LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • g21 na. 2 masa. 13-15
  • Kodi Zipangizo Zamakono Zimakhudza Bwanji Luso Lanu Lophunzila Zinthu?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Zipangizo Zamakono Zimakhudza Bwanji Luso Lanu Lophunzila Zinthu?
  • Galamuka!—2021
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • ZIMENE MUYENELA KUDZIŴA
  • ZIMENE MUNGACITE
  • Za M’kope Ino
    Galamuka!—2021
  • Mawu Oyamba
    Galamuka!—2021
  • Kodi Zipangizo Zamakono Zimakhudza Bwanji Cikwati Canu?
    Galamuka!—2021
  • Kodi Zipangizo Zamakono Zimakhudza Bwanji Ubwenzi Wanu na Ena?
    Galamuka!—2021
Onaninso Zina
Galamuka!—2021
g21 na. 2 masa. 13-15
Munthu akutamba vidiyo pamene akuphika.

Kodi Zipangizo Zamakono Zimakhudza Bwanji Luso Lanu Lophunzila Zinthu?

Anthu amafuna kuphunzila zinthu zambili, kaya za kusukulu, za kunchito, kapena zinthu zina. Ndipo zipangizo zamakono zingawathandize. Kuposa kale lonse, tsopano n’zosavuta anthu kuphunzila zinthu zambili ali kunyumba kwawo, ngakhale ali phee pampando.

Komabe, ambili amene amakonda kuseŵenzetsa kwambili zipangizo zamakono, amakhala na mavuto monga . . .

  • kulephela kuika maganizo awo pa zimene akuŵelenga.

  • kulephela kuika maganizo pa cinthu cimodzi.

  • kusungulumwa mwamsanga akakhala paokha.

ZIMENE MUYENELA KUDZIŴA

Mtsikana akucita zinthu zingapo pa nthawi imodzi. Akulembela mnzake meseji pa foni, akuceza na mnzake pa vidiyo, komanso akuseŵenzetsa kompyuta na buku pamene akuŵelenga.

KUŴELENGA

Anthu amene amakonda kuseŵenzetsa zipangizo zamakono, nthawi zina amangoŵelenga nkhani mwapatali-patali kapena mothamanga, moti sakwanitsa kumvetsa mfundo yaikulu ya nkhaniyo.

Kuŵelenga mothamanga kumathandiza ngati mufuna kupeza yankho mwamsanga pa funso linalake. Koma kuŵelenga kotelo si kwabwino ngati nkhani imene mukuŵelenga mufuna kuimvetsetsa.

ZOYENELA KUZIGANIZILA: Kodi mumakwanitsa kuŵelenga nkhani yaitali mosamala? Nanga kucita zimenezi kungakuthandizeni bwanji pophunzila zinthu?—MIYAMBO 18:15.

KUIKA MAGANIZO PA CINTHU CIMODZI

Anthu ena amaganiza kuti zipangizo zamakono zingawathandize kucita zinthu ziŵili pa nthawi imodzi—mwacitsanzo, kulembela meseji bwenzi lawo kwinaku akuŵelenga. Koma popeza kuti maganizo awo amakhala ogaŵikana, sangacite bwino zonse ziŵili makamaka ngati zonse zifuna kuikilapo mtima.

Kuika maganizo pa cinthu cimodzi cimene mukucita kungakhale kovuta, koma kumathandiza kuti muphunzile zinthu. Mtsikana wina dzina lake Grace anati: “Sulakwitsa zinthu zambili komanso supanikizika maganizo kwambili. Naphunzila kuti ni bwino kuika maganizo anga pa cinthu cimodzi na kupewa kuceutsidwa na zinthu zina.”

ZOYENELA KUZIGANIZILA: Kodi mumalephela kumvetsetsa na kukumbukila zimene mwaŵelenga cifukwa coyesa kucita zinthu zingapo pa nthawi imodzi?—MIYAMBO 17:24.

PAMENE MULI NOKHA

Anthu ena samvela bwino kukhala okha pamalo a zii, ndipo amayamba kuseŵenzetsa zipangizo zawo pofuna kudzisangulutsa. Mzimayi wina dzina lake Olivia anati: “Cimanivuta kungokhala phee kwa mphindi 15 popanda kugwila foni yanga, kapena tabuleti, kapenanso kuyatsa TV.”

Komabe, nthawi imene munthu ali yekha, imam’patsa mwayi wosinkhasinkha, ndipo kusinkhasinkha n’kofunika kwambili kuti munthu aphunzile zinthu, kaya ni mwana kapena wamkulu.

ZOYENELA KUZIGANIZILA: Pamene muli nokha, kodi mumakwanitsa kuseŵenzetsa mpata umenewo posinkhasinkha?—1 TIMOTEYO 4:15

ZIMENE MUNGACITE

PENDANI MMENE MUMASEŴENZETSELA ZIPANGIZO ZAMAKONO

Kodi mungaseŵenzetse bwanji zipangizo zamakono kuti zikuthandizeni pophunzila zinthu? Kodi kuseŵenzetsa zipangizo zamakono kungakulepheletseni bwanji kuganizila zinthu mozama pophunzila?

MFUNDO YA M’BAIBO: “Usunge nzelu zopindulitsa ndiponso kuganiza bwino.”—MIYAMBO 3:21.

DZIFUNSENI KUTI . . .

  • Nikamaŵelenga nkhani yaitali pa cipangizo, kodi nimalephela kuikabe maganizo pa zimene nikuŵelenga? Ngati n’conco, n’ciani cimapangitsa zimenezo nthawi zambili?

  • Ni zinthu ziti zimene ningacite kuti nicepetse kapena kuthetselatu vuto loceutsidwa na zinthu zina pamene niŵelenga?

Yesani izi: Yambani mwa kuŵelenga ndime zocepa cabe, ndiyeno pang’ono-m’pang’ono muziwonjezela zoŵelenga. Muziŵelenga mokweza komanso modekha kuti maganizo anu akhalebe pa zimene mukuŵelengazo.

  • Ningasinthe zinthu ziti kuti nizikhala na nthawi yokwanila yoganizila mozama zimene naŵelenga?

Yesani izi: Pamene muŵelenga, seŵenzetsani mphindi 10 zothela pobwelelamo m’zimene mwaphunzila.

  • Ni panthawi iti pamene nimaceutsidwa mosavuta na zinthu zina nikamaŵelenga?

  • Ni zinthu ziti zimene ningasinthe kuti nisamavutike kuika maganizo pa cinthu cimodzi?

Yesani izi: Musanayambe kuŵelenga, cotsani ciliconse cimene muona kuti cingakulepheleni kuikabe maganizo pa zimene mukuŵelengazo.

MFUNDO YA M’BAIBO: “Upeze nzelu, upezenso luso lomvetsa zinthu.”—MIYAMBO 4:5.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani