PHUNZILO 11
Zimene Mungacite Kuti Muzipindula Kwambili Poŵelenga Baibo
Kodi munadodomapo kuti muyambe kucita nchito inayake yaikulu? Kuti ioneke yopepukako, mwina munaigaŵa m’mbali zing’ono-zing’ono zimene zingagwilike mosavuta. N’cimodzimodzinso na kuŵelenga Baibo. Mungadzifunse kuti, ‘Kodi ningayambe bwanji?’ M’phunzilo lino, tikufotokozelani zinthu zosavuta zimene mungacite kuti muzisangalala poŵelenga Baibo panokha.
1. N’cifukwa ciyani tiyenela kuŵelenga Baibo nthawi zonse?
Munthu amene amaŵelenga Baibo nthawi zonse, kapena kuti “cilamulo ca Yehova,” amakhala wosangalala komanso zinthu zimamuyendela bwino. (Ŵelengani Salimo 1:1-3.) Monga poyambila, yesani kuŵelenga Baibo kwa mphindi zocepa tsiku lililonse. Pamene mukuwazolowela Mawu a Mulungu, cisangalalo canu coŵelenga Baibo cizikulilako-kulilako.
2. Cingakuthandizeni n’ciyani kuti muzipindula poŵelenga Baibo?
Kuti kuŵelenga Baibo kuzikupindulilani kwambili, muyenela kumaima na kuganizila pa zimene mukuŵelenga. Muzicita zinthu ziŵili, kuŵelenga na “kusinkhasinkha.” (Yoswa 1:8) Poŵelenga, muzidzifunsa mafunso monga akuti: ‘Kodi izi ziniuza ciyani za Yehova Mulungu? Kodi ningaziseŵenzetse bwanji mu umoyo wanga? Nanga mavesi awa ningawagwilitse nchito bwanji pothandiza anthu ena?’
3. Kodi mungapatule bwanji nthawi yoŵelenga Baibo?
Kodi cimakuvutani kupeza nthawi yoŵelenga Baibo? Ambili cimativuta. Muziyesetsa ‘kugwilitsa nchito bwino nthawi yanu.’ (Aefeso 5:16) Mungacite zimenezi mwa kukhazikitsa nthawi yoŵelenga Baibo tsiku na tsiku. Anthu ena amapatula nthawi yoŵelenga Baibo m’mamaŵa tsiku lililonse. Ena amasankha nthawi ina monga popuma masana. Ndiponso ena amaŵelenga Baibo usiku asanagone. Nanga inu, ni nthawi iti ingakukomeleni?
KUMBANI MOZAMILAPO
Dziŵani mocitila kuti muzisangalala nako kuŵelenga Baibo. Onani mmene mungamakonzekelele bwino kuti muzipindula kwambili pa phunzilo lanu la Baibo.
Monga mmene tingaphunzilile kukonda zakudya zosiyana-siyana, tingaphunzilenso
4. Dziŵani mocitila kuti muzikondwela nako kuŵelenga Baibo
Kuyamba kuiŵelenga Baibo kungakhale kovutilapo. Komabe, monga mmene munthu angayambile kukonda cakudya cacilendo, ifenso tingayambe ‘kulakalaka” kuŵelenga Baibo. Ŵelengani 1 Petulo 2:2, na kukambilana funso ili:
Kodi muganiza n’zothekadi kuti mukayamba kuŵelenga Baibo tsiku na tsiku, mungayambe kukondwela nayo cakuti n’kufika pomalakalaka kuiŵelenga?
Tambani VIDIYO kuti muone mmene anthu ena anayambila kukondwela nayo Baibo. Pambuyo pake kambilanani mafunso aya.
Mu vidiyo iyi, kodi ni zopinga zotani zimene acicepele anathana nazo?
Nanga n’ciyani cinawathandiza kuti asasiye colinga cawo coŵelenga Baibo?
Anacita ciyani kuti kuŵelenga Baibo kuziwakondweletsa?
Njila za mmene mungayambile:
Sankhani Baibo yodalilika, yomasulidwa m’cinenelo camakono. Yesani Baibulo la Dziko Latsopano ngati lilipo m’cinenelo canu.
Coyamba ŵelengani mbali zimene mungakonde kwambili. Kuti musankhe, onani chati yakuti “Pamene Mungayambile Kuŵelenga Baibo.”
Congani zimene mwaŵelenga. Seŵenzetsani chati yakuti “Congani Mbali Zimene Mwaŵelenga” imene ili m’buku lino.
Seŵenzetsani app ya JW Library®. Pa app imeneyi, mungaŵelenge Baibo, kapena kuimvetsela m’cinenelo cimene mumamva, kulikonse kumene muli, pa foni kapena zipangizo zotelo.
Gwilitsilani nchito zakumapeto mu Baibulo la Dziko Latsopano. Mudzapezako zokuthandizani poŵelenga, monga mamapu, machati, komanso mndandanda wa mawu.
5. Konzekelani phunzilo lanu la Baibo
Ŵelengani Salimo 119:34, na kukambilana funso ili:
N’cifukwa ciyani ni bwino kupemphela pofuna kuyamba kuŵelenga Baibo kapena kukonzekela phunzilo la Baibo?
Kodi mungacite ciyani kuti muzipindula kwambili pa phunzilo lililonse? Pokonzekela phunzilo lililonse yesani ndondomeko iyi:
Ŵelengani ndime zoyambilila pa phunzilo lililonse.
Ŵelengani malembawo, na kuona kugwilizana kwake na nkhaniyo.
Congani mawu ofunika amene akuyankha funso lililonse; izi zidzakuthandizani pokambilana phunzilo limenelo na mphunzitsi wanu.
Kodi mudziŵa?
Mboni za Yehova zaseŵenzetsapo ma Baibo a zimasulilo zosiyana-siyana. Koma timakonda kwambili Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika cifukwa ni lolondola, n’losavuta kumva, ndipo limachula dzina la Mulungu.—Onani nkhani ya Pawebusaiti “Kodi a Mboni za Yehova Ali na Baibo Yawo-yawo?”
ANTHU ENA AMAKAMBA KUTI: “Kuphunzila Baibo ni nchito yaikulu kwambili. Nilibe nthawi ndipo nimakhala wolema.”
Nanga inu muona bwanji?
CIDULE CAKE
Kuti Baibo ikupindulileni kwambili, patulani nthawi yoiŵelenga, pemphelani kuti mumvetsetse zimene muŵelenge, ndipo muzikonzekela phunzilo lanu la Baibo.
Mafunso Obweleza
Kodi n’ciyani cingakuthandizeni kuti Baibo ikupindulileni kwambili?
Kodi mungapatule nthawi iti yoŵelenga Baibo na kuiphunzila?
N’cifukwa ciyani kuli kothandiza kumakonzekela phunzilo la Baibo?
FUFUZANI
Ŵelengani njila zimene zingakuthandizeni kupindula kwambili poŵelenga Baibo.
“Mungacite Ciani Kuti Mupindule na Zimene Muŵelenga m’Baibo?” (Nsanja ya Mlonda Na. 1 2017)
Dziŵani njila zitatu zoŵelengela Baibo.
“Kodi Baibo Inganithandize Bwanji?—Mbali 1: Idziŵeni Bwino Baibo” (Nkhani ya pawebusaiti)
Dziŵani mmene kuŵelenga Baibo kungakhalile kokondweletsa.
Funsilani njila zoŵelengela Baibo kwa aciyambakale pa kuŵelenga Baibo.