LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lff phunzilo 38
  • Tiziiyamikila Mphatso ya Moyo

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Tiziiyamikila Mphatso ya Moyo
  • Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • KUMBANI MOZAMILAPO
  • CIDULE CAKE
  • FUFUZANI
  • Kodi Baibo Imati Ciyani pa Nkhani Yocotsa Mimba?
    Kuyankha Mafunso Okhudza Baibo
  • Kodi Mumaona Moyo Mmene Mulungu Amauonela?
    Mmene Tingakhalilebe mu Cikondi ca Mulungu
  • Kodi Mulungu Ali Nafe Colinga Canji?
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Kodi Imfa ya Yesu Ingatipulumutse Bwanji?
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
lff phunzilo 38
Phunzilo 38. Mwamuna na mkazi wake afungatila mwana wawo wakhanda.

PHUNZILO 38

Tiziiyamikila Mphatso ya Moyo

Yopulinta
Yopulinta
Yopulinta

Mu umoyo muli zinthu zokondweletsa zoculuka. Ngakhale tikumane na mavuto, pamakhalabe zinthu zosangalatsa zambili. Koma kodi tingaonetse bwanji kuti timayamikila mphatso ya moyo? Ndipo cifukwa cacikulu cocitila zimenezo n’ciyani?

1. N’cifukwa ciyani tiyenela kuyamikila kuti tili na moyo?

Tiyenela kuyamikila moyo umene tili nawo, cifukwa ni mphatso yocokela kwa Atate wathu wacikondi, Yehova. Iye ndiye “kasupe wa moyo,” kutanthauza kuti ndiye analenga zamoyo zonse. (Salimo 36:9) “Ndi iyeyo amene amapatsa anthu onse moyo, mpweya, ndi zinthu zonse.” (Machitidwe 17:25, 28) Yehova amatipatsa zonse zofunikila kuti tikhale na moyo. Koma sanasiyile pamenepo. Zinthu zimenezo amazipeleka zoculuka komanso zamitundu-mitundu kuti moyo tizikondwela nawo.—Ŵelengani Machitidwe 14:17.

2. Kodi tingamuonetse bwanji Yehova kuti mphatso ya moyo timaiyamikila?

Kucokela pa nthawi imene amayi anu anatenga pathupi panu, Yehova wakhala akukusamalilani. Davide, mmodzi wa alambili a Mulungu, anauza Mulungu kuti: “Maso anu anandiona pamene ndinali mluza.” (Salimo 139:16) Moyo wanu ni wamtengo wapatali kwa Yehova. (Ŵelengani Mateyu 10:29-31.) Yehova cimamuŵaŵa kwambili mumtima ngati munthu wina wapha munthu mnzake kapena kudzipha yekha.a (Ekisodo 20:13) Iye amakhumudwanso kwambili ngati mosasamala tiika moyo wathu paciopsezo, kapena kulephela kucita zofunikila kuti titeteze miyoyo ya anthu ena. Koma ngati moyo wathu timausamalila bwino, komanso tikamalemekeza miyoyo ya anthu ena, timaonetsa kuti timayamikila mphatso ya moyo umene tili nawo.

KUMBANI MOZAMILAPO

Onani njila zimene mungaonetsele kuti mphatso ya moyo wanu mumaiyamikila.

3. Samalilani thanzi lanu

Akhristu onse odzipatulila, amaonetsa kuti ni atumiki a Yehova mʼzocita zawo zonse pa umoyo wawo. Cili monga amapeleka matupi awo ngati nsembe kwa Mulungu. Ŵelengani Aroma 12:1, 2, na kukambilana mafunso aya:

  • N’ciyani ciyenela kukulimbikitsani kusamalila thanzi lanu?

  • Ndipo mungacite zimenezo m’njila ziti?

Mkazi wapathupi akambilana na dokotala wake.

4. Samalani kuti musaike anthu ena kapena inu mwini paciwopsezo

Baibo imatilangiza kuti tizipewa zinthu zimene zingavulaze anthu ena kapena kuika moyo wawo paciopsezo, ngakhalenso wa ife eni. Tambani VIDIYOYI kuti muone zinthu zimene mungacite pofuna kudziteteza.

VIDIYO: Yesetsani Kupewa Ngozi (8:34)

Ŵelengani Miyambo 22:3, kenako kambilanani mmene inuyo na anthu ena mungadzitetezele . . .

  • panyumba panu.

  • kumalo anu a nchito.

  • pocita zamaseŵelo.

  • poyendetsa motoka kapena mukakwela motoka.

Mwamuna akumanga lamba wa m’motoka.

5. Tizilemekeza moyo wa mwana ali m’mimba

Mzimayi agwila-gwila mimba yake.

M’mawu a ndakatulo, Davide anakamba za cidwi cimene Yehova ali naco pa mwana ali m’mimba na mmene amakulila. Ŵelengani Salimo 139:13-17, na kukambilana funso ili:

  • Kwa Yehova, kodi moyo wa munthu umayamba mimba ikangokhala, kapena pamene mwana wabadwa?

Yehova anapeleka malamulo kwa Aisiraeli akale oteteza mayi komanso mwana wake ali m’mimba. Ŵelengani Ekisodo 21:22, 23, na kukambilana mafunso aya:

  • Kodi Yehova anali kumuona bwanji munthu akapha mwana ali m’mimba mwangozi?

  • Kodi Mulungu anali kumva bwanji ngati munthu wacita zimenezo mwadala?b

  • Kodi mukugwilizana na maganizo a Yehova pa nkhani imeneyi?

Tambani VIDIYO.

VIDIYO: Muziona Moyo Mmene Mulungu Amauonela (5:00)

Ngakhale mkazi amene amayamikila mphatso ya moyo, nthawi zina angaone kuti kucotsa mimba ndiyo njila yokhayo yothandiza. Ŵelengani Yesaya 41:10, na kukambilana mafunso aya:

  • Ngati mkazi akuumilizidwa kuti acotse mimba, kodi ayenela kupempha thandizo kwa ndani? Ndipo cifukwa ciyani?

ANTHU ENA AMAKAMBA KUTI: “Nthawi zina n’koyenela mkazi kucotsa mimba cifukwa cokakamizidwa na mavuto ena.”

  • Kodi n’ciyani cimakupangitsani kukhulupilila kuti Yehova amaona moyo wa mayi komanso wa mwana wake ali m’mimba kukhala wamtengo wapatali?

CIDULE CAKE

Baibo imatiphunzitsa kuti moyo umene Yehova anatipatsa monga mphatso tiyenela kuukonda, kuulemekeza, komanso kuuteteza. Tiyenelanso kucita zimenezi ku miyoyo ya anthu ena.

Mafunso Obweleza

  • N’cifukwa ciyani moyo wa munthu ni wamtengo wapatali kwa Yehova?

  • Kodi Yehova amamva bwanji ngati munthu mwadala wacotsa moyo wake kapena moyo wa munthu wina?

  • Kodi mphatso ya moyo mumaiyamikila? Cifukwa ciyani?

Colinga

FUFUZANI

Kodi Yehova tingamuyamikile bwanji cifukwa ca mphatso ya moyo imene anatipatsa?

Nyimbo 141—Moyo ni Cozizwitsa (2:41)

Pezani yankho pa funso ili, Kodi Mulungu angam’khululukile mkazi amene anacotsapo mimba?

“Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani Yochotsa Mimba?” (Nkhani ya pawebusaiti)

Dziŵani mmene Mulungu amaonela moyo kuti muzisankha bwino zosangulutsa.

“‘Maseŵela Angozi’—Kodi Muyenela Kuika Moyo Wanu Paciswe Mwakuwacita?” (Galamuka!, October 8, 2000)

Bwanji ngati munthu ali na maganizo ofuna kudzipha? Onani mmene Baibo ingathandizile.

“Kodi Baibulo Lingandithandize Ngati Ndili ndi Maganizo Ofuna Kudzipha?” (Nkhani ya pawebusaiti)

a Anthu osweka mtima Yehova amasamala za iwo. (Salimo 34:18) Iye amamvetsa maganizo osautsa amene angapangitse munthu kufuna kudzipha, ndipo amafuna kuwathandiza anthu otelo. Kuti muone mmene iye amathandizila, ŵelengani nkhani yakuti “Kodi Baibulo Lingandithandize Ngati Ndili ndi Maganizo Ofuna Kudzipha?” pa mbali yakuti Fufuzani m’phunzilo lino.

b Awo amene anacotsapo mimba sayenela kuzunzika mumtima podziimba mlandu, Yehova angawakhululukile. Kuti mumve zambili onani nkhani yakuti, “Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani Yochotsa Mimba?” pa mbali yakuti Fufuzani m’phunzilo lino.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani