LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • g19 na. 2 masa. 14-15
  • Kufunika kwa Makhalidwe Abwino

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kufunika kwa Makhalidwe Abwino
  • Galamuka!—2019
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • KODI ANTHU A MAKHALIDWE ABWINO AMACITA MOTANI?
  • N’CIFUKWA CIANI MAKHALIDWE ABWINO ALI OFUNIKA?
  • MMENE MUNGAPHUNZITSILE ANA MAKHALIDWE ABWINO
  • 7 Makhalidwe
    Galamuka!—2018
  • Mmene Ambili Amasankhila Zocita
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila) —2024
  • Tonsefe Timafuna Malangizo Odalilika
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila) —2024
  • Nthawi Imene Makhalidwe Analowa Pansi Kwambili
    Galamuka!—2007
Galamuka!—2019
g19 na. 2 masa. 14-15
Kamtsikana kaona amayi ake abwezela mzimayi cikwama ca ndalama cimene cataika

PHUNZILO 6

Kufunika Kwa Makhalidwe Abwino

KODI ANTHU A MAKHALIDWE ABWINO AMACITA MOTANI?

Anthu a makhalidwe abwino, amasiyanitsa mosavuta cabwino na coipa. Pofuna kusiyanitsa cabwino na coipa, iwo sayendela maganizo awo apanthawiyo. Amayendela mfundo zabwino zowathandiza pa zimene afuna kucita, ngakhale pamene ali kwa okha.

N’CIFUKWA CIANI MAKHALIDWE ABWINO ALI OFUNIKA?

Ana amamvetsela maganizo osiyana-siyana opotoza makhalidwe abwino. Angamvetsele zimenezi kwa anzawo ku sukulu, m’nyimbo, m’mafilimu na m’mapulogilamu a pa TV amene amatamba. Ndipo izi zingapangitse ana amenewa kuyamba kukaikila zimene anaphunzitsidwa za cabwino na coipa.

Imeneyi imakhala vuto yaikulu maka-maka kwa ana azaka pakati pa 13 na 19. Buku lakuti Beyond the Big Talk limakamba kuti pa zaka zimenezi, acicepele amenewa “afunika kudziŵa kuti anthu ambili adzawatuntha kucita zinthu m’njila ina yake kuti ena aziwakonda. Ndiponso afunika kuti azicita zinthu zimene adziŵa kuti n’zoyenela, olo kuti anzawo asagwilizane nazo.” Mwacionekele, ana afunika kuphunzitsidwa na makolo awo, akalibe kufika zaka zosinkhukila.

MMENE MUNGAPHUNZITSILE ANA MAKHALIDWE ABWINO

Khazikitsani mfundo za makhalidwe abwino.

MFUNDO YA M’BAIBO: ‘Anthu okhwima anaphunzitsa mphamvu zawo za kuzindikila, kusiyanitsa coyenela ndi cosayenela.’—Aheberi 5:14.

  • Muzikamba mawu osiyanitsa cabwino na coipa. Muziseŵenzetsa zocitika za tsiku na tsiku, pothandiza mwana wanu kusiyanitsa cabwino na coipa. Mungamuuze kuti: “Uku ni kuona mtima. Uku si kuona mtima.” “Uku ndiye kukhulupilika. Uku si kukhulupilika.” “Uku ni kukoma mtima. Uku si kukoma mtima.” M’kupita kwa nthawi, mwana wanu adzadziŵa kucita zabwino na kupewa kucita zoipa.

  • Afotokozeleni zifukwa zimene munakhazikitsila mfundo zimenezo. Mwacitsanzo, mungafunse mafunso monga akuti: N’cifukwa ciani kuona mtima n’kwabwino? Kodi kunama bodza kungawononge bwanji maubwenzi? N’cifukwa ciani kuba n’koipa? Thandizani mwana wanu kuphunzitsa cikumbumtima cake kusiyanitsa cabwino na coipa.

    Gogomezani mapindu a kukhala na mfundo za makhalidwe abwino. Mungauze mwana wanu kuti: “Ngati ukhala oona mtima, anthu adzayamba kukudalila.” Mungamuuzenso kuti: “Ngati ukhala wokoma mtima, anthu adzakukonda.”

Banja lanu lizidziŵika na makhalidwe abwino amene munakhazikitsa.

MFUNDO YA M’BAIBO: “Pitilizani kudziyesa kuti mudziwe kuti ndinu munthu wotani.”—2 Akorinto 13:5.

  • Banja lanu lizidziŵika na makhalidwe abwino amene munakhazikitsa, kuti muzikamba mosakaikila kuti:

    • “M’banja mwathu sitikamba mabodza.”

    • “Ise siticita ndewo, kapena kukalipila anthu.”

    • “Ise sititukwana.”

Mwana wanu adzadziŵa kuti mfundo zimene munakhazikitsa si malamulo cabe iyayi, koma ni mfundo zimene mufuna kuti banja lanu lizidziŵika nazo.

  • Muzikambilana kaŵili-kaŵili na mwana wanu za makhalidwe abwino a banja lanu. Seŵenzetsani zocitika za tsiku na tsiku pophunzitsa mwana wanu makhalidwe amenewo. Mungayelekezele makhalidwe amene banja lanu limalimbikitsa, na makhalidwe amene amalimbikitsidwa pa TV kapena ku sukulu. Funsani mwana wanu mafunso monga aya: “Kodi iwe ukanacita bwanji apa?” “Nanga banja lathu likanacita bwanji apa?”

Alimbikitseni kukhala na makhalidwe abwino.

MFUNDO YA M’BAIBO: “Khalani ndi cikumbumtima cabwino.”—1 Petulo 3:16.

  • Yamikilani mwana wanu pa zimene wacita bwino. Ngati mwana wanu aonetsa makhalidwe abwino m’zimene acita, muyamikileni na kumuuza cifukwa cake wacita bwino. Mwacitsanzo, mungamuuze kuti: “Wacita zinthu moona mtima. Ndipo wanikondweletsa.” Komanso ngati wakuululilani kuti wacita cinthu cina coipa, muyamikileni coyamba mocokela pansi pa mtima pa kuona mtima kwake, mukalibe kumuwongolela.

  • Muwongoleleni akalakwitsa. Thandizani ana anu kuvomeleza zotulukapo za zocita zawo. Ana ayenela kudziŵa cimene alakwitsa, na kuwafotokozela mmene khalidwe lawo lasiyanilana na makhalidwe a banja lanu. Makolo ena amaopa kuuza ana awo kuti alakwa, cifukwa safuna kuti awakhumudwitse. Koma ngati muuza mwana wanu zimene walakwa, ndiye kuti mum’thandiza kuphunzitsa cikumbumtima cake, kuti azisiyanitsa mosavuta cabwino na coipa.

Kamtsikana kaona amayi ake abwezela mzimayi cikwama ca ndalama cimene cataika

APHUNZITSENI AKALI AANG’ONO

Ngati ana aona kuti makolo awo amacita zinthu moona mtima, nawonso amacita cimodzi-modzi ngakhale pamene ali kwa okha.

Aphunzitseni mwa Citsanzo Canu

  • Kodi ana anga amaona, mwa zocita na zokamba zanga, kuti nimatsatila mfundo za makhalidwe abwino zimene tinakhazikitsa monga banja?

  • Kodi ine na mnzanga wa m’cikwati timalimbikitsa makhalidwe amenewa?

  • Kodi nimapeleka zifukwa zodzikhululukila nikaphwanya mfundo zimene tinakhazikitsa, mwa kukamba kapena kuganiza kuti, “Izi zilibe vuto kwa ise akulu-akulu”?

Zimene Makolo Ena Anacita . . .

“Tinali kuuza ana athu mapindu amene anthu ena anapeza cifukwa cokhala na makhalidwe abwino. Tinali kuŵauzanso za mavuto amene anthu ena anakumana nawo, cifukwa copanga zosankha zopanda nzelu. Ana athu akatiuza za mnzawo amene anapanga cosankha coipa, tinali kukambilana nawo kuti iwo asakacite zimenezo.”—Nicole.

“Pamene mwana wathu wamkazi anali wamng’ono, tinali kumuuza kuti mu umoyo wake ali na zosankha ziŵili. Cina cabwino, cina coipa. Ndipo tinali kumufotokozela zotulukapo za cosankha ciliconse cimene angapange. Kucita izi kunam’phunzitsa kupanga zosankha. Kum’phunzitsa zimenezi kunali kofunika cifukwa munthu aliyense mu umoyo amafunika kupanga zosankha panthawi ina, olo akhale wamkulu bwanji.”—Yolanda.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani