LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • g23 na. 1 masa. 3-5
  • Madzi Abwino

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Madzi Abwino
  • Galamuka!—2023
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • Zimene Zikupangitsa Kuti Madzi Abwino Acepekele
  • Dziko Lapansi Analipanga Kuti Likhalepo Kwamuyaya
  • Kodi Anthu Akucitapo Ciyani?
  • Kodi Baibo Imatipatsa Ciyembekezo Cotani pa Nkhaniyi?
  • Kodi Baibo Imatipo Ciyani pa Vuto la Madzi Padziko Lonse?
    Nkhani Zina
Galamuka!—2023
g23 na. 1 masa. 3-5
Mzimayi akuseŵeletsa madzi abwino a mu mtsinje.

KODI DZIKO LAPANSI LIDZAPULUMUKA?

MADZI ABWINO

UMOYO padziko lapansi sukanakhala wotheka popanda madzi, maka-maka madzi abwino. Ndi iko komwe, mbali yaikulu m’matupi a zamoyo zonse ni madzi. Nyanja, mitsinje, madambo, komanso madzi apansi zimapeleka madzi akumwa kwa anthu na nyama, komanso kuti tithilile zomela.

Zimene Zikupangitsa Kuti Madzi Abwino Acepekele

Mbali yaikulu padziko lapansi ni madzi. Ngakhale n’conco, malinga na bungwe la padziko lonse loona za nyengo (World Meteorological Organization), “madzi abwino amene tingaseŵenzetse padziko lapansi ni ocepa kwambili.” Ngakhale kuti madzi abwino pamlingo wocepawu ni okwanila ku zamoyo zonse padziko, madziwa akuwonongedwa ndipo akhala ovuta kupeza cifukwa ca kusintha kwa nyengo, komanso cifukwa ciŵelengelo ca anthu cikuculukila-culukila. Akatswili amanena kuti m’zaka 30 zikubwela, anthu 5 biliyoni angakhale opanda madzi abwino okwanila.

Dziko Lapansi Analipanga Kuti Likhalepo Kwamuyaya

Dziko lapansi linapangidwa m’njila yakuti madzi padziko asathe. Dothi, zamoyo za m’madzi, komanso dzuwa zimagwilila nchito limodzi poyeletsa madzi. Onani umboni woonetsa kuti dziko lapansi linapangidwa kuti likhalepo kwamuyaya.

  • Zadziŵika kuti dothi lingayeletse madzi ku zoipa zambili. Ku madambo kumapezeka zomela zina zimene zimacotsa makemiko oipa m’madzi, monga nitrogen, phosphorus, na mankhwala ophela tudoyo.

  • Asayansi apeza njila zacilengedwe zimene zimayeletsa madzi owonongedwa na zinyalala. Madzi akamayenda, zinyalala zimasungunuka na kudyedwa na tuzilombo tung’ono-tung’ono.

  • Nkhono zopezeka m’madzi abwino zochedwa clam na mussel, m’masiku ocepa cabe zingacotse makemiko oipa m’madzi—ndipo zingacite zimenezi mwina kuposa njila zimene anthu amaseŵenzetsa poyeletsa madzi.

  • Pogwilitsa nchito zungulile-zungulile wa madzi, dziko lapansi limatha kusunga madzi. Zungulile wa madzi ameneyu na njila zina zacilengedwe zimathandiza kuti madzi asathe padziko.

    KODI MUDZIŴA?

    Dothi—Sefa Yacilengedwe Yoyeletsa Madzi

    Dothi limasefa madzi amene amayenda pansi mwa kucotsako tuzidutswa twazitsulo, makemiko apoizoni, zinyalala na zodetsa zina. Pa nthawi imene madzi amafika pokhazikika pa miyala ya pansi, angakhale abwino kumwa.

    Cithunzi coonetsa mmene dothi limayeletsela madzi. Madzi amvula akuloŵa pang’ono-pang’ono m’dothi, komanso m’miyala mpaka atafika pa madzi abwino a pansi.

    Sefa ya Mcenga na Miyala

    Mcenga na miyala nazonso zili ngati sefa, zimacotsa zinthu zoipitsa madzi.

    Sefa ya Tuzilombo

    Tuzilombo tung’ono-tung’ono twa m’dothi tumacepetsako mphamvu ya zinthu zapoizoni zopezeka m’dothi. Tuzilombo twina tumakwanitsa kusintha mafuta apoizoni kukhala mpweya wa carbon dioxide komanso kukhala madzi.

    Sefa ya Makemiko

    Mu dothi muli makemiko abwino omwe amasefa madzi pocotsamo makemiko oipa monga ammonium.

Kodi Anthu Akucitapo Ciyani?

Zithunzi: 1. Mwamuna akukonza galimoto yake kuti isamathonye mafuta. Ndipo akuseŵenzetsa ka dishi kuti mafuta asathonyele pansi. 2. Mwamuna wapeleka mabotolo a makemiko ku sitolo la otaya zinyalala.

Mwa kukonza magalimoto athu kuti asamathonye mafuta na kusamala mmene timatayila zinthu zapoizoni, timathandiza kuti madzi azikhala aukhondo

Akatswili amatilimbikitsa kuseŵenzetsa bwino madzi. Kuti ticepetseko kuwononga madzi, amatilimbikitsa kukonza magalimoto athu kuti asamathonye mafuta, komanso kuti tisamataye makhwala kapena kuthila poizoni m’matoileti.

Akatswili apeza njila yamakono yocotsela mcele m’madzi kuti akhale abwino. Colinga n’cakuti pakhale madzi abwino ambili.

Koma akufunika kucita zoposa pamenepa. Njila yocotsela mcele m’madzi ni yosathandiza kwenikweni cifukwa ni yodula kwambili ndiponso imaseŵenzetsa magetsi oculuka. Lipoti la bungwe la United Nations la mu 2021, lokamba za kasamalidwe ka madzi linati: “Padziko lonse, tiyenela kuwonjezela zimene tikucita pali pano posamalila madzi.”

Kodi Baibo Imatipatsa Ciyembekezo Cotani pa Nkhaniyi?

“Mulungu . . . amakoka madontho a madzi. Madonthowo amasefeka n’kutsika ngati mvula ndi nkhungu, moti mitambo imakha, imakhetsa madzi oculuka pa anthu.”—Yobu 36:​26-28.

Mulungu analenga zungulile-zungulile wa madzi kuti ateteze madzi a padziko lapansi.—Mlaliki 1:7.

Ganizilani izi: Ngati Mlengi ndiye anapanga njila zoyeletsela madzi abwino, kodi si pomveka kuganiza kuti amafuna ndipo angakwanitse kucotsapo mavuto a madzi obwela cifukwa ca zocita za anthu? Onani nkhani yakuti “Mulungu Analonjeza Kuti Dziko Lapansi Lidzakhalapo Kwamuyaya,” patsamba 15.

DZIŴANI ZAMBILI

Tuzigawo twa madzi pa maikulosikopu.

Madzi amathandizila kuti moyo ukhale wotheka. Tambani vidiyo yacingelezi yakuti The Wonders of Creation Reveal God’s Glory—Water pa jw.org.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani