LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lff phunzilo 36
  • Khalani Woona Mtima pa Zinthu Zonse

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Khalani Woona Mtima pa Zinthu Zonse
  • Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • KUMBANI MOZAMILAPO
  • CIDULE CAKE
  • FUFUZANI
  • Khalani Oona Mtima M’zinthu Zonse
    Mmene Tingakhalilebe mu Cikondi ca Mulungu
  • Citani Zinthu Zonse Moona Mtima
    “Khalanibe m’Cikondi ca Mulungu”
  • Khalidwe Labwino Kwambili Kuposa Dayamondi
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2016
Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
lff phunzilo 36
Phunzilo 36. Munthu akusainila cikalata.

PHUNZILO 36

Khalani Woona Mtima pa Zinthu Zonse

Yopulinta
Yopulinta
Yopulinta

Munthu aliyense amafuna kukhala na mabwenzi oona mtima. Nayenso Yehova amafuna mabwenzi oona mtima. Koma imeneyi si nkhani yapafupi cifukwa anthu ambili m’dziko ni osaona mtima. Kodi pali mapindu otani tikamakhala oona mtima nthawi zonse?

1. Kodi cifukwa cacikulu cokhalila oona mtima n’ciyani?

Tikakhala oona mtima kwa ena, timaonetsa kuti timakonda Yehova na kumulemekeza. Tangoganizani: Yehova amadziŵa ciliconse cimene timaganiza kapena kucita. (Aheberi 4:13) Tikamacita zinthu moona mtima, iye amaona ndipo amakondwela nafe. Mawu ake amati: “Munthu wocita zaciphamaso Yehova amanyansidwa naye, koma amakonda anthu owongoka mtima.”—Miyambo 3:32.

2. Kodi tiyenela kukhala oona mtima m’mbali ziti pa umoyo wathu wa tsiku na tsiku?

Yehova amafuna kuti ‘tizilankhulana zoona zokha-zokha.’ (Zekariya 8:16, 17) Kodi zimenezi zimatanthauza ciyani? Zitanthauza kuti pokambilana na a m’banja mwathu, anzathu akunchito, abale na alongo acikhristu, kapena akulu-akulu a boma, sitiyenela kunama kapena kuwauza zimene sizoona. Anthu oona mtima sabela anthu ena, kapena kuwabela m’njila zacinyengo. (Ŵelengani Miyambo 24:28, komanso Aefeso 4:28.) Iwo amalipilanso misonkho yonse ku boma. (Aroma 13:5-7) M’mbali zimenezi komanso zina, tikufuna “kucita zinthu zonse moona mtima.”—Aheberi 13:18.

3. Kodi pali mapindu otani tikakhala oona mtima?

Tikadziŵika kukhala munthu woona mtima, anthu amatidalila. Tidzathandiza aliyense kudzimva wotetezeka mu mpingo monga banja lokondana. Komanso timakhala na cikumbumtima cabwino. Kuona mtima kwathu ‘kumakometselanso ciphunzitso ca mpulumutsi wathu, Mulungu.’ Ndiponso kumathandiza aja amene si mboni kufuna kum’tumikila Yehova.—Tito 2:10.

KUMBANI MOZAMILAPO

Onani mmene kuona mtima kwanu kumakhudzila Yehova komanso inu mwini. Ndipo dziŵani mmene mungakhalile woona mtima m’zocitika zosiyana-siyana pa umoyo wanu.

4. Mukakhala oona mtima mumam’kondweletsa Yehova

Ŵelengani Salimo 44:21, komanso Malaki 3:16, na kukambilana mafunso aya:

  • N’cifukwa ciyani n’kupanda nzelu kuganiza kuti tingabise coona?

  • Muganiza Yehova amamva bwanji tikanena zoona, ngakhale pamene n’covuta kucita zimenezo?

Mwana akambilana na tate wake amene wagwada kuti alingane naye. Tambula yagwa pathebulo cakumwaco n’kutayikila pansi.

Pamene ana akamba zoona amakondweletsa makolo awo. Ifenso tikamakamba zoona timakondweletsa Yehova

5. Citani zinthu moona mtima nthawi zonse

Anthu ambili amaganiza kuti n’zosatheka kukhala woona mtima nthawi zonse. Koma onani cifukwa cake n’kofunika kukhala woona mtima nthawi zonse. Tambani VIDIYO.

VIDIYO: Kodi N’ciani Cimabweletsa Cimwemwe?—Cikumbumtima Coyela (2:32)

Cocitika ca mu vidiyo yakuti ‘Kodi N’ciyani Cimabweletsa Cimwemwe?—Cikumbumtima Coyela.’ Ben atauza bwana wake kuti anacita colakwa cacikulu iwo akugwilana m’manja.

Ŵelengani Aheberi 13:18, na kukambilana mmene tingakhalile oona mtima . . .

  • kwa a m’banja mwathu.

  • kunchito kapena kusukulu.

  • pa zocitika zina.

6. Kuona mtima kumatipindulila

N’zoona kuti tingakumane na mavuto cifukwa cokhala oona mtima. Koma m’kupita kwa nthawi, imadzaoneka kuti ndiyo njila yabwino koposa yoitsatila. Ŵelengani Salimo 34:12-16, na kukambilana funso ili:

  • Kodi kuona mtima kumathandiza bwanji kuti umoyo wanu ukhale wabwino?

A. Mwamuna na mkazi wake akukambilana pamene akumwa khofi pamodzi. B. Makanika akuyamikilidwa na bwana wake mu galaji. C. Mwamuna ali m’motoka yake akuonetsa wapolisi citupa cake.
  1. Mwamuna na mkazi wake akakhala oona mtima, ukwati wawo umakhala wolimba

  2. Anchito oona mtima mabwana awo amawadalila

  3. Nzika za dziko zoona mtima zimakhala na mbili yabwino kwa akulu-akulu a boma

ANTHU ENA AMAKAMBA KUTI: “Tumabodza twina n’tothandiza, malinga tusaululike.”

  • Muganiza n’cifukwa ciyani Yehova amadana na bodza la mtundu uliwonse?

CIDULE CAKE

Yehova amafuna kuti mabwenzi ake azikhala oona mtima, m’zokamba zawo komanso m’zocita zawo zonse.

Mafunso Obweleza

  • Kodi tiyenela kukhala oona mtima pa mbali ziti?

  • N’cifukwa ciyani n’kupanda nzelu kuganiza kuti tingabise coona?

  • N’cifukwa ciyani muyenela kukhala oona mtima nthawi zonse?

Colinga

FUFUZANI

Kodi makolo angaphunzitse bwanji ana awo kukhala oona mtima?

Lankhulani Zoona (1:44)

Kodi timapindula bwanji tikamakwanilitsa malonjezo athu?

Kwanilitsani Malonjezo, Landilani Madalitso (9:09)

Onani ngati tiyenela kupelekabe misonkho ngakhale igwilitsidwe nchito molakwika.

“Kodi Muyenela Kukhoma Misonkho?” (Nsanja ya Mlonda, September 1, 2011)

N’ciyani cinalimbikitsa munthu wosaona mtima kusintha umoyo wake, na kuyamba kucita zinthu moona mtima?

“Ndinaphunzila Kuti Yehova ndi Wacifundo ndi Wokhululukila” (Nsanja ya Mlonda, May 1, 2015)

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani