwa imene ikuthilidwa pansembe ndi pa nchito yotumikila anthu imene cikhulupililo cakupatsani, ndine wokondwa.” Pamenepa, iye anayelekezela kudzipeleka kwake potumikila Akhristu anzake na nsembe yacakumwa. (Afil. 2:17) Atatsala pang’ono kuphedwa, analembela Timoteyo kuti: “Ine ndayamba kale kukhuthulidwa ngati nsembe yacakumwa, ndipo nthawi yakuti ndimasuke yatsala pang’ono kukwana.”—2 Tim. 4:6.
MAY 10-16
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | NUMERI 30-31
“Muzikwanilitsa Malumbilo Anu”
it-2 1162
Lumbilo
Lopangidwa Modzifunila, Koma Likapangidwa Linafunika Kukwanilitsidwa. Munthu anali kupanga lumbilo mwa kufuna kwake. Koma munthu akacita lumbilo, Cilamulo ca Mulungu cinali kufuna kuti alikwanilitse zivute zitani. Ndiye cifukwa cake Malemba amati lumbilo limene munthu wapanga linali “kumangila moyo wake,” kutanthauza kuti anali wokonzeka kutaya moyo wake ngati sanakwanilitse zimene walonjeza. (Num. 30:2; Buku Lopatulika; onaninso Aroma 1:31, 32.) Popeza munthu akanatha kutaya moyo wake, mpake kuti Malemba amalimbikitsa munthu kusamala kwambili asanapange lumbilo. Ayenela kuganizila mosamala zimene adzafunika kucita kuti akwanilitse lumbilo lake. Cilamulo cinati: “Ukapeleka lonjezo kwa Yehova . . . Mulungu wako adzafuna ndithu kuti ukwanilitse cimene walonjezaco. Koma ukapanda kulonjeza, sunacimwe.”—Deut. 23:21, 22.
w17 04 3¶2
Lumbilo
M’Baibo, liwu lakuti lonjezo limatanthauza cowinda cimene munthu amapanga kwa Mulungu. Munthu angalonjeze kucita zinthu, kupeleka mphatso, kuyamba utumiki, kapena kupewa kucita zinazake. Munthu amapanga lonjezo mwa kufuna kwake. Komabe, Mulungu amaona kuti malonjezo amene timapanga ni opatulika, ndipo ni osasinthika cifukwa amalowetsamo lumbilo lakuti munthu adzacita zinthu zina kapena sadzacita. (Gen. 14:22, 23; Aheb. 6:16, 17) Kodi Malemba amaonetsa bwanji kuti kupanga malonjezo kwa Mulungu ni nkhani yaikulu?
w04 8/1 27 ¶3
Mfundo Zazikulu za M’buku la Numeri
30:6-8—Kodi mwamuna wacikhristu angafafanize zowinda za mkazi wake? Nkhani ya zowinda masiku ano imakhala pakati pa Yehova na wolambila aliyense payekha. Mwacitsanzo, kudzipatulila kwa Yehova ni cowinda cimene munthu amapanga payekha. (Agalatiya 6:5) Mwamuna alibe mphamvu yofafaniza cowinda coteloco. Komabe, mkazi ayenela kuonetsetsa kuti asawinde kucita zinthu zotsutsana ndi Mawu a Mulungu kapena nchito zake kwa mwamuna wake.
Kufufuza Cuma Cauzimu
it-2 28 ¶1
Yefita
Nthawi zina anthu anali kupelekedwa kwa Yehova kuti azikam’tumikila pacihema copatulika nthawi zonse. Makolo anali na ufulu wopeleka ana awo kwa Yehova. Samueli anali mmodzi wa ana otelo. Asanabadwe, amayi ake a Hana anacita lumbilo lakuti adzam’peleka kwa Yehova kuti azikam’tumikila pacihema copatulika. Mwamuna wake Elikana anavomeleza lumbilo limeneli. Samueli atangoleka kuyamwa, Hana anakam’peleka kucihema. Pokamupeleka, Hana anatenganso nsembe ya nyama. (1 Sam. 1:11, 22-28; 2:11) Nayenso Samisoni ali mwana anapelekedwa kwa Mulungu kuti am’tumikile monga Mnaziri.—Ower. 13:2-5, 11-14; yelekezelani na ulamulilo umene tate anali nawo pa mwana wake wamkazi, malinga na zimene zinalembedwa pa Num. 30:3-5, 16.
MAY 17-23
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | NUMERI 32-33
“Mukapitikitse Anthu Onse a m’Dzikolo”
w10 8/1 23
Kodi Mudziŵa?
Kodi “misanje” kapena kuti malo opatulika amene amachulidwa kaŵili-kaŵili m’Malemba Aciheberi anali ciani?
Aisiraeli atatsala pang’ono kulowa m’Dziko Lolonjezedwa, Yehova anawauza kuti ayenela kuwononga malo onse amene Akanani anali kupembedzelapo milungu yawo. Mulungu anawalamula kuti: “Mukawononge zifanizilo zawo zonse zamiyala, ndi mafano awo onse acitsulo. Mukawonongenso malo awo onse opatulika olambilila.” (Numeri 33:52) Malo amenewa amene anali kupembedzelapo milungu yonyenga ayenela kuti anali kupezeka pamwamba pa mapili kapena anali kumanga pulatifomu pamalo ena monga pansi pa mtengo kapena pamalo ena m’mizinda. (1 Mafumu 14:23; 2 Mafumu 17:29; Ezekieli 6:3) Pamalo amenewa panali kupezeka zinthu monga maguwa ansembe, zoimilitsa, kapena kuti zipilala zopatulika, zifanizilo na zinthu zinanso zimene anali kuzigwilitsa nchito popembedza.
w08 2/15 27 ¶5-6
Titengelepo Phunzilo Pazolakwa za Aisiraeli
Masiku ano, timakumana na ziyeso zofanana ndi zimene Aisiraeli anakumana nazo. M’dziko lamakonoli, anthu ali na milungu yawo. Milungu imeneyi ni monga ndalama, akatswili a zosangalatsa ndi a maseŵelo, ndale, atsogoleli ena a zipembedzo ndipo mwinanso acibale. N’zotheka kukondetsa zinthu zimenezi kapena anthu amenewa pamoyo wathu na kumalamulidwa nawo. Kukhala mabwenzi apamtima a anthu amene sakonda Yehova kungationonge mwauzimu.
Kupembedza Baala kunaphatikizapo kucita ciwelewele, ndipo Aisiraeli ambili anakopeka naco. Misampha yoteleyi ikukolanso anthu ena a Mulungu masiku ano. Mwacitsanzo, munthu amene ali na mtima wakuti bwanji nione kapena wacibwana, angawononge cikumbumtima cake cabwino mwa kungodiniza tumabatani pakompyuta ali m’nyumba kwayekha. Zingakhale zacisoni ngati Mkhristu angakopeke na zolaula za pa Intaneti.
it-1 404 ¶2
Kanani
Powononga Akanani, “palibe mawu alionse amene Yoswa anasiya pa mawu onse amene Yehova analamula Mose.” (Yos. 11:15) Koma Aisiraeli analephela kutsatila utsogoleli wake wabwino, ndipo sanacotse zinthu zonse zodetsa zimene zinaipitsa dzikolo. Mtundu wa Aisiraeli unaipitsidwa cifukwa unalola Akanani kukhalabe pakati pawo, ndipo m’kupita kwa nthawi izi zinacititsa anthu ambili kufa (upandu, ciwelewele, na kulambila mafano zinali zosacita kukamba). Mosakayikila, amene anafa anali ambili kuposa amene akanafa Aisiraeli akanawononga Akanani onse, monga mmene Yehova anawalamulila. (Num. 33:55, 56; Ower. 2:1-3, 11-23; Sal. 106:34-43) Yehova anali atacenjezelatu Aisiraeli kuti cilungamo cake na ziweluzo zake zidzakhala zosakondela. Anawacenjeza kuti ngati adzapanga mgwilizano na Akanani, kukwatilana nawo, kugwilizana nawo pa kulambila, komanso kucita nawo miyambo yawo ya cipembedzo na makhalidwe ena oipa, mosalephela adzawonongedwa kothelatu monga Akanani, ndipo ‘dziko lidzawasanza’ nawonso.—Eks. 23:32, 33; 34:12-17; Lev. 18:26-30; Deut. 7:2-5, 25, 26.
Kufufuza Cuma Cauzimu
it-1 359 ¶2
Malile
Pambuyo pakuti maele aonetsa kumene fuko lidzalandila coloŵa cake ca malo, panafunika kudziŵa ukulu wa malowo potengela kukula kwa fukolo. Mulungu anati: “Mukagaŵile dzikolo kwa mabanja anu monga coloŵa canu mwa kucita maele. Banja la anthu ambili mukaliwonjezele colowa cawo, ndipo banja la anthu ocepa mukalicepetsele colowa cawo. Malo alionse amene maele akagwele banja, akapatsidwe kwa banjalo.” (Num. 33:54) Conco akacita maele, dela kumene fuko lapatsidwa malo monga coloŵa silinali kusintha, koma nthawi zina cimene cinali kusintha ni kukula kwa malowo. Ndiye cifukwa cake ataona kuti malo a fuko la Yuda akula kwambili, anawacepetsako mwa kupeleka mbali ina ya malowo ku fuko la Simiyoni.—Yos. 19:9.
