LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lv nkhani 222-nkhani 223 pala. 3
  • Kuthetsa Mikangano Pankhani Zamalonda

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kuthetsa Mikangano Pankhani Zamalonda
  • “Khalanibe m’Cikondi ca Mulungu”
  • Nkhani Zofanana
  • Kusunga Mtendele na Ciyelo ca Mpingo
    Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova
  • Inu Akulu—Pitilizani Kutsanzila Mtumwi Paulo
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2022
“Khalanibe m’Cikondi ca Mulungu”
lv nkhani 222-nkhani 223 pala. 3

ZAKUMAPETO

Kuthetsa Mikangano Pankhani Zamalonda

Pa lemba la 1 Akorinto 6:1-8, mtumwi Paulo anakamba za milandu ya pakati pa abale. Iye anakhumudwa cifukwa cakuti Akristu ena a ku Korinto anali ‘kulimba mtima . . . kupita kukhoti kwa anthu osalungama.’ (Vesi 1) Paulo anapeleka zifukwa zomveka zimene Akristu sayenela kupelekela Akristu anzao kukhoti, koma kuthetsa milandu yao mumpingo. Tsopano tiyeni tikambilane zifukwa zina zimene Paulo anapelekela malangizo ouzilidwa amenewa, kenako tidzaona zocitika zina zimene sizikhudzidwa kwenikweni ndi malangizowa.

Ngati takangana ndi Mkristu mnzathu pa zamalonda, coyamba tiyenela kuyesetsa kuthetsa nkhaniyo mwa kutsatila malangizo a Yehova, osati mwa nzelu zathu. (Miyambo 14:12) Monga mmene Yesu anaonetsela, zili bwino kuthetsa nkhani mwamsanga isanakhale mlandu waukulu. (Mateyu 5:23-26) Koma n’zacisoni kuti Akristu ena amakangana kwambili cakuti amapelekana kukhoti. Paulo anakamba kuti: “Ndiye kuti mwalephelelatu ngati mukutengelana kukhoti.” N’cifukwa ciani anatelo? Cifukwa cacikulu n’cakuti, mlandu wotelo ungaipitse mbili ya mpingo ndi dzina la Mulungu amene timalambila. Conco, tiyenela kuganizila funso la Paulo lakuti: “Bwanji osangolola kulakwilidwa?—Vesi 7.

Paulo anafotokozanso kuti Mulungu anakhazikitsa dongosolo labwino lothetsela mikangano mumpingo. Akulu acikristu ndi amuna anzelu cifukwa amadziŵa coonadi ca m’Baibulo, ndipo Paulo ananena kuti io “angaweluze mlandu pakati pa abale” pa “nkhani za m’moyo uno.” (Mavesi 3-5) Yesu anaonetsa kuti milandu yaikulu monga misece ndi cinyengo iyenela kuthetsedwa mwa kutsatila malangizo atatu awa: Coyamba, yesani kuthetsa nkhaniyo panokha ndi amene munalakwilana naye, caciŵili, ngati njila yoyamba imeneyi yalepheleka, tengani munthu mmodzi kapena aŵili kuti akhale mboni, ndipo cacitatu, ngati zimenezo sizinathandize, uzani akulu mumpingo.—Mateyu 18:15-17.

Komabe, akulu si maloya kapena anthu amalonda, ndipo si udindo wao kupeleka malangizo pa nkhani zamalamulo kapena zamalonda. Iwo sakhazikitsa malangizo othetsela mikangano ya zamalonda pakati pa abale. Koma amafuna kuthandiza onse okhudzidwa ndi nkhaniyo kugwilitsila nchito Malemba kuti athetse nkhaniyo mwamtendele. Pa nkhani zovuta kwambili, io angafunse malangizo kwa woyang’anila dela kapena ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova. Koma pali zocitika zina zimene sizikhudzidwa kwenikweni ndi malangizo a Paulo. Kodi zinthu zimenezi ndi ziti?

Nthawi zina, kupita kukhoti kungakhale dongosolo lake losamalila nkhaniyo kapena njila ya lamulo yosadyelana masuku pamutu ndi yothetsela mikangano mwamtendele. Mwacitsanzo, kupita kukhoti ingakhale njila yokha yothetsela cikwati mwalamulo kapena yopezela cilolezo cotenga ana cikwati cikatha. Ndipo mwina ndi kukhoti cabe kumene angakuuzeni kuculuka kwa ndalama zimene mwamuna ayenela kulipila mkazi wake cikwati cikatha, kapena kumene mungapezele cilolezo colandila ndalama za inshuwalansi. Kungakhalenso kukhoti kumene munthu angathandizidwile kulandila ndalama zake kampani ikatsekedwa, ndipo ndi kumene angasainitse wilo mwalamulo. Ndiponso m’bale angagulile saimoni anthu amene anamutengela kukhoti kuti adziteteze pa mlandu wake.a

Ngati tipita kukhoti pamilandu yotelo popanda mzimu wamkangano, sikuti tasemphana ndi malangizo ouzilidwa a Paulo.b Ngakhale zili conco, Mkristu ayenela kuona kuti cinthu cofunika kwambili ndi kuyeletsa dzina la Yehova ndi kukhala amtendele ndi ogwilizana mumpingo. Cinthu cacikulu cimene cimadziŵikitsa otsatila a Kristu ndi cikondi cao, ndipo “cikondi . . . sicisamala zofuna zake zokha.”—1 Akorinto 13:4, 5; Yohane 13:34, 35.

a Nthawi zina, Mkristu angacitile Mkristu mnzake colakwa cacikulu monga kugona naye mwacikakamizo, kumumenya, kumupha, kapena kumubela zinthu. Zotelo zikacitika, sikulakwa kupeleka nkhaniyo kupolisi ngakhale kuti kucita zimenezo kungapangitse kuti nkhaniyo ikafike kukhoti.

b Kuti mudziŵe zambili, onani Nsanja Ya Olonda ya March 15, 1997, patsamba 17 mpaka 22, ndi ya October 15, 1991, patsamba 25 mpaka 28.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani