LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lff phunzilo 34
  • Kodi Tingaonetse Bwanji Kuti Yehova Timamukonda?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Tingaonetse Bwanji Kuti Yehova Timamukonda?
  • Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • KUMBANI MOZAMILAPO
  • CIDULE CAKE
  • FUFUZANI
  • Kodi Cikondi Cosasintha ca Yehova N’ciani?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2021
  • Mmene Mungakhalile Bwenzi La Mulungu
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
  • Cikondi Cokhulupilika Cimam’kondweletsa Yehova—Nanga Imwe?
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano —2017
  • Cikondi ca Mulungu Cokhulupilika Cidzakhalapo Mpaka Kale-kale
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
Onaninso Zina
Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
lff phunzilo 34
Phunzilo 34. Munthu uyu ali m’tauni, ndipo akulingalila atayang’ana kumwamba.

PHUNZILO 34

Kodi Tingaonetse Bwanji Kuti Yehova Timamukonda?

Yopulinta
Yopulinta
Yopulinta

Kucokela pamene munayamba kuphunzila Baibo, kodi muona kuti cikondi canu pa Yehova cikukula? Kodi mungakonde kupitiliza kulimbitsa ubwenzi wanu na iye? Ngati n’telo, kumbukilani kuti pamene Yehova akuona cikondi canu cikukula pa iye, adzakukondani kwambili na kukusamalilani. Koma mungaonetse bwanji kuti mumamukonda?

1. Kodi timamuonetsa bwanji Yehova kuti timamukonda?

Timaonetsa cikondi cathu kwa Yehova mwa kumumvela. (Ŵelengani 1 Yohane 5:3.) Iye sakakamiza munthu aliyense kumumvela. Amafuna munthu aliyense asankhe yekha kumumvela kapena kusamumvela. N’cifukwa ciyani amatelo? Cifukwa Yehova amafuna kuti tizimumvela “mocokela pansi pa mtima.” (Aroma 6:17) Kunena kwina, iye safuna kuti muzimumvela mokakamizika ayi, koma cifukwa cakuti mumamukonda. Zigawo 3 na 4 za buku lino, zidzakuthandizani mmene mungaonetsele cikondi canu kwa Yehova, pocita zimene zimamukondweletsa na kupewa zomukhumudwitsa.

2. N’cifukwa ciyani nthawi zina kungakhale kovuta kuonetsa cikondi cathu pa Yehova?

“Masoka a munthu wolungama ndi oculuka.” (Salimo 34:19) Tonsefe timalimbana na kupanda ungwilo kwathu. Timakhalanso na mavuto azacuma, kucitilidwa zosalungama, na mavuto ena ambili. Cifukwa ca zimenezi, kungakhale kovuta kucita zimene Yehova amafuna kwa ife. Koma kucita zimene Yehova amaletsa, ndiko kumakhala kosavuta. Mukakhulupilika kucita zimene Yehova amakuuzani, mumaonetsa kuti mumam’konda kuposa cinthu cina ciliconse. Umenewo ndiwo umboni wakuti ndinu wokhulupilikadi kwa iye. Mukatelo, iyenso adzakhalanso wokhulupilika kwa inu, ndipo sadzakusiyani konse.—Ŵelengani Salimo 4:3.

KUMBANI MOZAMILAPO

Onani cifukwa cake kukhala kwanu womvela ni nkhani yaikulu kwa Yehova. Ndipo dziŵani cimene cingakuthandizeni kukhalabe wokhulupilika kwa iye.

3. Nkhani imene inunso imakukhudzani

Buku la Yobu m’Baibo, lionetsa kuti Satana sananeneze Yobu yekha, ananenezanso anthu onse ofuna kutumikila Yehova. Ŵelengani Yobu 1:1, 6–2:10, na kukambilana mafunso aya:

  • Kodi Satana anakamba kuti Yobu amamvela Yehova cifukwa ciyani?—Onani Yobu 1:9-11.

  • Ndipo Satana anati ciyani ponena za anthu onse, kuphatikizapo inuyo?—Onani Yobu 2:4.

Ŵelengani Yobu 27:5b, na kukambilana funso ili:

  • Kodi Yobu anaonetsa bwanji kuti anali kukondadi Yehova?

Satana akutsutsa Yehova. Akukayikila kukhulupilika kwa Yobu amene ali na zilonda thupi lonse. Akukayikilanso kukhulupilika kwa mlongo amene akutumikila Yehova masiku ano.

Yobu anaonetsa kuti amakonda Yehova pokhalabe wokhulupilika kwa iye

Timaonetsa kuti Yehova timamukonda tikakhalabe wokhulupilika kwa iye

4. Kondweletsani mtima wa Yehova

Ŵelengani Miyambo 27:11, na kukambilana mafunso aya:

  • Kodi Yehova amamva bwanji mukamacita zinthu mwanzelu komanso kumumvela? Ndipo cifukwa ciyani?

5. Mungathe kukhala wokhulupilika kwa Yehova

Cifukwa Yehova timamukonda, timauzako ena za iye. Ngakhale zinthu zikhale zovuta, cikhulupililo cathu cimatilimbikitsa kuuzabe ena za iye. Tambani VIDIYO, kenako kambilanani mafunso otsatila.

VIDIYO: Tetezani Cikhulupililo Canu Pamene Mutsutsidwa (5:09)

  • Kodi nthawi zina zimakuvutani kuuzako ena za Yehova?

  • Mu vidiyo imene mwaona, kodi n’ciyani cinathandiza Grayson kuthetsa mantha ake?

Kukhala okhulupilika kwa Yehova n’kosavuta ngati tikonda zimene iyenso amakondwela nazo, na kuzonda zimene iye amadana nazo. Ŵelengani Salimo 97:10, na kukambilana mafunso aya:

  • Malinga na zimene mwaphunzila, kodi ni zinthu ziti zimene Yehova amakondwela nazo? Nanga ni zinthu ziti zimene amadana nazo?

  • Kodi cingakuthandizeni n’ciyani kuti muzikonda zabwino komanso kudana na zoipa?

6. Tikamvela Yehova timapindula

Kumvela Yehova ni kwanzelu nthawi zonse. Ŵelengani Yesaya 48:17, 18, na kukambilana mafunso aya:

  • Kodi muganiza n’zoona kuti Yehova amatifunila zabwino nthawi zonse? Mwayankha conco cifukwa ciyani?

  • Pofika pano, kodi kuphunzila kwanu Baibo komanso za Mulungu woona Yehova, kwakupindulilani motani?

ANTHU ENA AMAKAMBA KUTI: “Zocita zanga sizimukhudza kwenikweni Mulungu.”

  • Kodi mungamuŵelengele lemba liti pomuonetsa kuti zocita zathu zimamukhudza Yehova?

CIDULE CAKE

Ngakhale mukumane na mavuto otani, mungaonetse kuti Yehova mumamukonda pomumvela na kukhalabe wokhulupilika kwa iye.

Mafunso Obweleza

  • Kodi mwaphunzilapo ciyani pa citsanzo ca Yobu?

  • Kodi muyenela kucita ciyani poonetsa kuti Yehova mumamukonda?

  • Kodi n’ciyani cidzakuthandizani kukhalabe wokhulupilika kwa Yehova?

Colinga

FUFUZANI

Pezani mmene mungakhalile wokhulupilika kwa Yehova komanso ku mpingo.

“Munthu Wokhulupirika, Mudzamuchitira Mokhulupirika” 16:49

Onaninso zina zimene Satana amakamba zoneneza anthu.

“Yobu Anapitiriza Kutumikira Mulungu ndi Mtima Wosagawanika” (Kodi Baibulo Lili Ndi Uthenga Wotani? gawo 6)

Onani mmene ana aang’ono nawonso angaonetsele cikondi cawo pa Yehova.

Uzikondweletsa Yehova (8:16)

Kodi wacicepele amene akuvutitsidwa na anzake, angacite ciyani kuti akhalebe wokhulupilika kwa Mulungu?

Musagonje Anzanu Pokunyengelelani! (3:59)

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani