NKHANI YA PACIKUTO: KODI MUYENELA KUKHULUPILILA CIPEMBEDZO?
Cifukwa Cake Muyenela Kucidziŵa Bwino Cipembedzo Canu
Tiyelekezele kuti muli ndi matenda aakulu ndipo mufunikila opaleshoni. Mudzafunikila kuonetsetsa kuti dokotala amene adzakucitani opaleshoni ndi wodalilika, cifukwa cakuti moyo wanu udzadalila zimene adzacita. Conco, kodi si kungakhale kwanzelu kufufuza bwino ngati amaidziŵadi nchito yake?
Mofananamo, ndi kwanzelu kucifufuza bwino cipembedzo canu. Ngati mumapita ku cipembedzo cina cake, umoyo wanu wa kuuzimu umadalila cipembedzo cimeneco. Ndipo kuti mukapulumuke, zidzadalilanso cipembedzo cimene mulimo.
Yesu anapeleka mfundo imene ingatithandize kufufuza bwino cipembedzo. Iye anati: “Mtengo uliwonse umadziŵika ndi cipatso cake.” (Luka 6:44) Mwacitsanzo, mukaganizila cipembedzo cina cake, kodi mumaona kuti cimabala zipatso zotani? Kodi atsogoleli a cipembedzo cimeneco amaonetsa kuti amakonda kwambili ndalama? Kodi anthu a m’cipembedzo cimeneco amatsatila mfundo za m’Baibo pankhani zokhudza nkhondo ndi makhalidwe? Nanga kodi pali cipembedzo cimene mungakhulupilile? Tikupemphani kuti muŵelenge nkhani zotsatila.
[Mau okopa papeji 3]
“Mtengo uliwonse umadziŵika ndi cipatso cake.”—Luka 6:44