LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w23 October masa. 6-11
  • Kodi Ndinu ‘Wokonzeka Kumvela’?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Ndinu ‘Wokonzeka Kumvela’?
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • MUZIMVELA MAKOLO ANU
  • MUZIMVELA OLAMULILA AKULU-AKULU
  • MUZITSATILA CITSOGOZO CA GULU LA YEHOVA
  • Nthawi Zonse Yesu Anali Womvela
    Phunzitsani Ana Anu
  • Khalani Omvera Kuti Mulandire Madalitso
    Imbirani Yehova
  • Mvela Udalitsike
    ‘Imbani Mokweza ndi Mosangalala’ kwa Yehova
  • Cikondi Ca Mulungu N’camuyaya
    Mmene Tingakhalilebe mu Cikondi ca Mulungu
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
w23 October masa. 6-11

NKHANI YOPHUNZILA 42

Kodi Ndinu ‘Wokonzeka Kumvela’?

“Nzelu yocokela kumwamba. . . ndi yokonzeka kumvela.”—YAK. 3:17.

NYIMBO 101 Tisunge Umodzi Wathu

ZIMENE TIKAMBILANEa

1. N’cifukwa ciyani nthawi zina zingakhale zovuta kukhala womvela?

KODI kukhala womvela kumakuvutani? Davide nayenso, zinali kumuvuta nthawi zina. Ndiye cifukwa cake anapemphela kuti: “Ndicilikizeni ndi mzimu wofunitsitsa,” kuti ndikumveleni. (Sal. 51:12) Davide anali kukonda Yehova. Ngakhale n’telo, nthawi zina Davide zinali kumuvuta kuonetsa mtima womvela, ndipo ni mmenenso zilili kwa ise. Cifukwa ciyani? Coyamba, cifukwa cakuti tinatengela mzimu wa kusamvela kwa makolo athu. Caciŵili, Satana amayesetsa kutinyengelela kuti tipandukile Yehova mmene iye anacitila. (2 Akor. 11:3) Cacitatu, tikukhala m’dziko mmene khalidwe la kupanduka lili paliponse, ndipo “mpweya umenewu, kapena kuti kaganizidwe kameneka, tsopano kakugwila nchito mwa ana a kusamvela.” (Aef. 2:2) Tiyenela kucita zonse zothekha kuti tilimbane na ucimo, Satana, komanso dziko, kuti timvele Yehova komanso aja amene wapatsa ulamulilo.

2. Kodi kukhala ‘wokonzeka kumvela’ kumatanthauza ciyani? (Yak. 3:17)

2 Ŵelengani Yakobo 3:17. Yakobo anauzilidwa kulemba kuti anthu anzelu ni ‘okonzeka kumvela.’ Kodi zimenezi zitanthauza ciyani? Tiyenela kukhala ofunitsitsa kumvela aja amene Yehova waapatsako ulamulilo. Komabe, Yehova satiyembekezela kumvela munthu aliyense amene angatiuze kuphwanya malamulo ake.—Mac. 4:​18-20.

3. N’cifukwa ciyani Yehova amafuna kuti tizimvela anthu omwe ali na olamulilo pa ife?

3 N’capafupi kumvela Yehova kuposa kumvela anthu. Ndiiko komwe, Yehova nthawi zonse amapeleka citsogozo cangwilo. (Sal. 19:7) Koma umu si mmene zilili kwa anthu amene ali na ulamulilo. Ngakhale n’telo, Yehova wagaŵilako mphamvu zake za ulamulilo kwa makolo, akulu-akulu a boma, komanso akulu mu mpingo. (Miy. 6:20; 1 Ates. 5:12; 1 Pet. 2:​13, 14) Ngati tiwamvela, ndiye kuti tikumvelanso Yehova. Koma nthawi zina kungakhale kotivuta kuti timvele citsogozo ca anthu amene Yehova wapatsa ulamulilo. Conco tiyeni tikambilane zimene tingacite kuti tiziwamvelabe.

MUZIMVELA MAKOLO ANU

4. N’cifukwa ciyani acicepele ambili samvela makolo awo?

4 Acicepele amakumana na acicepele ena omwe ni “osamvela makolo.” (2 Tim. 3:​1, 2) N’cifukwa ciyani ena zimawavuta kumvela makolo awo? Makolo ena sacita zimene amaphunzitsa ana awo. Conco ana awo amaona kuti cimeneci si cilungamo. Ena amaona kuti malangizo a makolo awo ni acikale-kale, osathandiza komanso ovuta kuwatsatila. Ngati ndinu wacicepele, kodi inunso mumaona conco? Acicepele ambili zimawavuta kumvela lamulo la Yehova lakuti: “Muzimvela makolo anu mwa Ambuye, pakuti kucita zimenezi n’cilungamo.” (Aef. 6:1) N’ciyani cingakuthandizeni kumvela lamulo limeneli?

