NYIMBO 94
Tiyamikila Mau a Mulungu
Yopulinta
(Afilipi 2:16)
1. Tikuyamikani Atate wathu,
Cifukwa mwatipatsa Mau anu.
Amatitsogolela atipatsa nzelu.
Coonadi cake catimasula.
2. Mau anu M’lungu, ali na mphamvu.
Akhudza zolinga za mtima wathu.
Mfundo zanu, Yehova, zitipatsa nzelu.
Zititsogolela m’zocita zathu.
3. Mau anu M’lungu, atithandiza.
Kuphunzila kwa aneneli anu.
Conde tithandizeni tikhale olimba.
Tikuyamikani Mulungu wathu.
(Onaninso Sal. 19:9; 119:16, 162; 2 Tim. 3:16; Yak. 5:17; 2 Pet. 1:21.)