NYIMBO 44
Pemphelo la Munthu Wovutika
Yopulinta
(Salimo 4:1)
1. Yehova, nipempha mvelani pemphelo langa.
Nkhawa zanga zanivutitsa; nithandizeni.
Navutika mu maganizo ndipo nafo’ka.
O Yehova nipempha; conde munisamale.
(KOLASI)
N’thandizeni kupilila.
Nkhawa zanga zicotseni.
Nikafo’ka na mavuto
Yehova nilimbitseni.
2. Mau anu amanitonthoza nikafo’ka,
Niyamikila moti siningafotokoze.
N’thandizeni kudziŵa kuti mumanikonda.
Nikhulupilila kuti mudzanithandiza.
(KOLASI)
N’thandizeni kupilila.
Nkhawa zanga zicotseni.
Nikafo’ka na mavuto
Yehova nilimbitseni.
(Onaninso Sal. 42:6; 119:28; Aroma 8:26; 2 Akor. 4:16; 1 Yoh. 3:20.)