5. N’cifukwa ciyani n’zocititsa cidwi kuona kuti Yesu anali womvela kwa makolo ake? (Luka 2:​46-52)

5 Mungaphunzile kukhala omvela ku citsanzo cabwino kwambili ca Yesu. (1 Pet. 2:​21-24) Ngakhale kuti iye anali wangwilo, analeledwa na makolo opanda ungwilo. Ndipo olo kuti makolo ake anali kuphonyetsa zina zake, komanso panthawi zina sanali kumumvetsa, Yesu anali kuwamvelabe . (Eks. 20:12) Ganizilani zimene zinacitika Yesu anali na zaka 12. (Ŵelengani Luka 2:​46-52.) Nthawi ina Yesu na makolo ake anapita ku Yerusalemu. Koma pobwelako makolo ake sanazindikile kuti Yesu sanali nawo limodzi. Unali undido wa Yosefe na Mariya kuonetsetsa kuti ana awo onse ali nawo limodzi pa gululo pobwelela ku nyumba pambuyo pa cikondwelelo. Yosefe na Mariya atapeza Yesu, Mariya anaimba Yesu mlandu cifukwa cokhalila ku Yerusalemu! Akanafuna Yesu akananena kuti makolo ake akum’citila zinthu mopanda cilungamo. M’malo mwake, iye anawayankha mwacidule komanso mwaulemu. Koma “iwo sanamvetse zimene anali kuwauzazo.” Ndipo Yesu “anapitiliza kuwamvela.”

6-7. N’ciyani cingathandize acicepele kuti azimvela makolo awo?

6 Acicepele, kodi zimakuvutani kumvela makolo anu akaphonyetsa zina zake, komanso pamene sakukumvetsani? Ngati n’telo, n’ciyani cingakuthandizeni? Coyamba, ganizilani mmene zimakhudzila Yehova. Baibo imati ngati mumvela makolo anu, ‘ambuye amakondwela.’ (Akol. 3:20) Yehova amadziŵa ngati makolo anu sakukumvetsani, komanso ngati akukuikilani malamulo ooneka ovuta kuwatsatila. Koma ngati muwamvelabe makolo anu, Yehova amakondwela.

7 Caciŵili, ganizilani mmene makolo anu zimawakhudzila. Mukamamvela makolo anu, iwo amasangalala, ndipo amayamba kukudalilani. (Miy. 23:​22-25) Mwacionekele, ubwenzi wanu na iwo udzalimba. Mnyamata wina wa ku Belgium, dzina lake Alexandre anati, “N’tayamba kutsatila zimene makolo anga anali kuniuza, ubwenzi wanga na iwo unalimba, ndipo tonse tinakhala acimwemwe.”b Cacitatu, ganizilani mmene kukhala womvela pali pano kudzakuthandizilani m’tsogolo. Paulo amene akhala ku Brazil, anati, “Kumvela makolo kwanithandiza kuti nizimvela Yehova, komanso aja amene ali na ulamulilo.” Baibo imapeleka cifukwa camphamvu cimene ana ayenela kumvela makolo. Imati: “Kuti zinthu zikuyendele bwino, ndiponso kuti ukhale ndi moyo wautali padziko lapansi.”—Aef. 6:​2, 3.

8. N’cifukwa ciyani acicepele ambili amasankha kumvela makolo awo?

8 Acinyamata ambili amaona kuti zinthu zimawayendela bwino ngati akhala omvela. Mtsikana wina wa ku Brazil dzina lake Luiza, anafotokoza kuti poyamba sanamvetse cifukwa cake sanali kumulola kukhala na foni. Zinali conco cifukwa cakuti anzake ambili anali na mafoni. Koma pamapeto pake anazindikila kuti makolo ake anali kumuteteza. Iye anati, “nimaona kuti kumvela makolo sikumaniphela ufulu koma kumaniteteza.” Mlongo wina wacitsikana amene akhala ku America dzina lake Elizabeth, zimamuvutabe kumvela makolo ake nthawi zina. Iye anafotokoza kuti, “Nikalephela kumvetsa cifukwa cake makolo aniikila malamulo ena ake, nimayesetsa kuganizila nthawi ina pamene malamulo awo ananiteteza.” Mtsikana wina wa ku Armenia dzina lake Monica, anafotokoza kuti, zinthu zimamuyendela bwino akasankha kumvela malamulo a makolo ake m’malo mowasuliza.

MUZIMVELA OLAMULILA AKULU-AKULU

9. Kodi anthu ambili amaiona bwanji nkhani yomvela malamulo?

9 Anthu ambili amavomeleza kut timafunikila otiyang’anila, ndiponso kuti tiyenela kumvela ku malamulo ena a “akulu-akulu” a boma. (Aroma 13:1) Koma anthu amodzi-modziwo amawayawaya kumvela malamulo amene amaoneka kuti ni opanda cilungamo komanso amene sanawakonde. Mwacitsanzo, pa nkhani yolipila msonkho, malinga na kafukufuku amene anacitika ku Europe aonetsa kuti anthu ambili amaona kuti “m’poyenela kusalipila, msonkho ngati simukugwilizana nazo, komanso ngati mukuona kuti n’zopanda cilungamo.” Ndiye n’cifukwa cake n’zosadabwitsa kuti nzika za dzikoli sizimalipila misonkho yonse imene boma limafuna kuti ziziliplila.

Mariya ali pa bulu pamene Yosefe akutsogolela paulendo wawo wopita ku Betelehemu. Zithunzi: 1. M’bale akuona liwilo ya galimoto yake pomwe akudutsa pa cikwangwani ca pamsewu. 2. M’bale akulemba pa pepala la msonkho. 3. Mlongo wavala masiki ndipo waimilila motalikilana polankhulana na wa zacipatala.

Kodi nkhani ya Yosefe na Mariya imatiphunzitsa ciyani za kukhala omvela? (Onani ndime 10-12)c

10. Ngakhale pamene sitinakonde malamulo ena, n’cifukwa ciyani timasankha kukhalabe omvela?

10 Baibo imaonetsa kuti maulamulilo a anthu awonjezela mavuto, ali pansi pa ulamulilo wa Satana, komanso kuti adzawonongedwa posacedwa. (Sal. 110:​5, 6; Mlal. 8:9; Luka 4:​5, 6) Imatiuzanso kuti “amene akutsutsana ndi ulamulilo akutsutsana ndi dongosolo la Mulungu.” Pali pano Yehova walola olamulila akulu-akulu amenewa kuti akhalepo kwa kanthawi kuti asungitse dongosolo, ndipo amafuna kuti tiziwamvela. Conco, ‘tizipeleka kwa onse zimene amafuna,’ zomwe ziphatikizapo msonkho, ulemu, komanso kuwamvela. (Aroma 13:​1-7) Tingaone lamulo lina kukhala losayenela, lopanda cilungamo, kapena lovuta kulitsatila. Koma timamvela Yehova, ndipo amatiuza kuti tiyenela kumvela olamulila malinga ngati satiuza kuphwanya malamulo ake.—Mac. 5:29.

11-12. Kodi Yosefe na Mariya anacita ciyani pomvela lamulo limene linapelekedwa? Nanga panakhala zotulukapo zotani? (Luka 2:​1-6) (Onaninso zithunzi)

11 Tingatengele citsanzo ca Yosefe na Mariya amene anali okonzeka kumvela olamulila ngakhale pamene cinali covuta kutelo. (Welengani Luka 2:​1-6.) Mariya atatsala pang’ono kubeleka, boma linapeleka lamulo limene likanapangitsa kuti zikhale zovuta kwa iye na Yosefe kulitsatila. Bwanamkubwa waciroma, dzina Augusito, analamula kuti nzika zonse za ufumuwo zipite ku mizinda yakwawo kukalembetsa m’kaundula. Yosefe na Mariya anafunika kupita ku Betelehemu, ulendo wodutsa m’mapili wa makilomita 150. Ulendowu unali wosautsa maka-maka kwa Mariya. N’kutheka kuti iwo analinso kudela nkhawa za umoyo wa Mariya komanso za mwana wosabadwayo. Mwina iwo anadzifunsa kuti, bwanji ngati nthawi yobeleka yakwana pamene tikali paulendowu? Nkhawa yawo inali yomveka cifukwa mwana wobadwayo anali kudzakhala Mesiya wolonjezedwa na Yehova. Kodi zifukwa zimenezi zinawacititsa kuti asamvele lamulo la boma?

12 Yosefe na Mariya sanalole kuti zimenezo ziwalepheletse kutsatila lamulo la boma. Yehova anawadalitsa cifukwa ca kumvela kwawo. Mariya anafika bwino ku Betelehemu, anabeleka mwana wathanzi, ndipo anathandiza kukwanilitsa ulosi wa m’Baibo.—Mika 5:2.

13. Kodi kukhala kwathu omvela kungakhudze bwanji abale athu?

13 Kumvela akulu-akulu a boma kumatipindulila ife eni komanso anthu ena. Motani? Mwa zina, timapewa cilango cobwele cifukwa cosamvela malamulo. (Aroma 13:4) Kumvela kwathu kungakhudze mmene akulu-akulu a boma amaonela gulu lonse la Mboni za Yehova. Mwacitsanzo, zaka zambili kumbuyoku, asilikali ku Nigeria analoŵa mu Nyumba ya Ufumu misonkhano ili mkati. Iwo anali kufuna-funa anthu amene anali kucita zionetselo cifukwa cosafuna kulipila misonkho ina yake. Mkulu wa asilikali anauza asilikaliwo kuti “tiyeni ticoke, Mboni za Yehova zimalipila misonkho nthawi zonse.” Mukamamvela malamulo, mumathandiza kukometsela mbili ya Mboni za Yehova—ndipo zimenezi zikhoza kudzathandiza abale na alongo m’tsogolo.—Mat. 5:16.

14. N’ciyani cinathandiza mlongo wina kukhala ‘wokonzeka kumvela’ olamulila akulu-akulu?

14 Ngakhale n’telo, si nthawi zonse pamene tingafune kumvela olamulila akulu-akulu. Joanna wa ku America anati, “Sicinali copepuka kwa ine kukhala womvela, cifukwa ena mwa a m’banja mwathu anacitidwapo zinthu zopanda cilungamo.” Koma Joanna anacitapo kanthu kuti asinthe kaganizidwe kake. Coyamba, iye anasiya kuŵelenga nkhani za pa soshomidiya zimene zimakamba zoipa pa akulu-akulu a boma. (Miy. 20:3) Caciŵili, anapemphela kwa Yehova kuti am’thandize kuika cidalilo cake mwa iye, m’malo modalila maulamulilo a anthu. (Sal. 9:​9, 10) Cacitatu, anaŵelenga zofalitsa zathu zimene zikamba pa kusakhalila mbali m’zandale. (Yoh. 17:16) Joanna anati “tsopano nili na mtendele cifukwa cakuti nimalemekeza komanso kumvela akulu-akulu a boma.”

MUZITSATILA CITSOGOZO CA GULU LA YEHOVA

15. N’cifukwa ciyani nthawi zina zingativute kutsatila citsogozo cocokela ku gulu la Yehova?

15 Yehova akutipempha kuti “muzimvela amene akutsogolela” mu m’mpingo. (Aheb. 13:17) Mtsogoleli wathu Yesu, ni wangwilo. Koma anthu amene akuseŵenzetsa kuti atitsogolele pano padziko lapansi, ni opanda ungwilo. Cingakhale covuta kuwamvela maka-maka ngati atipempha kucita zinthu zimene sitifuna. Panthawi ina, mtumwi Petulo sanafune kutsatila malangizo amene anapatsidwa. Mngelo atamuuza kuti adye nyama zimene zinali zoletsedwa malinga na Cilamulo ca Mose, mtumwi Petulo anakana—osati kamodzi, koma katutu konse! (Mac. 10:​9-16) Cifukwa ciyani? Cifukwa sanawakonde malangizo atsopano amenewo, iye anali atazoloŵela kacitidwe kakale ka zinthu. Ngati zinali zovuta kwa Petulo kutsatila citsogozo ca mngelo wangwilo, ndiye kuti zingakhale zovutilapo kwa ife kutsatila citsogozo ca anthu opanda ungwilo.

16. Kodi mtumwi Paulo anatani atalandila citsogozo cimene mwina anaona kuti n’cosathandiza? (Mac. 21:​23, 24, 26)

16 Mtumwi Paulo anali ‘wokonzeka kumvela’ ngakhale pamene anapatsidwa citsogoza cimene cinaoneka ngati cosathandiza. Akhristu aciyuda anamva mphekesela zakuti mtumwi Paulo anali kuphunzitsa anthu kuti “apandukila Cilamulo ca Mose,” komanso kuti asamacilemekeze. (Mac. 21:21) Akhristu acikulile ku Yerusalemu, anauza Paulo kuti atenge amuna anayi na kupita nawo ku kacisi kuti akadziyeletse malinga na mwambo poonetse kuti anali kusunga Cilamulo ca Mose. Ngakhale kuti Paulo anali kudziŵa kuti Akhristu sanalinso pansi pa Cilamulo ca Mose, ndipo sanalakwitse ciliconse, iye sanazengeleze kutsatila citsogozo cimeneco. Iye “anatenga amunawo tsiku lotsatila ndi kukacita mwambo wa kudziyeletsa pamodzi ndi iwo.” (Ŵelengani Machitidwe 21:​23, 24, 26.) Kumvela kwa Paulo kunalimbikitsa mgwilizano pakati pa abale.—Aroma 14:​19, 21.

