LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwbr22 March
  • Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki
  • Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu—2022
  • Tumitu
  • MARCH 7-13
  • MARCH 14-20
  • MARCH 21-27
  • MARCH 28–APRIL 3
  • APRIL 4-10
  • APRIL 18-24
  • APRIL 25–MAY 1
Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu—2022
mwbr22 March

Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki

MARCH 7-13

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 SAMUELI 12-13

“Kudzikweza Kumanyazitsa Munthu”

w00 8/1 13 ¶17

Kudzikuza Kumadzetsa Manyazi

17Poyamba, zimene Sauli anacitazo zingaoneke ngati zolondola. Ndiiko komwe, anthu a Mulungu “anaona kuti zinthu zawathina,” anali “atapanikizika,” ndipo anali kunjenjemela cifukwa cakuti anali mu mkhalidwe wovuta. (1 Samueli 13:6, 7) Kwenikweni, si kulakwa kucita zinthu mofulumila ngati mikhalidwe ikutikakamiza kutelo. Koma kumbukilani kuti Yehova amapenda mitima ndipo amadziŵa malingalilo athu. (1 Samueli 16:7) Conco, n’kutheka kuti iye anaona mikhalidwe ina mwa Sauli yomwe sanaichule mwacindunji m’nkhani ya m’Baibo. Mwacitsanzo, mwinamwake Yehova anaona kuti kudzikuza n’kumene kunasonkhezela kusaleza mtima kwa Sauli. Mwinamwake Sauli sanamve bwino mumtima kuti iye—mfumu ya Isiraeli yense—anafunikila kudikila winawake amene anali kumuona ngati mneneli wokalamba komanso wozengeleza! Mulimonse mmene zinalili, Sauli analingalila kuti kucedwa kwa Samueli kunam’patsa ufulu wocita zonse yekha na kusalabadila malangizo acimvekele omwe anali atapatsidwa. Zotsatila zake? Samueli sanavomeleze kufulumiza kwa Sauliko. M’malomwake, iye anamuweluza Sauli nati: “Ufumu wako sukhalitsa . . . cifukwa iwe sunasunge zimene Yehova anakulamula.” (1 Samueli 13:13, 14) Apanso, kudzikuza kunadzetsa manyazi.

w07 6/15 27 ¶8

Yehova Amakondwela Mukamamumvela

8Nkhani ya m’Baibo yonena za Mfumu Sauli imasonyeza kuti kumvela n’kofunika kwambili. Poyamba, Sauli anali mfumu yodzicepetsa ndipo ‘anadziona ngati mwana.’ Koma patapita nthawi, anayamba kunyada n’kukhala na maganizo olakwika pa zocita zake. (1 Samueli 10:21, 22; 15:17) Nthawi ina, Sauli akukamenyana na Afilisiti, Samueli anamuuza kuti amudikile kuti iye adzapeleke nsembe kwa Yehova ndiponso kuti adzapatse mfumuyo malangizo ena. Koma Samueli anacedwa kubwela ndipo anthu anayamba kubalalika. Ataona zimenezo, Sauli ‘anapeleka nsembe zopseleza.’ Zimenezi Yehova sanakondwele nazo. Samueli atabwela, mfumu inapeleka zifukwa pofuna kudzilungamitsa pa kusamvela kwake. Inafotokoza kuti ‘inakakamizika’ kupeleka nsembe yopseleza pofuna kukhazika pansi mtima wa Yehova cifukwa cakuti Samueli anacedwa. Mfumu Sauli anaona kuti kupeleka nsembeyo kunali kofunika kwambili kuposa kumvela malangizo oti adikile Samueli kudzapeleka nsembe. Samueli anamuuza kuti: “Wacita cinthu copusa. Sunatsatile lamulo limene Yehova Mulungu wako anakupatsa.” Mapeto ake, Sauli anataya ufumu wake cifukwa cosamvela Yehova.—1 Samueli 10:8; 13:5-13.

Kufufuza Cuma Cauzimu

w11 7/15 13 ¶15

Kodi Mukutsatila Malangizo Acikondi a Yehova?

15Kodi Aisiraeli anali kuganiza kuti munthu akhoza kukhala mfumu yeniyeni ndiponso yodalilika kuposa Yehova? Ngati n’conco, ndiye kuti anali kutsatila zinthu zopanda pake. Iwo anali pa ngozi yotsatila zinthu zinanso zopanda pake zocokela kwa Satana. Zikanakhala zosavuta kuti mafumu otele awacititse kulambila mafano. Anthu olambila mafano amaganiza kuti milungu yopangidwa kucokela ku mitengo kapena miyala, imakhala yeniyeni ndiponso yodalilika kuposa Yehova Mulungu wosaoneka, amene analenga zinthu zonse. Koma malinga na zimene mtumwi Paulo ananena, mafano ni ‘opanda pake.’ (1 Akor. 8:4) Sangaone, kumva, kulankhula kapena kucita ciliconse. Mungawaone ndiponso kuwakhudza mafanowo, koma mukawalambila ndiye kuti mukutsatila cinthu copanda pake, kapena kuti cinthu cimene si ceniceni, comwe cingakucititseni kukumana na mavuto.—Sal. 115:4-8.

MARCH 14-20

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 SAMUELI 14-15

“Kumvela Kumaposa Nsembe”

w07 6/15 26 ¶4

Yehova Amakondwela Mukamamumvela

4Popeza kuti Yehova ndiye Mlengi, zinthu zonse zimene tili nazo ni zake. Ndiyeno, kodi pali ciliconse cimene tingamucitile? Inde, cilipo ndipo ni camtengo wapatali. Tingamucitile ciani? Tikupeza yankho pamalangizo otsatilawa akuti: “Mwana wanga, khala wanzelu ndi kukondweletsa mtima wanga, kuti ndimuyankhe amene akunditonza.” (Miyambo 27:11) Zimene tingamucitile Mulungu ni kumumvela basi. Ngakhale kuti tinabadwila kosiyanasiyana ndipo tili na moyo wosiyanasiyana, ifeyo mwa kumvela, tingatsutse bodza lamkunkhuniza la Satana Mdyelekezi lakuti anthufe sitingakhale okhulupilika kwa Mulungu tikamayesedwa. Ndithudi, Mulungu watilemekeza zedi potipatsa mwayi wotsutsa zimenezi!

it-2 521 ¶2

Kumvela

Palibe cimene cingaloŵe m’malo kumvela. Ndipo munthu sangayanjidwe na Mulungu ngati ni wosamvela. N’cifukwa cake Samueli anauza Mfumu Sauli kuti: “Kodi Yehova amakondwela ndi nsembe zopseleza ndi nsembe zina kuposa kumvela [kucokela ku liwu lakuti sha·maʽʹ] mawu a Yehova? Taona! Kumvela [mawu ake eni-eni, kumvetsela] kuposa nsembe, ndipo kumvetsela mosamala kuposa mafuta a nkhosa zamphongo.” (1 Sam. 15:22) Kusamvela, ni kukana mawu a Yehova. Izi zimaonetsa kuti munthu sakhulupilila kweni-kweni mawuwo, sawadalila, ndipo sakhulupilila gwelo lake. Cotelo, munthu wosamvela sasiyana na munthu woombeza kapena wopembedza mafano. (1 Sam. 15:23; yelekezelani na Aroma 6:16.) Kungovomela kuti ucita zinazake zimene wauzidwa koma osacitapo kanthu, n’kopanda phindu. Kusacitapo kanthuko kumaonetsa kuti sukhulupilila kapena kulemekeza munthu amene wapeleka malangizowo. (Mat. 21:28-32) Anthu amene amangomva na kuvomeleza mfundo za coonadi ca Mulungu koma osacitapo kanthu, amadzinyenga na maganizo onama ndipo salandila dalitso. (Yak. 1:22-25) Mwana wa Mulungu anakamba momveka bwino kuti ngakhale anthu amene amacita zofanana na zimene alamulidwa koma m’njila yolakwika kapena na colinga colakwika, sadzaloŵa mu Ufumu wa Mulungu; adzakanidwa kothelatu.—Mat. 7:15-23.

Kufufuza Cuma Cauzimu

it-1 493

Cifundo

Kukakamizika kuonetsa cifundo pamene kucita zimenezo n’kosagwilizana na cifunilo ca Mulungu kungakhale na zotulukapo zoipa. Cimene cionetsa zimenezi ni zimene zinacitikila Mfumu Sauli. Nthawi inali itakwana yakuti Mulungu apeleke ciweluzo kwa Aamaleki, anthu oyamba kuukila Aisiraeli popanda kuwaputa atangocoka ku Iguputo. Sauli analamulidwa kuti asawacitile cifundo. Cifukwa coopa anthu ake, iye sanacite zonse zimene Yehova anam’lamula. Conco, Yehova anam’kana Sauli kuti asakhale Mfumu. (1 Sam. 15:2-24) Kukhulupilila kwambili kuti njila za Yehova ndizo zoyenela, komanso kuona kuti kukhala wokhulupilika kwa iye ndiye kofunika kwambili, kungathandize munthu kuti asacite colakwa monga anacitila Sauli, n’kutaya ciyanjo ca Mulungu.

MARCH 21-27

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 SAMUELI 16-17

“Yehova Ndiye Mwini Nkhondo”

wp16.5 11 ¶2-3

“Yehova Ndiye Mwini Nkhondo”

Davide anatsimikizila Sauli kuti angagonjetse Goliyati. Anacita zimenezi mwa kufotokozela Sauli mmene anaphela mkango na cimbalangondo. Kodi anali kudzitama? Iyai. Davide anadziŵa kuti Mulungu ndiye anamuthandiza. Iye anati: “Yehova amene anandilanditsa m’kamwa mwa mkango ndi m’kamwa mwa cimbalangondo andilanditsanso m’manja mwa Mfilisiti ameneyu.” Atamva zimenezi, Sauli anangomuuza kuti: “Pita, ndipo Yehova akhale nawe.”—1 Samueli 17:37.

Kodi mufuna kukhala na cikhulupililo ngati ca Davide? Ngati n’conco, dziŵani kuti cikhulupililo ca Davide sicinali ngati maloto cabe koma cinali na maziko ake. Iye anali na cikhulupililo mwa Mulungu cifukwa ca zimene anaphunzila na zimene zinam’citikila paumoyo. Anadziŵa kuti Yehova ni Mtetezi wacikondi komanso Wosunga malonjezo. Kuti tikhale na cikhulupililo cotelo, tifunika kuphunzila za Mulungu woona. Tikamacita zimene timaphunzila, timakhala na umoyo wabwino ndipo cikhulupililo cathu cimalimba.—Aheberi 11:1.

wp16.5 11-12

“Yehova Ndiye Mwini Nkhondo”

Mawu amene Davide anakamba poyankha Goliyati ni olimbikitsa ngakhale masiku ano. Yelekezelani kuti mukumva wacicepele ameneyu akuuza Goliyati kuti: “Iwe ukubwela kwa ine ndi lupanga, mkondo ndi nthungo, koma ine ndikubwela kwa iwe m’dzina la Yehova wa makamu, Mulungu wa asilikali a Isiraeli, amene iweyo wam’tonza.” Davide anadziŵa kuti mphamvu za munthu kapena zida sizinali zofunika kwenikweni. Goliyati ananyoza Yehova Mulungu, ndipo Yehovayo anacitapo kanthu. Davide anakamba kuti: “Yehova ndiye mwini nkhondo.”—1 Samueli 17:45-47.

Davide anaona kutalika kwa Goliyati na zida zake zankhondo. Koma sanalole zimenezo kumucititsa mantha. Iye sanacite zinthu mofanana na mmene Sauli na asilikali ake anacitila. Davide sanadziyelekezele na Goliyati. Mmalomwake, anayelekezela Goliyati na Yehova. N’zoona kuti Goliyati anali wamtali mamita 2.9, ndipo anali kuposa anthu onse, koma sanali kanthu poyelekezela na Mulungu wacilengedwe conse. Iye anali ngati nyelele m’maso mwa Yehova, ndipo Mulungu anali wokonzeka kumuwononga kothelatu.

wp16.5 12 ¶4

“Yehova Ndiye Mwini Nkhondo”

Masiku ano, atumiki a Mulungu samenya nkhondo yeniyeni. Zimenezi zinatha. (Mateyu 26:52) Komabe, tifunika kutengela cikhulupililo ca Davide. Mofanana na Davide, tifunika kukhulupilila Yehova. Tifunikanso kutumikila iye yekha na kumuopa. Nthawi zina tingathedwe nzelu na mavuto athu, koma tiyenela kukumbukila kuti palibe vuto limene Yehova angalephele kuthetsa cifukwa ali na mphamvu zopanda malile. Tikasankha Yehova kukhala Mulungu wathu na kumukhulupilila monga mmene Davide anacitila, tidzakhala olimba mtima tikakumana na mavuto. Palibe vuto limene Yehova angalephele kuthetsa.

Kufufuza Cuma Cauzimu

it-2 871-872

Sauli

Zimenezi zitacitika komanso pambuyo pakuti Davide wadzozedwa kuti adzakhale mfumu yakutsogolo ya Isiraeli, m’pamene mzimu wa Yehova unam’cokela Sauli. Kuyambila nthawi imeneyo, “mzimu woipa wocokela kwa Yehova” unam’vutitsa. Yehova atacotsa mzimu wake pa Sauli, anapangitsa kuti mzimu woipa upeze mpata woloŵa mwa iye. Mzimu woipawo unali kumusoŵetsa mtendele wa maganizo Sauli, ndipo unali kulamulila mtima na maganizo ake m’njila yolakwika. Kusamvela Yehova kwa Sauli kunaonetsa kuti maganizo na mtima wake zinali zitaipa, ndipo mzimu wa Mulungu sunam’teteze Sauli ku mzimu woipawo. Komabe, popeza kuti Yehova anali atalola “mzimu woipa” kuloŵa m’malo mzimu wake na kum’vutitsa Sauli, mzimuwo ungachedwe kuti “mzimu woipa wocokela kwa Yehova.” Ndiye cifukwa cake atumiki a Sauli anaucha “mzimu woipa wa Mulungu.” Pomvela zimene mmodzi wa atumiki ake anakamba, Sauli anapempha kuti Davide azikam’tumikila m’nyumba yake yacifumu monga woimba, n’colinga cakuti “mzimu woipa” ukayamba kum’vutitsa, azikam’khazika mtima pansi.—1 Sam. 16:14-23; 17:15.

MARCH 28–APRIL 3

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 SAMUELI 18-19

“Khalanibe Odzicepetsa Zinthu Zikakuyendelani Bwino”

w04 4/1 15 ¶4

Dalilani Mzimu wa Mulungu Zinthu Zikasintha pa Moyo Wanu

4Posakhalitsa m’busa wacinyamata ameneyu anachuka m’dziko lonselo. Anamuitana kuti azikatumikila mfumu na kumaiimbila nyimbo. Anapha Goliyati yemwe anali katswili wa nkhondo, cimphona, komanso woopsa, moti ngakhale asilikali odziŵa bwino nkhondo a Isiraeli anaopa kulimbana naye. Atamusankha kuti atsogolele asilikaliwo, Davide anagonjetsa Afilisiti. Anthu anamukonda kwambili ndipo anapeka nyimbo zomutamanda. Izi zisanacitike, mlangizi wina wa Mfumu Sauli anafotokoza za Davide kuti anali na “luso loimba” zeze komanso kuti anali “mwamuna wolimba mtima ndiponso wamphamvu, mwamuna wankhondo, wolankhula mwanzelu ndi wooneka bwino.”—1 Samueli 16:18; 17:23, 24, 45-51; 18:5-7.

w18.01 28 ¶6-7

Muziona Kusiyana Pakati pa Anthu

6Anthu ena amayamba kunyada na kudzikweza cifukwa ca kukongola, kuchuka, maluso a kuimba, mphamvu, kapena udindo umene ali nawo. Davide anali na zonse zimenezi. Koma anakhalabe na mtima wodzicepetsa mu umoyo wake wonse. Davide atapha Goliyati na kupatsidwa mwana wamkazi wa Mfumu Sauli kukhala mkazi wake, anakamba kuti: “Ndine yani ine, ndipo abale anga, anthu a m’banja la bambo anga ndani mu Isiraeli monse muno kuti ndikhale mkamwini wa mfumu?” (1 Sam. 18:18) N’ciani cinathandiza Davide kukhalabe wodzicepetsa? Iye anadziŵa kuti anakhala na maluso, mphamvu, na maudindo cifukwa cakuti Mulungu ‘anatsika m’munsi,’ kapena kuti anadzicepetsa, kuti amuthandize. (Sal. 113:5-8) Davide anadziŵanso kuti zabwino zonse zimene anali nazo anapatsiwa na Yehova.—Yelekezelani na 1 Akorinto 4:7.

7Mofanana na Davide, anthu a Yehova lelolino amayesetsa kukhala odzicepetsa. Timacita cidwi podziŵa kuti Yehova, amene ni wamkulu koposa m’cilengedwe conse, ali na khalidwe labwino la kudzicepetsa. (Sal. 18:35) Conco, timatsatila malangizo ouzilidwa akuti: “Valani cifundo cacikulu, kukoma mtima, kudzicepetsa, kufatsa, ndi kuleza mtima.” (Akol. 3:12) Komanso, timadziŵa kuti cikondi “sicidzitama, sicidzikuza.” (1 Akor. 13:4) Tikakhala odzicepetsa, anthu ena adzakopeka na kufuna kuphunzila za Yehova. Malemba amakamba kuti mwamuna amakopeka na khalidwe labwino la mkazi wake popanda mawu. Mofananamo, anthu ena amayandikila Mulungu cifukwa ca kudzicepetsa kwa anthu ake.—1 Pet. 3:1.

Kufufuza Cuma Cauzimu

it-2 695-696

Mneneli

Ngakhale kuti aneneli anali kuikidwa na mzimu wa Yehova, cioneka kuti si nthawi zonse pamene iwo anali kukamba zinthu mouzilidwa. Koma pa nthawi zina, mzimu wa Mulungu ‘unali kuwafikila’ na kuwauza uthenga umene anayenela kulengeza. (Ezek. 11:4, 5; Mika 3:8) Zimenezi zinali kuwasonkhezela kulankhula uthengawo. (1 Sam. 10:10; Yer. 20:9; Amosi 3:8) Iwo anali kucita zinthu zacilendo, ndipo mosakayikila anali kukamba na kucita zinthu mokangalika komanso mokhudzika mtima kwambili kuposa mmene anthu ena anali kucitila. Izi zingatithandize kumvetsa cimene Malemba amatanthauza akamanena kuti anthu ena “anali kucita zinthu ngati aneneli.” (1 Sam. 10:6-11; 19:20-24; Yer. 29:24-32; yelekezelani na Mac. 2:4, 12-17; 6:15; 7:55.) Iwo anali kuikilapo mtima pa nchito imene apatsidwa, ndipo anali kuigwila mokangalika komanso molimba mtima cakuti nthawi zina kacitidwe kawo ka zinthu kanali kuoneka kacilendo, komanso anali kuoneka ngati osaganiza bwino. Umu ni mmene atsogoleli a asilikali anaonela mneneli wina pamene Yehu anadzozedwa. Koma atsogoleliwo atazindikila kuti munthuyo anali mneneli, analabadila uthenga wake ndipo anauona kukhala wofunika. (2 Maf. 9:1-13; yelekezelani na Mac. 26:24, 25.) Pamene Sauli anali kufuna-funa Davide, Sauliyo anayamba ‘kucita zinthu ngati mneneli.’ Iye anavula zovala zake na kugona pansi ali wosavala “usana wonse na usiku wonse.” Zioneka kuti pa nthawiyi m’pamene Davide anathaŵa. (1 Sam. 19:18–20:1) Izi sizitanthauza kuti nthawi zambili aneneli anali kukhala osavala, cifukwa Baibo sionetsa zimenezi. Pa zocitika zina ziŵili zolembedwa m’Baibo, mneneli anayenda wosavala pofuna kumveketsa mbali zina za ulosi wake. (Yes. 20:2-4; Mika 1:8-11) Baibo siifotokoza cifukwa cake Sauli anayenda wosavala. N’kutheka kuti izi zinacitika pofuna kumuonetsa monga munthu wamba wosavala zovala zacifumu, wopanda mphamvu poyelekezela na ulamulilo wa Yehova komanso mphamvu zake zazikulu. Koma n’kuthekanso kuti izi zinacitika pa zifukwa zina.

APRIL 4-10

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 SAMUELI 20-22

“Mmene Mungakhalile Bwenzi Labwino”

w19.11 7 ¶18

Limbitsani Ubwenzi Pakati Panu Mapeto Asanafike

18Masiku ano, abale na alongo athu amakumana na mavuto osiyana-siyana. Mwacitsanzo, ambili amavutika cifukwa ca ngozi zacilengedwe kapena masoka ena obwela cifukwa ca zocita za anthu. Zotelo zikacitika, ena a ife tingawalandile abale athu amenewa kuti azikhala nafe m’nyumba zathu. Enanso angathe kuthandiza mwa kupeleka ndalama. Koma ife tonse tingapemphe Yehova kuti athandize abale na alongo athu amenewa. Tikadziŵa kuti m’bale kapena mlongo wathu ali na nkhawa, tingasoŵe cocita kapena cokamba kuti tim’limbikitse. Koma pali zambili zimene tonsefe tingacite. Mwacitsanzo, tingapatule nthawi yokaceza naye. Tingamvetsele mokoma mtima pamene akutifotokozela nkhawa zake. Ndiponso tingamufotokozeleko lemba lolimbikitsa limene timakonda. (Yes. 50:4) Cofunika kwambili ni kukhala pafupi na bwenzi lanu pamene lakumana na vuto.—Ŵelengani Miyambo 17:17.

w08 2/15 8 ¶7

Yendani M’njila za Yehova

7Mulungu amafuna kuti tikhale mabwenzi odalilika. (Miy. 17:17) Yonatani mwana wa Mfumu Sauli anakhala bwenzi la Davide. Atamva kuti Davide anapha Goliyati, “Yonatani anagwilizana kwambili ndi Davide, moti anayamba kukonda Davide ngati mmene anali kudzikondela yekha.” (1 Sam. 18:1, 3) Yonatani anacenjezanso Davide pamene Sauli anafuna kumupha. Davide atathaŵa, Yonatani anakakumana naye na kucita pangano. Iye anatsala pang’ono kutaya moyo wake cifukwa colankhula za Davide kwa Sauli. Ngakhale n’conco, anthu aŵiliwa anakumananso na kulimbitsa ubwenzi wawo. (1 Sam. 20:24-41) Ulendo womaliza umene anakumana, Yonatani analimbikitsa Davide “kudalila Mulungu.”—1 Sam. 23:16-18.

w09 10/15 19 ¶11

Mungathe Kukhalabe ndi Mabwenzi M’dziko Lopanda Cikondi Lino

11Khalani okhulupilika. Solomo analemba kuti: “Bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse, ndipo ilo ndi m’bale amene anabadwila kuti akuthandize pakagwa mavuto.” (Miy. 17:17) Polemba mawu amenewo, mwina Solomo anali kuganiza za ubwenzi wa bambo ake Davide na Yonatani. (1 Sam. 18:1) Mfumu Sauli anali kufuna kuti mwana wake Yonatani adzakhale mfumu ya Isiraeli iye akadzamwalila. Koma Yonatani anazindikila kuti Yehova anasankha Davide kuti ndiye adzakhale na udindo umenewo. Mosiyana na Sauli, Yonatani sanacitile nsanje Davide. Iye sanaipidwe poona kuti anthu akutamanda Davide, ndiponso sanakhulupilile mabodza amene Sauli anali kufalitsa onena za Davide. (1 Sam. 20:24-34) Kodi ifeyo tili ngati Yonatani? Mabwenzi athu akapatsidwa maudindo, kodi timasangalala? Akakumana na mavuto, kodi timawatonthoza ndi kuwathandiza? Tikauzidwa miseche yonena za bwenzi lathu, kodi timafulumila kuikhulupilila? Kapena, mofanana na Yonatani, kodi timasonyeza kuti ndife okhulupilika kwa bwenzi lathulo poliikila kumbuyo?

Kufufuza Cuma Cauzimu

w05 3/15 24 ¶4

Mfundo Zazikulu za M’buku la Samueli ­Woyamba

21:12, 13. Yehova amayembekezela kuti tizigwilitsa nchito nzelu zathu ndi maluso athu pothana ndi mavuto m’moyo wathu. Watipatsa Mawu ake ouzilidwa, omwe amatithandiza kukhala ocenjela, odziŵa zinthu, ndiponso aluso la kulingalila. (Miyambo 1:4) Palinso akulu oikidwa acikhristu omwe amatithandiza.

APRIL 18-24

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 SAMUELI 23-24

“Yembekezelani Yehova Moleza Mtima”

w04 4/1 16 ¶8

Dalilani Mzimu wa Mulungu Zinthu Zikasintha pa Moyo Wanu

8Davide anakana kupha Sauli. Posonyeza cikhulupililo na kuleza mtima, anaganiza zongosiya nkhaniyo m’manja mwa Yehova. Mfumuyo itacoka m’phangamo, Davide anaifuulila na kunena kuti: “Yehova aweluze pakati pa ine ndi inu, ndipo Yehova andibwezelele, koma dzanja langali silidzakukhudzani.” (1 Samueli 24:12) Ngakhale kuti Davide anali kudziŵa kuti Sauli anali kulakwitsa, sanabwezele yekha, ndiponso sanalankhule kwa Sauli monyoza kapena kumunyoza pamaso pa anthu ena. Pa maulendo ena angapo, Davide anadziletsa kubwezela yekha coipa. M’malomwake, anadalila Yehova kuti adzakonza zinthu.—1 Samueli 25:32-34; 26:10, 11.

w04 6/1 22-23

Kodi Mavuto Amene Mumakumana Nawo Amalamulila Moyo Wanu?

Mfundo yacitatu imene tikuphunzilapo ni yakuti tiyenela kudikila Yehova m’malo mogwilitsa nchito njila zosemphana na Malemba kuti tithetse mavuto athu. Wophunzila Yakobo analemba kuti: “Mulole kuti kupilila kumalize kugwila nchito yake, kuti mukhale okwanila ndi opanda cilema m’mbali zonse, osapelewela kalikonse.” (Yakobo 1:4) Tiyenela kulola kupilila ‘kumaliza nchito yake,’ mwa kulola ciyeso kupitiliza mpaka conse citatha popanda kutsatila njila zosemphana na Malemba kuti ciyesoco cithe msanga. Tikalola ciyesoco kupitiliza, ndiye kuti cikhulupililo cathu cidzayesedwa na kuyengedwa, ndipo mphamvu yake yolimbitsa munthu idzaonekela. Ni mmene kupilila kwa Yosefe na Davide kunalili. Iwo sanayese kupeza njila zawo-zawo zothetsela mavuto awo zoti Yehova sakanakondwela nazo. Koma anayesetsa kucita zimene akanatha ngakhale anali pamavuto. Iwo anadikila Yehova, ndipo analandila madalitso aakulu. Yehova anawagwilitsa nchito onse aŵili kulanditsa na kutsogolela anthu ake.—Genesis 41:39-41; 45:5; 2 Samueli 5:4, 5.

Ifenso tingakumane na mavuto amene angatiyese kuti ticite zinthu zosemphana na Malemba pofuna kuwathetsa. Mwacitsanzo, kodi ndinu wokhumudwa cifukwa cakuti simunapezebe munthu woyenela kumanga naye banja? Ngati limeneli ni vuto lanu, musayese ngakhale pang’ono kuphwanya lamulo la Yehova la kukwatila “mwa Ambuye.” (1 Akorinto 7:39) Kodi ukwati wanu uli pamavuto? M’malo motengela mzimu wa dziko umene umalimbikitsa anthu kupatukana na kusudzulana, yesetsani kuthandizana kuthetsa mavuto anuwo. (Malaki 2:16; Aefeso 5:21-33) Kodi zikukuvutani kusamalila banja lanu cifukwa ca vuto la zacuma? Kudikila Yehova kumatanthauzanso kuti mupewe kucita nchito zokayikitsa kapena zosaloleka pofuna kuti mupeze ndalama. (Salimo 37:25; Aheberi 13:18) Inde, tonsefe tiyenela kulimbikila kucita zimene tingathe ngakhale tili pa mavuto kuti Yehova apeze potidalitsila. Pamene tikutelo, tisasiye kudikila Yehova kuti apeleke njila yabwino yothetsela mavuto athuwo.—Mika 7:7.

Kufufuza Cuma Cauzimu

w17.11 27 ¶11

Musalole Ciliconse Kukumanitsani Mphoto

11Kukhala acikondi na okoma mtima kudzatithandiza kupewa kucitila nsanje anthu ena. Mawu a Mulungu amati: “Cikondi n’coleza mtima ndiponso n’cokoma mtima. Cikondi sicicita nsanje.” (1 Akor. 13:4) Kuti nsanje isazike mizu mu mtima mwathu, tifunika kuyesetsa kuona zinthu mmene Mulungu amazionela. Tiyenela kukumbukila kuti ise na Akhristu anzathu ndise ziwalo za thupi limodzi. Kucita izi kudzatilimbikitsa kutsatila malangizo ouzilidwa akuti: “Ciwalo cimodzi cikalemekezedwa, ziwalo zina zonse zimasangalalila naco limodzi.” (1 Akor. 12:16-18, 26) Conco, sitiyenela kucitila nsanje m’bale wathu ngati zinthu zamuyendela bwino, koma tiyenela kukondwela naye. Ganizilani za Yonatani, mwana wa Mfumu Sauli. Iye sanacite nsanje pamene Davide anadzozedwa kuti adzakhale mfumu ya Isiraeli yotsatila. Koma anam’limbikitsa. (1 Sam. 23:16-18) Na ise tiyenela kukhala okoma mtima komanso acikondi ngati Yonatani.

APRIL 25–MAY 1

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 SAMUELI 25-26

“Kodi Mumaugwila Mtima?”

ia 78 ¶10-12

Anacita Zinthu Mwanzelu

10Kodi asilikaliwa anali kucita ciani akakumana na abusawo? Zinali zosavuta kuti aziba nkhosa za Nabala, koma iwo sanali kucita zimenezi. M’malomwake, iwo anali kuteteza nkhosazo ndiponso abusawo. (Ŵelengani 1 Samueli 25:15, 16.) Abusa pamodzi na nkhosa zawo anali kukumana na mavuto ambili-mbili cifukwa kudelali kunali kupezeka zilombo zambili zolusa. Komanso delali linali pafupi kwambili na malile a kum’mwela a dziko la Isiraeli, moti akuba ocokela m’madela ena anali kubwela kudelali pafupi-pafupi.

11Davide ayenela kuti anali na udindo waukulu kwambili wopezela cakudya anthu ake, omwe anali nawo m’cipululumo. Motelo tsiku lina anatumiza anyamata ake 10 kuti akapemphe cakudya kwa Nabala. Nthawi imene Davide anatumiza anyamatawa inali yabwino cifukwa inali nthawi yometa ubweya wankhosa ndiponso yamadyelelo. Pa nthawiyi anthu anali kukonda kugaŵana zinthu. Komanso Davide anasankha bwino mawu oti anyamata ake akalankhule kwa Nabala ndipo anawauza kuti akalankhule naye mwaulemu kwambili. Anawalangiza anyamatawo kukanena kuti ‘mwana wanu Davide’ ni amene akupempha zinthuzi ndipo mwina anacita zimenezi posonyeza kuti anali kuzindikila zoti Nabala ni munthu wamkulu. Koma kodi Nabala anatani?—1 Sam. 25:5-8.

12Iye anakwiya kwambili moti mnyamata wake, yemwe wachulidwa kumayambililo kwa nkhani ino, pouza Abigayeli za nkhaniyi ananena kuti “mbuyanga walalatila nthumwizo.” Nabala anali munthu womana kwambili moti anauza anyamatawo kuti sangawononge nyama, madzi ndiponso mkate wake kupatsa Davide ndi anyamata ake. Iye ananyoza Davide ponena kuti anali wacabe-cabe ndiponso anali ngati kapolo amene wathaŵa mbuye wake. N’kutheka kuti Nabala anali kuona Davide mofanana na mmene Sauli, yemwe anali kudana na Davideyo, anali kumuonela. Nabala na Sauli sanali kuona Davide ngati mmene Yehova anali kumuonela. Mulungu anali kukonda kwambili Davide ndipo anali kumuona kuti ni mfumu ya m’tsogolo ya Isiraeli, osati ngati kapolo wothaŵa mbuye wake.—1 Sam. 25:10, 11, 14.

ia 80 ¶18

Anacita Zinthu Mwanzelu

18Abigayeli analankhula ngati kuti walakwitsa ni iyeyo ndipo anapempha Davide kuti am’khululukile. Iye anavomeleza kuti mwamuna wake anali wopanda nzelu, mogwilizana na tanthauzo la dzina lake. Conco anapempha Davide, yemwe anali waulemu wake, kuti asalimbane na munthu wopanda nzeluyo. Iye analankhula mosonyeza kuti anali kudziŵa zoti Davide ni mtumiki wa Yehova ndiponso kuti akumenya “nkhondo za Yehova.” Abigayeli anasonyezanso kuti anali kudziŵa zakuti Yehova analonjeza Davide kuti adzamupatsa ufumu. Tikutelo cifukwa polankhula na Davide, iye anati: “Yehova . . . adzakuikani kukhala mtsogoleli wa Isiraeli.” Kenako anapempha Davide kuti asacite ciliconse cimene cingam’cititse kuti akhale na mlandu wamagazi kapena zimene ‘zikanavutitsa cikumbumtima’ cake. (Ŵelengani 1 Samueli 25:24-31.) Apa iye analankhuladi mokoma mtima ndiponso mogwila mtima.

Kufufuza Cuma Cauzimu

ia 80 ¶16

Anacita Zinthu Mwanzelu

16Kodi zimenezi zikutanthauza kuti Abigayeli sanali kugonjela mwamuna wake monga mutu wa banjalo? Ayi si conco. Nabala anali atacita zinthu zoipa kwa mtumiki wodzozedwa wa Yehova ndipo zimenezi zikanaphetsa anthu ambili osalakwa a panyumba pake. Komanso Abigayeli akanapanda kucita ciliconse, akanakhala ngati akugwilizana na zimene mwamuna wake anacita. Conco, iye anaona kuti anayenela kugonjela Mulungu m’malo mogwilizana na zinthu zoipa zimene mwamuna wake anacita.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani