NYIMBO 101
Tisunge Umodzi Wathu
Yopulinta
(Aefeso 4:3)
1. M’dzikoli logaŵikana,
Yehova watibweletsa
Mu gulu logwilizana.
Tili na cimwemwe,
Tikonda umodzi,
Wa m’gulu lathu.
Mu nchito ya M’lungu wathu,
Muli zocita zambili.
Tikhale ogwilizana
Pomutumikila.
2. Cikondi, kukoma mtima,
Zimabweletsa umodzi,
Zimatipatsa mtendele,
Timasangalala.
Yehova ‘tipatsa
Mtendele wake.
Iye amatithandiza
Kukhala ogwilizana.
Ise tidzapitiliza
Kumutumikila.
(Onaninso Mika 2:12; Zef. 3:9; 1 Akor. 1:10.)