17. Kodi mwaphunzila ciyani ku cocitika ca Stephanie?

17 Cinali covuta kwa mlongo wina dzina lake Stephanie kutsatila citsogozo cimene amuna audindo m’dziko lake anaika. Iye na mwamuna wake anali kusangalala kutumikila m’kagulu ka cinenelo cina. Posakhalitsa ofesi ya nthambi inatseka kaguluko, ndipo inapempha banjali kuti libwelele ku mpingo wa cinenelo cawo. Mlongo Stephanie anati “sin’nakondwele na citsogozoci, cifukwa sin’naganize kuti mpingo wa cinenelo cathu unali kufunikila thandizo.” Ngakhale n’telo, iye anatsatilabe citsogozoco. Pambuyo pake anati, “N’naona ubwino wa citsogozo cimeneci, tinakhala makolo auzimu kwa ambili amene makolo awo si Mboni. Nimaphunzila na mlongo wina amene anali wozilala, ndipo nili na nthawi yambili yocita phunzila la ine mwini. Nili na cikumbumtima coyela podziŵa kuti nacita zonse zotheka kuti nikhale womvela kwa amene akutsogolela.”

18. Kodi timapindula motani tikakhala omvela?

18 Tingaphunzile kukhala omvela. Yesu “anaphunzila kumvela cifukwa ca mavuto amene anakumana nawo.” (Aheb. 5:8) Mofanana na Yesu, ifenso timaphunzila kumvela m’mikhalidwe yovuta. Mwacitsanzo, mlili wa COVID-19 utayamba, kodi zinali zovuta kwa inu kutsatila citsogozo cakuti tileke kusonkhana pa Nyumba ya Ufumu na kuleka ulaliki wa khomo na khomo? Kumvela kwanu kunakutetezani, kunakuthandizani kukhala ogwilizana na alambili anzanu, ndipo munakondweletsa Yehova. Tsopano tonsefe ndife okonzeka kutsatila citsogozo ciliconse cimene tidzalandila pa cisautso cacikulu. Kupulumuka kwanu kudzadalila pamenepo.—Yobu 36:11.

19. N’cifukwa ciyani mufuna kukhala omvela?

19 Taphunzila kuti kukhala omvela kumabweletsa madalitso oculuka. Koma cifukwa cacikulu cimene timamvela Yehova n’cakuti timamukonda ndipo timafuma kum’kondweletsa. (1 Yoh. 5:3) Sitingakwanitse kumubwezela Yehova pa zonse zimene anaticila. (Sal. 116:12) Koma n’zothekha kumumvela, komanso awo ali na ulamulila pa ife. Tikakhala omvela, timaonetsa kuti ndife anzelu. Ndipo anthu anzelu amakondweletsa mtima wa Yehova.—Miy. 27:11.

N’CIYANI CINGATILIMBIKITSE KUMVELA . . .

  • makolo athu ngati ndife acicepele?

  • “olamulila akulu-akulu”?

  • citsogozo ca gulu la Yehova?

NYIMBO 89 Mvela Udalitsidwe

a Pokhala anthu opanda ungwilo, nthawi zina zimativuta kutsatila malangizo ngakhale kuti amene akupeleka malangizowo ali na udindo wocita zimenezo. Nkhani ino ifotokoza mapindu amene amabwela kwa awo amene amamvela makolo awo, “olamulila akulu-akulu,” komanso abale amene akutsogolela mu mpingo wacikhristu.

b Kuti mupeze malangizo othandiza a mmene mungakambile na makolo anu pa malamulo amene muona kuti ni ovuta kuwatsatila, onani nkhani yakuti “Kodi Ndingakambirane Bwanji ndi Makolo Anga za Malamulo Amene Anakhazikitsa?” pa jw.org ku chichewa.

c MAU OFOTOKOZELA CITHUNZI: Yosefe na Mariya anamvela lamulo la Kaisara lopita ku Betelehemu kukalembetsa m’kaundula. Akhristu masiku ano amamvela malamulo a pa msewu, okhudza msonkho komanso a zaumoyo oikidwa na “olamulila akulu-akulu.”

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani