LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lff phunzilo 39
  • Mmene Mulungu Amawaonela Magazi

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mmene Mulungu Amawaonela Magazi
  • Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • KUMBANI MOZAMILAPO
  • CIDULE CAKE
  • FUFUZANI
  • Tuzigawo twa Magazi Ndiponso Njila Zimene Amatsatila Pocita Opaleshoni
    “Khalanibe m’Cikondi ca Mulungu”
  • Kodi Mumalemekeza Moyo Mmene Mulungu Amaulemekezela?
    “Khalanibe m’Cikondi ca Mulungu”
  • Kodi Mumaona Moyo Mmene Mulungu Amauonela?
    Mmene Tingakhalilebe mu Cikondi ca Mulungu
  • Mfundo za Kumapeto
    Mmene Tingakhalilebe mu Cikondi ca Mulungu
Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
lff phunzilo 39
Phunzilo 39. Mmene magazi amaonekela pa makina ochedwa microscope.

PHUNZILO 39

Mmene Mulungu Amawaonela Magazi

Yopulinta
Yopulinta
Yopulinta

Magazi ni cinthu cofunika kwambili. Palibe aliyense wa ife angakhale na moyo popanda magazi. Popeza Mulungu ndiye anatilenga, iye yekha ndiye ayenela kutiuza mmene tingagwilitsile nchito magazi. Kodi iye anakambapo ciyani za magazi? Kodi kudya magazi kapena kuikidwa magazi n’koyenela? Ndipo mungapange bwanji cisankho cabwino pa nkhani imeneyi?

1. Kodi Yehova amawaona bwanji magazi?

Mu nthawi zakale, Yehova anauza olambila ake kuti: “Moyo wa nyama iliyonse ndi magazi ake.” (Levitiko 17:14) Kwa Yehova, magazi amaimila moyo. Conco, popeza kuti moyo ni mphatso yocokela kwa Mulungu yopatulika komanso yoyela, magazi nawonso ni opatulika.

2. Kodi Mulungu anaika ciletso cotani pa magazi?

Mpingo wacikhristu usanakhazikitsidwe, Yehova analamula olambila ake kuti sayenela kudya magazi. (Ŵelengani Genesis 9:4 komanso Levitiko 17:10.) Pambuyo pakuti mpingo wacikhristu wakhazikitsidwa, Yehova anabwelezanso lamulo limeneli. Bungwe lolamulila linalangiza Akhristu “kupitiliza kupewa . . . magazi.”​—Ŵelengani Machitidwe 15:​28, 29.

Kodi kupewa magazi kumatanthauza ciyani? Ngati dokotala wakuuzani kupewa moŵa, mungaleke kumwa moŵa. Koma kodi mungayambe kudya zakudya zimene amaikamo moŵa, kapena mungalole kuikidwa moŵa m’thupi mwa kulasidwa nyeleti? Mwacidziŵikile simungalole zimenezo. Mofananamo, lamulo la Mulungu la kupewa magazi litanthauza kuti sitiyenela kudya magazi kapena kuwamwa m’njila iliyonse, kapena kudya nyama yosakhetsa. Ndiponso sitiyenela kudya cakudya ciliconse cimene aikako magazi.

Koma bwanji za kugwilitsa nchito magazi pa cithandizo ca mankhwala? N’zoonekelatu kuti njila zina zothandizila wodwala zimaphwanya lamulo la Mulungu. Njila zimenezi zimaphatikizapo kuika munthu magazi athunthu kapena iliyonse ya magawo akulu-akulu a magazi​—maselo ofiila, maselo oyela, maselo othandizila magazi kuundana, komanso madzi acikasu a m’magazi. Njila zina zothandizila odwala sitinganeneletu kuti zimaphwanya lamulo la Mulungu. Mwacitsanzo, pa njila zina zothandizila odwala amagwilitsila nchito tumagawo tung’ono-tung’ono twa magawo akulu-akulu a magazi. Pa njila zina amagwilitsila nchito magazi a munthu mwiniwakeyo. Poganizila njila zimenezi, aliyense wa ife ayenela kupanga cisankho ca iye mwini.a​—Agalatiya 6:5.

KUMBANI MOZAMILAPO

Onani mmene mungapangile zisankho zanu pa nkhani yokhudza magazi pa njila zothandizila odwala.

3. Pangani zisankho zokondweletsa Yehova pa cithandizo ca mankhwala

Pa cithandizo ca mankhwala cokhudza magazi, kodi mungapange bwanji cisankho cokondweletsa Mulungu? Tambani VIDIYO, kenako kambilanani funso ili. N’cifukwa ciyani n’kofunika kutenga masitepe otsatila aya?

VIDIYO: Kupanga Cisankho pa Cithandizo ca Cipatala Cofuna Magazi (5:​47)

  • Pemphelani kuti mupeze nzelu.​—Yakobo 1:5.

  • Fufuzani mfundo za m’Baibo na kuona mmene zingakuthandizileni pa nkhaniyo.​—Miyambo 13:16.

  • Pezani njila zina zimene zilipo zothandizila odwala kwanuko.

  • Pezaninso njila zothandizila odwala zoonekelatu kuti simungazivomeleze.

  • Onetsetsani kuti cisankho cimene mupange cikusiyeni na cikumbumtima coyela.​—Machitidwe 24:16.b

  • Dziŵani kuti palibe aliyense ayenela kukuuzani cisankho cimene muyenela kupanga pa nkhani yokhudza cikumbumtima. Kaya ni mnzanu wa mu ukwati, mkulu, kapena amene amakuphunzitsani Baibo.—Aroma 14:12.

  • Citani kulemba cisankho canu.

Zithunzi: Mwamuna uyu akupanga cisankho cokhudza cithandizo ca cipatala. 1. Akupemphela. 2. Akufufuza pogwilitsila nchito Baibo, zofalitsa zozikika m’Baibo, komanso pa tabuleti. 3. Akukambilana na dokotala wake.

4. Mboni za Yehova zimafuna cithandizo cabwino ca cipatala

N’zotheka ndithu kusunga lamulo la Mulungu lokhudza magazi, komanso n’kulandila cithandiza cabwino ca cipatala cosafuna magazi. Tambani VIDIYO.

VIDIYO: Zimene Ananena Pulofesa Massimo P. Franchi, M.D. (1:​36)

Ŵelengani Tito 3:​2, na kukambilana funso ili:

  • N’cifukwa ciyani tiyenela kukhala okambika komanso odzicepetsa pamene tikucita na madokotala?

Kagilasi ka kucipatala kolekanitsila magawo akulu-akulu anayi a magazi olembedwa A, B, C, na D.

Zosavomelezeka

Mkhristu apange yekha cisankho

A. Madzi acikasu a m’magazi (plasma).

Tumagawo twa madzi acikasu a m’magazi

B. Maselo Oyela (White cells).

Tumagawo twa maselo oyela

C. Maselo othandiza magazi kuundana (Platelets).

Tumagawo twa maselo othandiza magazi kuundana

D. Maselo ofiila (Red cells).

Tumagawo twa maselo ofiila

5. Pakafunikila tumagawo twa magazi

Magazi ali na magawo akulu-akulu anayi​—maselo ofiila (red cells), maselo oyela (white cells), maselo othandizila magazi kuundana (platelets), komanso madzi acikasu a m’magazi (plasma). Magawo a magazi amenewa alinso na tumagawo twake tung’ono-tung’ono.c Tumagawo tung’ono-tung’ono tumenetu amatugwilitsila nchito m’mankhwala pofuna kucilitsa matenda kapena pofuna kuleketsa kutaya magazi.

Kunena za tumagawo tung’ono-tung’ono twa magazi, Mkhristu aliyense ayenela kupanga cisankho cake malinga na cikumbumtima cake cophunzitsidwa Baibo. Akhristu ena angakane cithandizo ca cipatala cophatikizapo tumagawo tung’ono-tung’ono twa magazi. Koma ena cikumbumtima cawo cingawalole kulandila tumagawo tumeneto.

Popanga cisankho canu dzifunseni funso ili:

  • Kodi ningafotokoze bwanji kwa dokotala cifukwa cimene nikukanila kapena kuvomela tumagawo tung’ono-tung’ono twa magazi?

MUNTHU WINA ANGAFUNSE KUTI: “Kodi pali vuto lanji kuikidwa magazi kapena kupeleka magazi?”

  • Inu mungayankhe bwanji?

CIDULE CAKE

Yehova amafuna kuti tizipewa magazi.

Mafunso Obweleza

  • N’cifukwa ciyani kwa Yehova magazi ni cinthu copatulika?

  • Tidziŵa bwanji kuti lamulo la Mulungu la kupewa magazi limakhudzanso nkhani ya kuikidwa magazi?

  • Kodi mungapange bwanji cisankho cabwino pa cithandizo ca cipatala cophatikizapo magazi?

Colinga

FUFUZANI

Pa njila yothandizila odwala yofuna kugwilitsa nchito magazi anu, kodi ni mfundo ziti zingakuthandizeni kupanga zisankho zabwino?

“Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga” (Nsanja ya Mlonda, October 15, 2000)

Pofuna kuvomela kapena kukana tumagawo tung’ono-tung’ono twa magazi, kodi muyenela kuganizila mfundo ziti?

“Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga” (Nsanja ya Mlonda, June 15, 2004)

Kodi n’ciyani cinapangitsa dokotala wina kuvomeleza kuti kapenyedwe ka Yehova ka magazi n’komveka?

“N’navomeleza Mfundo ya Mulungu pa Nkhani ya Magazi” (Galamuka!, December 8, 2003)

Dziŵani mmene akulu otumikila pa makomiti olankhulana na cipatala amathandizila abale na alongo athu.

Yehova Amasamalila Odwala (10:23)

a Onani Phunzilo 35, “Mmene Tingapangile Zisankho Zabwino.”

b Onani mfundo 5 yakuti “Pakafunikila Tumagawo twa Magazi,” komanso Mfundo yakumapeto 3 yakuti “Njila Zothandizila Odwala Zofuna Magazi”; komanso Utumiki Wathu wa Ufumu wa November 2006, masamba 3-6.

c Madokotala ena amaona magawo akulu-akulu anayi aja a magazi kukhalanso tumagawo tung’ono-tung’ono. Conco, muyenela kufotokoza bwino cisankho canu ca kusalandila magazi athunthu kapena maselo ofiila (red cells), maselo oyela (white cells), maselo othandiza magazi kuundana (platelets), kapena madzi acikasu a m’magazi (plasma).

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani