Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki
JULY 4-10
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 SAMUELI 18-19
“Barizilai Ni Citsanzo ca Kudzicepetsa”
w07 7/15 14 ¶5
Barizilai Anali Munthu Wodzicepetsa
N’zosakayikitsa kuti Davide anayamikila kwambili thandizo la Barizilai lija. Zikuoneka kuti Davide sanamuitane Barizilai pofuna kungobwezela zabwino zimene anam’citilazo, cifukwa Barizilai anali munthu wacuma moti sakanafunikila thandizo lotele. N’kutheka kuti Davide anali kufuna kuti Barizilai akakhale m’nyumba yacifumu cifukwa coti munthu wacikulileyu anali na makhalidwe abwino. Unali ulemu waukulu kwambili kwa Barizilai kukakhala ku nyumba imeneyi nthawi zonse, n’kukhala paubwenzi na mfumu.
w07 7/15 14 ¶7
Barizilai Anali Munthu Wodzicepetsa
N’kutheka kuti cimodzi mwa zifukwa zimene Barizilai anakanila pempholi cinali cakuti iye anali wokalamba ndipo sakanatha kucita zinthu zina na zina. Mwinanso anali kuona kuti watsala pang’ono kufa. (Salimo 90:10) Iye anacita zonse zimene akanatha pothandiza Davide. Komabe anali kudziŵanso kuti pali malile a zimene angathe kucita malingana na msinkhu wake. Barizilai sanalole kuti kuganizila za ulemelelo wake ndiponso kudziŵika kwake kum’sokoneze maganizo n’kulephela kuona kuti sangathe kucita zinthu zina. Mosiyana na Abisalomu, amene anali odzikweza kwambili, Barizilai anacita zinthu mwanzelu podzicepetsa.—Miyambo 11:2.
w07 7/15 15 ¶1-2
Barizilai Anali Munthu Wodzicepetsa
Nkhani ya Barizilai ikutithandiza kuti tiziona zinthu m’njila yoyenela. Koma sikuti zimene iye anacitazi zizitipangitsa kukana mwayi wautumiki poganiza kuti sitingakwanitse, mwinanso pofuna kungokhala na moyo wosatanganidwa. Komanso zisamatipangitse kusafuna udindo mumpingo. M’malo mwake, tiyenela kudalila Mulungu kuti atipatse mphamvu ndiponso nzelu kuti tim’tumikile.—Afilipi 4:13; Yakobo 4:17; 1 Petulo 4:11.
Ngakhale zili conco, tiyenela kuzindikila zinthu zimene sitingakwanitse. Mwacitsanzo, zingatheke kuti munthu ali na maudindo ambili mumpingo. N’zodziŵikilatu kuti kulandila maudindo enanso owonjezela pamenepa, kungam’cititse kunyalanyaza maudindo ena a m’malemba monga kusamalila banja lake. Ngati zitakhala conco, kodi sizingakhale bwino kukana maudindo ena owonjezelawo? Kucita zimenezi kungaonetse kuti munthuyo amaona zinthu m’njila yoyenela ndiponso ni wodzicepetsa.—Afilipi 4:5; 1 Timoteyo 5:8.
Kufufuza Cuma Cauzimu
“Nathamanga Panjilayo Mpaka pa Mapeto”
19Ngati muona kuti anthu ena samvetsetsa vuto limene muli nalo, mungalimbikitsidwe na citsanzo ca Mefiboseti. (2 Sam. 4:4) Iye anali wolemala, ndiponso Mfumu Davide anamukayikila moti anamucitila zinthu mopanda cilungamo. Mefiboseti sanalakwe ciliconse kuti akumane na mavuto amenewa. Ngakhale n’conco, iye sanakhumudwe na zimenezi. Koma anayamikila zabwino zimene zinamucitikila pa umoyo. Anayamikilanso zabwino zimene Davide anamucitila kumbuyoko. (2 Sam. 9:6-10) Conco, pamene Davide anamuweluza mopanda cilungamo, Mefiboseti sanasumike maganizo ake pa zinthu zopanda cilungamo zimenezo. Sanalole zinthu zimenezo kum’khumudwitsa. Komanso sanaimbe mlandu Yehova cifukwa ca zimene Davide anacita. Koma anaganizila kwambili zimene akanacita pocilikiza Davide, mfumu yoikidwa na Yehova. (2 Sam. 16:1-4; 19:24-30) Yehova anaonetsetsa kuti citsanzo cabwino ca Mefiboseti calembedwa m’Baibo kuti ife tiphunzilepo kanthu.—Aroma 15:4.
JULY 11-17
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 SAMUELI 20-21
“Yehova ni Mulungu Wacilungamo”
it-1 932 ¶1
Agibeoni
Mtundu wa anthu ochedwa Agibeoni unakhalapo kwa zaka mahandiledi, ngakhale kuti Mfumu Sauli anapanga ciwembu cakuti awaononge. Komabe, Agibeoni anayembekezela Yehova moleza mtima kuti aulule zinthu zopanda cilungamozo. Iye anacita izi mwa kubweletsa njala ya zaka zitatu mu ulamulilo wa Davide. Davide atafunsila kwa Yehova, anazindikila kuti panacitika chimo la magazi. Conco iye anafunsa Agibeoni kuti adziŵe zoyenela kucita kuti aphimbe chimolo. Agibeoni anayankha kuti “sitikufuna siliva kapena golide.” Yankho lawo linali loyenela cifukwa, malinga na Cilamulo, palibe dipo limene likanapelekedwa pofuna kuwombola munthu wopha mnzake. (Num. 35:30, 31) Agibeoni anazindikilanso kuti analibe ufulu wopha munthu popanda cilolezo. Conco Davide atawafunsa mowonjezeleka, iwo anapempha kuti awapatse “ana” 7 a Sauli. Malemba amakamba kuti Sauli pamodzi na nyumba yake anali na mlandu wa magazi. Izi zionetsa kuti ngakhale kuti Sauli ndiye anatsogolela pa ciwembu cofuna kufafaniza Agibeoni, ana ake nawonso anatengako mbali, kaya mwacindunji kapena m’njila ina. (2 Sam. 21:1-9) Conco pa cocitika cimeneci, sitinganene kuti ana anafela macimo a atate awo, (Deut. 24:16) koma analandila ciweluzo colungama, mogwilizana na lamulo lakuti “moyo kulipila moyo.”—Deut. 19:21.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w13 1/15 31 ¶14
Akulu Acikhristu Ni Anchito Anzathu Otipatsa Cimwemwe
14Ife anthu a Yehova padziko lonse lapansi tikutumikila Mulungu ngakhale kuti Satana na anthu ake akuyesetsa kutisokoneza. Ena a ife talimbana na mavuto akuluakulu okhala ngati Goliati ndipo tawagonjetsa cifukwa codalila Yehova. Komabe nthawi zina timatopa ndiponso kukhumudwa cifukwa cokhalila kulimbana na mavuto a m’dzikoli. Tikafooka conco, timakhala pa ngozi yogonjetsedwa na mavuto amene tikanatha kulimbana nawo bwinobwino. Pa nthawi ngati zimenezi, thandizo limene mkulu angapeleke lingatilimbikitse ndiponso kutithandiza kukhalanso na cimwemwe. Zimenezi zacitikila abale na alongo ambili. Mwacitsanzo, mlongo wina wa zaka zoposa 60, amene akucita upainiya, anati: “Nthawi ina m’mbuyomu, sin’nali kumva bwino m’thupi ndipo n’nali kutopa kwambili nikaloŵa mu utumiki. Mkulu wina anazindikila kuti nikuoneka wofooka ndipo ananithandiza. Tinakambilana nkhani ina yolimbikitsa ya m’Baibo. N’natsatila malangizo ake ndipo zinanithandiza.” Mlongoyu ananenanso kuti: “Nimayamikila kwambili kuti mkuluyo ananionetsa cikondi. Anazindikila kuti n’nafooka ndipo ananithandiza.” Zimatilimbikitsa kwambili kudziŵa kuti akulu amatikonda ndipo amacita nafe cidwi. Komanso, mofanana na Abisai, iwo amakhala okonzeka kutithandiza.’
JULY 18-24
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 SAMUELI 22
“Muzidalila Thandizo la Yehova”
cl 19 ¶11
Kodi ‘Mungayandikiledi kwa Mulungu’?
11Munthu angaŵelenge kuti Mulungu ali “ndi mphamvu zambili.” (Yesaya 40:26) Koma akhoza kumva mfundoyi mosiyana pamene aŵelenga za mmene Mulungu analanditsila Aisiraeli pa Nyanja Yofiila ndiyeno n’kukhala akusamalila mtunduwo m’cipululu kwa zaka 40. Mungathe kuona m’maganizo mwanu madzi oyenda mwamphamvu akugaŵikana. Mungauone mtunduwo, mwinamwake anthu 3,000,000 onse pamodzi, akuyenda pansi pa nyanjayo pouma, madzi oundanawo ataima ngati makoma akuluakulu kumbali zonse ziŵili. (Ekisodo 14:21; 15:8) Mukhoza kuona umboni wakuti Mulungu anali kuwasamalila bwino m’cipululu. Madzi anatuluka m’thanthwe. Cakudya, cokhala ngati zipatso zoyela, cinali kupezeka pansi. (Ekisodo 16:31; Numeri 20:11) Pano Yehova akuulula kuti si kuti ali na mphamvu zokha, komanso kuti amazigwilitsa nchito pothandiza anthu ake. Kodi si zokhazika mtima pansi kudziŵa kuti mapemphelo athu amapita kwa Mulungu wamphamvu amene “ndiye pothaŵilapo pathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezekelatu m’masautso”?—Salimo 46:1.
w10 6/1 26 ¶4-6
“Mudzakhala Wokhulupilika”
Tiyeni tiganizile mofatsa mawu a Davide amenewa. Mawu acihebeli omasulilidwa kuti “mudzakhala wokhulupilika” angatanthauzenso “kucita zinthu mokoma mtima.” Conco, munthu wokhulupilikadi amacita zinthu cifukwa ca cikondi ndipo Yehova amakonda anthu amene ali okhulupilika kwa iye.
Cinanso n’cakuti munthu wokhulupilika samangomva mumtima mwake kuti ni wokhulupilika koma amacita zinthu zoonetsa kuti ni wokhulupilika. Yehova amacita zinthu mokhulupilika ndipo Davide anaona yekha kuti mfundo imeneyi ni yoona. Panthawi imene iye anakumana na mavuto aakulu, Yehova anamuthandiza mwa kum’teteza mokhulupilika na kumutsogolela. Davide anazindikila kuti Yehova na amene anamuteteza ‘pomupulumutsa m’dzanja la adani ake onse.’—2 Samueli 22:1.
Kodi tikuphunzilapo ciyani pa mawu a Davide amenewa? Tikuphunzila kuti Yehova sasintha. (Yakobo 1:17) Iye amacita zinthu motsatila mfundo zake ndipo amakwanilitsa malonjezo ake mokhulupilika. Mu Salimo lina limene Davide analemba, iye anati: “Yehova . . . sataya okondedwa [okhulupilika ake].”—Salimo 37:28.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w12 11/15 17 ¶7
Yesetsani Kukhala Ngati Wamng’ono
7Davide anakhudzidwa kwambili ataona kudzicepetsa kwa Mulungu. Iye anaimbila Yehova kuti: “Inu mudzandipatsa cishango canu ca cipulumutso, ndipo kudzicepetsa kwanu n’kumene kumandikweza.” (2 Sam. 22:36) Davide anali kuona kuti udindo uliwonse umene anali nawo mu Isiraeli anaupeza cifukwa ca kudzicepetsa kwa Yehova. Zili ngati Mulungu anadzicepetsa na kutsika m’munsi kuti amuone Davideyo. (Sal. 113:5-7) Izi n’zimene Yehova amacitanso na ife. Kaya tili na khalidwe linalake labwino, kaya luso kapena udindo winawake, tizikumbukila kuti ‘tinangocita kulandila’ kucokela kwa Yehova. (1 Akor. 4:7) Munthu amene amakhala ngati wamng’ono amakhala “wamkulu” cifukwa Yehova akhoza kumugwilitsa nchito kwambili. (Luka 9:48) N’cifukwa ciyani tikutelo?
JULY 25-31
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 SAMUELI 23-24
“Kodi Mumapeleka Nsembe Zanu Modzimana?”
it-1 146
Arauna
Cioneka kuti Arauna anapeleka malowo pamodzi na nkhuni komanso ng’ombe popanda malipilo aliwonse. Koma Davide anaumilila kuti amulipila. Lemba la 2 Samueli 24:24 limaonetsa kuti Davide anagula malo opunthila mbewu komanso ng’ombe pa mtengo wa masekeli 50 a siliva (madola 110). Koma lemba la 1 Mbiri 21:25 limakamba kuti Davide anagula malowo na masekeli 600 a golide (madola pafupifupi 77,000). Wolemba buku la 2 Samueli anafotokoza cabe zogula malo omangapo guwa la nsembe komanso zinthu zopelekela nsembeyo. Conco, cioneka malipilo amene iye anachula anali cabe ogulila zinthu zimenezi. Koma pofotokoza nkhaniyi, wolemba buku la 2 Mbiri anaigwilizanitsa na kacisi amene anadzamangidwa pamalowo pambuyo pake. Iye anachula mtengo wa ndalama zogulila malo onse amene panamangidwa kacisi. (1 Mbiri 22:1-6; 2 Mbiri 3:1) Malo onse amene panamangidwa kacisi anali aakulu kwambili. Conco, cioneka kuti ndalama zokwana masekeli 600 a golide ni zimene zinalipilidwa pogula malo aakulu amenewo, osati cabe malo ocepa amene Davide anamangapo guwa la nsembe poyambapo.
w12 1/15 18 ¶8
Phunzilani Kucokela ku Coonadi ca M’cilamulo
8Nthawi zina munthu waciisiraeli anali kusankha kupeleka nsembe yaufulu poonetsa kuyamikila Yehova. Kapena anali kusankha kupeleka nsembe yopseleza imene inali yaufulu pofuna kuti asangalatse Yehova. Pa zocitika zimenezi iye sakanavutika kusankha nyama yabwino kwambili. Masiku ano, Akhristu sapeleka nsembe za nyama zimene zinachulidwa m’Cilamulo ca Mose. Komabe iwo amapeleka nsembe pogwilitsa nchito nthawi, mphamvu ndiponso cuma cawo kuti atumikile Yehova. Mtumwi Paulo ananena kuti pamene ‘tikulengeza’ cikhulupililo cathu ndiponso “kucita zabwino ndi kugawana zinthu ndi ena” timakhala tikupeleka nsembe zimene Mulungu amakondwela nazo. (Aheb. 13:15,16) Mtima umene anthu a Yehova amakhala nawo pocita zinthu zimenezi umaonetsa ngati amayamikiladi zinthu zonse zimene Mulungu wawapatsa. Conco mofanana na Aisiraeli, tiyenela kuonanso mtima umene tili nawo potumikila Mulungu ndiponso zolinga zimene timakhala nazo.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w05 5/15 19 ¶6
Mfundo Zazikulu za M’buku la Samueli Waciŵili
23:15-17. Davide anali kulemekeza kwambili lamulo la Mulungu lokhudza moyo na magazi moti panthawiyi, anapewa kucita zimene zinaoneka ngati zofanana na kuswa lamulo limenelo. Tiyenela kuphunzila kuwaona cimodzimodzi malamulo onse a Mulungu.
AUGUST 1-7
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 MAFUMU 1-2
“Kodi Mumaphunzilapo Kanthu pa Zolakwa Zanu?”
it-2 987 ¶4
Solomo
Adoniya atamva kulila kwa nyimbo mumzinda wapafupi wa Gihoni komanso congo ca anthu amene anali kufuula kuti: “Mfumu Solomo ikhale ndi moyo wautali,” iye na anzake amene anapanga nawo ciwembu anathawa cifukwa ca mantha komanso kusokonezeka. Solomo anapewa kuyamba ulamulilo wake na mbili yoipa mwa kubwezela anthu amene anam’pandukila. Mwa ici, iye anapeleka cithunzi ca mtendele umene udzakhala mu ulamulilo wake. Cikanakhala kuti Adoniya ndiye anali mfumu, ndipo Solomo wam’pandukila, mosakaikila Solomoyo akanaphedwa. Adoniya pofuna citetezo anathaŵila ku malo opatulika. Conco, Solomo anatumiza anthu kuti akamutenge na kubwela naye kwa iye. Solomo anauza Adoniya kuti adzakhalabe na moyo ngati coipa sicidzapezeka mwa iye. Kenako anamuuza kuti apite kunyumba kwake.—1 Maf. 1:41-53.
it-1 49
Adoniya
Komabe, Davide atamwalila, Adoniya anapita kwa Bati-seba kukamunyengelela kuti akapemphe Solomo kuti amupatse Abisagi, mlezi wa Davide kuti akhale mkazi wake. Adoniya anavomeleza kuti Yehova ndiye anapeleka ufumuwo kwa Solomo. Komabe, mawu ake akuti “ufumu unayenela kukhala wanga, ndipo Aisiraeli onse maso awo anali pa ine kuti ndikhala mfumu” asonyeza kuti iye anali kuona ngati anamanidwa mwayi wokhala mfumu. (1 Maf. 2:13-21) N’kutheka kuti Adoniya anapempha mkaziyo kuti angokhala monga cipukuta misozi kaamba kotaikilidwa ufumu. Koma pempho lakelo linaonetselatu kuti anali akali na cilakolako camphamvu cofuna kukhala mfumu. Tikutelo cifukwa malinga na lamulo la anthu akale a Kum’mawa, akazi komanso akazi apambali a mfumu anali kutengedwa na munthu yekhayo woloŵa m’malo mwa mfumuyo mwalamulo. (Yelekezelani 2 Sam. 3:7; 16:21.) Solomo atamva pempho limeneli, anazindikila maganizo olakwika amene Adoniya anali nawo, ndipo analamula kuti Adoniya aphedwe. Adoniya anaphedwadi nthawi yomweyo na Benaya.—1 Maf. 2:22-25.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w05 7/1 30 ¶2
Mfundo Zazikulu za M’buku la Mafumu Woyamba
2:37, 41-46. N’zoopsa kwambili kuganiza kuti munthu angaphwanye malamulo a Mulungu koma osalandila cilango. Amene amapatuka mwadala pa cipata copapatiza “colowela ku moyo” adzakumana na zotsatila za cisankho cawo copanda nzeluco.—Mateyu 7:14.
AUGUST 8-14
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 MAFUMU 3-4
“Phindu la Nzelu”
w11 12/15 8 ¶4-6
Kodi Solomo Ni Citsanzo Cabwino Kapena Coipa?
4Kumayambililo kwa ulamulilo wake, Mulungu anaonekela kwa Solomo m’maloto n’kumuuza kuti apemphe zimene akufuna. Cifukwa cakuti Solomo anali kuzindikila zoti sadziŵa zambili iye anapempha nzelu. (Welengani 1 Mafumu 3:5-9.) Ndiyeno Mulungu anasangalala kuti Solomo wapempha nzelu osati cuma kapena ulemelelo. Conco anamupatsa “mtima wanzelu ndi womvetsa zinthu” komanso cuma. (1 Maf. 3:10-14) Malinga na zimene Yesu ananena, nzelu za Solomo zinamveka patali kwambili, moti mfumukazi ya ku Sheba inamva n’kuyenda mtunda wautali kwambili kuti ikadzionele yokha.—1 Maf. 10:1, 4-9.
5 Ife sitiyembekezela kulandila nzelu m’njila yozizwitsa. Solomo ananena kuti “Yehova amapeleka nzelu,” koma analemba kuti tiyenela kucita khama kuti tipeze nzeluzo. Iye anati tiyenela ‘kumvetsela nzelu ndi khutu lathu ndi kuika mtima wathu pa kuzindikila.’ Pa nkhani yopeza nzeluyi, iye anagwilitsanso nchito mawu ngati ‘kuitana,’ ‘kufunafuna’ ndiponso ‘kufufuza.’ (Miy. 2:1-6) Izi zikusonyezelatu kuti tikhoza kupeza nzelu.
6 Ni bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi nikutsatila citsanzo ca Solomo pa nkhani yoona kuti nzelu yocokela kwa Mulungu ni yamtengo wapatali?’ Mavuto a zacuma acititsa anthu ambili kuganizila kwambili za nchito komanso ndalama zawo. Ena amalola kuti zimenezi ziwacititse kusankha maphunzilo apamwamba. Nanga bwanji za inu na banja lanu? Kodi zosankha zanu zimasonyeza kuti mumaona kuti nzelu yocokela kwa Mulungu ni yamtengo wapatali ndipo mukufuna kuipeza? Kodi kusintha zolinga zanu kungakuthandizeni kuti mupeze nzelu zambili? Dziŵani kuti kupeza nzelu ndiponso kuitsatila kudzakuthandizani kwa moyo wanu wonse. Solomo analemba kuti: “Ukacita zimenezi udzamvetsa zinthu zolondola, zolungama, zowongoka, ndiponso njila yonse ya zinthu zabwino.”—Miy. 2:9.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w98 2/1 11 ¶15
Yehova Ni Mulungu Wamapangano
15Mbadwa za Aburahamu zitalinganizidwa kukhala mtundu wotsogozedwa na Cilamulo, Yehova anawadalitsa mogwilizana na lonjezo lake kwa kholo lawo lija. Mu 1473 B.C.E., woloŵa m’malo mwa Mose, Yoswa, anatsogolela Aisiraeli kukaloŵa m’Kanani. Lonjezo la Yehova la kupeleka dzikolo kwa mbewu za Aburahamu linakwanilitsidwa pamene mafuko anagaŵana dzikolo. Pamene Aisiraeli anali okhulupilika, Yehova anakwanilitsa lonjezo lake lakuti adzawathandiza kugonjetsa adani awo. Zimenezi zinacitikadi makamaka m’nthaŵi ya ulamulilo wa Mfumu Davide. Podzafika nthaŵi ya mwana wa Davide Solomo, mbali yacitatu ya pangano la Aburahamu inakwanilitsidwa. “Ayuda ndi Aisiraeli anaculuka kwambili. Kuculuka kwake anali ngati mcenga wa m’phepepete mwa nyanja, ndipo anali kudya, kumwa ndi kusangalala.”—1 Mafumu 4:20.
AUGUST 15-21
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 MAFUMU 5-6
“Anagwila Nchito Molimbika Cifukwa Cokonda Yehova”
Kodi Mukudziŵa?
Matabwa a ku Lebanoni anali odziŵika kwambli cifukwa anali olimba, okongola, akafungo kabwino ndiponso sankafumbwa. Conco Solomo anagwilitsa ntchito matabwa apamwamba kwambili pomanga kacisi. Masiku ano, dela lamapili ku Lebanoni kumene kalelo kunali nkhalango yaikulu ya mikungudza, kunangotsala nkhalango zing’onozing’ono za apo na apo.
it-1 424
Mtengo wa Mkungudza
Popeza mitengo ya mkungudza inagwilitsidwa nchito kwambili, panali kufunika anchito masauzande ambili odula mitengoyo na kuitumiza ku Turo kapena ku Sidoni, mizinda imene inali m’mbali mwa Nyanja ya Mediterranean. Akatelo, anali kumanga pamodzi mitengoyo n’kupanga maphaka, na kuwayandamitsa pamadzi, mwacionekele kupita nawo ku Yopa. Kenako, anali kuika mitengoyo pa mtunda na kuyamba kuikoka mpaka ku Yerusalemu. Izi zinatheka cifukwa ca pangano la pakati pa Solomo na Hiramu. (1 Maf. 5:6-18; 2 Mbiri 2:3-10) Pambuyo pake, matabwa a mkungudza anapitiliza kubwela ku Yerusalemu, ndipo anaculuka kwambili moti Malemba amati Solomo anacititsa ‘matabwa a mkungudza kuculuka kwambili ngati mitengo ya mkuyu’ mu ulamulilo wake.—1 Maf. 10:27; yelekezelani na Yes. 9:9, 10.
it-2 1077 ¶1
Kacisi
Polinganiza nchitoyo, Solomo analemba nchito amuna 30,000 a Isiraeli, ndipo anali kuwatumiza ku Lebanoni m’magulu a anthu 10,000 pa mwezi. Gulu limodzi likapita panali kutenga miyezi iŵili kuti likapitenso. (1 Maf. 5:13, 14) Iye analembanso amuna 70,000 amene “sanali ana a Isiraeli” kuti akhale onyamula katundu, komanso ena 80,000 kuti akhale osema miyala. (1 Maf. 5:15; 9:20, 21; 2 Mbiri 2:2) Solomo anasankha amuna 550 kuti akhale akapitawo oyang’anila nchitoyo, komanso amuna ena 3,300 owathandizila kuyang’anila. (1 Maf. 5:16; 9:22, 23) Cioneka kuti mwa amuna amenewa, 250 anali Aisiraeli koma amuna 3,600 anali “alendo” mu Isiraeli.—2 Mbiri 2:17, 18.
Kufufuza Cuma Cauzimu
g 5/12 17, bokosi
Baibulo Ni Buku la Maulosi Olondola, Gawo 1
BAIBULO LIMANENA NDENDENDE NTHAWI YOMWE ZINTHU ZINACITIKA
Pa lemba la 1 Mafumu 6:1 pali citsanzo cosonyeza kuti Baibo imanena ndendende nthawi imene zinthu zinacitika. Lembali limanena za nthawi imene Mfumu Solomo inayamba nchito yomanga kacisi ku Yerusalemu. Limati: “Solomo anayamba kumanga nyumba ya Yehova. Anayamba kucita zimenezi m’caka ca 480 [patatha zaka 479] kucokela pamene ana a Isiraeli anatuluka m’dziko la Iguputo, m’mwezi waciwili wa Zivi. Ici cinali caka cacinayi ca ulamulilo wake monga mfumu ya Isiraeli.”
Baibulo limaonetsa kuti caka cacinayi ca ulamulilo wa Solomo cinali 1034 B.C.E. Tikawelengetsela cobwelela m’mbuyo, zaka 479 zikutifikitsa m’caka ca 1513 B.C.E., caka comwe Aisiraeli anatuluka mu Iguputo.
AUGUST 22-28
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 MAFUMU 7
“Zimene Tingaphunzilepo pa Zipilala Ziŵili”
“M’mapili Ake Mudzakumbamo Mkuwa”
Mfumu Solomo inagwilitsa nchito mkuwa wambili pomanga kacisi ku Yelusalemu. Wambili mwa mkuwa umene Solomo anagwilitsa nchito, unali wocokela kwa Davide, bambo ake, womwe anaupeza atagonjetsa Asiriya kunkhondo. (1 Mbiri 18:6-8) “Thanki yamkuwa” imene ansembe anali kugwillitsa nchito pa utumiki wawo inali yaikulu malita 66,000 ndipo mwina inali kulemela matani 30. (1 Mafumu 7:23-26, 44-46) Ndiye panalinso zipilala ziwili za mkuwa zomwe zinali pakhomo la kacisi. Zipilalazi zinali na mphako zazikulu kuposa mita imodzi, khoma lake linali lonenepa masentimita 7 na hafu ndipo zinali zazitali mamita 8. Pamwamba pa zipilalazi panali mitu yotalika kupitilila pang’ono mamita aŵili. (1 Mafumu 7:15, 16; 2 Mbiri 4:17) Ndiye tangoganizani kuculuka kwa mkuwa umene anagwilitsa nchito kupanga zinthu zimenezi.
it-1 348
Boazi, II
Zipilala ziŵili zikuluzikulu zamkuwa zinaikidwa pakhonde la kacisi waulemelelo wa Solomo. Cipilala cimene cinali mbali ya kumanzele cinali kuchedwa, Boazi, mwina kutanthauza “Mwamphamvu.” Ndipo cipilala cimene cinali kudzanja lamanja cinali kuchedwa Yakini, kutanthauza kuti “[Yehova] Akhazikitse.” Conco, mawuwo akaikidwa pamodzi, munthu n’kuwaŵelenga kucokela kumanja kupita kumanzele atayang’ana kum’maŵa, akanamvapo lingalilo lakuti ‘[Yehova] akhazikitse [kacisi] mwamphamvu.’—1 Maf. 7:15-21.
Kufufuza Cuma Cauzimu
it-1 263
Kusamba
Ukhondo ni wofunika kwa anthu amene amalambila Yehova m’njila yoyela komanso yosaipitsidwa. Cimene cionetsa zimenezi ni ndongosolo limene Aisiraeli anali kutsatila potumikila pa cihema komanso pa kacisi amene anamangidwa pambuyo pake. Pa nthawi imene Aroni anaikidwa kukhala Mkulu wa Ansembe, iye na ana ake anasamba asanavale zovala zaunsembe. (Eks. 29:4-9; 40:12-15; Lev. 8:6, 7) Posamba m’manja na mapazi, ansembe anali kugwilitsilitsa nchito madzi a m’beseni lamkuwa limene linali m’bwalo la cihema copatulika. Ndipo kacisi wa Solomo atamangidwa, ansembe anali kusamba madzi a m’thanki yamkuwa imene inali kukhala pa kacisipo. (Eks. 30:18-21; 40:30-32; 2 Maf. 4:2-6) Pa Tsiku Lophimba Macimo, mkulu wa ansembe anali kusamba kaŵili. (Lev. 16:4, 23, 24) Anthu amene anali kutenga mbuzi ya Azazeli, zinthu zotsalila popeleka nsembe za nyama, na ng’ombe yaikazi yofiila yopeleka nsembe kupita nazo kunja kwa msasa anali kufunika kusamba matupi awo na kucapa zovala zawo asanaloŵenso mumsasa.—Lev. 16:26-28; Num. 19:2-10.
AUGUST 29–SEPTEMBER 4
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 MAFUMU 8
“Pemphelo la Solomo Lodzicepetsa Komanso Locokela Pansi pa Mtima”
w09 11/15 9 ¶9-10
Kuphunzila Baibulo Kungathandize Kuti Mapemphelo Anu Azikhala Atanthauzo
9Kuti Mulungu ayankhe pemphelo lathu, liyenela kucokela mumtima. Anthu asanasonkhane ku Yerusalemu pa mwambo wotsegulila kacisi wa Yehova mu 1026 B.C.E., Solomo anapemphela kucokela mumtima ndipo pemphelo limeneli linalembedwa pa 1 Mafumu caputala 8. Solomo anatamanda Mulungu likasa la cipangano litaikidwa m’Malo Oyela Koposa ndiponso mtambo wa Yehova utadzaza m’kacisi.
Ŵelengani bwino-bwino pemphelo la Solomo ndipo onani mmene akuchulila mobweleza-bweleza mawu akuti mtima. Solomo ananena kuti Yehova yekha na amene amadziŵa mtima wa munthu. (1 Maf. 8:38, 39) Pempheloli limaonetsanso kuti pali ciyembekezo cakuti wocimwa amene ‘wabwelela kwa Mulungu ndi mtima wake wonse,’ angakhululukidwe. Ngati anthu a Mulungu atagwidwa kukhala akapolo, mapemphelo awo akanamvedwa ngati mtima wawo unali wangwilo kwa Yehova. (1 Maf. 8:48, 58, 61) Motelo mapemphelo anu ayenela kucokela mumtima.
w99 1/15 17 ¶7-8
Kwezani Manja Okhulupilika m’Pemphelo
7Kaya tikupemphela poyela kapena patokha, mfundo yofunika ya m’Malemba imene tiyenela kukumbukila ni yakuti tiyenela kuonetsa mtima wodzicepetsa m’mapemphelo athu. (2 Mbiri 7:13, 14) Mfumu Solomo inaonetsa kudzicepetsa papemphelo lake lapoyela popatulila kacisi wa Yehova m’Yerusalemu. Solomo anali atangomaliza imodzi ya nyumba zaulemelelo koposa zomangidwa padziko lapansi. Komabe, anapemphela modzicepetsa kuti: “Kodi Mulungu angakhaledi padziko lapansi? Taonani! Kumwamba ngakhale kumwambamwamba simungakwaneko. Kuli bwanji nyumba imene ndamangayi?”—1 Mafumu 8:27.
8Monga Solomo, tiyenela kukhala odzicepetsa poimila ena m’pemphelo lapoyela. Ngakhale kuti tiyenela kupewa kumveka ngati wolungama kwambili, tingaonetse kudzicepetsa mwa kamvekedwe ka mawu athu. Mapemphelo odzicepetsa sakhala okometsela mopambanitsa kapena oyelekeza kukhudzidwa mtima. Amapangitsa anthu kuganiza, osati za amene akupemphelayo, koma amene akupemphelakoyo. (Mateyu 6:5) Kudzicepetsa kumaonekelanso mwa zimene tinena popemphela. Ngati tipemphela modzicepetsa, sitidzamveka monga ngati tikum’lamulila Mulungu kucita zimene tikufuna. M’malo mwake, tidzapempha Yehova kucita zimene zikugwilizana na cifunilo cake copatulika. Wamasalmo anaonetsa mzimu woyenela pamene anacondelela kuti: “Inu Yehova, conde tipulumutseni. Haa! Inu Yehova, conde tithandizeni kuti zinthu zitiyendele bwino.”—Salmo 118:25; Luka 18:9-14.
Kufufuza Cuma Cauzimu
it-1 1060 ¶4
Kumwamba
Solomo, amene anamanga kacisi wa ku Yerusalemu, anakamba kuti “kumwamba, ngakhale kumwambamwamba” Mulungu sangakwaneko. (1 Maf. 8:27) Popeza Yehova ndiye Mlengi wa kumwamba, kumene iye amakhala ni malo aulemelelo kwambili kuposa kumwamba, ndipo “dzina lake lokhalo lili pamwamba posafikilika. Ulemelelo wake uli pamwamba kuposa dziko lapansi ndi kumwamba.” (Sal. 148:13) Yehova amapima kumwamba konse mosavuta ngati mmene munthu angapimile cinthu na dzanja lake, moti cinthuco n’kukhala pakati pa cala cake cacing’ono na cacikulu akatambasula zalazo. (Yes. 40:12) Mawu a Solomo amenewa satanthauza kuti Mulungu alibe malo ake eni-eni okhala. Satanthauzanso kuti Mulungu amakhala paliponse komanso m’cinthu ciliconse ayi. Cimene cionetsa zimenezi n’cakuti Solomo anakambanso kuti Yehova amamva mapemphelo ali “kumwamba, malo [ake] okhala okhazikika,” kutanthauza kumwamba kokhala zamoyo zauzimu.—1 Maf. 8:30, 39.