MAY 24-30
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | NUMERI 34-36
“Thaŵilani kwa Yehova”
Kodi Mumathaŵila kwa Yehova?
4Nanga bwanji za milandu ya kupha munthu mwangozi? Kodi Aisiraeli anali kuiweluza bwanji? Munthu akapha mnzake mwangozi, anali kukhalabe na mlandu wa magazi cifukwa ca kupha munthu wosalakwa. (Gen. 9:5) Komabe, mwa cifundo ca Mulungu, munthuyo anali kuloledwa kuthaŵila ku umodzi mwa mizinda 6 yothaŵilako kuti wobwezela magazi asamuphe. Kumeneko, iye anali kukhala wotetezeka. Munthu wakupha mnzake mwangozi anali kufunika kukhalabe mumzinda wothaŵilako mpaka mkulu wa ansembe akamwalile.—Num. 35:15, 28.
Kodi Mumathaŵila kwa Yehova?
6Munthu amene wapha mnzake mwangozi akafika pacipata coloŵela mumzinda wothaŵilako, coyamba anali kufunika ‘kufotokoza nkhani yake kwa akulu.’ Iwo anali kufunika kumulandila bwino. (Yos. 20:4) Pakapita nthawi, wolakwayo anali kum’tumiza kwa akulu a mumzinda umene anaphela munthu, ndipo akulu a kumeneko ndiwo anali kuweluza mlandu wake. (Ŵelengani Numeri 35:24, 25.) Munthuyo anali kum’bwezela ku mzinda wothaŵilako kokha ngati apeza kuti sanaphe mnzake mwadala.
Kodi Mumathaŵila kwa Yehova?
13Akakhala mumzinda wothaŵilako, munthu wopha mnzake mwangozi anali kukhala wotetezeka. Pokamba za mizindayo, Yehova anati: “Mizindayo nchito yake ikhale yoti wopha munthu mwangozi azithaŵilako.” (Yos. 20:2, 3) Yehova sanalole kuti wopha mnzakeyo adzapatsiwenso cilango mtsogolo cifukwa ca chimo lakelo. Komanso, munthu wobwezela magazi sanali kuloledwa kuloŵa mumzinda wothaŵilako kuti akaphe wothaŵayo. Conco, wothaŵayo sanali kukhala mwamantha poopa kuti mwina adzaphedwa na wobwezela magazi. Akakhala mumzindawo, anali kutetezedwa na Yehova. Kumeneko, iye sanali kukhala ngati ali ku jele. Anali na ufulu woseŵenza, kuthandiza anthu ena, na kutumikila Yehova mwamtendele. Inde, anali na mwayi wokhala na umoyo wacimwemwe ndi wokhutilitsa.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w91 2/15 13 ¶13
Dipo Lolinganila kwa Onse
13Komabe, Adamu na Hava sakupindula na dipo limeneli. M’Cilamulo ca Mose munali lamulo ili: “Musalandile dipo lowombolela moyo wa munthu wakupha mnzake.” (Numeri 35:31) Adamu sananyengedwe, cotelo chimo lake linali lodzifunila, ladala. (1 Timoteyo 2:14) Mwa kucita chimolo, iye anapha mbadwa zake cifukwa izo zinatengela kupanda ungwilo kwake, motelo zinalandila ciweluzo ca imfa. N’zoonekelatu kuti Adamu anayelela kufa cifukwa monga munthu wangwilo, iye anasankha mwadala kusamvela lamulo la Mulungu. Kukanakhala kusemphana na miyezo yolungama ya Yehova kuti iye agwilitsile nchito dipolo poombola Adamu. Komabe, kulipila mtengo wa chimo la Adamu, kumafafaniza ciweluzo ca imfa pa mbadwa za Adamu! (Aroma 5:16) Mwalamulo, mphamvu yowononga ya uchimo inacotsedwa mwa kuthetselatu magwelo ake eni-eni. Wopelekedwa dipoyo ‘analaŵa imfa m’malo mwa munthu aliyense,’ ananyamula zoŵaŵa za uchimo kaamba ka ana onse a Adamu.—Aheberi 2:9; 2 Akorinto 5:21; 1 Petulo 2:24.
MAY 31–JUNE 6
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | DEUTERONOMO 1-2
“Mulungu Ndiye Woweluza”
w96 3/15 23 ¶1
Yehova Wokonda Cilungamo ndi Ciweluzo
Akulu a mpingo oikidwa ali na udindo woweluza milandu ya colakwa cacikulu. (1 Akorinto 5:12, 13) Pocita zimenezo, amakumbukila kuti ciweluzo ca Mulungu cimafuna kuti aonetse cifundo ngati n’koyenela. Ngati palibe maziko ake—monga momwe zilili na ocimwa osalapa—cifundo sicingasonyezedwe. Koma akulu samacotsa wolakwa mumpingo cifukwa cofuna kubwezela. Amakhulupilila kuti mcitidwe wa kucotsawo udzam’cititsa kulingalila bwino. (Yelekezelani na Ezekieli 18:23.) Pansi pa umutu wa Khristu, akulu amacilikiza cilungamo, ndipo zimenezi zimaphatikizapo kukhala monga “malo obisalilapo mphepo.” (Yesaya 32:1, 2) Cotelo ayenela kucita zinthu mosakondela ndiponso mwanzelu.—Deuteronomo 1:16, 17.
w02 8/1 9 ¶4
Gonjelani Mokhulupilika Ulamulilo Umene Mulungu Waika
4Komabe, oweluza anafunika kucita zambili osati kungodziŵa kokha Cilamulo. Popeza anali opanda ungwilo, akuluwo anafunika kupewa makhalidwe awo oipa acibadwa, monga kudzikonda, kukondela, na dyela, zimene zikanapotoza kaweluzidwe kawo. Mose anawauza kuti: “Musamakondele poweluza. Munthu wamba ndi munthu wolemekezeka onse muziwamvetsela cimodzi-modzi. Musamaope munthu cifukwa mukuweluzila Mulungu.” Inde, oweluza a Isiraeli anali kuweluza m’malo mwa Mulungu. Imeneyi inali nchito yapamwamba ndiponso yapadela!—Deuteronomo 1:16, 17.
Kufufuza Cuma Cauzimu
Zikumbutso za Yehova Ndi Zodalilika
9Pamene Aisiraeli anayamba ulendo wa ‘m’cipululu cocititsa mantha’ umene unawatengela zaka 40, Yehova sanawauze zonse zokhudza mmene anali kudzawatsogolela, kuwateteza, na kuwasamalila. Komabe Mulungu nthawi zambili anaonetsa kuti ni wodalilika mwakuti Aisiraeli anali na zifukwa zokwanila zomukhulupilila na kudalila malangizo ake. Mwa kugwilitsila nchito mtambo masana na moto usiku, Yehova anakumbutsa Aisiraeli kuti iye anali nawo limodzi paulendo wawo wodutsa m’dela loopsa limenelo. (Deut. 1:19; Eks. 40:36-38) Iye anali kuwasamalila mwakuthupi. “Zovala zawo sizinathe ndipo mapazi awo sanatupe.” Inde “iwo sanasowe kanthu.”—Neh. 9:19-21.
JUNE 7-13
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | DEUTERONOMO 3-4
“Malamulo a Yehova ni Anzelu Komanso Olungama”
it-2 1140 ¶5
Kumvetsa Zinthu
Ngati munthu amaŵelenga na kuseŵenzetsa Mawu a Mulungu na malamulo ake, amakhala wozindikila kwambili kuposa aphunzitsi ake, komanso amakhala womvetsa zinthu kwambili kuposa acikulile. (Sal. 119:99, 100, 130; yelekezelani na Luka 2:46, 47.) Izi zili conco cifukwa m’malangizo oyela a Mulungu na m’zigamulo zake muli nzelu na kumvetsa zinthu. Conco, Aisiraeli akanamvela mokhulupilika malangizo na zigamulo za Mulungu, mitundu yowazungulila ikanaona kuti iwo “ni anthu anzeludi ndi ozindikila.” (Deut. 4:5-8; Sal. 111:7, 8, 10; yelekezelani na 1 Maf. 2:3.) Munthu womvetsa zinthu amazindikila kuti Mawu a Mulungu ni oyela, amafuna kuwatsatila pa umoyo wake, ndipo amapempha Mulungu kuti amuthandize kucita zimenezo. (Sal. 119:169) Amalola Mawu a Mulungu kumufika pamtima (Mat. 13:19-23), amawalemba pamtima pake (Miy. 3:3-6; 7:1-4), ndipo amayamba kuzonda “njila iliyonse yacinyengo” (Sal. 119:104). Pamene Mwana wa Mulungu anali padziko lapansi anaonetsa kuti anali womvetsa zinthu. Iye analolela kufa imfa ya pamtengo wozunzikilapo cifukwa cofuna kukwanilitsa Malemba.—Mat. 26:51-54.
w99 11/1 20 ¶6-7
Pamene Ambili Akhala Ooloŵa Manja
Podabwa na zimene anamva na kuona, mfumu yaikaziyo inayankha kuti: “Odala atumiki anuwa amene amatumikila pamaso panu nthawi zonse, n’kumamva nzelu zanu.” (1 Mafumu 10:4-8) Sananene kuti atumiki a Solomo anali odala cifukwa cakuti anazingidwa na cuma camwanaalilenji—ngakhale kuti zinalidi motelo. M’malo mwake, atumiki a Solomo anali odala cifukwa cakuti nthaŵi zonse anali kumvetsela nzelu za Solomo zopatsidwa na Mulungu. Mfumu yaikazi ya ku Seba ni citsanzo cabwino kwambili kwa anthu a Yehova lelolino, amene azingidwa na nzelu ya Mlengi iyemwini na ya Mwana wake, Yesu Khristu!
Mawu otsatila a mfumuyo kwa Solomo ni ocititsanso cidwi: “Adalitsike Yehova Mulungu wanu.” (1 Mafumu 10:9) Iye anaonadi dzanja la Yehova m’nzelu ya Solomo na cuma. Zimenezi zikugwilizana na zimene Yehova analonjeza Aisiraeli poyamba. ‘Mukasunga malangizo,’ iye anatelo, “mudzakhala anzelu na ozindikila pamaso pa anthu a mitundu ina amene adzamva za malangizo onsewa. Pamenepo, anthuwo adzanena kuti, ‘Mtundu waukulu umenewu ndi wa anthu anzeludi ndi ozindikila.’—Deuteronomo 4:5-7.
w07 8/1 29 ¶13
Kodi Ndinu “Wolemela kwa Mulungu”?
13Yehova akamadalitsa anthu ake, nthawi zonse madalitsowo amakhala osayelekezeka. (Yakobo 1:17) Mwacitsanzo, dziko limene Yehova anapatsa Aisiraeli, linali “dziko loyenda mkaka ndi uci.” Ngakhale kuti dziko la Iguputo analifotokozanso conco, panali cinthu cimodzi cofunika kwambili cimene cinali kulisiyanitsa na dziko limene Yehova anapeleka kwa Aisiraeli. Pofotokozela Aisiraeli za dzikolo, Mose ananena kuti ni “dziko limene Yehova Mulungu wanu akulisamalila.” Zimenezi zinatanthauza kuti iwo adzasangalala na dzikolo cifukwa cakuti Yehova azikawasamalila. Aisiraeliwo akakhala okhulupilika kwa Yehova, iye anali kuwadalitsa kwambili ndipo anali kusangalala na moyo kuposa mitundu ina yonse yowazungulila. Zoonadi, madalitso a Yehova ni amene “amalemeletsa”!—Numeri 16:13; Deuteronomo 4:5-8; 11:8-15.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w04 9/15 25 ¶3
Mfundo Zazikulu za M’buku la Deuteronomo
4:15, 20, 23, 24—Kodi kuletsa kupanga mafano osema kukutanthauza kuti n’kulakwa kupanga cifanizo ca zinthu zina n’colinga cokongoletsela malo? Ayi siconco. Nkhani imene anali kuletsa apa inali yopanga cifanizo n’colinga coti azicilambila, anali kuletsa ‘kugwadila mafano ndi kuwatumikila.’ Malemba saletsa kusema ziboliboli kapena kujambula zinthu n’colinga cokongoletsela malo.—1 Mafumu 7:18, 25.
JUNE 14-20
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | DEUTERONOMO 5-6
“Phunzitsani Ana Anu Kukonda Yehova”
w05 6/15 20 ¶11
Makolo, Pezelani a M’banja Lanu Zosoŵa Zawo
11Pankhani imeneyi, mwina palibe lemba lina limene timaligwila mawu kuposa Deuteronomo 6:5-7. Tsegulani Baibo lanu muŵelenge mavesiwo. Onani kuti coyamba makolo akuuzidwa kulimbitsa umoyo wawo wauzimu, kukulitsa cikondi cawo pa Yehova na kumvela mawu ake. Inde, muyenela kukhala wophunzila Mawu a Mulungu wakhama, kuŵelenga Baibo nthawi zonse na kusinkha-sinkha zimene mumaŵelenga. Zimenezi zidzakuthandizani kumvetsa na kukonda njila za Yehova, mfundo zake za makhalidwe abwino, na malamulo ake. Zotsatila zake n’zakuti, mtima wanu udzadzala na mfundo za coonadi ca m’Baibo zimene zidzakupangitsani kukhala wosangalala, wolemekeza Yehova na kum’konda. Mudzakhala na zophunzitsa ana anu zabwino komanso zambili.—Luka 6:45.
w07 5/15 15-16
Kodi Ndingatani Kuti Niphunzitse Bwino Ana Anga?
Zinthu zimene mumalakalaka, kukonda, na kusangalala nazo, zimaonekela m’zocita zanu osati m’zonena zanu zokha. (Aroma 2:21, 22) Kuyambila ali khanda, ana amaphunzila zinthu mwa kuona citsanzo ca makolo awo. Amatha kuzindikila zinthu zimene makolo awo amaziona kukhala zofunika, ndipo zinthu zimenezi ndi zimene zimakhalanso zofunika kwa iwo. Mukamakonda kwambili Yehova, ana anunso amaona zimenezi. Mwacitsanzo, angaone kuti mumaona kuŵelenga na kuphunzila Baibo kuti n’zofunika. M’kupita kwa nthawi amazindikila kuti mumaika Ufumu poyamba mu umoyo wanu. (Mateyu 6:33) Mukamapezeka ku misonkhano yacikhristu na kulalikila za Ufumu nthawi zonse, ana anu amazindikila kuti kutumikila Yehova n’kofunika kwambili kwa inu.—Mateyu 28:19, 20; Aheberi 10:24, 25.
w05 6/15 21 ¶14
Makolo, Pezelani a M’banja Lanu Zosoŵa Zawo
14Monga limaonetsela lemba la Deuteronomo 6:7, mipata ilipo yambili imene makolo mungakambilane zinthu zauzimu ndi ana anu. Kaya ni pamene muli nawo paulendo, pogwila nchito za pakhomo, kapena poceza, mungapeze mipata yopelekela zosoŵa zauzimu kwa ana anu. Komabe, sikuti nthawi zonse muzingokhalila kuphunzitsa ana anu mfundo za coonadi ca m’Baibo ayi. M’malo mwake, monga banja yesani kumakhala na maceza auzimu ndiponso olimbikitsa. Mwacitsanzo, magazini ya Galamukani! imakhala na nkhani zambili zosiyana-siyana. Nkhani zotelozo zingatsegule mpata wokambilana za zinyama zimene Yehova analenga, malo okongola acilengedwe m’madela osiyana-siyana a dziko lapansi, na zikhalidwe za anthu zosangalatsa na umoyo wawo. Makambilano otelowo angalimbikitse acicepele kumaŵelenga mabuku ambili opelekedwa na gulu la kapolo wokhulupilika ndi wanzelu.—Mateyu 24:45-47.
Kufufuza Cuma Cauzimu
Cikondi na Cilungamo M’nthawi ya Aisiraeli
11Zimene tiphunzilapo: Yehova saona cabe maonekedwe akunja a munthu. Koma amaonanso zimene zili mu mtima. (1 Sam. 16:7) Iye amaona zonse zimene timacita, kuganiza na kulaka-laka. Amayang’ana zabwino mwa ife, ndipo amatilimbikitsa kupitiliza kucita zabwino. Iye amafuna kuti maganizo oipa akabwela mu mtima mwathu, tiziwacotsa mwamsanga kuti asatigwetsele m’chimo.—2 Mbiri 16:9; Mat. 5:27-30.
JUNE 21-27
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | DEUTERONOMO 7-8
“Usadzacite Nawo Mgwilizano wa Ukwati”
w12 7/1 29 ¶2
N’cifukwa Ciani Mulungu Anauza Aisiraeli Kuti Asamakwatilane ndi Anthu a Mitundu Ina?
Cifukwa coyamba n’cakuti, Yehova anadziŵa kuti Satana anali kufuna kusokoneza anthu a Mulungu powacititsa kuti azitumikila milungu yonyenga. N’cifukwa cake ponena za anthu a mitundu ina Mulungu anawauza anthu ake kuti: “Adzapatutsa ana ako aamuna kuti asanditsatile ndipo adzatumikila ndithu milungu ina.” Nkhani imeneyi inali yaikulu cifukwa Mesiya anayenela kubadwila mu mtundu wa Isiraeli. Koma Aisiraeli akanayamba kutumikila milungu ina, Mulungu akanasiya kuwakonda komanso kuwateteza ndipo izi zikanacititsa kuti adani awo awagonjetse. Zimenezi zikanacititsa kuti mtunduwu usatulutse Mesiya wolonjezedwa. Apa n’zoonekelatu kuti Satana anali kufuna kuti Aisiraeli akwatile anthu a mitundu ina n’colinga coti asokoneze mzele wobadwila wa Mesiya.
Kodi Kukwatiwa “Mwa Ambuye” N’kofunikabe?
Ngakhale zili conco, Yehova waika malangizo m’Mawu ake okhudza kukwatiwa kokha mwa Ambuye. N’cifukwa ciani? Cifukwa cakuti iye amadziŵa bwino zimene anthu ake amafunikila. Sikuti iye amangofuna cabe kuteteza atumiki ake ku mavuto amene angakumane nawo cifukwa cosankha zinthu mopanda nzelu, koma amafunanso kuti tikhale osangalala. M’nthawi ya Nehemiya, Ayuda ambili anali kukwatila akazi omwe sanali kulambila Yehova. Iye anachula za citsanzo coipa ca Solomo. Nehemiya anati Solomo “anakondedwa ndi Mulungu wake, mwakuti Mulungu anamuika kukhala mfumu ya Isiraeli yense. Koma akazi acilendo anamucimwitsa.” (Neh. 13:23-26) Conco, pofuna kuti atumiki ake zinthu ziziwayendela bwino, Mulungu watipatsa malangizo akuti tiyenela kukwatila olambila oona. (Sal. 19:7-10; Yes. 48:17, 18) Timayamikila kwambili kuti Mulungu amatipatsa malangizo acikondi ndi odalilika. Tikamamvela Yehova monga Wolamulila wathu, timaonetsa kuti iye ni woyenela kutiuza zimene tiyenela kucita.—Miy. 1:5.
Samalani ndi Anthu Ogwilizana Nawo Masiku Ano Otsiliza
12Akhristu amene afuna kukwatila kapena kukwatiwa afunika kusamala ndi anthu amene amagwilizana nawo. Mawu a Mulungu amanena mosapita m’mbali kuti: “Musamangidwe m’goli ndi osakhulupilila, cifukwa ndinu osiyana. Pali ubale wotani pakati pa cilungamo ndi kusamvela malamulo? Kapena pali kugwilizana kotani pakati pa kuwala ndi mdima?” (2 Akor. 6:14) Baibo limalangiza atumiki a Mulungu kuti ayenela kukwatila kapena kukwatiwa kokha “mwa Ambuye,” kutanthauza kuti ayenela kupeza Mboni yodzipeleka ndi yobatizidwa imene imatsatila ziphunzitso za m’Malemba. (1 Akor. 7:39) Akhristu amene amakwatila kapena kukwatiwa kwa Mkhristu mnzake, amapeza bwenzi lodzipeleka kwa Yehova ndipo limawathandiza kukhalabe okhulupilika kwa Mulungu.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w04 2/1 13 ¶4
Yehova Amatipatsa Zimene Timafunikila Tsiku Lililonse
4Kupemphelela kwathu cakudya ca tsiku lililonse kuyenela kutikumbutsanso kuti timafunikila cakudya cauzimu tsiku lililonse. Ngakhale kuti Yesu anali na njala atasala cakudya kwa nthaŵi yaitali, iye anakana ciyeso ca Satana coti asandutse miyala kukhala cakudya, ponena kuti: “Malemba amati, ‘Munthu sangakhale ndi moyo ndi cakudya cokha, koma ndi mawu onse otuluka pakamwa pa Yehova.’ (Mateyu 4:4) Pano Yesu anagwila mawu a mneneli Mose, amene anauza Aisiraeli kuti: “[Yehova] anakuphunzitsani kudzicepetsa pokukhalitsani ndi njala ndi kukudyetsani mana, amene inu kapena makolo anu sanawadziŵe. Anacita zimenezi kuti mudziŵe kuti munthu sakhala ndi moyo ndi cakudya cokha, koma ndi mawu onse ocokela m’kamwa mwa Yehova.” (Deuteronomo 8:3) Mmene Yehova anali kuwapatsila mana Aisiraeli sikunali kungowapatsa cakudya ceni-ceni cokha komanso maphunzilo auzimu. Phunzilo limodzi lauzimu n’lakuti, anali kufunika ‘kutola muyezo wom’kwanila pa tsikulo.’ Akatola zoposa zimene akanadya tsiku limenelo, zotsalazo zinali kuyamba kununkha ndi kugwa mphutsi. (Ekisodo 16:4, 20) Koma zimenezi sizinali kucitika tsiku lacisanu ndi cimodzi pamene amafunika kutola cakudya ca masiku aŵili kuti adzadye tsiku la Sabata. (Ekisodo 16:5, 23, 24) Motelo mana anali kuwakumbutsa nthaŵi zonse kuti anali kufunika kukhala omvela ndiponso kuti miyoyo yawo inali kudalila osati pa cakudya cokha koma pa “mawu onse ocokela m’kamwa mwa Yehova.”
JUNE 28–JULY 4
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | DEUTERONOMO 9-10
“Kodi Yehova Mulungu Wanu Akufuna Kuti Muzicita Ciani?”
w09 10/1 10 ¶3-4
Kodi Yehova Amafuna Kuti Tizicita Ciani?
Kodi n’ciani cingatithandize kuti tizicita zimenezi? Mose anachula mfundo imodzi, kuti: ‘Muziopa Yehova Mulungu wanu.’ (Vesi 12) Zimenezi sizikutanthauza kuti tiziopa Mulungu cifukwa ca zoipa zimene zingaticitikile cifukwa cosamumvela, koma tiziopa Mulungu cifukwa coti timamulemekeza. Conco ngati timakonda kwambili Mulungu, tidzayesetsa kupewa kucita zinthu zimene zingamukhumudwitse.
Kodi ni cifukwa cacikulu citi cimene cingaticititse kuti tizimvela Mulungu? Mose ananena kuti: ‘Muzikonda ndi kutumikila Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse.’ (Vesi 12) Kukonda Mulungu kumafuna zambili osati kungomva mu mtima mwathu kuti timamukonda. Buku lina limati: “Mawu aciheberi otanthauza mmene munthu akumvela mu mtima, amatanthauzanso zimene munthu akucita cifukwa ca zimene akumva mumtima mwake.” Buku lomweli limanenanso kuti kukonda Mulungu kumatanthauza “kucita zinthu zoonetsa kuti timamukonda.” Zimenezi zikutanthauza kuti ngati timakondadi Mulungu, tidzayesetsa kucita zinthu zimene tikudziŵa kuti zimukondweletsa.—Miyambo 27:11.
w09 10/1 10 ¶6
Kodi Yehova Amafuna Kuti Tizicita Ciani?
Mulungu adzatidalitsa kwambili ngati timamumvela mwakufuna kwathu. Mose analemba kuti: ‘Muzisunga malamulo amene ndikukupatsani lelo, kuti zinthu zikuyendeleni bwino.’ (Vesi 13) Inde, ciliconse cimene Yehova amatiuza kuti tizicita cimakhala cotikomela kapena kuti cotithandiza. Conco, sicingatilepheletse kusangalala. Baibo imati: “Mulungu ndiye cikondi.” (1 Yohane 4:8) N’cifukwa cake anatipatsa malamulo amene angatithandize kuti tikhale na umoyo wabwino kwambili. (Yesaya 48:17) Kucita zonse zimene Yehova amafuna kuti tizicita kumatithandiza kupewa zokhumudwitsa zambili panopa ndipo kudzatithandiza kuti mtsogolomu, tidzapeze madalitso ambili mu ulamulilo wa Ufumu wake.
cl 16 ¶2
Kodi ‘Mungayandikiledi kwa Mulungu’?
2Abulahamu, amene anakhalapo kale-kalelo, anali woyandikana naye motelomo. Polankhula za kholo limenelo Yehova anati “bwenzi langa.” (Yesaya 41:8) Ee, Yehova anamuona Abulahamu kuti anali bwenzi lake leni-leni. Abulahamu anali naye pa unansi wabwino conci cifukwa “anakhulupilila mwa Yehova.” (Yakobo 2:23) Lelolinonso, Yehova amafuna-funa mipata ‘yodziphatika’ kwa amene amamutumikila mwacikondi. (Deuteronomo 10:15) Mawu ake amatilimbikitsa kuti: “Yandikilani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikilani.” (Yakobo 4:8) Mawu ameneŵa akutiuza kucita kanthu kena ndiponso akutipatsa lonjezo.
Kufufuza Cuma Cauzimu
it-1 103
Aanaki
Mtundu wa anthu a matupi akulu-akulu okhala m’madela a mapili a ku Kanani, na m’madela a m’mbali mwa nyanja, maka-maka Kum’mwela kwa dzikolo. Pa nthawi ina, mbadwa zitatu zochuka za Anaki, Ahimani, Sesai, na Talimai zinali kukhala ku Heburoni. (Num. 13:22) Uku n’kumene azondi 12 aciheberi anaona mbadwa za Anaki kwa nthawi yoyamba. Ndipo pambuyo pake, 10 mwa azondiwo anakapeleka lipoti locititsa mantha kwa Aisiraeli. Anakamba kuti Aanakiwo anali mbadwa za Anefili amene anakhalako Cigumula cisanacitike, komanso kuti anali kudziona ngati “ziwala” podziyelekezela na Aanakiwo. (Num. 13:28-33; Deut. 1:28) Aanaki anali anthu akulu-akulu kwambili matupi, moti Baibo pofotokoza za anthu enanso akulu-akulu matupi ochedwa Aemi na Arefai limawayelekezela ndi Aanaki. Cioneka kuti popeza Aanaki anali amphamvu kwambili, anthu anayamba kukamba mawu akuti: “Ndani angaime pamaso pa ana a Anaki?”—Deut. 2:10, 11, 20, 21; 9:1-3.