LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w15 3/15 masa. 7-11
  • “Munavomeleza Kuti Zimenezi Zicitike”

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • “Munavomeleza Kuti Zimenezi Zicitike”
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • KUFOTOKOZA MFUNDO ZOZAMA ZA COONADI KWA ONSE
  • KUFOTOKOZA NKHANI ZA M’BAIBULO MOMVEKA BWINO
  • KUFOTOKOZA MOMVEKA BWINO MAFANIZO A YESU
  • Kodi Mumacita Zinthu Mogwilizana ndi Cilungamo ca Yehova?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
  • Mfumukazi Yoipa Inalangiwa
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Yezebeli—mfumukazi Yoipa
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
w15 3/15 masa. 7-11
Yesu akumwetulila kwambili pamene ophunzila ake 70 akubwelako ali ndi cimwemwe cacikulu, ndipo akufotokoza zimene zawacitikila mu ulaliki. Koma alembi ndi afarisi akung’ung’uza ca munsimunsi

“Munavomeleza Kuti Zimenezi Zicitike”

“Zinthu izi mwazibisa kwa anzelu ndi ozama m’maphunzilo, koma mwaziulula kwa tiana.”—LUKA 10:21.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • Ndi zitsanzo ziti zamakono zimene zionetsa kuti Yehova amavomeleza ziphunzitso zomveka bwino?

  • Kodi tasintha bwanji mmene timafotokozela nkhani za Baibulo m’kupita kwa nthawi?

  • Kodi kamvedwe kathu pa mafanizo a Yesu kasintha bwanji?

1. N’cifukwa ciani Yesu “anakondwela kwambili mwa mzimu woyela? (Onani cithunzi cili pamwamba.)

GANIZILANI mmene mukanamvelela kuona Yesu Kristu ‘akukondwela kwambili mwa mzimu woyela.’ Mwina anali kumwetulila kwambili ndipo nkhope yake inali kuoneka yowala ndi cimwemwe. N’ciani cimene cinam’cititsa kukhala ndi cimwemwe? Iye anali atangotumiza ophunzila ake 70 kukalalikila uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Panali adani amphamvu ambili a uthenga wa ufumu, koma Yesu anali kufunitsitsa kudziŵa kuti ophunzilawo adzakwanitsa bwanji kugwila nchitoyo. Adani amenewa anali alembi ndi Afalitsi amene anali ophunzila kwambili ndi anzelu. Iwo anali kusonkhezela anthu kuti aziona Yesu monga kalipentala wamba ndiponso ophunzila ake monga “osaphunzila ndiponso anthu wamba.” (Mac. 4:13; Maliko 6:3) Ngakhale zinali conco, ophunzila ake anabwelako ali ndi cisangalalo cacikulu. Iwo anali atalalikila ngakhale kuti anatsutsidwa ndi anthu komanso ziwanda. N’ciani cinawathandiza kukhalabe ndi cimwemwe ndiponso olimba mtima?—Ŵelengani Luka 10:1, 17-21.

2. (a) Kodi otsatila a Yesu anali monga ana m’njila yotani? (b) N’ciani cinathandiza otsatila a Yesu kumvetsa coonadi cofunika?

2 Yesu anauza Yehova kuti: “Ndikutamanda inu Atate pamaso pa onse, Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi, cifukwa mwabisila zinthu zimenezi anthu anzelu ndi ozindikila ndipo mwaziulula kwa tiana. Inde Atate wanga, ndikukutamandani cifukwa inu munavomeleza kuti zimenezi zicitike.” (Mat. 11:25, 26) N’cifukwa ciani Yesu anacha ophunzila ake kuti tiana? Cifukwa cakuti mosiyana ndi alembi ndi Afalitsi amene anali ophunzila kwambili ndi kuziona kuti ndi anzelu, ophunzila a Yesu anali ofunitsitsa kuphunzitsidwa monga ana. Iwo anali odzicepetsa, osati odzitukumula. (Mat. 18:1-4) Cifukwa ca kudzicepetsa kwao, Yehova anawathandiza kumvetsa zinthu zozama za m’Baibulo mwa mzimu wake woyela. Koma atsogoleli acipembedzo aciyuda onyada anacititsidwabe khungu ndi Satana komanso cifukwa ca mzimu wao wonyada.

3. Tidzakambilana ciani m’nkhani ino?

3 Mpake kuti Yesu anali wosangalala. Anasangalala kuona mmene Yehova anali kuvumbulila coonadi ca m’Baibulo kwa anthu odzicepetsa ngakhale kuti anali osaphunzila. Iye anasangalala kuti Atate wake anavomeleza kaphunzitsidwe kameneko. Kodi Yehova anasintha? Nanga amaonetsa bwanji kuti akali kuvomeleza kaphunzitsidwe kameneka? Pamene tikambilana mayankho a mafunso amenewa, ifenso tidzakhala osangalala monga Yesu.

KUFOTOKOZA MFUNDO ZOZAMA ZA COONADI KWA ONSE

4. Kodi Nsanja ya Mlonda yokhala ndi cingelezi cosavuta yakhala mphatso m’njila yotani?

4 M’zaka za posacedwapa, gulu la Yehova lakhala likupeleka malangizo akuuzimu osavuta ndi omveka bwino. Tiyeni tikambilane zitsanzo zitatu. Coyamba tili ndi Nsanja ya Mlonda imene imalembedwa m’cingelezi cosavuta.a Imeneyi yakhala mphatso yabwino kwa anthu amene amavutika kuŵelenga kapena kumvetsetsa cingelezi. Mitu yabanja yambili yaona kuti kugwilitsila nchito magazini yokhala ndi cingelezi cosavuta imeneyi kwathandiza ana ao kuti azimvetsetsa kwambili Nsanja ya Mlonda. Ambili a io alemba makalata oyamikila cifukwa cokhala ndi Nsanja ya Mlonda imeneyi. Mlongo wina anakamba kuti anali kucita mantha kuyankhapo pa phunzilo la Nsanja ya Mlonda. Koma panopa sakucitanso mantha. Atayamba kugwilitsila nchito Nsanja ya Mlonda yokhala ndi cingelezi cosavuta kumva, iye analemba kuti: “Panopa ndimayankhapo maulendo angapo, ndipo mantha anathelatu. Ndikuyamikila kwambili Yehova komanso inuyo.”

5. Kodi Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika lokonzedwanso la cingelezi ndi labwino motani?

5 Caciŵili, tili ndi Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika lacingelezi lokonzedwanso limene linatulutsidwa pa October 5, 2013, pa msonkhano wapacaka.b Panopa, malemba ambili ali ndi mau ocepa kuposa kale, koma matanthauzo ake sanasinthe, ndipo ndi osavuta kumvetsa. Mwacitsanzo, mogwilizana ndi Baibulo lacingelezi, lemba la Yobu 10:1 linali ndi mau 27 m’Baibulo lakale, koma tsopano lili ndi mau 19 okha. Ndipo lemba la Miyambo 8:6 linali ndi mau 20 m’Baibulo lakale, koma tsopano lili ndi mau 13 okha. Mavesi onse aŵiliwa, ndi omveka bwino m’Baibulo lokonzedwanso kuposa m’lakale. M’bale wina wodzozedwa amene watumikila mokhulupilika kwa zaka zambili anati: “Ndangomaliza kumene kuŵelenga buku la Yobu m’Baibulo lokonzedwanso, ndipo ndikuona kuti kwa nthawi yoyamba, ndi pamene ndalimvetsetsa.” Anthu ena akambanso zofanana ndi mfundo imeneyi.

6. Kodi mukumva bwanji kukhala ndi kamvedwe katsopano kokhudza lemba la Mateyu 24:45-47?

6 Cacitatu, taganizilani ponena za kusintha kwa kamvedwe pa mfundo za coonadi kumene kwacitika posacedwapa. Mwacitsanzo, tinasangalala kukhala ndi kamvedwe katsopano ponena za “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu,” mogwilizana ndi nkhani imene inafalitsidwa mu Nsanja ya Mlonda ya July 1, 2013. (Mat. 24:45-47) Nkhaniyo inafotokoza kuti kapolo wokhulupilika ndi Bungwe Lolamulila, ndipo “anchito ake apakhomo” ndi anthu onse amene amadyetsedwa mwakuuzimu, kaya ndi odzozedwa kapena a “nkhosa zina.” (Yoh. 10:16) N’zosangalatsa kwambili kuphunzila mfundo za coonadi zimenezi komanso kuziphunzitsa kwa atsopano. Kodi Yehova waonetsanso bwanji kuti amavomeleza kuphunzitsa m’njila yosavuta ndi yomveka bwino?

KUFOTOKOZA NKHANI ZA M’BAIBULO MOMVEKA BWINO

7, 8. Ndi zitsanzo ziti zoonetsa nkhani zina zokhudza ulosi zimene zili m’Baibulo?

7 Ngati mwakhala mukutumikila Yehova kwa zaka zambili, mwina mwaona kuti pakhala kusintha mmene zofalitsa zathu zakhala zikufotozela zocitika zina za m’Baibulo. Kale, tinali kukonda kukamba kuti nkhani zina zinali kuimila zinthu zazikulu zimene zinali kudzacitika mtsogolo. Kodi pali zifukwa zabwino zofotokozela nkhani za m’Baibulo mwa njila imeneyi? Inde zilipo. Mwacitsanzo, Yesu anakamba za “cizindikilo ca mneneli Yona.” (Ŵelengani Mateyu 12:39, 40) Yesu anakamba kuti nthawi imene Yona anali m’mimba mwa nsomba, inali kuimila nthawi imene Yesu adzakhala m’manda.

8 M’Baibulo, mulinso nkhani zina zimene zimaimila zinthu zazikulu zodzacitika mtsogolo. Mtumwi Paulo anafotokoza zina mwa nkhanizo. Mwacitsanzo, pangano la ukwati lomwe linali pakati pa Abulahamu, Hagara ndi Sara, linali kuimila pangano la Yehova ndi mtundu wa Isiraeli komanso mbali yakumwamba ya gulu la Mulungu. (Agal. 4:22-26) Mofananamo, cihema, kacisi, Tsiku la Mwambo Wophimba Macimo, mkulu wansembe, komanso mbali zina za Cilamulo ca Mose, zinali ‘mthunzi cabe wa zinthu zabwino zimene zinali kubwela.’ (Aheb. 9:23-25; 10:1) Zimakhala zocititsa cidwi ndi zolimbitsa cikhulupililo kuphunzila nkhani zokhudza ulosi zimenezi. Koma kodi zimenezi zitanthauza kuti munthu aliyense, cocitika ciliconse, ndi cinthu ciliconse cofotokozedwa m’Baibulo, zimaimila winawake kapena cinacake?

9. Kodi nkhani ya m’Baibulo yokhudza Naboti inali kufotokozedwa bwanji m’nthawi zakale?

9 Kale, zofalitsa zathu zinali kufotokoza kuti munthu aliyense, cocitika ciliconse, ndi cinthu ciliconse m’nkhani zopezeka m’Baibulo, zinali kuimila winawake kapena cinacake. Mwacitsanzo, Mfumukazi yoipa Yezebeli, inalamula kuti Naboti aphedwe kotelo kuti Ahabu mwamuna wake atenge munda wa mpesa wa Naboti. (1 Maf. 21:1-16) Nsanja ya Mlonda yacingelezi ya mu 1932, inafotokoza kuti Ahabu ndi Yezebeli anali kuimila Satana ndi gulu lake, ndi kuti Naboti anali kuimila Yesu, ndipo imfa yake inali kuimila kuphedwa kwa Yesu. Komabe m’kupita kwa nthawi, buku lochedwa “Let Your Name Be Sanctified,” limene linafalitsidwa mu 1961, linati Naboti anali kuimila odzozedwa, ndipo Yezebeli anali kuimila Machalichi Acikristu. Linafotokozanso kuti kunzunzidwa kwa Naboti kumene Yezebeli anacititsa kunali kuimila kunzunzidwa kwa odzozedwa m’masiku otsiliza. Kwa zaka zambili, anthu a Mulungu anali kuona kuti kufotokoza nkhani za Baibulo mwa njila imeneyi kunali kolimbitsa cikhulupililo. Nanga n’cifukwa ciani zinthu zasinthanso?

10. (a) Kodi kapolo wokhulupilika waonetsa bwanji kuti ali maso kwambili pofotokoza nkhani zina za m’Baibulo? (b) Kodi zofalitsa zathu zimafotokoza kwambili pa ciani masiku ano?

10 Kwa zaka zambili, Yehova wathandiza “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu” kukhala wanzelu kwambili, kapena kukhala maso. Kodi wacita zimenezi mwa njila yotani? Pofuna kufotokoza kuti nkhani inayake ya m’Baibulo imaimila cinacake, kapolo wokhulupilika masiku ano amaonetsetsa kuti pali umboni womveka bwino wa m’Malemba. Komanso anthu ambili sanali kumvetsetsa kafotokozedwe kakale kokhudza zocitika za m’Baibulo ndi zinthu zimene zinali kuimila mtsogolo. Zofalitsa zathu zinali kufotokoza kwambili tanthauzo la ulosi wa m’Baibulo. Zimenezo zinali kuphimba kwambili mfundo zothandiza zofunika kuphunzilapo pa nkhanizo. Conco, masiku ano, zofalitsa zathu zimafotokoza kwambili mfundo zothandiza ndi zomveka bwino zimene zingalimbitse cikhulupililo, kutithandiza kupilila, kukhala odzipeleka kwa Mulungu, ndiponso makhalidwe ena ofunika amene tingaphunzile m’nkhani za m’Baibulo.c

Mfumu Ahabu akamba ndi Naboti m’munda wa mpesa

Citsanzo ca Naboti cimatiphunzitsa mfundo yofunika kwambili (Onani ndime 11)

11. (a) Kodi nkhani ya Naboti timaimvetsetsa bwanji masiku ano? Nanga citsanzo cake ndi cothandiza bwanji? (b) N’cifukwa ciani zofalitsa zathu sizifotokoza kwambili zocitika za m’Baibulo ndi zimene zimaimila masiku ano? (Onani nkhani yakuti “Mafunso Ocokela kwa Aŵelengi” m’magazini ino.)

11 Nkhani ya Naboti timaimvetsa bwino kwambili masiku ano. Imfa ya Naboti sinali kuimila imfa ya Yesu kapena odzozedwa. Naboti anaphedwa cifukwa cakuti anali wotsimikiza mtima kukhalabe wokhulupilika kwa Mulungu. Iye anakhalabe wokhulupilika ku Cilamulo ca Yehova mosasamala kanthu kuti olamulila ankhanza anamuzunza kwambili. (Num. 36:7; 1 Maf. 21:3) Citsanzo cake n’cothandiza kwa ife cifukwa cakuti aliyense wa ife angazunzidwe cifukwa ca kukhala wokhulupilika. (Ŵelengani 2 Timoteyo 3:12.) Akristu onse angathe kumvetsa nkhaniyi, kuikumbukila, kuigwilitsila nchito pa umoyo wao ndi kulimbitsa cikhulupililo cao.

12. (a) Tiyenela kupewa kuganiza ciani ponena za nkhani za m’Baibulo? (b) N’cifukwa ciani timatha kumvetsa kafotokozedwe komveka bwino ka zinthu zozama? (Onani mau amunsi.)

12 Kodi tingakambe kuti nkhani za m’Baibulo zimakhala ndi mfundo zothandiza cabe, ndipo zilibe matanthauzo ena? Iyai. M’malo mofotokoza cabe zocitika za m’Baibulo ndi zimene zimaimila, zofalitsa zathu masiku ano zimafotokoza mmene nkhani ina ya m’Baibulo imagwilizanilana ndi inzake. Mwacitsanzo, Naboti anakhalabe wokhulupilika ngakhale kuti anazunzidwa ndi kuphedwa. Nkhani imeneyi imatikumbutsa za kukhulupilika kwa Kristu ndi odzozedwa. Imatikumbutsanso za kukhulupilika kwa anthu ambili a “nkhosa zina.” Tikhoza kuona kuti Yehova amatiphunzitsa mwa njila yosavuta kumva.d

KUFOTOKOZA MOMVEKA BWINO MAFANIZO A YESU

13. Ndi zitsanzo ziti zimene zikuonetsa kuti panopa tingathe kufotokoza mafanizo a Yesu momveka bwino?

13 Yesu Kristu anali Mphunzitsi wamkulu woposa onse amene anakhalapo padziko lapansi. Iye anali kukonda kwambili kugwilitsila nchito mafanizo pophunzitsa. (Mat. 13:34) Mafanizo amagwila mtima, ndipo mfundo zake zimakhudza mtima mosavuta. Kwa zaka zambili, zofalitsa zathu zakhala zikufotokoza mafanizo a Yesu mwa njila yomveka bwino. Mwacitsanzo, Nsanja ya Olonda ya July 15, 2008 inatithandiza kumvetsa bwino mafanizo a Yesu okhudza cofufumitsa, kambeu ka mpilu, ndi khoka. Panopa tikudziŵa kuti mafanizo amenewa amanena za Ufumu wa Mulungu, umene wathandiza anthu ambili kukana dziko loipali ndi kukhala ophunzila a Kristu.

14. (a) Kodi fanizo la Msamariya wacifundo tinali kulifotokoza bwanji? (b) Nanga fanizoli timalimva bwanji masiku ano?

14 Nanga bwanji ponena za mafanizo ena amene Yesu anafotokoza mwatsatanetsatane? Mafanizo ena amaphiphilitsila zinazake ndipo amakhala ulosi, koma ena amatsindika mfundo inayake yofunika. Nanga tingadziŵe bwanji kuti fanizo ili likuphiphilitsila cina cake kapena ai? M’kupita kwa nthawi, yankho lake lakhala loonekela bwino. Mwacitsanzo, taganizani mmene tinali kufotokozela fanizo la Yesu lokhudza Msamariya wacifundo. (Luka 10:30-37) Magazini ya The Watch Tower ya mu 1924, inati Msamariyayo anali kuimila Yesu, mseu wocokela ku Yerusalemu kupita ku Yeriko, umene unali wotsetseleka, unali kuimila makhalidwe a anthu amene akhala akuipilaipila kuyambila pa cipanduko ca mu Edeni. Acifwamba amene anakumana nao pa njila anali kuimila mabungwe akuluakulu komanso amalonda adyela, ndipo wansembe ndi Mlevi anali kuimila machalichi acikristu. Koma masiku ano, zofalitsa zathu zimagwilitsila nchito fanizoli pokumbutsa Akristu onse kuti ayenela kupewa tsankho. Tiyenela kuthandiza anthu onse ovutika, makamaka kuwaphuzitsa coonadi conena za Mulungu. N’zosangalatsa kwambili kuona mmene Yehova akumveketsela bwino coonadi.

15. Kodi tidzakambilana ciani m’nkhani yotsatila?

15 M’nkhani yathu yotsatila, tidzaphunzila za fanizo lina la Yesu lokhudza anamwali 10. (Mat. 25:1-13) Kodi Yesu anafuna kuti ophunzila ake m’masiku otsiliza azilimva bwanji fanizo logwila mtima limeneli? Kodi munthu aliyense, cinthu ciliconse, ndi cocitika ciliconse m’fanizoli, cimaimila cinacake codzacitika mtsogolo? Kapena kodi anali kufuna kutiphunzitsa zinthu zinazake zimene zingakhale zothandiza m’masiku otsiliza ano? Tiona zimenezi m’nkhani yotsatila.

a Nsanja ya Mlonda yokhala ndi cingelezi cosavuta inayamba kufalitsidwa mu July 2011. Pambuyo pake, magaziniwa afalitsidwanso m’zinenelo zina.

b Palinso makonzedwe oti Baibulo lokonzedwanso liyambe kupezeka m’zinenelo zinanso.

c Mwacitsanzo, buku lakuti Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo limafotokoza bwino kwambili za anthu 14 ochulidwa m’Baibulo. Buku limeneli limafotokoza zimene tingaphunzile kwa io, osati ponena za zimene nkhanizo zimaimila.

d Mau a Mulungu alinso ndi mfundo zimene zingaoneke “zovuta kuzimvetsa,” kuphatikizapo mbali zina zimene Paulo analemba. Komabe, onse amene analemba Baibulo anatsogoleledwa ndi mzimu woyela. Masiku ano, mzimu wa Mulungu umathandizanso Akristu oona kumvetsetsa Baibulo, “ngakhale zinthu zozama za Mulungu.”—2 Pet. 3:16, 17; 1 Akor. 2:10.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani