NYIMBO 40
Kodi Ndife a Ndani?
Yopulinta
1. M’lungu wako n’ndani?
Umamvelela uti?
Ni uja amene umam’gwadila,
Na kum’tumikila.
Milungu iŵili,
Sungaitumikile.
Sankhapo cabe Mulungu mmodzi
Amene umakonda.
2. M’lungu wako n’ndani?
Udzamvelela uti?
Cili kwa iwe, sankha wekha,
Wabodza olo woona.
Wasankha kumvela
Mafumu a dzikoli
Olo wasankha kumvela M’lungu,
Na kucita zabwino?
3. M’lungu wanga n’ndani?
Nidzamvela Yehova.
Nidzam’tumikila mokondwa
Komanso modzipeleka.
Mokhulupilika
Nidzayenda na M’lungu.
Nidzam’tumikila nthawi zonse,
Na kumulemekeza.
(Onaninso Yos. 24:15; Sal. 116:14, 18; 2 Tim. 2:19.)